Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amuna, Kodi Mumagonjera Khristu Monga Mutu Wanu?

Amuna, Kodi Mumagonjera Khristu Monga Mutu Wanu?

Amuna, Kodi Mumagonjera Khristu Monga Mutu Wanu?

“Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.”​—1 AKOR. 11:3.

1. Perekani umboni wakuti Yehova ndi Mulungu wa dongosolo.

LEMBA la Chivumbulutso 4:11 limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Chifukwa chakuti analenga zonse, Yehova Mulungu ndi Mfumu yaikulu m’chilengedwe chonse ndipo ndi wolamulira wa zonse zimene analenga. Umboni wakuti Yehova “si Mulungu wa chisokonezo, koma wa mtendere,” umaoneka ndi mmene iye walinganizira angelo ake.​—1 Akor. 14:33; Yes. 6:1-3; Aheb. 12:22, 23.

2, 3. (a) Kodi poyambirira Yehova analenga ndani? (b) Kodi Mwana woyamba kubadwa ali ndi udindo wotani poyerekeza ndi Atate?

2 Zinthu zonse zisanalengedwe, Mulungu analiko yekhayekha kwa zaka zosawerengeka. Poyambirira penipeni, iye analenga munthu wauzimu wotchedwa “Mawu” chifukwa anali Wolankhulira Yehova. Zinthu zina zonse zinalengedwa pogwiritsa ntchito Mawuyo. Kenako iye anabwera padziko lapansi ngati munthu ndipo anatchedwa Yesu Khristu.​—Werengani Yohane 1:1-3, 14.

3 Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya udindo umene Mulungu ndiponso Mwana wake woyamba ali nawo? Polemba mouziridwa ndi Mulungu mtumwi Paulo anati: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Khristu amagonjera Atate monga mutu wake. Mfundo ya umutu ndiponso kugonjera n’zofunika kuti pakati pa angelo komanso anthu pakhale mtendere ndiponso kuti zinthu zizichitika mwadongosolo. Ngakhale Yesu amene “kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa,” amafunika kugonjera Mulungu yemwe ndi mutu wake.​—Akol. 1:16.

4, 5. Kodi Yesu ankaona bwanji udindo wake poyerekezera ndi wa Yehova?

4 Kodi Yesu anamva bwanji ndi mfundo yoti ayenera kugonjera Yehova ndiponso kubwera padziko lapansi? Malemba amati: ‘Khristu Yesu ngakhale kuti anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande. Sanatero ayi, koma anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo, nakhala wofanana ndi anthu. Kuposanso pamenepo, atakhala munthu, anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa, inde, imfa ya pa mtengo wozunzikirapo.’​—Afil. 2:5-8.

5 Nthawi zonse Yesu ankagonjera modzichepetsa chifuniro cha Atate wake. Iye anati: “Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha;  . . . ndipo chiweruzo chimene ndimapereka n’cholungama, chifukwa sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma ine.” (Yoh. 5:30) Pa nthawi ina iye ananenanso kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa [Atate] nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Chakumapeto kwa moyo wake padziko lapansi Yesu popemphera kwa Atate wake anati: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.” (Yoh. 17:4) N’zoonekeratu kuti Yesu ankazindikira ndiponso kuvomereza kuti Mulungu ndiye mutu wake.

Mwana Amapindula Chifukwa Chogonjera Atate

6. Kodi Yesu anasonyeza makhalidwe abwino ati?

6 Yesu ali padziko lapansi anasonyeza makhalidwe abwino ambiri. Khalidwe lina linali chikondi chachikulu chimene anasonyeza Atate wake. Iye anati: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Iye ankakondanso kwambiri anthu. (Werengani Mateyo 22:35-40.) Yesu anali wokoma mtima ndi wachifundo, osati wankhanza kapena wopondereza. Iye anati: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Anthu onse onga nkhosa amisinkhu yonse makamaka amene ankaponderezedwa anatsitsimulidwa ndi Yesu ndiponso uthenga wake wolimbikitsa.

7, 8. Malinga ndi Chilamulo, kodi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi sanayenere kutani, koma Yesu anamuthandiza bwanji mayiyu?

7 Taganizirani mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi. Kuyambira kale amuna ambiri amachitira nkhanza akazi. N’chimodzimodzinso ndi atsogoleri a zipembedzo mu nthawi ya Isiraeli. Koma Yesu ankalemekeza akazi. Umboni wa zimenezi, ndi mmene anachitira ndi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. Ochiritsa ambiri “anam’chititsa kumva zopweteka zambiri” ndipo iye anawononga chuma chake chonse kuti achire. Ngakhale kuti anayesetsa, “matendawo anangokulirakulira.” Malinga ndi Chilamulo, iye anali wodetsedwa ndipo aliyense amene akanamukhudza akanakhalanso wodetsedwa.​—Lev. 15:19, 25.

8 Mayiyu atamva kuti Yesu akuchiritsa odwala, iyenso anakhala nawo pagulu la anthu omwe anazungulira Yesu. Mumtima mwake ankati: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” Iye anagwiradi Yesu, ndipo nthawi yomweyo anachira. Yesu ankadziwa kuti mayiyu sanayenera kugwira malaya ake. Koma sanamukalipire. M’malomwake anamukomera mtima. Yesu ankadziwa mmene mayiyu anamvera pazaka zonse zimene ankadwala ndipo anazindikira kuti ankafuna thandizo. Mwachifundo anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”​—Maliko 5:25-34.

9. Kodi Yesu anatani ophunzira ake ataletsa ana kuti asabwere kwa iye?

9 Ngakhale ana ankakhala omasuka akakhala ndi Yesu. Panthawi ina anthu atabweretsa ana kwa Yesu, ophunzira ake anawakalipira poganiza kuti Yesu sangafune kuti ana amusokoneze. Koma umu si mmene Yesu ankaonera zinthu. Baibulo limati: “Ataona zimenezi Yesu anakwiya ndi kuwauza [ophunzira ake] kuti: “Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine; musawaletse iyayi, pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa onga amenewa.” Ndipo iye “anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuwaika manja.” Yesu sanali kungolola ana kubwera kwa iye, koma ankawalandiranso mwachikondi.​—Maliko 10:13-16.

10. Kodi Yesu anaphunzira kuti makhalidwe amene ankasonyeza?

10 Kodi Yesu anaphunzira kuti makhalidwe amene ankasonyeza ali padziko lapansi? Iye asanakhale munthu, anakhala ndi Atate wake wa kumwamba kwa nthawi yaitali zedi. Iye ankaona mmene ankachitira zinthu ndipo anatengera zimenezi. (Werengani Miyambo 8:22, 23, 30.) Ali kumwamba ankaona mmene Yehova ankachitira umutu wake mwachifundo pa zolengedwa zake zonse ndipo anatengera kwambiri zochita za Atate wake. Kodi Yesu akanatha kuchita zimenezi akanakhala kuti sanali wogonjera? Iye ankasangalala kugonjera Atate wake ndipo Yehova ankasangalalanso kukhala ndi Mwana wotereyu. Ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe ochititsa chidwi a Atate wake wa kumwamba. Ndi mwayi wapadera kugonjera Khristu yemwe ndi Wolamulira wa Ufumu wakumwamba amene Mulungu wamusankha.

Tsanzirani Makhalidwe a Khristu

11. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kutsanzira ndani? (b) Mumpingo wachikhristu, n’chifukwa chiyani makamaka amuna ayenera kuyesetsa kutsanzira Yesu?

11 Anthu onse mumpingo wachikhristu, makamaka amuna, ayenera kupitirizabe kuyesetsa kutsanzira makhalidwe a Khristu. Monga taonera kale, Baibulo limati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.” Khristu amatsanzira Mutu wake yemwe ndi Yehova Mulungu, choncho amuna achikhristu ayeneranso kutsanzira Khristu mutu wawo. Atakhala Mkhristu, mtumwi Paulo nayenso ankatsanzira Yesu. Iye analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.” (1 Akor. 11:1) Ndipo mtumwi Petulo anati: “Anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Pet. 2:21) Malangizo onena kuti tiyenera kutsanzira Khristu ndi ofunikanso makamaka kwa amuna pa chifukwa china. Iwo ndi amene amakhala akulu ndi atumiki othandiza. Popeza Yesu ankasangalala kutsanzira Yehova, amuna achikhristu nawonso ayenera kusangalala kutsanzira Khristu ndiponso makhalidwe ake.

12, 13. Kodi akulu ayenera kuchita zinthu motani ndi nkhosa zimene apatsidwa kuti aziyang’anire?

12 Akulu mumpingo wachikhristu ayenera kuyesetsa kukhala ngati Khristu. Petulo analangiza akulu kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse; osati mochita ufumu pa aja ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:1-3) Akulu sayenera kukhala opondereza kapena ankhanza. Potsanzira Khristu, ayenera kuyesetsa kukhala achikondi, achifundo, odzichepetsa ndiponso okoma mtima akamachita zinthu ndi nkhosa zimene apatsidwa kuti azisamalire.

13 Anthu amene akutsogolera mumpingo ndi opanda ungwiro ndipo nthawi zonse ayenera kukumbukira zimenezi. (Aroma 3:23) Choncho ayenera kuyesetsa kuphunzira za Yesu ndi kutsanzira chikondi chake. Ayenera kuganizira mmene Mulungu ndi Khristu amachitira zinthu ndi anthu n’kumatsanzira zimenezo. Petulo akutilangiza kuti: “Nonsenu khalani odzichepetsa kwa wina ndi mnzake, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo chake.”​—1 Pet. 5:5.

14. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani posonyeza kulemekeza ena?

14 Pochita zinthu ndi nkhosa za Mulungu akulu mumpingo afunika kusonyeza makhalidwe abwino. Lemba la Aroma 12:10 limati: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” Akulu ndi atumiki othandiza ayenera kulemekeza ena. Mofanana ndi Akhristu onse, amuna amenewa sayenera kuchita ‘kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndipo ayenera kuona ena kukhala owaposa.’ (Afil. 2:3) Oyang’anira ayenera kuona ena kukhala owaposa. Akamachita zimenezi, akulu amatsatira malangizo a Paulo akuti: “Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba, osati kumadzikondweretsa tokha. Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.”​—Aroma 15:1-3.

Kulemekeza Akazi

15. Kodi amuna ayenera kuchita zinthu motani ndi akazi awo?

15 Tsopano taganizirani malangizo a Petulo kwa amuna okwatira. Iye analemba kuti: “Inunso amuna pitirizani kukhala nawo [akazi anu] mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba.” (1 Pet. 3:7) Kupatsa ulemu munthu kumatanthauza kuona munthuyo kuti ndi wofunika. Motero mumaganizira zofuna ndiponso maganizo a munthuyo ndipo mumakhala ololera ngati mukuona kuti palibe vuto kuchita zimene wanena. Izi n’zimene mwamuna ayenera kuchitira mkazi wake.

16. Kodi ndi chenjezo lotani limene Mawu a Mulungu amapereka kwa amuna pa nkhani yolemekeza akazi awo?

16 Pouza amuna kuti azilemekeza akazi awo, Petulo anachenjeza kuti: “Kuti mapemphero anu asatsekerezedwe.” (1 Pet. 3:7) Zimenezi zikusonyeza kuti mmene mwamuna amachitira ndi mkazi wake ndi nkhani yaikulu kwa Yehova. Kulephera kulemekeza mkazi kungachititse kuti mapemphero a mwamunayo atsekerezedwe. Ndipotu mwachibadwa akazi ambiri samavutika kugonjera ngati amalemekezedwa ndi amuna awo.

17. Kodi mwamuna ayenera kukonda mkazi wake mpaka pati?

17 Pa nkhani ya kukonda mkazi, Mawu a Mulungu amati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. . . . Pakuti palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo,  . . . aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini.” (Aef. 5:28, 29, 33) Kodi amuna ayenera kukonda akazi awo mpaka pati? Paulo analemba kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Choncho mwamuna ayenera kukhala wokonzeka kufera mkazi wake ngati mmene Khristu anachitira pofera anthu ena. Mwamuna wachikhristu akamachita zinthu ndi mkazi wake mwachikondi, mwachifundo, momuganizira ndiponso mopanda dyera, mkaziyo savutika kugonjera umutu wake.

18. Kodi n’chiyani chingathandize amuna kukwaniritsa udindo wawo mu ukwati?

18 Kodi kulangiza amuna kuti azilemekeza akazi awo mwa njira imeneyi, n’kuwapempha kuchita zimene sangathe? Ayi. Yehova sangawapemphe kuchita zinthu zimene sangakwanitse. Ndiponso atumiki a Yehova onse ali ndi mwayi woti atha kulandira mzimu woyera wa Mulungu womwe ndi wamphamvu koposa m’chilengedwe chonse. Yesu anati: “Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Akamapemphera, amuna angapemphe Yehova kuti awapatse mzimu wake woyera kuti uwathandize pochita zinthu ndi ena kuphatikizapo akazi awo.​—Werengani Machitidwe 5:32.

19. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Ndithudi, amuna ali ndi udindo waukulu wophunzira kugonjera Khristu ndiponso kutsanzira umutu wake. Nanga bwanji akazi, makamaka okwatiwa? Nkhani yotsatira ifotokoza mmene ayenera kuonera udindo wawo m’makonzedwe a Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi makhalidwe ati a Yesu amene tiyenera kutsanzira?

• Kodi akulu ayenera kuchita zinthu motani ndi nkhosa?

• Kodi mwamuna ayenera kuchita zinthu motani ndi mkazi wake?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Tsanzirani Yesu mwa kulemekeza ena