Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumalola Yehova Kukufunsani Mafunso?

Kodi Mumalola Yehova Kukufunsani Mafunso?

Kodi Mumalola Yehova Kukufunsani Mafunso?

BAIBULO lili ndi mafunso ambiri amene angatithandize kudzifufuza. Ndipotu, Yehova Mulungu amagwiritsa ntchito mafunso pophunzitsa mfundo zofunikira za choonadi. Mwachitsanzo, Yehova anagwiritsa ntchito mafunso angapo pochenjeza Kaini kuti asinthe maganizo ake oipa. (Gen. 4:6, 7) Nthawi ina, Yehova ankafunsa funso limodzi chabe kuti lithandize munthu kuchitapo kanthu. Mneneri Yesaya atamva Yehova akufunsa kuti: “Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?” Iye anayankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.”​—Yes. 6:8.

Yesu, Mphunzitsi Waluso, nayenso ankafunsa mafunso mogwira mtima. M’Mauthenga Abwino muli mafunso a Yesu oposa 280. Ngakhale kuti nthawi zina ankagwiritsa ntchito mafunso kuyankha anthu om’tsutsa, nthawi zambiri cholinga chake pogwiritsa ntchito mafunso chinali kuwafika pamtima omvera ake, kuti aganizire mmene moyo wawo wauzimu ulili. (Mat. 22:41-46; Yoh. 14:9, 10) Mofananamo, mtumwi Paulo, yemwe analemba makalata 14 omwe ali mbali ya Malemba Achigiriki Achikristu, anagwiritsa ntchito mafunso pofuna kukopa chidwi cha anthu. (Aroma 10:13-15) Mwachitsanzo, m’kalata imene analembera Aroma muli mafunso ambiri. Mafunso a Paulo amathandiza anthu amene amawerenga kalata imeneyi kuti aphunzire ndi kuyamikira kuchuluka kwa chuma cha Mulungu ndi nzeru zake zozama, komanso kuti azindikire kuti kudziwa kwake zinthu n’kozama zedi.​—Aroma 11:33.

Mafunso ena amafunika kuyankhidwa nthawi yomweyo, koma ena cholinga chake ndi kuthandiza munthu kuganiza mwakuya. M’Mauthenga Abwino muli mafunso ambiri a Yesu othandiza anthu kuganizira mfundo. Nthawi ina, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Khalani maso, chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.” Iye ankatanthauza chinyengo ndi ziphunzitso zonyenga. (Maliko 8:15; Mat. 16:12) Ophunzira a Yesu sanadziwe zimene ankatanthauza ndipo iwo anayamba kukangana chifukwa choiwala kubweretsa mkate. Taonani mmene Yesu anagwiritsira ntchito mafunso pokambirana nawo mwachidule. Iye anawafunsa kuti: “Chifukwa chiyani mukukangana nkhani yosowa mikate? Kodi simukuzindikira ndi kumvetsa tanthauzo lake mpaka pano? Kodi mitima yanu ikali yosazindikira? ‘Ngakhale maso muli nawo, kodi simuona; ndipo ngakhale makutu muli nawo, kodi simumva?’ . . . Kodi simukumvetsabe tanthauzo lake?” Cholinga cha mafunso a Yesu amenewa, chinali kuthandiza ophunzira ake kuganiza n’kumvetsa tanthauzo la mawu ake.​—Maliko 8:16-21.

“Ndikufunsa”

Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito mafunso kukonza maganizo a mtumiki wake Yobu. Mwa kugwiritsa ntchito mafunso, Yehova anaphunzitsa Yobu kuona kuti anali wochepa kwambiri poyerekezera ndi Mlengi wake. (Yobu machaputala 38-41) Kodi Yehova ankafuna kuti Yobu ayankhe mafunso amenewa? Zikuoneka kuti sanafunikire kutero. Funso monga lakuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?” cholinga chake chinali kuthandiza Yobu kuganiza. Atafunsidwa mafunso amenewa, Yobu anasowa chonena. Iye anangoti: “Ndidzakubwezerani mawu otani? Ndigwira pakamwa.” (Yobu 38:4; 40:4) Yobu anaona mfundo yake ndipo anadzichepetsa. Koma Yehova sanaphunzitse Yobu kudzichepetsa kokha. Maganizo ake nawonso anakonzedwa. Kodi anakonzedwa motani?

Ngakhale kuti Yobu anali “munthu wangwiro ndi woongoka,” nthawi zina zonena zake zinkasonyeza kuti anali ndi maganizo olakwika. Elihu anaona zimenezi ndipo anadzudzula Yobu chifukwa “anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.” (Yobu 1:8; 32:2; 33:8-12) Motero, mafunso a Yehova anakonzanso mmene Yobu ankaonera zinthu. Polankhula kwa Yobu m’kavumvulu, Mulungu anati: “Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mawu opanda nzeru? Udzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziwitse.” (Yobu 38:1-3) Ndiyeno kudzera m’mafunso, Yehova anasonyeza nzeru ndi mphamvu zake zopanda malire zomwe zinaonekera m’ntchito zake zodabwitsa. Mfundo imeneyi inathandiza Yobu kuposa n’kale lonse kukhulupirira kwambiri chiweruzo cha Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu. Zinali zochititsa mantha kwambiri kwa Yobu, kufunsidwa mafunso ndi Mulungu Wamphamvuyonse.

Kodi Tingatani Kuti Yehova Azitifunsa Mafunso?

Ifenso tingapindule ndi mafunso olembedwa m’Baibulo. Tikamalola mafunso amenewa kutichititsa kuganiza, tidzapindula kwambiri mwauzimu. Mafunso okhudza mtima omwe ali m’Mawu a Mulungu, ndi zina mwa zinthu zimene zimachititsa Baibulo kukhala lothandiza kwambiri. Ndithudi, “mawu a Mulungu . . . ndi amphamvu. . . . Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheb. 4:12) Koma kuti tipindule kwambiri, tiyenera kuganizira mafunso amenewo, kuwaona kuti Yehova akutifunsa ifeyo. (Aroma 15:4) Tiyeni tione zitsanzo.

“Kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” (Gen. 18:25) Abulahamu anafunsa Yehova funso losafuna yankho limeneli pa nthawi imene Mulungu ankaweruza Sodomu ndi Gomora. Abulahamu anaona kuti zinali zosatheka kuti Yehova achite zinthu zosalungama mwa kuwononga anthu olungama ndi oipa. Funso la Abulahamu limasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri chilungamo cha Yehova.

Masiku ano, anthu ena angakhale ndi mtima wofuna kunena maganizo awo pa zinthu zokhudza ziweruzo za Yehova, monga amene kwenikweni adzapulumuka Armagedo kapena amene adzaukitsidwa. Koma m’malo molola maganizo amenewa kutisokoneza, tizikumbukira funso la Abulahamu. Tikamadziwa kuti Yehova ndi Atate wa kumwamba wokoma mtima ndiponso tikamakhulupirira kwambiri kuti ndi wachilungamo ndi chifundo, ngati mmene ankachitira Abulahamu, zidzatithandiza kwambiri. Tidzapewa kuwononga nthawi ndi mphamvu zathu pa zinthu monga kuda nkhawa kwambiri, mikangano yosapindulitsa ndiponso tidzapewa kukhala ndi maganizo okayikira amene angatilefule.

“Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” (Mat. 6:27) Polalikira khamu lalikulu lomwe linaphatikizapo ophunzira ake, Yesu anagwiritsa ntchito funso limeneli potsindika mfundo yakuti, iwo anafunika kuika moyo wawo m’manja mwa Yehova. Chifukwa choti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo loipali la zinthu, timakhala ndi nkhawa zambiri, koma kuganizira kwambiri zinthu zimene zikutidetsa nkhawa sikungatalikitse moyo wathu kapena kusintha moyo wathu kuti ukhale wabwinopo.

Tikakhala ndi nkhawa zokhudza moyo wathu kapena wa achibale athu, kukumbukira funso la Yesu kungatithandize kuona moyenera zinthu zimene zikutidetsa nkhawa. Funso limeneli lingatithandizenso kusiya kuda nkhawa kwambiri ndiponso kupewa maganizo osalimbikitsa omwe angatifooketse. Yesu anatitsimikizira kuti Atate wathu wa kumwamba amene amadyetsa mbalame ndi kuveka zomera zakuthengo, amadziwa bwino zimene timafunikira.​—Mat. 6:26-34.

“Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?” (Miy. 6:27) Machaputala 9 oyambirira a buku la Miyambo ali ndi nkhani zazifupi zosimbidwa ndi bambo yemwe akuuza mwana wake malangizo anzeru. Funso lomwe lili pamwambali likusonyeza mavuto amene munthu wachigololo angakhale nawo. (Miy. 6:29) Ngati tikuona kuti tikukopana ndi mkazi kapena mwamuna wina, kapena tili ndi chilakolako choipa pa nkhani yogonana, funso limeneli liyenera kutichenjeza. Funso limeneli lingatithandizenso pa nthawi iliyonse imene tikuyesedwa kuchita choipa. Likutsindika bwino mfundo ya m’Baibulo yakuti: ‘Mudzakolola zimene mwafesa.’​—Agal. 6:7.

“Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wapakhomo wa mnzako?” (Aroma 14:4) M’kalata yomwe analembera Aroma, Paulo anafotokozamo mavuto amene anali mumpingo woyambirira. Popeza Akhristu anali ndi zikhalidwe zosiyana, ena ankakonda kuweruza Akhristu anzawo pa zinthu zimene anasankha kuchita. Funso la Paulo linawakumbutsa kuti azilandirana wina ndi mnzake ndipo asiye kuweruzana chifukwa kuweruza ndi kwa Yehova.

N’chimodzimodzinso masiku ano, anthu a Yehova ali ndi zikhalidwe zosiyanasiyana. Koma Yehova watigwirizanitsa bwino kwambiri. Kodi timachita zinthu zolimbikitsa mgwirizano umenewu? Ngati timafulumira kutsutsa zochita za abale athu, ndi bwino kudzifunsa funso la Paulo lomwe lili pamwambali.

Mafunso Amatithandiza Kuti Tikhale ndi Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

Zitsanzo zochepa zimenezi, zikusonyeza mmene mafunso omwe ali m’Mawu a Mulungu angatithandizire kudzifufuza. Kuona nkhani yonse imene inachititsa kuti funsolo lifunsidwe, kungatithandize kuti tiligwiritse ntchito pamoyo wathu. Tikamawerenga Baibulo, tidzapeza mafunso ena othandiza kwambiri.​—Onani bokosi patsamba 14.

Kulola mafunso okhudza mtima opezeka m’Mawu a Mulungu kutifika pamtima kudzatithandiza kuti maganizo ndi mitima yathu ikhale yogwirizana ndi njira zolungama za Yehova. Yehova atamaliza kufunsa Yobu, iye ananena kuti: “Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso.” (Yobu 42:5) Ndithudi, Yobu anayamba kuona kuti Yehova ndi weniweni, zinali ngati akumuona ndi maso ake. Nthawi ina, wophunzira Yakobe anafotokoza zimenezi kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Tiyeni tiziyesetsa kulola mbali iliyonse ya Mawu a Mulungu, kuphatikizapo mafunso ake, kutithandiza kukula mwauzimu ndiponso ‘kuona’ bwino Yehova.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi kudzifunsa mafunso otsatirawa kungakuthandizeni bwanji kuona zinthu mmene Yehova amazionera?

▪ “ Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova?”​—1 Sam. 15:22.

▪ “ Kodi Iye wakuumba diso ndi wosapenya?”​—Sal. 94:9.

▪ Anthu akamafunafuna okha ulemerero, kodi umenewo ndi ulemererodi?​—Miy. 25:27.

▪ “ Uyenera kupsa mtima kodi?”​—Yona 4:4.

▪ “ Munthu angapindulenji ngati apata dziko lonse ndi kutaya moyo wake?”​—Mat. 16:26.

▪ “ Ndani adzatilekanitsa ndi chikondi cha Khristu?”​—Aroma 8:35.

▪ “ Uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira?”​—1 Akor. 4:7.

▪ “ Pali kuyanjana kwanji pakati pa kuwala ndi mdima?”​—2 Akor. 6:14.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi mafunso a Yehova anam’phunzitsa chiyani Yobu?