Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Olimba Mwauzimu Mukamasamalira Wachibale Amene Akudwala

Khalanibe Olimba Mwauzimu Mukamasamalira Wachibale Amene Akudwala

Khalanibe Olimba Mwauzimu Mukamasamalira Wachibale Amene Akudwala

KIM, yemwe ndi wa Mboni, anam’peza ndi chotupa pafupi ndi fupa lamsana ndipo atamuyeza anam’pezanso ndi matenda a khansa. Mwamuna wake, Steve, anati: “Atam’panga opaleshoni n’kumuchotsa chotupacho, anam’patsa chithandizo cha matenda a khansa. * Thandizo limene analandiralo linachititsa kuti afooke kwambiri. Iye sankathanso kuyenda bwinobwino.”

Kodi mukuganiza kuti Steve anamva bwanji kuona mkazi wake wokondedwa akuvutika ndi matenda osautsa kwambiri amenewa? Mwina muli ndi wachibale amene akudwala matenda osachiritsika kapena akuvutika ndi ukalamba. (Mlal. 12:1-7) Ngati n’choncho, ndi bwino kudziwa kuti muyenera kudzisamalira kuti muthe kusamalira bwino wokondedwa wanu amene akudwalayo. Mukafooka mwauzimu, maganizo ndiponso thanzi lanu zimakhudzidwanso, choncho simungathe kusamalira wachibale amene akudwala. Kodi mungatani kuti mukhale wolimba mwauzimu mukamasamalira wachibale wanu amene akudwala kapena ndi wokalamba? Kodi pali chilichonse chimene anthu a mumpingo angachite posonyeza kuti akuganizira anthu amene akudwala?

Kodi Mungatani Kuti Muzichita Zonse Bwinobwino?

Kuti mukhalebe olimba mwauzimu ndiponso athanzi mukamasamalira wachibale amene akudwala, muyenera kusintha zinthu zina pa moyo wanu ndiponso kugawa bwino nthawi. Lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” Pa lembali, mawu akuti ‘kudzichepetsa’ akutanthauza kuzindikira zimene munthuwe sungathe kuchita. Kuti musamapanikizike kwambiri, muyenera kuonanso bwino ndandanda yanu yochitira zinthu ndiponso maudindo amene muli nawo.

Steve anasonyeza nzeru ndiponso kudzichepetsa mwa kuonanso zinthu zimene ankachita. Iye ankagwira ntchito yolembedwa, anali wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu, komanso anali woyang’anira utumiki mumpingo wa Mboni za Yehova ku Ireland. Analinso mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala ya kudera lawo. Steve anati: “Kim sankadandaula kuti ntchito zimenezi zinkapangitsa kuti ndisamapeze nthawi yokwanira yomusamalira. Koma ndinkadziwa kuti ndikudzipanikiza kwambiri.” Kodi Steve anatani? Iye anati: “Nditaganizira nkhaniyi ndiponso kupemphera, ndinaona kuti ndi bwino kusiya kutumikira monga wogwirizanitsa. Ndinapitiriza kutumikira monga mkulu, koma popeza ndinapatsa anthu ena maudindo ena amene ndinali nawo mumpingo, ndinkapeza nthawi yokwanira yosamalira Kim bwinobwino.”

Patapita nthawi, Kim anawongokera. Kenako, Steve ndi Kim anaonanso mmene zinthu zinalili pa moyo wawo, ndipo mothandizidwa ndi mkazi wake, Steve anayambiranso kusamalira maudindo ake mumpingo. Ndipo Steve anati: “Tonse tinaphunzira kuchita zinthu mogwirizana ndi thanzi lathu. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza. Ndikuyamikiranso mkazi wanga chifukwa chondithandiza popanda kudandaula ngakhale kuti ankadwala.”

Taganiziraninso zimene zinachitikira Jerry, yemwe ndi woyang’anira woyendayenda, ndiponso mkazi wake, Maria. Iwo anasintha zolinga zawo kuti asamalire makolo awo okalamba. Maria anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinali ndi cholinga chokatumikira kudziko lina ngati amishonale. Koma Jerry ndi mwana yekhayo m’banja mwawo, ndipo makolo ake anafunika kuwasamalira. Choncho, tinaganiza zokhala ku Ireland kuti tiziwasamalira. Zimenezi zinathandiza kuti tizitha kusamalira bambo a Jerry pa nthawi imene anagonekedwa kuchipatala mpaka pamene anamwalira. Ndipo tsopano timatha kulankhulana ndi amayi ake a Jerry tsiku lililonse, moti akafuna thandizo sizivuta chifukwa tili pafupi. Abale ndi alongo mumpingo umene mayi ake a Jerry amasonkhana atithandiza kwambiri, ndipo zimenezi zachititsa kuti tipitirizebe kugwira ntchito yoyendayenda.”

Mmene Anthu Ena Angathandizire

Pofotokoza zinthu zimene amasiye okalamba mumpingo angapatsidwe, mtumwi Paulo anati: “Ngati munthu sasamalira ake a iye mwini, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.” Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti ngati akufuna kuti zochita zawo zikhale ‘zokondweretsa Mulungu,’ ayenera kumathandiza makolo awo okalamba komanso agogo awo. (1 Tim. 5:4, 8) Koma anthu ena mumpingo nawonso ayenera kuthandizapo.

Taganiziraninso zimene zinachitikira Hakan ndi mkazi wake Inger, omwe ndi okalamba ndipo amakhala ku Sweden. Hakan anati: “Mkazi wanga atam’peza ndi matenda a khansa, tonse tinadabwa kwambiri. M’mbuyomu Inger anali wathanzi ndiponso wamphamvu. Koma tsopano tinkafunika kupita kuchipatala tsiku lililonse kuti akalandire thandizo ndipo mankhwala omwe ankamwa, ankayambitsanso mavuto ena. Pa nthawi imeneyi, Inger ankangokhala panyumba, ndipo ndinkafunika kukhala naye kuti ndizimusamalira.” Kodi anthu a mumpingo wa Hakan ndi Inger ankawathandiza bwanji?

Akulu mumpingo anakonza zoti banjali lizimvetsera misonkhano kudzera pa foni. Ndipo abale ndi alongo ankacheza nawo mwa kuwayendera ndiponso kuwaimbira mafoni. Ankawatumiziranso makalata ndi makadi. Hakan anati: “Tinkaona kuti Yehova ndiponso abale athu akutisamalira. Zimenezi zinathandiza kwambiri kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Zosangalatsa n’zoti Inger wachira, ndipo timathanso kufika pamisonkhano yampingo ku Nyumba ya Ufumu.” Abale ndi alongo mumpingo akamachita zimene angathe posamalira odwala ndi okalamba, amasonyeza kuti iwo ndi ‘mabwenzi amene amakonda nthawi zonse; ndiponso abale amene anabadwira kuti athandize pooneka tsoka.’​—Miy. 17:17.

Yehova Amayamikira Zimene Mukuchita

Kusamalira wachibale yemwe akudwala n’kovuta zedi. Koma Mfumu Davide anati: “Wodala iye amene asamalira wosauka.” Ena mwa anthu otere, ndi amene akufunikira thandizo chifukwa chakuti akudwala.​—Sal. 41:1.

N’chifukwa chiyani anthu amene akusamalira anthu amene akudwala ayenera kusangalala? Lemba la Miyambo 19:17 limati: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” Yehova Mulungu amachita chidwi kwambiri ndi atumiki ake okhulupirika amene akuvutika ndi matenda, ndipo amadalitsa anthu amene akuwasonyeza chikondi. Wamasalmo Davide anaimba kuti: ‘Yehova adzam’gwiriziza [munthu wotereyu] pa kama wodwalira; podwala iye akonza pogona pake.’ (Sal. 41:3) N’zosakayikitsa kuti ngati munthu, yemwe akusamalira mwachikondi munthu amene akudwala, atakumana ndi vuto linalake Yehova adzam’thandiza.

N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti Yehova Mulungu amaona ndiponso amasangalala tikamasamalira wachibale amene akudwala. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kumafunikira khama, Malemba amatitsimikizira kuti “nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.”​—Aheb. 13:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Maina asinthidwa.

[Zithunzi patsamba 18]

Khalanibe olimba mwauzimu ndipo muzilola ena kukuthandizani