Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musamvetse Chisoni Mzimu Woyera wa Yehova

Musamvetse Chisoni Mzimu Woyera wa Yehova

Musamvetse Chisoni Mzimu Woyera wa Yehova

“Musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu, umene mwaikidwa chisindikizo chake.”​—AEF. 4:30.

1. Kodi Yehova wachitira anthu ambiri chiyani ndipo anthuwo ayenera kutani?

YEHOVA wachitira anthu ambirimbiri m’dziko lamavutoli zinthu zapadera. Kudzera mwa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu, iye watsegula njira yothandiza anthu kuti amuyandikire. (Yoh. 6:44) Ngati munadzipereka kwa Mulungu ndipo mukuchita zinthu zogwirizana ndi kudzipereka kwanuko, ndiye kuti ndinu mmodzi mwa anthu amenewa. Popeza munabatizidwa m’dzina la mzimu woyera, khalidwe lanu liyenera kukhala logwirizana ndi mzimuwo.​—Mat. 28:19.

2. Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Anthu amene ‘tikufesera mzimufe,’ tiyenera kuvala umunthu watsopano. (Agal. 6:8; Aef. 4:17-24) Koma mtumwi Paulo anatipatsa malangizo ndiponso anatichenjeza kuti sitiyenera kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu. (Werengani Aefeso 4:25-32.) Tiyeni tsopano tikambirane bwinobwino malangizo a mtumwi Paulo amenewa. Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena za kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu? Kodi zingatheke bwanji kuti munthu wodzipereka kwa Yehova amvetse chisoni mzimu? Ndipo kodi tingapewe bwanji kumvetsa chisoni mzimu wa Yehova?

Zimene Paulo Ankatanthauza

3. Kodi mawu a pa Aefeso 4:30 amatanthauza chiyani?

3 Choyamba, onani mawu a Paulo opezeka pa Aefeso 4:30. Iye anati: “Musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu, umene mwaikidwa chisindikizo chake, cha patsiku limene mudzamasulidwa ndi dipo.” Paulo sanafune kuti Akhristu anzake awononge khalidwe lawo labwino ndiponso ubwenzi wawo ndi Mulungu. Mzimu woyera wa Yehova ndi umene unawathandiza ‘kuikidwa chisindikizo chake, cha patsiku limene adzamasulidwa ndi dipo.’ Mzimu woyera wa Mulungu unali, ndipo udakali chisindikizo kapena kuti “chikole cha zinthu za m’tsogolo” cha odzozedwa okhulupirika. (2 Akor. 1:22) Chisindikizochi chimasonyeza kuti iwo ndi chuma chapadera cha Mulungu ndipo adzalandira mphoto ya moyo wakumwamba. Anthu oikidwa chisindikizo alipo okwana 144,000.​—Chiv. 7:2-4.

4. N’chifukwa chiyani tifunika kupewa kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu?

4 Kumvetsa chisoni mzimu kungachititse kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu isiye kugwira ntchito pa moyo wa Mkhristu. Umboni wa zimenezi, ndi zimene Davide ananena atachimwa ndi Bateseba. Davide analapa n’kupempha Yehova kuti: “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere mzimu wanu woyera.” (Sal. 51:11) Odzozedwa amene amakhalabe ‘okhulupirika mpaka imfa,’ ndi amene adzalandire “kolona” wa moyo wosafa kumwamba. (Chiv. 2:10; 1 Akor. 15:53) Nawonso Akhristu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi amafunika mzimu woyera kuti azitumikirabe Mulungu ndi mtima wosagawanika ndiponso kuti akalandire mphatso ya moyo chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu. (Yoh. 3:36; Aroma 5:8; 6:23) Choncho, tonsefe tiyenera kupewa kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Yehova.

Kodi Mkhristu Angamvetse Chisoni Mzimu M’njira Ziti?

5, 6. Zingatheke bwanji kuti Mkhristu amvetse chisoni mzimu wa Yehova?

5 Popeza ndife Akhristu odzipereka, tingapewe kumvetsa chisoni mzimu. Tingathe kuchita zimenezi ngati ‘tipitirizabe kuyenda mwa mzimu’ chifukwa tikatero zilakolako za thupi sizingatigonjetse ndipo sitingakhale ndi makhalidwe oipa. (Agal. 5:16, 25, 26) Koma zimenezi zitha kusintha. Tingamvetse chisoni mzimu wa Mulungu mwa kutengeka pang’onopang’ono, mwina mosadziwa, n’kuyamba khalidwe loletsedwa m’Mawu ouziridwa ndi mzimu wa Mulungu.

6 Ngati tipitirizabe kuchita zinthu zosemphana ndi mzimu woyera, tingaumvetse chisoni ndipo tingamvetsenso chisoni Yehova yemwe ndi mwiniwake wa mzimuwo. Kukambirana lemba la Aefeso 4:25-32, kutithandiza kuona mmene tiyenera kuchitira zinthu ndiponso mmene tingapewere kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu.

Zimene Tingachite Kuti Tisamvetse Chisoni Mzimu Woyera

7, 8. N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula zoona?

7 Tizinena zoona. Pa Aefeso 4:25, Paulo analemba kuti: “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake, chifukwa ndife ziwalo kwa wina ndi mnzake.” Popeza ndife ogwirizana monga “ziwalo kwa wina ndi mnzake,” tifunika kupewa kuchita zinthu mwachiphamaso ndiponso kupusitsa Akhristu anzathu chifukwa kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi kuwanamiza. Munthu amene angamachitebe zimenezi, sangakhale pa ubwenzi ndi Mulungu.​—Werengani Miyambo 3:32.

8 Chinyengo chingasokoneze mgwirizano mumpingo. Choncho tiyenera kukhala ngati mneneri wokhulupirika Danieli amene mwa iye simunapezeke chinyengo. (Dan. 6:4) Ndipo tiyenera kukumbukira malangizo amene Paulo anauza Akhristu omwe ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. Iye anawauza kuti aliyense wa iwo ali mbali ya “thupi la Khristu” ndipo amadalirana. Choncho tifunika kukhalabe ogwirizana ndi odzozedwa okhulupirika a Yesu. (Aef. 4:11, 12) Ngati tili ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi m’Paradaiso, ifenso tifunika kulankhula zoona nthawi zonse. Zimenezi zidzathandiza kuti mgwirizano wa abale padziko lonse upitirire.

9. N’chifukwa chiyani tifunika kumvera malangizo opezeka pa Aefeso 4:26, 27?

9 Tifunika kutsutsa Mdyerekezi, osam’patsa mpata woti atiwononge mwauzimu. (Yak. 4:7) Mzimu woyera umatithandiza kutsutsa Satana. Mwachitsanzo, tingachite zimenezi mwa kupewa kukwiya mosadziletsa. Paulo analemba kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aef. 4:26, 27) Ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka, kupemphera cha mumtima nthawi yomweyo kungatithandize kukhala “wofatsa mtima” ndiponso wodziletsa m’malo mochita zinthu zimene zingamvetse chisoni mzimu wa Mulungu. (Miy. 17:27) Choncho, kuti tisapatse mpata Satana wotichititsa zinthu zoipa, tiyenera kupewa kukhalabe okwiya. (Sal. 37:8, 9) Njira imodzi imene ingatithandize kutsutsa Satana ndiyo kuthetsa mwamsanga kusiyana maganizo mogwirizana ndi malangizo a Yesu.​—Mat. 5:23, 24; 18:15-17.

10, 11. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuba kapena kuchita zinthu mosaona mtima?

10 Tisamakopeke ndi maganizo ofuna kuba kapena kuchita zinthu mosaona mtima. Pa nkhani ya kuba, Paulo analemba kuti: “Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbika, kugwira ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (Aef. 4:28) Ngati Mkhristu wobatizidwa angabe, ndiye kuti akunyozetsa dzina la Mulungu. (Miy. 30:7-9) Munthu sayenera kuba, ngakhale atakhala wosauka. Amene amakonda Mulungu ndiponso anthu anzawo, amadziwa kuti kuba n’kulakwa.​—Maliko 12:28-31.

11 Paulo sanangotchula zimene tiyenera kupewa koma ananenanso zoyenera kuchita. Tikamayenda mwa mzimu, tidzayesetsa kugwira ntchito molimbika kuti tisamalire banja lathu ndiponso kuti tikhale ndi “kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (1 Tim. 5:8) Yesu ndi atumwi ake anali ndi thumba la ndalama zothandizira osauka, koma Yudasi Isikarioti ankaba ndalamazo. (Yoh. 12:4-6) N’zoonekeratu kuti iye sanali kutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Ife amene timatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, timafuna “kuchita zinthu zonse moona mtima” ngati mmene Paulo ankachitira. (Aheb. 13:18) Motero, timapewa kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Yehova.

Njira Zina Zopewera Kumvetsa Chisoni Mzimu

12, 13. (a) Malinga ndi Aefeso 4:29, kodi ndi malankhulidwe ati amene tiyenera kupewa? (b) Kodi zolankhula zathu ziyenera kukhala zotani?

12 Tiyenera kusamala polankhula. Paulo anati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse omanga monga kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” (Aef. 4:29) Apanso mtumwi Paulo sanangotiuza zimene sitiyenera kuchita, koma akutiuzanso zimene tiyenera kuchita. Mzimu wa Mulungu ukamatitsogolera, udzatithandiza kulankhula mawu amene angakhale “omanga monga kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” Ndiponso tiyenera kupewa kulankhula ‘mawu owola.’ Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuwola,’ amafotokoza za chipatso, nsomba kapena nyama yowola. Tifunika kudana ndi nkhani zimene Yehova amaona kuti n’zoipa, ngati mmene timachitira ndi chipatso, nsomba kapena nyama yowola.

13 Zolankhula zathu zizikhala zoyenera, zabwino ndiponso ‘zokoleretsa ndi mchere.’ (Akol. 3:8-10; 4:6) Anthu azitha kuona kuti ndife osiyana akamva zolankhula zathu. Motero, tiyeni tizithandiza anthu ena mwa kulankhula mawu “omanga,” kapena kuti olimbikitsa. Ndipo tiyenera kumva monga wamasalmo yemwe anayimba kuti: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.”​—Sal. 19:14.

14. Malinga ndi Aefeso 4:30, 31, kodi tiyenera kupewa zinthu ziti?

14 Tiyenera kupewa kuwawidwa mtima, mkwiyo, mawu achipongwe ndiponso zoipa zonse. Paulo atachenjeza kuti sitiyenera kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu analemba kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aef. 4:30, 31) Popeza ndife opanda ungwiro, tonsefe tifunika kuyesetsa kuti tizidziletsa poganiza ndi pochita zinthu. Tikamalola zinthu monga ‘kuwawidwa mtima kwa njiru, kupsa mtima, ndiponso mkwiyo’ kuti zizitilamulira, tizimvetsa chisoni mzimu wa Mulungu. N’chimodzimodzinso tikamasungira zifukwa anthu amene atilakwira ndiponso tikamakana kuyanjananso ndi anthu amene anatilakwira. Tikangoyamba kunyalanyaza malangizo a m’Baibulo, tikhoza kukhala ndi makhalidwe amene angatichititse kuchimwira mzimu ndipo zotsatira zake zingakhale zoopsa.

15. Ngati wina watilakwira, kodi tiyenera kuchita chiyani?

15 Tifunika kukhala okoma mtima, achifundo ndiponso okhululukira ena. Paulo analemba kuti: “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aef. 4:32) Ngakhale titakhala kuti takhumudwa kwambiri ndi zimene wina watilakwira, tiyenera kukhululuka ngati mmene Mulungu amachitira. (Luka 11:4) Tiyerekeze kuti Mkhristu mnzathu watinenera zoipa. Ndiyeno pofuna kukonza zinthu, ifeyo tikupita kukakambirana naye. Iye akusonyeza kuti akumva chisoni ndi zimene anachitazo, ndipo akupempha kuti timukhululukire ndipo tikumukhululukiradi. Koma pali zinanso zimene tiyenera kuchita. Lemba la Levitiko 19:18 limati: “Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; ine ndine Yehova.”

Tifunika Kukhala Maso

16. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tifunika kusintha zinthu zina n’cholinga chakuti tisamvetse chisoni mzimu wa Yehova.

16 Ngakhale pamene tili patokha, tingayesedwe kuchita zinthu zosakondweretsa Mulungu. Mwachitsanzo, m’bale wina angakhale kuti amakonda kumvetsera nyimbo zokayikitsa. Kenako chikumbumtima chake chingayambe kumuvutitsa poona kuti akunyalanyaza malangizo a m’Baibulo opezeka m’mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Angapemphere kwa Yehova chifukwa cha vuto limeneli ndipo angakumbukire mawu a Paulo opezeka pa Aefeso 4:30. Chifukwa chofunitsitsa kupewa zinthu zimene zingamvetse chisoni mzimu wa Mulungu, iye watsimikiza kusiyiratu kumvetsera nyimbo zokayikitsa. Mosakayikira, Yehova angadalitse m’baleyu chifukwa cha mtima umenewu. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizionetsetsa kuti sitikumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu.

17. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitikhala maso ndiponso ngati tilibe chizolowezi chopemphera?

17 Popanda kukhala maso ndiponso kupemphera, tingayambe kuchita zinthu zoipa zimene zingamvetse chisoni mzimu. Popeza zipatso za mzimu woyera zimasonyeza makhalidwe amene Atate wathu wakumwamba ali nawo, kumvetsa chisoni mzimuwo n’chimodzimodzinso kumvetsa chisoni Yehova, ndipo sitingakonde kuchita zimenezi. (Aef. 4:30) M’nthawi ya Yesu, alembi achiyuda analakwa kwambiri ponena kuti Yesu ankachita zozizwitsa mwa mphamvu ya Satana. (Werengani Maliko 3:22-30.) Adani a Khristu amenewa ‘ananyoza mzimu woyera,’ ndipo mwakutero anachita tchimo losakhululukidwa. Tisalole kuti zimenezi zitichitikire.

18. Kodi tingadziwe bwanji kuti sitinachite tchimo losakhululukidwa?

18 Popeza sitikufuna m’pang’ono pomwe kuchita zinthu zimene zingatichititse tchimo losakhululukidwa, tifunika kukumbukira zimene Paulo ananena zoti sitiyenera kumvetsa chisoni mzimu. Bwanji ngati tachita tchimo lalikulu? Ngati talapa ndiponso tathandizidwa ndi akulu, tingakhulupirire kuti Mulungu watikhululukira ndiponso sitinachimwire mzimu woyera. Mulungu angatithandize kuti tisadzachitenso zinthu zilizonse zimene zingamvetse chisoni mzimu.

19, 20. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kupewa? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

19 Mulungu akugwiritsa ntchito mzimu wake woyera polimbikitsa chikondi, chimwemwe ndiponso mgwirizano pakati pa anthu ake. (Sal. 133:1-3) Choncho, sitiyenera kumvetsa chisoni mzimu mwa kupewa miseche kapena kulankhula zinthu zosonyeza kuti sitikulemekeza abusa amene anaikidwa ndi mzimu. (Mac. 20:28; Yuda 8) Koma tiyenera kuchita zinthu zimene zingathandize kuti anthu mumpingo azigwirizana ndiponso azilemekezana. Zoonadi, sitifunikira kuyambitsa timagulu pakati pa anthu a Mulungu. Paulo analemba kuti: “Ndikukudandaulirani abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula chinthu chimodzi, ndi kuti pasakhale magawano pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana bwino lomwe pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.”​—1 Akor. 1:10.

20 Yehova ndi wofunitsitsa ndipo angathe kutithandiza kupewa kumvetsa chisoni mzimu wake. Choncho, tiyeni tipitirize kupempha mzimu woyera ndiponso kuyesetsa kuti tisaumvetse chisoni. Tipitirizenso ‘kufesera mzimu’ ndipo tilole kuti uzititsogolera panopa ndiponso kosatha.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu kumatanthauza chiyani?

• Kodi munthu wodzipereka kwa Yehova angamvetse bwanji chisoni mzimu wa Mulungu?

• Kodi tingapewe bwanji kumvetsa chisoni mzimu woyera?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 30]

Muzithetsa mwamsanga kusiyana maganizo

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi zolankhula zanu zili ngati zipatso ziti?