Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchita Zinthu Zauzimu Kumatsitsimula

Kuchita Zinthu Zauzimu Kumatsitsimula

Kuchita Zinthu Zauzimu Kumatsitsimula

“Senzani goli langa . . .  ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu.”​—MAT. 11:29.

1. Kodi Mulungu anakonza zotani pa phiri la Sinai ndipo n’chifukwa chiyani?

PANGANO la Chilamulo limene linakhazikitsidwa pa phiri la Sinai, linalinso ndi dongosolo la Sabata. Kudzera mwa Mose, Yehova analamula mtundu wa Isiraeli kuti: “Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.” (Eks. 23:12) Choncho, Yehova ankawaganizira anthu ake amene ankatsatira Chilamulo, ndipo mwachikondi anakonza zoti pakhale tsiku loti azipumula n’cholinga chakuti ‘azitsitsimulidwa.’

2. Kodi kusunga Sabata kunathandiza bwanji Aisiraeli?

2 Kodi Sabata linali tsiku longosangalala? Ayi. Tsikuli linali lofunika kwambiri kwa Aisiraeli pa nkhani yolambira Yehova. Kusunga Sabata kunkathandiza kuti mitu ya mabanja izikhala ndi nthawi yophunzitsa mabanja awo ‘kuti asunge njira ya Yehova ndiponso kuchita chilungamo.’ (Gen. 18:19) Kunkaperekanso mwayi kwa mabanja ndiponso mabwenzi kuti asonkhane ndi kuganizira zimene Yehova wawachitira komanso kuti asangalale. (Yes. 58:13, 14) Chofunika kwambiri n’chakuti, Sabata linkasonyeza kuti mtsogolo, mu Ulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000, anthu adzapeza mpumulo weniweni. (Aroma 8:21) Koma bwanji masiku ano? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatsitsimule Akhristu oona, ndipo kodi zimenezi zingachitike bwanji?

Kucheza ndi Akhristu Anzanu Kumatsitsimula

3. Kodi Akhristu oyambirira ankalimbikitsana bwanji ndipo panali zotsatira zotani?

3 Mtumwi Paulo ananena kuti mpingo wachikhristu ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Tim. 3:15) Akhristu oyambirira ankathandizana mwa kulimbikitsana mwachikondi. (Aef. 4:11, 12, 16) Paulo ali ku Efeso analimbikitsidwa pamene anthu ena a mumpingo wa ku Korinto anamuyendera. Taganizirani mmene zinamukhudzira. Iye anati: “Ndikusangalala kuti Sitefana ndi Fotunato ndi Akayiko ali kuno ndi ine, . . .  Pakuti atsitsimutsa mtima wanga.” (1 Akor. 16:17, 18) Pamenenso Tito anapita ku Korinto kukatumikira abale kumeneko, Paulo analembera mpingowo kuti: “Mtima wake watsitsimutsidwa ndi nonsenu.” (2 Akor. 7:13) Masiku anonso, Mboni za Yehova zimatsitsimulidwa chifukwa cholimbikitsana ndi Akhristu anzawo.

4. Kodi misonkhano ya mpingo imatilimbikitsa bwanji?

4 Inunso mukudziwa kuti misonkhano imatithandiza kukhala osangalala. Ku misonkhano ‘timalimbikitsana mwa chikhulupiriro cha wina ndi mnzake.’ (Aroma 1:12) Abale ndi alongo anthu achikhristu si anthu wamba amene timangokumana nawo kawirikawiri. Iwo ndi mabwenzi enieni ndipo timawakonda komanso timawalemekeza. Tikamasonkhana nawo timasangalala kwambiri ndiponso timalimbikitsidwa.​—File. 7.

5. Kodi tingatani kuti tizitsitsimulana pa misonkhano yachigawo ndi yadera?

5 Timatsitsimulidwanso pa misonkhano yachigawo ndi yadera imene imachitika chaka ndi chaka. Misonkhano imeneyi imatipatsa madzi opatsa moyo a choonadi cha m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Imatipatsanso mipata ‘yofutukula mitima yathu’ kapena kuti kudziwana ndi anthu ambiri. (2 Akor. 6:12, 13) Koma bwanji ngati ndife amanyazi ndipo zimativuta kucheza ndi anthu? Njira imodzi imene ingatithandize kudziwana ndi abale ndi alongo athu ndiyo kudzipereka kuti tigwire nawo ntchito pa misonkhano. Mlongo wina atagwira nawo ntchito pa msonkhano wa mayiko ananena kuti: “Sindinkadziwa anthu ambiri pa msonkhanopo kupatulapo abale anga ndi anzanga ochepa basi. Koma nditagwira nawo ntchito yoyeretsa ndinadziwana ndi abale ndi alongo ambiri. Zimenezi zinali zosangalatsa kwambiri.”

6. Kodi tingatani kuti titsitsimulidwe tikakhala pa tchuthi?

6 Aisiraeli ankapita ku Yerusalemu katatu pachaka kukachita zikondwerero zokhudza kulambira. (Eks. 34:23) Zimenezi zikutanthauza kuti ankasiya minda ndi mabizinesi awo n’kuyenda wapansi masiku angapo m’misewu yafumbi. Komabe kupita kukachisi kunkawapatsa “chimwemwe chachikulu” akaona anthu ‘akulemekeza Yehova.’ (2 Mbiri 30:21) Masiku anonso atumiki a Yehova amasangalala kwambiri akapita ndi mabanja awo kukaona malo ku Beteli, amene ndi maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Kodi inunso mungapeze nthawi yopita ndi banja lanu kumalo amenewa?

7. (a) Kodi nthawi yocheza imathandiza bwanji? (b) Kodi tingatani kuti nthawi yocheza ikhale yosangalatsa ndiponso yolimbikitsa?

7 Kupeza nthawi yocheza ndi banja lathu komanso mabwenzi athu kumalimbikitsanso. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake?” (Mlal. 2:24) Nthawi yocheza imathandiza kuti titsitsimulidwe ndiponso kuti tizikondana kwambiri ndi Akhristu anzathu, chifukwa timadziwana nawo bwino. Kuti nthawiyi ikhale yosangalatsa kwambiri komanso yolimbikitsa, ndi bwino kuti pazikhala anthu ochepa otheka kuwayang’anira, makamaka ngati pali mowa.

Kugwira Nawo Ntchito Yolalikira Kumatsitsimula

8, 9. (a) Fotokozani kusiyana pakati pa uthenga wa Yesu ndi wa alembi ndi Afarisi. (b) Kodi timapindula bwanji tikamauza ena choonadi cha m’Baibulo?

8 Yesu ankalalikira mwakhama ndipo analimbikitsa ophunzira ake kuchita chimodzimodzi. Umboni wa zimenezi ndi mawu ake akuti: “Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Uthenga umene Yesu ankaphunzitsa unali wotsitsimula ndipo unalidi “uthenga wabwino.” (Mat. 4:23; 24:14) Uthengawu unali wosiyana kwambiri ndi malamulo olemetsa amene Afarisi ankauza anthu kuti azitsatira.​—Werengani Mateyo 23:4, 23, 24.

9 Tikamauza anthu uthenga wa Ufumu timawatsitsimula mwauzimu ndipo ifenso timamvetsa bwino ndiponso kuyamikira choonadi chamtengo wapatali cha m’Baibulo. M’pake kuti wamasalmo ananena kuti: “Haleluya; pakuti kuimbira zom’lemekeza Mulungu wathu n’kokoma; pakuti chikondweretsa ichi.” (Sal. 147:1) Inunso mukhoza kupeza chimwemwe potamanda Yehova mwa kulalikira kwa anzanu.

10. Kodi zimene anthu amachita akamva uthenga wabwino n’zimene zimasonyeza kuti utumiki wathu ukuyenda bwino kapena ayi? Fotokozani.

10 M’madera ena anthu amachita chidwi kwambiri ndi uthenga wabwino kusiyana ndi m’madera ena. (Werengani Machitidwe 18:1, 5-8.) Ngati mukukhala m’dera limene anthu sachita chidwi kwenikweni ndi uthenga wa Ufumu, muziganizira kwambiri ubwino wa ntchito imene mukugwira. Kumbukirani kuti khama limene mumachita polengeza za dzina la Yehova silipita pachabe. (1 Akor. 15:58) Ndipotu zimene anthu amachita akamva uthenga wabwino si chizindikiro chakuti utumiki wathu ukuyenda bwino kapena ayi. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzaonetsetsa kuti anthu a mitima yabwino amvetsera uthenga wa Ufumu.​—Yoh. 6:44.

Kulambira kwa Pabanja Kumatsitsimula

11. Kodi Yehova wapereka udindo wotani kwa makolo, ndipo makolo angakwaniritse bwanji udindo umenewu?

11 Makolo oopa Mulungu ali ndi udindo wophunzitsa ana awo za Yehova ndi njira zake. (Deut. 11:18, 19) Ngati ndinu kholo, kodi mumapatula nthawi yophunzitsa ana anu za Atate wathu wakumwamba amene amatikonda? Pofuna kukuthandizani kuti mukwaniritse udindo wofunika kwambiri umenewu, Yehova wapereka chakudya chauzimu chochuluka kudzera m’mabuku, magazini, mavidiyo ndiponso ma CD ndi matepi.

12, 13. (a) Kodi mabanja angatani kuti azipindula ndi Kulambira kwa Pabanja? (b) Kodi makolo angatani kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kotsitsimula?

12 Kuwonjezera pamenepo, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakonzanso zoti mabanja azikhala ndi Kulambira kwa Pabanja. Imeneyi ndi nthawi imene banja limaphunzira Baibulo mlungu uliwonse. Anthu ambiri aona kuti kuphunzira monga banja kwawathandiza kuti azigwirizana ndiponso kukondana kwambiri. Kwawathandizanso kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Koma kodi makolo angatani kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kotsitsimula mwauzimu?

13 Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja iyenera kukhala yosangalatsa osati yotopetsa. Iyenera kukhala nthawi yosangalatsa chifukwa chakuti timalambira “Mulungu wa chisangalalo,” ndipo iye amafuna kuti tizimulambira mosangalala. (1 Tim. 1:11; Afil. 4:4) Kupeza nthawi yokambirana mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo ndi dalitso lalikulu. Makolo ayenera kusintha njira zawo zophunzitsira ndipo ayenera kudziwa bwino ana awo komanso kuyesetsa kuwaphunzitsa mwaluso. Mwachitsanzo, banja lina linauza mwana wawo wa zaka 10 dzina lake Brandon, kuti adzafotokoze nkhani ya mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani m’Baibulo Satana Amatchedwa Njoka?” Nkhani imeneyi inkamuvutitsa maganizo Brandon. Iye amakonda njoka, ndiye sankamvetsa kuti n’chifukwa chiyani Baibulo limati Satana ndi njoka. Mabanja ena nthawi zina amachita masewero a nkhani za m’Baibulo. Iwo amagawana kuti aliyense akhale munthu winawake wa m’Baibulo ndipo amawerenga mawu a munthuyo. Nthawi zina amachita sewero la zochitika zina za m’Baibulo. Kuphunzira mwa njira imeneyi kumakhala kosangalatsa ndipo kumachititsa kuti mwana aliyense akhale ndi zochita pa phunzirolo komanso zimathandiza kuti mfundo za m’Baibulo ziwafike pamtima anawo. *

Pewani Zinthu Zimene Zingakulemetseni

14, 15. (a) Kodi zinthu zodetsa nkhawa ndiponso zochititsa mantha zawonjezeka bwanji m’masiku otsiriza ano? (b) Kodi ndi mavuto ena ati amene Akhristufe timakumana nawo?

14 Zinthu zodetsa nkhawa komanso zochititsa mantha zikuwonjezeka kwambiri m’masiku otsiriza a dongosolo loipa lino. Anthu ambiri ali paulova ndipo akukumana ndi mavuto a zachuma. Ngakhale anthu amene ali pantchito amaona kuti ndalama zimene amalandira zimangofikira m’matumba obowoka ndipo izi zimachititsa kuti mabanja awo azivutika. (Yerekezerani ndi Hagai 1:4-6.) Nawonso andale ndi atsogoleri ena akulephera kuthetsa uchigawenga ndi mavuto ena. Palinso anthu ambiri amene akuvutika chifukwa cha zolakwa zawo.​—Sal. 38:4.

15 Nawonso Akhristu oona amakumana ndi mavuto a m’dongosolo la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Nthawi zina, ophunzira a Khristu amakumananso ndi mavuto ena pamene akuyesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Yesu anati: “Ngati anazunza ine, adzakuzunzani inunso.” (Yoh. 15:20) Komabe pamene ‘tikuzunzidwa sitisowa kolowera.’ (2 Akor. 4:9) N’chifukwa chiyani zili choncho?

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe osangalala?

16 Yesu anati: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mat. 11:28) Tikamakhulupirira ndi mtima wonse dipo la Khristu, timakhala tikulola Yehova kuti atisamalire. Mwa njira imeneyi timapeza “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Mzimu woyera womwe ndi “mthandizi” umalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti tithe kupirira mavuto amene timakumana nawo, komanso kuti tikhalebe osangalala.​—Yoh. 14:26; Yak. 1:2-4.

17, 18. (a) Kodi tiyenera kusamala ndi mzimu uti? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati tiika maganizo athu onse pa zinthu zakuthupi?

17 Masiku ano, Akhristu oona ayenera kusamala kuti asamayendere mzimu wa dzikoli wongofuna kudzisangalatsa. (Werengani Aefeso 2:2-5.) Ngati sitingachite zimenezi, tikhoza kukodwa mumsampha wa “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Kapena tikhoza kumaganiza molakwa kuti kutsatira zilakolako za thupi kungachititse kuti tikhale osangalala. (Aroma 8:6) Mwachitsanzo, anthu ena amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, amaledzera, amaonera zolaula, amachita masewera oika moyo pachiswe ndiponso amachita zinthu zina zoipa pongofuna kusangalala. Cholinga cha “machenjera” a Satana, ndi kusocheretsa anthu mwa kuwachititsa kukhala ndi maganizo olakwika pa zinthu zosangalatsa.​—Aef. 6:11.

18 Kunena zoona, palibe cholakwika ndi kudya, kumwa ndiponso kusangalala ndi zinthu zabwino koma modziletsa. Komabe sitiyenera kulola kuti zinthu zimenezi zikhale zofunika kwambiri pa moyo wathu. Chifukwa cha nthawi imene tikukhalayi, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru ndiponso modziletsa. Zofuna za mtima wathu zingatilemetse kwambiri moti tikhoza kukhala “ozirala kapena osabala zipatso pa kum’dziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.”​—2 Pet. 1:8.

19, 20. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti titsitsimulidwedi?

19 Tikamaona zinthu ngati mmene Yehova amazionera tidzazindikira kuti chilichonse chimene dzikoli lingapereke ndi chakanthawi. Mose ankadziwa zimenezi ndipo ife tiyenera kuteronso. (Aheb. 11:25) Zoona zake n’zakuti, kuchita chifuniro cha Atate wathu wakumwamba n’kumene kumatitsitsimuladi chifukwa kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo chodzasangalala mpaka kalekale.​—Mat. 5:6.

20 Choncho tiyeni tipitirizebe kuchita zinthu zauzimu chifukwa n’zimene zimatitsitsimula. Tikamachita zimenezi timakana “moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko . . . pamene tikuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chosangalatsa ndi kuonetsedwa kwa ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu.” (Tito 2:12, 13) Motero tiyeni titsimikize mtima kupitirizabe kusenza goli la Yesu ndipo tizichita zimenezi pomvera ndiponso kutsatira malangizo ake. Tikamachita zimenezi tidzakhaladi osangalala ndipo tidzatsitsimulidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene phunziro la banja lingakhalire losangalatsa ndiponso lothandiza, onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2002, tsamba 1.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatsitsimula anthu a Yehova masiku ano?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira imatsitsimula ifeyo ndiponso anthu amene tikuwalalikira?

• Kodi mitu ya mabanja ingatani kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kotsitsimula?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilemetse mwauzimu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 26]

Timatsitsimulidwa m’njira zambiri tikasenza goli la Yesu