Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito ya Mzimu Woyera Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

Ntchito ya Mzimu Woyera Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

Ntchito ya Mzimu Woyera Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

“Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga . . . adzakula mmene ndinawatumizira.”​—YES. 55:11.

1. Kodi Yehova amasiyana bwanji ndi anthu pa nkhani yokwaniritsa zolinga zake?

MOSIYANA ndi anthu, Yehova sachita kukonzeratu mapulani omuthandiza kukwaniritsa zolinga zake. Tiyerekezere motere: Mwamuna ndi mkazi wake angafunitsitse kukhala ndi banja losangalala ndiponso kumanga nyumba yabwino. Kuti zimenezi zitheke, iwo angafunike kuchita khama komanso kukonza mapulani abwino. Komabe mapulani awowo angathe kusokonezeka ndi zinthu zina monga masoka achilengedwe, kuchotsedwa ntchito, matenda kapenanso imfa. Koma zimenezi n’zosiyana ndi Yehova chifukwa iye sangalephere kukwaniritsa cholinga chake.

2, 3. (a) Kodi cholinga cha Yehova chimaphatikizapo chiyani, ndipo iye anatani Adamu ndi Hava atachimwa? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuzindikira njira imene Yehova amakwaniritsira cholinga chake ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chakecho?

2 Kuti achite zimene akufuna, Yehova sanafunikire kukonza mapulani koma anangokhala ndi cholinga chomwe akufuna kudzakwaniritsa. (Aef. 3:11) Cholinga chimenechi chikuphatikizapo zimene anafuna kuchita pachiyambi, zokhudza anthu ndiponso dziko lapansi. Iye ankafuna kuti dziko lapansi likhale paradaiso mmene anthu angwiro angakhalemo kosatha mwamtendere ndiponso mosangalala. (Gen. 1:28) Adamu ndi Hava atachimwa, Yehova anachitapo kanthu ndipo anaonetsetsa kuti cholinga chake chisadzalephereke. (Werengani Genesis 3:15.) Yehova anakonza zoti mkazi wake wophiphiritsa adzabereke “mbewu” kapena kuti Mwana. Iye anakonzanso zoti Mwana ameneyu adzawononge Satana, yemwe anayambitsa mavuto, kenako n’kuthetsa mavuto onse amene Satanayo anayambitsa.​—Aheb. 2:14; 1 Yoh. 3:8.

3 Palibe chilichonse kumwamba kapena padziko lapansi, chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chake. (Yes. 46:9-11) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti akwaniritse cholinga chake. Mzimu woyera umenewu umachititsa kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwedi. (Yes. 55:10, 11) Tiyenera kuzindikira njira imene Mulungu amakwaniritsira cholinga chake ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chakecho. Zinthu zonse zimene tikuyembekezera zimadalira kukwaniritsidwa kwa cholinga chimenechi. Ndiponso n’zolimbikitsa kwambiri kuona mmene Yehova amagwiritsira ntchito mzimu woyera. Tiyeni tsopano tikambirane ntchito ya mzimu woyera pokwaniritsa cholinga cha Yehova m’nthawi yakale, panopo, ndiponso m’tsogolo.

Zimene Mzimu Woyera Unachita M’nthawi Yakale

4. Kodi Yehova anaulula bwanji pang’onopang’ono cholinga chake?

4 M’nthawi ya Baibulo, Yehova ankaulula pang’onopang’ono cholinga chake. Poyamba, Mbewu yolonjezedwa sinadziwike chifukwa inali “chinsinsi chopatulika.” (1 Akor. 2:7) Koma patapita zaka pafupifupi 2,000, Yehova anatchulanso za mbewu. (Werengani Genesis 12:7; 22:15-18.) Yehova anapatsa Abulahamu lonjezo lomwe lidzakwaniritsidwa pa anthu enanso. Mawu akuti “m’mbewu zako” anasonyeza bwino kuti Mbewuyo idzakhala munthu, mbadwa ya Abulahamu. N’zoonekeratu kuti Satana ankayang’anitsitsa mwachidwi pamene mfundo zokhudza cholinga chimenechi zinkadziwika. Mosakayikira, Mdani ameneyu ankafunitsitsa kuwononga kapena kusokoneza mzera wa mbadwa za Abulahamu kuti cholinga cha Mulungu chisakwaniritsidwe. Koma zimenezi sizikanatheka chifukwa mzimu wa Mulungu unali kugwira ntchito. Motani?

5, 6. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji mzimu wake kuteteza anthu amene anali m’mzera wobadwira Mbewu?

5 Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake kuteteza anthu amene anali m’mzera wobadwira Mbewu. Iye anauza Abramu (kapena kuti Abulahamu) kuti: “Ine ndine chikopa chako.” (Gen. 15:1) Mawu amenewa anali ndi tanthauzo lalikulu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika cha mu 1919 B.C.E., Abulahamu ndi Sara ali ku Gerari. Abimeleki, yemwe anali mfumu ya Gerari, sankadziwa kuti Sara ndi mkazi wa Abulahamu ndipo anam’tenga kuti akhale mkazi wake. Kodi Satana ndi amene ankayendetsa zinthu, iwo asakudziwa, n’cholinga choti alepheretse Sara kum’berekera mbewu Abulahamu? Baibulo silinena, koma zimene limatiuza n’zoti Yehova analowererapo. M’maloto, Yehova anachenjeza Abimeleki kuti asakhudze Sara.​—Gen. 20:1-18.

6 Si nthawi yokhayi imene Yehova anateteza Abulahamu ndi Sara. Yehova anapulumutsa Abulahamu ndi apabanja lake maulendo angapo. (Gen. 12:14-20; 14:13-20; 26:26-29) Motero, ponena za Abulahamu ndi mbadwa zake, wamasalmo anati: “[Yehova] sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa; ndi kuti musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.”​—Sal. 105:14, 15.

7. Kodi Yehova anateteza bwanji mtundu wa Isiraeli?

7 Kudzera mwa mzimu wake, Yehova anateteza mtundu wa Isiraeli wakale, ndipo mu mtundu umenewu ndi mmene Mbewu yolonjezedwa inabadwira. Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anapereka Chilamulo chake kwa Aisiraeli. Chilamulo chimenechi chinateteza kulambira koona komanso Ayuda kuti akhale oyera mwauzimu, mwa makhalidwe ndiponso kuti akhale aukhondo. (Eks. 31:18; 2 Akor. 3:3) M’nthawi ya Oweruza, mzimu wa Yehova unathandiza anthu ena kupulumutsa Aisiraeli kwa adani awo. (Ower. 3:9, 10) Kutatsala zaka zochepa kuti Yesu yemwe ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu abadwe, mzimu woyera uyenera kuti unagwiritsidwa ntchito kuteteza Yerusalemu, Betelehemu ndiponso kachisi. Zinthu zitatuzi, zinathandiza pa kukwaniritsidwa kwa maulosi onena za Yesu.

8. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mzimu woyera unkagwira ntchito pamoyo ndiponso utumiki wa Mwana wa Mulungu?

8 Mzimu woyera unkagwira ntchito mwachindunji pamoyo ndiponso utumiki wa Yesu. Pamene mzimu woyera unkagwira ntchito m’mimba mwa namwali Mariya, unachita chinthu chimene sichinachitikepo n’kale lonse. Unachititsa kuti mkazi wopanda ungwiro akhale ndi pakati n’kubereka Mwana wangwiro amene sanakhudzidwe ndi chilango cha imfa. (Luka 1:26-31, 34, 35) Kenako mzimu woyera unateteza Yesu ali wakhanda kuti asafe msanga. (Mat. 2:7, 8, 12, 13) Pamene Yesu anali ndi zaka 30, Mulungu anam’dzoza ndi mzimu woyera. Mwa kuchita zimenezi, anamuika kuti alowe ufumu wa Davide ndiponso anam’patsa ntchito yolalikira. (Luka 1:32, 33; 4:16-21) Mzimu woyera unathandiza Yesu kuchita zozizwitsa monga kuchiritsa odwala, kudyetsa makamu, ndiponso kuukitsa akufa. Zinthu zimenezi, zinkachitira chithunzi madalitso amene tikuwayembekezera mu ulamuliro wa Yesu.

9, 10. (a) Kodi mzimu woyera unkagwira ntchito bwanji pa ophunzira oyambirira a Yesu? (b) Kodi n’chiyani chinachitika m’nthawi ya atumwi chimene chinasonyeza kuti Yehova wayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopano pokwaniritsa cholinga chake?

9 Pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova anayamba kugwiritsa ntchito mzimu wake kudzoza anthu amene anali mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu. Ndipo ambiri mwa anthu amenewa sanali mbadwa za Abulahamu. (Aroma 8:15-17; Agal. 3:29) Mzimu woyera unkagwira ntchito pa ophunzira oyambirira a Yesu ndipo unkawathandiza kulalikira mwachangu ndiponso kuchita zozizwitsa. (Mac. 1:8; 2:1-4; 1 Akor. 12:7-11) Mphatso zozizwitsa za mzimu woyera zimene analandira, zinasonyeza kuti Yehova wayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopano pokwaniritsa cholinga chake. Yehova sanafunenso kuti anthu azimulambira pogwiritsa ntchito dongosolo limene anakhazikitsa kalekale lopita kukachisi yemwe anali ku Yerusalemu. Panthawiyi, iye anayamba kuyanja mpingo wachikhristu womwe unali utangoyamba kumene. Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito mpingo wa odzozedwa pokwaniritsa cholinga chake.

10 M’nthawi ya m’Baibulo, Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera m’njira zosiyanasiyana ndipo zina mwa njira zimenezi ndi kuteteza anthu, kuwapatsa mphamvu ndiponso kuwadzoza. Iye anachita zimenezi pofuna kutsimikizira kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwa. Nanga bwanji masiku ano? Kodi Yehova akugwiritsa ntchito bwanji mzimu wake pokwaniritsa cholinga chake? Tifunika kudziwa chifukwa tikufuna kuchita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera. Tiyeni tsopano tikambirane njira zinayi zimene Yehova akugwiritsa ntchito mzimu wake masiku ano.

Zimene Mzimu Woyera Ukuchita Masiku Ano

11. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti mzimu woyera umathandiza anthu a Mulungu kukhala oyera, ndipo tingasonyeze bwanji kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi mzimuwo?

11 Choyamba, mzimu woyera umathandiza anthu a Mulungu kukhala oyera. Anthu amene amatumikira Yehova mogwirizana ndi zimene amafuna, amenenso adzapindule ndi cholinga chake, ayenera kukhala oyera mwa makhalidwe. (Werengani 1 Akorinto 6:9-11.) Anthu ena amene akhala Akhristu oona, poyamba ankachita zinthu zoipa monga dama, chigololo, ndipo ankagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Zilakolako zimene zimabala uchimo zingakhale zozikika molimba. (Yak. 1:14, 15) Koma anthu amenewa ‘anasambitsidwa kukhala oyera,’ ndipo izi zimasonyeza kuti asintha moyo wawo kuti asangalatse Mulungu. Kodi n’chiyani chimathandiza munthu amene amakonda Mulungu kuti athe kupewa kuchita zinthu zoipa zimene amalakalaka? Lemba la 1 Akorinto 6:11, limanena kuti “mzimu wa Mulungu wathu” ndi umene umam’thandiza. Tikamakhala oyera mwa makhalidwe, timasonyeza kuti tikufuna mzimu wa Mulungu uzititsogolera.

12. (a) Malinga ndi masomphenya a Ezekieli, kodi Yehova amatsogolera bwanji gulu lake? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera?

12 Chachiwiri, Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kutsogolera gulu lake kuti liziyenda mmene akufunira. M’masomphenya a Ezekieli, mbali ya kumwamba ya gulu la Yehova imaimiridwa ndi galeta la kumwamba lomwe likuyenda mwamphamvu kuti likwaniritse cholinga cha Yehova. Kodi n’chiyani chimachititsa galetalo kuti lizipita komwe likupitako? Ndi mzimu woyera. (Ezek. 1:20, 21) Tisaiwale kuti gulu la Yehova lili ndi mbali ziwiri, mbali ya kumwamba ndiponso ya padziko lapansi. Ngati mbali ya kumwamba imatsogoleredwa ndi mzimu woyera, ndiye kuti n’chimodzimodzinso mbali ya padziko lapansi. Tikamamvera mokhulupirika malangizo ochokera ku mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu, timasonyeza kuti tikuyendera limodzi ndi galeta la kumwamba la Yehova, ndipo tikuchita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera.​—Aheb. 13:17.

13, 14. (a) Kodi ndani amapanga “m’badwo uwu” umene Yesu anatchula? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti mzimu woyera ukutithandiza kuti tizimvetsa mfundo za choonadi cha m’Baibulo. (Onani bokosi lakuti, “Kodi Mukuyendera Limodzi ndi Kusintha kwa Kamvedwe ka Choonadi?”)

13 Chachitatu, Yehova akugwiritsa ntchito mzimu woyera kuti atithandize kumvetsa mfundo za m’Baibulo. (Miy. 4:18) “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala akugwiritsa ntchito magazini ya Nsanja ya Olonda monga njira yaikulu yofotokozera pang’onopang’ono mfundo za choonadi. (Mat. 24:45) Mwachitsanzo, taganizirani zimene tadziwa pa mfundo yonena za anthu amene amapanga “m’badwo uwu” umene Yesu anatchula. (Werengani Mateyo 24:32-34.) Kodi Yesu ankatanthauza m’badwo uti? Nkhani yakuti: “Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?” inafotokoza kuti, Yesu sankanena za anthu oipa, koma ankatanthauza ophunzira ake, omwe posapita nthawi anadzozedwa ndi mzimu woyera. * Otsatira a Yesu a m’nthawi ya atumwi ndiponso a masiku ano, ndi amene anaona chizindikiro komanso kuzindikira tanthauzo lake loti Yesu “ali pafupi, inde pakhomo penipeni.”

14 Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife? Ngakhale kuti sitingadziwe zaka zenizeni za “m’badwo uwu,” ndi bwino kukumbukira zinthu zingapo zokhudza mawu oti “m’badwo.” Nthawi zambiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu okhala ndi moyo panthawi inayake, ndipo nthawi imeneyi sikhala yaitali kwambiri komanso imakhala ndi pothera. (Eks. 1:6) Ndiyeno, kodi tiyenera kuwamva bwanji mawu a Yesu onena za “m’badwo uwu”? Iye ayenera ankatanthauza kuti Akhristu odzozedwa amene anali ndi moyo nthawi imene chizindikiro chinayamba kuoneka mu 1914, adzakhala alipo pamene Akhristu odzozedwa ena amene adzaone chiyambi cha chisautso chachikulu azidzabadwa. M’badwo umenewu uli ndi pamene unayambira, ndiponso pamene udzathera. Kukwaniritsidwa kwa mbali zosiyanasiyana za chizindikiro kukusonyeza bwino kuti chisautso chachikulu chili pafupi. Mukamakhalabe maso ndiponso achangu, mumasonyeza kuti mukuyendera limodzi ndi kusintha kwa kamvedwe kathu ka choonadi. Mumasonyezanso kuti mukuchita zinthu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.​—Maliko 13:37.

15. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mzimu woyera ndi umene umatipatsa mphamvu kuti tilengeze uthenga wabwino?

15 Chachinayi, mzimu woyera umatithandiza kulengeza uthenga wabwino. (Mac. 1:8) N’chiyaninso china chimene chikanathandiza kuti uthenga wabwino uzilalikidwa padziko lonse? Tangoganizani, n’kutheka kuti inunso mwina chifukwa chochita manyazi kwambiri kapena mantha, nthawi ina munkaganiza kuti, ‘Sindingathe kulalikira kunyumba ndi nyumba.’ Koma panopo mumagwira nawo ntchito imeneyi mwachangu. * Mboni za Yehova zokhulupirika zambiri zapitirizabe kulalikira ngakhale zikuzunzidwa kapena kutsutsidwa. Mzimu woyera wa Mulungu wokha ndi umene ungatipatse mphamvu zothana ndi mavuto adzaoneni ndiponso kutithandiza kuchita zinthu zimene sitingathe kuchita ndi mphamvu zathu zokha. (Mika 3:8; Mat. 17:20) Mukamagwira nawo mokwanira ntchito yolalikira, mumasonyeza kuti mukugwirizana ndi mzimu.

Zimene Mzimu Woyera Udzachita M’tsogolo

16. N’chifukwa chiyani tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzateteza anthu ake pa nthawi ya chisautso chachikulu?

16 M’tsogolomu, Yehova adzagwiritsa ntchito mzimu wake woyera m’njira zochititsa chidwi kwambiri kuti akwaniritse cholinga chake. Taganizirani choyamba nkhani yoteteza. Monga taonera, Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake m’nthawi yakale kuteteza anthu paokha komanso mtundu wonse wa Isiraeli. Motero, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti adzagwiritsanso ntchito mzimu wake wa mphamvu umenewu kuteteza anthu ake pa nthawi ya chisautso chachikulu chimene chayandikira. Sitifunikira kumanena maganizo athu pa nkhani ya mmene Yehova adzatisamalire panthawi imeneyo. Koma tiyeni tiyembekezere zam’tsogolo molimba mtima, podziwa kuti anthu amene amakonda Yehova sadzaiwalika kwa iye ndipo mzimu woyera sudzalephera kuwathandiza.​—2 Mbiri 16:9; Sal. 139:7-12.

17. Kodi Yehova adzagwiritsa ntchito motani mzimu wake woyera m’dziko latsopano limene likubwerali?

17 Kodi Yehova adzagwiritsa ntchito motani mzimu wake woyera m’dziko latsopano limene likubwerali? Mzimu wake umenewu ndi umene udzagwiritsidwa ntchito polemba mipukutu yatsopano imene idzatsegulidwe pa nthawi imeneyo. (Chiv. 20:12) Kodi m’mipukutu imeneyi mudzakhala chiyani? Mosakayikira, mudzakhala malangizo a Yehova ofotokoza zimene tidzafunikira kuchita m’zaka 1,000. Kodi mumalakalaka kuti mudzaone zomwe zidzakhala mu mipukutu imeneyi? Tikuyembekezera mwachidwi dziko latsopano limeneli. Idzakhala nthawi yosangalatsa zedi, Yehova akadzagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kukwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu amene adzakhalapo.

18. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

18 Tisaiwale kuti cholinga cha Yehova chidzakwaniritsidwadi chifukwa akugwiritsa ntchito mzimu wake woyera, womwe ndi mphamvu yoposa mphamvu zonse m’chilengedwe. Cholinga chimenechi chimakukhudzani. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake ndipo tizichita zinthu mogwirizana ndi mzimuwo. (Luka 11:13) Tikatero, tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, mmene Yehova anafunira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Kuti mupeze chitsanzo cha munthu amene anathetsa manyazi ndipo anayamba kuchita utumiki mwa changu, onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, tsamba 19.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova anagwiritsa ntchito motani mzimu wake woyera m’nthawi ya m’Baibulo kuti akwaniritse cholinga chake?

• Kodi Yehova akugwiritsa ntchito motani mzimu wake masiku ano?

• Kodi Yehova adzagwiritsa ntchito bwanji mzimu wake m’tsogolo kuti akwaniritse cholinga chake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi Mukuyendera Limodzi Ndi Kusintha kwa Kamvedwe ka Choonadi?

Yehova akupitirizabe kuthandiza anthu ake kumvetsa bwino mfundo za choonadi cha m’Baibulo. Kodi ndi mfundo zotani zomwe zafotokozedwanso mu Nsanja ya Olonda?

▪ Kodi fanizo la Yesu la chofufumitsa limafotokoza phunziro labwino lotani lonena za kukula kwauzimu? (Mat. 13:33)​—July 15, 2008, masamba 19 ndi 20.

▪ Kodi kusankha Akhristu odzozedwa kunatha liti?​—May 1, 2007, masamba 30 ndi 31.

▪ Kodi kulambira Yehova “ndi mzimu” kumatanthauza chiyani? (Yoh. 4:24)​—July 15, 2002, tsamba 15.

▪ Kodi a khamu lalikulu akutumikira m’bwalo liti? (Chiv. 7:15)​—May 1, 2002, masamba 30 ndi 31.

▪ Kodi kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi kudzachitika liti? (Mat. 25:31-33)​—October 15, 1995, masamba 18 mpaka 28.