Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Okalamba?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Okalamba?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Okalamba?

M’MPHEPETE mwa gombe la California ku America, muli umodzi mwa mitengo yomwe yajambulidwa kwambiri padziko lonse. Mtengo umenewu umatchedwa kuti Lone Cypress. Anthu amanena kuti mtengo umenewu watha zaka zoposa 250. Chifukwa chakuti mtengo wokongola umenewu umadziwika kuti ndi wopirira, anthu amausamalira m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kuti mtengowu usagwe anaumangirira zingwe ndipo patsinde lake anaikapo miyala.

Mtengo wa Lone Cypress ukutikumbutsa za Akhristu okalamba omwe tili nawo amene amasonyeza kwambiri mzimu wopirira. Njira ina imene amachitira zimenezi ndi mwa kulengeza uthenga wabwino. Mneneri Yoweli analosera kuti “akuluakulu” adzalengeza uthenga wa m’Baibulo. (Yow. 2:28-32; Mac. 2:16-21) Taganizirani maola ambiri amene okalamba amenewa amathera pothandiza ena ndi mtima wonse kuphunzira za ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ (Mat. 24:14) Ena mwa okalamba amenewa, omwe amalengeza Ufumu, apirira chizunzo ndi mavuto ena kwa zaka zambiri. Ngati mtengo wa Cypress umadziwika kuti ndi wopirira ndipo umalimbitsidwa ndi miyala ndiponso zingwe, kuli bwanji okalamba amene tili nawo? Tiyenera kuona zabwino zimene amachita ndiponso kuwalemekeza.

Kale Yehova Mulungu analamula anthu ake kuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” (Lev. 19:32) Masiku ano, m’gulu la atumiki a Yehova timapeza zitsanzo zabwino kwambiri za anthu okhulupirika omwe akhala ‘akuyenda ndi Mulungu’ kwa zaka zambiri. (Mika 6:8) Pamene akupitiriza kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba, imvi zawo zimakhaladi “korona wa ulemu.”​—Miy. 16:31.

Mtumwi Paulo analangiza Timoteyo yemwe anali wachinyamata kuti: “Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa.” Koma Timoteyo ankafunika ‘kuwadandaulira monga bambo wake’ ndipo ‘akazi achikulire monga amayi ake.’ (1 Tim. 5:1, 2) Mwakuchita zimenezi, Timoteyo akanasonyeza kuti ‘akugwadira’ aimvi. Ndiyetu n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti zolankhula zathu zizisonyeza kuti timalemekeza okalamba.

Lemba la Aroma 12:10 limati: “Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” Oyang’anira mumpingo ayenera kulemekeza Akhristu okalamba. Koma tonsefe tifunikanso kukhala patsogolo posonyezana ulemu wina ndi mnzake.

Koma anthu am’banja la okalamba ndi amene ali ndi udindo wapadera wosamalira makolo ndiponso agogo awo. Anthu amapeza njira zothandizira kuti mtengo wa Lone Cypress usaume, ndipo amachita zimenezi nthawi zonse. Ndithudi nafenso tifunika kupeza njira zoti tipitirize kulemekeza makolo athu okalamba ndiponso agogo athu. Mwachitsanzo, kumvetsera mwatcheru akamalankhula, kudzatithandiza kupewa kuchita zinthu zotikomera popanda kuganiza mmene zingawakhudzire.​—Miy. 23:22; 1 Tim. 5:4.

Yehova amaona kuti okalamba ndi anthu amtengo wapatali ndipo iye samawasiya. (Sal. 71:18) Ndipotu Yehova Mulungu amawalimbitsa kuti apitirizebe kumutumikira mokhulupirika. Choncho, ifenso tiyeni tipitirizebe kuthandiza ndiponso kulemekeza okalamba.

[Chithunzi patsamba 7]

Mtengo wa Lone Cypress umafunika kuusamalira, nawonso okalamba amafunika kuwalemekeza

[Mawu a Chithunzi]

American Spirit Images/​age fotostock