Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Popeza Yehova amaletsa kulambira mafano, n’chifukwa chiyani sanalange Aroni atapanga fano la mwana wa ng’ombe?

Chaputala 32 cha Eksodo, chimafotokoza kuti Aroni anapanga fano la mwana wa ng’ombe. Mwa kuchita zimenezi, iye anaswa lamulo la Mulungu loletsa kulambira mafano. (Eks. 20:3-5) Zotsatira zake zinali zakuti ‘Yehova anakwiya kwambiri ndi Aroni ndipo anafuna kumuwononga; koma Mose anamupempherera Aroni nthawi yomweyo.’ (Deut. 9:19, 20) Kodi pemphero la Mose, yemwe anali wolungama, linagwira ntchito “mwamphamvu kwambiri” pa nkhani ya Aroni? (Yak. 5:16) Inde, chifukwa zikuoneka kuti Yehova anayankha pemphero la Mose ndipo pa chifukwa chimenechi komanso pa zifukwa zina ziwiri, sanalange Aroni.

Zikuoneka kuti chifukwa china chinali chakuti Aroni anali wokhulupirika kwa nthawi yaitali. Mose atapemphedwa kuti akaonekere pamaso pa Farao ndiponso kuti akatulutse Aisiraeli m’dziko la Iguputo, Yehova anasankha Aroni kuti apite ndi Mose kuti azikamuyankhulira. (Eks. 4:10-16) Anthu awiriwa anamvera ndipo anakaonekera pamaso pa mfumu ya Iguputo maulendo angapo ngakhale kuti Farao anali wouma khosi. Choncho pa nthawi imene anali ku Iguputo, Aroni anali atasonyeza kale kuti anali munthu wokhulupirika ndiponso wachangu potumikira Yehova.​—Eks. 4:21.

Taganiziraninso zimene zinachititsa kuti Aroni apange fano la mwana wa ng’ombe. Pa nthawiyi n’kuti Mose ali kuphiri la Sinai kwa masiku 40. Ndiyeno pamene anthu “anaona kuti Mose anachedwa kutsika m’phiri,” anamukakamiza Aroni kuti awapangire fano. Aroni anamvera zimenezi n’kupanga fano la mwana wa ng’ombe. (Eks. 32:1-6) Koma zimene Aroni anachita pambuyo pake, zimasonyeza kuti iye kwenikweni sanagwirizane ndi kulambira fano kumeneku. Zikuoneka kuti iye anachita zimenezi chifukwa chomukakamiza. Mwachitsanzo, Mose atawatsimikizira kuti kumeneku kunali kulambira mafano, ana a Levi onse kuphatikizapo Aroni anakhala ku mbali ya Yehova. Koma anthu 3,000 omwe anachititsa kuti mtunduwu ulambire fano anaphedwa.​—Eks. 32:25-29.

Kenako Mose anauza anthuwo kuti: “Mwachimwa kuchimwa kwakukulu.” (Eks. 32:30) Choncho si Aroni yekha amene anali ndi mlandu. Iye ndiponso anthu ena, anapindula ndi chifundo chachikulu cha Yehova.

Itatha nkhani yokhudza mwana wa ng’ombeyi, Yehova analamula kuti Aroni akhale mkulu wa ansembe. Mulungu anauza Mose kuti: ‘Uveke Aroni zovala zopatulikazo; ndi kum’dzoza, ndi kum’patula andichitire ine ntchito ya nsembe.’ (Eks. 40:12, 13) N’zoonekeratu kuti Yehova anakhululukira Aroni zimene analakwitsa. Aroni analibe mtima wofuna kupandukira Mulungu koma anali munthu wokhulupirika ndipo ankakonda kulambira koona.