Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kuphunzitsa Luntha Lanu la Kuzindikira

Pitirizani Kuphunzitsa Luntha Lanu la Kuzindikira

Pitirizani Kuphunzitsa Luntha Lanu la Kuzindikira

ZIMAKHALA zosangalatsa kwambiri kuona katswiri wa masewera olimbitsa thupi akulumpha ndi kutembenuka mwaluso. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuphunzitsa luso lawo loganiza ngati mmene katswiri wa masewerayu amachitira.

M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anati: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima, aja amene pogwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira, aphunzitsa lunthalo [ngati katswiri wa masewera] kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.” (Aheb. 5:14) N’chifukwa chiyani Paulo analimbikitsa Akhristu achiheberi kuti aziphunzitsa luso lawo loganiza ngati mmene katswiri wa masewera amaphunzitsira thupi lake. Kodi tingaphunzitse bwanji luntha lathu la kuzindikira?

“Muyenera Kukhala Aphunzitsi”

Pofotokoza udindo wa Yesu monga “mkulu wa ansembe monga mwa unsembe wa Melekizedeki,” Paulo analemba kuti: “Kunena za iye, [Yesu] tili ndi zambiri zoti tinene, zovutanso kuzifotokoza, popeza mwakhala ogontha m’kumva kwanu. Pakuti, ngakhale muyenera kukhala aphunzitsi malinga ndi nthawi ino, mufunikanso wina woti akuphunzitseni kuyambira pachiyambi, mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu. Ndipo mwakhala monga ofunika mkaka, osati chakudya chotafuna.”​—Aheb. 5:10-12.

Zikuoneka kuti Akhristu achiyuda ena m’nthawi ya atumwi anali asanamvetse bwino nkhani zina, choncho analephera kupita patsogolo mwauzimu. Mwachitsanzo, zinali zovuta kuti avomereze kusintha kumene kunachitika pa nkhani ya Chilamulo ndi mdulidwe. (Mac. 15:1, 2, 27-29; Agal. 2:11-14; 6:12, 13) Ena ankaona kuti n’zovuta kusiya miyambo yokhudza Sabata ndiponso zimene ankachita chaka chilichonse pa Tsiku la Chitetezo. (Akol. 2:16, 17; Aheb. 9:1-14) Choncho Paulo anawalimbikitsa kuphunzitsa luntha lawo la kuzindikira kuti azitha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika ndipo anawauza kuti ‘ayesetse mwakhama kufika pa uchikulire.’ (Aheb. 6:1, 2) Malangizo akewa ayenera kuti anathandiza anthu ena kuonanso bwino mmene akugwiritsira ntchito luso lawo loganiza ndipo mwina zinawathandiza kupita patsogolo mwauzimu. Nanga bwanji ifeyo?

Phunzitsani Luntha Lanu la Kuzindikira

Kodi tingaphunzitse bwanji luntha lathu lakuzindikira kuti tikule mwauzimu? Paulo anati tingachite zimenezi mwa ‘kuligwiritsa ntchito.’ Mofanana ndi ochita masewera olimbitsa thupi amene amaphunzitsa matupi awo kuti azitha kulumpha ndi kutembenuka mwaluso, ifenso tiyenera kuphunzitsa luso lathu loganiza kuti tizitha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.

John Ratey, yemwe ndi katswiri wa matenda a maganizo pa sukulu ya zachipatala ya Harvard, ananena kuti: “Ubongo umagwira ntchito bwino mukamaugwiritsa ntchito kwambiri.” Mkulu wa za maphunziro okhudza ukalamba ndiponso moyo wa anthu, pa yunivesite ya George Washington dzina lake Gene Cohen, ananena kuti, “tikamagwiritsa ntchito kwambiri ubongo, umapanga minyewa ina yatsopano imene imachititsa kuti ubongo uzigwira ntchito mwachangu.”

Choncho ndi bwino kuti tiziphunzitsa luso lathu loganiza ndipo tiziwonjezera zimene timadziwa m’Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi, tidzakhala okonzeka kuchita ‘chifuniro cha Mulungu changwiro.’​—Aroma 12:1, 2.

Khalani ndi Mtima Wofuna “Chakudya Chotafuna”

Ngati tikufuna ‘kuyesetsa mwakhama kufika pa uchikulire,’ tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikupita patsogolo pa nkhani yomvetsa choonadi cha m’Baibulo? Kodi anthu ena amaona kuti ndine wachikulire mwauzimu?’ Mwana akakhala wakhanda, mayi amasangalala kumuyamwitsa mkaka ndiponso kumudyetsa zakudya za ana. Koma kodi mayi angamve bwanji ngati zaka zikupita mwanayo osafuna kudya chakudya cholimba? Nafenso timasangalala kuona munthu amene tikuphunzira naye Baibulo akupita patsogolo mpaka kufika podzipereka n’kubatizidwa. Kodi tingamve bwanji ngati munthuyo sakupitanso patsogolo pambuyo poti wabatizidwa? Kodi zimenezi sizingakhale zokhumudwitsa? (1 Akor. 3:1-4) Tikamaphunzira ndi munthu, timayembekezera kuti nayenso nthawi ina adzakhala mphunzitsi.

Kuti tigwiritse ntchito luntha lathu la kuzindikira pa nkhani zina, tifunika kusinkhasinkha ndiponso kuchita khama. (Sal. 1:1-3) Zinthu monga kuonera TV ndiponso zizolowezi zina sizifuna kuganiza kwenikweni. Sitiyenera kulola zinthu zimenezi kutilepheretsa kupeza nthawi yosinkhasinkha. Kuti tikulitse luso lathu la kuganiza, tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira Baibulo ndi mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Kuwonjezera pa pulogalamu yathu yowerenga Baibulo, ndi bwinonso kukhala ndi nthawi yochita Kulambira kwa Pabanja ndiponso kuphunzira mozama nkhani zina za m’Baibulo.

Jerónimo yemwe ndi woyang’anira woyendayenda ku Mexico anati amaphunzira magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ikangofika. Amapezanso nthawi yophunzira pamodzi ndi mkazi wake. Jerónimo anati: “Ine ndi mkazi wanga tili ndi chizolowezi chowerenga Baibulo limodzi tsiku lililonse ndipo timagwiritsa ntchito mabuku monga ‘Dziko Lokoma.’” Mkhristu wina dzina lake Ronald ananena kuti nthawi zonse amatsatira ndandanda ya kuwerenga Baibulo ya mpingo. Iye nthawi ndi nthawi amasankhanso nkhani zina zimene amafuna kuti aziphunzire mozama ndipo amazimaliza pambuyo pa nthawi yaitali. Ronald anati: “Zimenezi zimachititsa kuti ndikamaliza kuphunzira, ndizilakalaka tsiku lotsatira kuti ndidzaphunzirenso.”

Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakhala ndi nthawi yokwanira yophunzira ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu? Kodi tikuphunzitsa luso lathu loganiza kuti tizitha kusankha zochita mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba? (Miy. 2:1-7) Tiyeni tikhale ndi cholinga chokhala achikulire mwauzimu, odziwa zinthu ndiponso tipeze nzeru imene anthu amene aphunzitsa luntha lawo losiyanitsa choyenera ndi cholakwika amakhala nayo.

[Chithunzi patsamba 23]

Timaphunzitsa luntha lathu lakuzindikira mwa ‘kuligwiritsa ntchito’