Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzilimbikitsana Mumpingo

Muzilimbikitsana Mumpingo

Muzilimbikitsana Mumpingo

“Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake.”​—1 ATES. 5:11.

1. Kodi tapeza madalitso ati chifukwa chokhala mumpingo wachikhristu, nanga ndi mavuto ati amene timakumana nawo?

NDI mwayi waukulu kukhala mumpingo wachikhristu. Mwachitsanzo, muli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Chifukwa chakuti mumadalira Mawu a Mulungu kuti azikutsogolerani, mumatetezeka ku zotsatira zakuchita zinthu zoipa zimene anthu amene si Akhristu amakumana nazo. Muli ndi mabwenzi enieni ambiri omwe amakufunirani zabwino. Choncho, tingati mwadalitsidwa m’njira zambiri. Komabe Akhristu ambiri akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ena afunika kuthandizidwa kuti amvetse bwino zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu. Ena akudwala kapena kuvutika maganizo ndipo pali ena amene akuvutika chifukwa chakuti nthawi ina anasankha zinthu molakwika. Ndipo tonsefe tikukhala m’dziko la anthu osaopa Mulungu.

2. Kodi tiyenera kutani ngati abale athu akukumana ndi mavuto, ndipo n’chifukwa chiyani?

2 Palibe amene amasangalala kuona Mkhristu mnzake akuvutika. Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo ndi thupi la munthu ndipo anati, “chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutika limodzi nacho.” (1 Akor. 12:12, 26) Izi zikachitika tiyenera kuyesetsa kuthandiza abale ndi alongo athu. Pali nkhani zambiri m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti anthu anathandiza anzawo amene anali ndi mavuto mumpingo. Pamene tikukambirana nkhani zimenezi, onani mmene inunso mungathandizire anthu amene akuvutika. Kodi mungathandize bwanji mwauzimu abale anu kuti mulimbikitse mpingo wa Yehova?

“Anam’tenga”

3, 4. Kodi Akula ndi Purisikila anamuthandiza bwanji Apolo?

3 Pa nthawi imene Apolo ankakhala ku Efeso n’kuti ali kale mlaliki wachangu. Buku la Machitidwe limati, Apolo anali ‘wotentha ndi mzimu, ndipo anali kulankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma iye anali kudziwa za ubatizo wa Yohane wokha basi.’ Popeza Apolo sankadziwa za kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera,” ndiye kuti mwina iye anaphunzitsidwa ndi ophunzira a Yohane M’batizi, apo ayi anaphunzitsidwa ndi otsatira a Yesu pasanafike pa Pentekosite 33  C.E. Ngakhale kuti Apolo anali wachangu, panali zinthu zina zofunika zimene sankazidziwa. Kodi kukhala ndi Akhristu anzake kunamuthandiza bwanji?​—Mac. 1:4, 5; 18:25; Mat. 28:19.

4 Mkhristu wina dzina lake Akula ndi mkazi wake Purisikila atamva Apolo akulankhula molimba mtima m’sunagoge, anam’tenga n’kumuphunzitsa zinthu zina ndi zina. (Werengani Machitidwe 18:24-26.) Pamenepatu banjali linasonyeza chikondi kwabasi. N’zachidziwikire kuti Akula ndi Purisikila analankhula naye mosamala kuti iye asaone ngati akumuimba mlandu koma adziwe kuti akufuna kumuthandiza. Iye anali munthu wabwino kungoti sankadziwa bwino mbiri ya mpingo wachikhristu. Ndipo n’zosakayikitsa kuti Apolo anayamikira kwambiri anzakewo atamufotokozera mfundo zofunika zimenezi. Iye ataphunzitsidwa bwino “anathandiza kwambiri” abale ake ku Akaya ndipo ankalalikira mogwira mtima.​—Mac. 18:27, 28.

5. Kodi anthu amene amalalikira Ufumu amathandiza ena motani ndipo kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

5 Masiku ano, anthu ambiri mumpingo wachikhristu amayamikira kwambiri anthu amene anawathandiza kumvetsa Baibulo. Anthu ambiri amene anaphunzira choonadi, panopa ndi mabwenzi a pamtima a anthu amene anawaphunzitsa. Nthawi zambiri, kuti munthu amvetse choonadi pamafunika kupatula nthawi yophunzira naye ndipo izi zingachitike kwa miyezi yambiri. Koma anthu amene amalalikira Ufumu, amachita zimenezi mofunitsitsa chifukwa amadziwa kuti imeneyi ndi nkhani ya moyo kapena imfa. (Yohane 17:3) Ndipotu zimakhala zosangalatsa kwambiri kuona anthu akumvetsa choonadi, kuchitsatira pa moyo wawo ndiponso kuchita chifuniro cha Yehova.

“Anam’chitira Umboni Wabwino”

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani Paulo anasankha Timoteyo kuti aziyenda naye? (b) Kodi Timoteyo atathandizidwa anapita patsogolo motani?

6 Mtumwi Paulo ndi Sila atafika ku Lusitara pa ulendo wawo wachiwiri waumishonale, anapeza wachinyamata wina dzina lake Timoteyo. Pa nthawiyi Timoteyo ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 20 kapena kuposerapo pang’ono. “Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anam’chitira umboni wabwino.” Mayi ake a Yunike ndi agogo ake a Loisi anali Akhristu koma bambo ake sanali Mkhristu. (2 Tim. 1:5) Paulo ayenera kuti anadziwana ndi banja limeneli pa ulendo wake woyamba wa kuderali zaka zingapo m’mbuyomo. Koma pa nthawiyi mtumwi Paulo anachita chidwi ndi Timoteyo chifukwa chakuti anali wosiyana kwambiri ndi achinyamata anzake. Choncho atavomerezedwa ndi akulu a kuderalo, Timoteyo anayamba kuthandiza Paulo pa ntchito yaumishonale.​—Werengani Machitidwe 16:1-3.

7 Panali zinthu zambiri zimene Timoteyo anafunika kuphunzira kwa mnzake wachikulireyu. Iye anaphunziradi moti pa nthawi ina Paulo anamutuma kuti akayendere mipingo m’malo mwa iyeyo. Pa zaka pafupifupi 15 zimene Timoteyo anayenda ndi Paulo, anapita patsogolo kwambiri moti anakhala woyang’anira wabwino zedi. Timoteyo anachita zimenezi ngakhale kuti mwina poyamba sankadziwa zambiri ndiponso anali wamanyazi.​—Afil. 2:19-22; 1 Tim. 1:3.

8, 9. Kodi abale ndi alongo mumpingo angalimbikitse bwanji achinyamata? Perekani chitsanzo.

8 Achinyamata ambiri mumpingo wachikhristu angathe kuchita bwino zinthu zambiri. Ngati atalimbikitsidwa ndiponso kuthandizidwa ndi abale ndi alongo okonda zinthu zauzimu, achinyamata amenewa akhoza kuyenerera ndiponso kulandira maudindo akuluakulu m’gulu la Yehova. Taganizirani za achinyamata a mumpingo mwanu. Kodi muli achinyamata amene angafune kutumikira ngati mmene Timoteyo anachitira? Ngati mutawathandiza ndiponso kuwalimbikitsa akhoza kukhala apainiya, atumiki a pa Beteli, amishonale kapena oyang’anira oyendayenda. Kodi mungatani kuti muwathandize kukwaniritsa zolinga zimenezi?

9 Martin wakhala akutumikira pa Beteli kwa zaka 20. Iye amasangalala kwambiri akakumbukira mmene woyang’anira dera wina anamusonyezera chidwi zaka 30 zapitazo pamene anayendera limodzi mu utumiki. Woyang’anira derayu anamufotokozera mmene ankasangalalira pa nthawi imene ankatumikira pa Beteli ali wachinyamata. Iye anamulimbikitsa kuganizira zimene angachite kuti nayenso atumikire m’gulu la Yehova. Martin amaona kuti zinthu zosaiwalika zimene anakambirana pa tsikuli, ndi zimene zinamuthandiza kwambiri kuti asankhe zinthu mwanzeru. Dziwani kuti nanunso mukhoza kulimbikitsa mabwenzi anu achinyamata mwa kukambirana nawo kuti akhale ndi zolinga zauzimu.

“Lankhulani Molimbikitsa kwa a Mtima Wachisoni”

10. Kodi Epafurodito anakumana ndi zotani ndipo anamva bwanji?

10 Epafurodito anayenda ulendo wautali ndiponso wotopetsa kuchoka ku Filipi kupita ku Roma kuti akaone mtumwi Paulo. Pa nthawiyi n’kuti Paulo ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake. Epafurodito anali ngati nthumwi ya Akhristu a ku Filipi. Iye anatenga mphatso zimene Akhristuwo anamupatsira kuti akapereke kwa Paulo, komanso anakonza zoti akakhale ndi Pauloyo kuti azikamuthandiza pa nthawi yake yovutayo. Koma ali ku Roma, Epafurodito anadwala kwambiri “kutsala pang’ono kufa.” Poona kuti walephera kuchita zimene ankafuna, Epafurodito anavutika kwambiri maganizo.​—Afil. 2:25-27.

11. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ena mumpingo akamavutika maganizo? (b) Pa nkhani ya Epafurodito, kodi Paulo analimbikitsa anthu kuti achite chiyani?

11 Masiku ano, pali zinthu zambiri zimene zimachititsa kuti anthu azivutika maganizo. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse akhoza kudwala matenda a maganizo pa nthawi ina. Zimenezi zingachitikirenso anthu a Yehova. Zinthu monga kusamalira banja, matenda ndiponso kukhumudwa chifukwa cholephera kuchita zinazake kapena zinthu zina, zingachititse kuti munthu azivutika maganizo. Kodi Afilipi akanathandiza bwanji Epafurodito? Paulo analemba kuti: “M’landireni monga mwa nthawi zonse, mwa Ambuye ndi chimwemwe chonse. Ndipo anthu a mtundu umenewu muziwalemekeza kwambiri, pakuti chifukwa cha ntchito ya Ambuye, anatsala pang’ono kufa. Anaika moyo wake pachiswe, kuti anditumikire bwino lomwe m’malo mwanu, popeza simuli kuno.”​—Afil. 2:29, 30.

12. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene akuvutika maganizo?

12 Ifenso tiyenera kulimbikitsa abale amene akhumudwa kapena amene akuvutika maganizo. N’zosakayikitsa kuti pali zinthu zabwino zimene akuchita potumikira Yehova zomwe tinganene. N’kutheka kuti asintha zinthu zambiri pamoyo wawo n’cholinga chakuti akhale Akhristu kapenanso kuti ayambe utumiki wa nthawi zonse. Tiziwayamikira chifukwa cha zimenezo ndipo tiziwatsimikizira kuti Yehova nayenso amawayamikira. Ngati anthu ena akulephera kuchita zimene ankachita poyamba chifukwa cha ukalamba kapena matenda, timafunika kuwayamikira chifukwa cha utumiki umene akhala akuchita kwa zaka zambiri. Kaya anthu akuvutika pa zifukwa zotani, Yehova amalangiza atumiki ake okhulupirika kuti: “Lankhulani molimbikitsa kwa a mtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.”​—1 Ates. 5:14.

“M’khululukireni ndi Mtima Wonse ndi Kum’tonthoza”

13, 14. (a) Kodi mpingo wa ku Korinto unachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani unachita zimenezi? (b) Kodi kuchotsa munthu wolakwa kunathandiza bwanji?

13 M’nthawi ya atumwi, mumpingo wa Korinto munali munthu wina amene ankachita chigololo mosalapa. Zochita zakezi zikanatha kudetsa mpingo ndipo zinali zochititsa manyazi ngakhale kwa anthu akunja. Motero mpake kuti Paulo anauza abale kuti achotse munthuyo mumpingo.​—1 Akor. 5:1, 7, 11-13.

14 Chilangochi chinathandiza kwambiri. Mpingo unatetezeka ndipo munthuyo anazindikira kulakwa kwake komanso analapa moona mtima. Popeza iye anachita zinthu zosonyeza kuti walapa, m’kalata yake yachiwiri, Paulo analembera mpingowo kuti um’bwezeretse munthuyo. Komatu sizokhazi zimene anafunika kuchita. Paulo analangizanso mpingowo kuti: “M’khululukireni ndi mtima wonse ndi kum’tonthoza, [munthu wochimwa amene analapayo] kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe kotheratu ndi chisoni chake chopitirira malire.”​—Werengani 2 Akorinto 2:5-8.

15. Kodi anthu amene alapa n’kubwezeretsedwa mumpingo tiyenera kuwaona bwanji?

15 Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani? Zimakhala zomvetsa chisoni munthu wina akachotsedwa mumpingo. Munthu wochotsedwayo amakhala atanyozetsa dzina la Mulungu ndiponso mpingo. Mwina angakhale atatilakwiranso ifeyo. Choncho ngati akulu amene asamalira nkhaniyo, aona kuti malinga ndi malangizo a Yehova munthu wolapayo akufunika kubwezeretsedwa mumpingo, umakhala umboni wakuti Yehova wamukhululukira. (Mat. 18:17-20) Kodi ifenso sitiyenera kutsanzira Yehova? Ndithudi, kulephera kumukomera mtima ndiponso kumukhululukira munthuyo, kungakhale kutsutsana ndi Yehova. Kuti tilimbikitse mtendere ndi umodzi mumpingo wa Mulungu ndiponso kuti Yehova azikondwera nafe, ‘tiyenera kukonda’ anthu ochimwa amene alapa n’kubwezeretsedwa.​—Mat. 6:14, 15; Luka 15:7.

“Iye Ndi Wofunika”

16. N’chifukwa chiyani Paulo anakhumudwa ndi Maliko?

16 M’Malemba muli nkhani inanso imene ikusonyeza kuti sitiyenera kusungira chakukhosi anthu amene atikhumudwitsa. Mwachitsanzo, Yohane Maliko anakhumudwitsa mtumwi Paulo koopsa. Kodi chinachitika n’chiyani? Pamene Paulo ndi Baranaba ankapita pa ulendo wawo woyamba waumishonale, Maliko anapita nawo kuti azikawathandiza. Koma atafika pa malo ena, Yohane Maliko anawasiya n’kubwerera kwawo ndipo Baibulo silitchula chifukwa chake anabwerera. Paulo anakhumudwa kwambiri chifukwa cha zimene Maliko anachitazi moti pamene ankakonzekera ulendo wachiwiri, anakangana ndi Baranaba pa nkhani yakuti Maliko apite nawo kapena ayi. Paulo sankafuna kuti Maliko apite nawo chifukwa cha zimene zinachitika paulendo woyamba uja.​—Werengani Machitidwe 13:1-5, 13; 15:37, 38.

17, 18. Kodi tikudziwa bwanji kuti Paulo ndi Maliko anathetsa vuto lawo, ndipo kodi tikuphunzirapo chiyani?

17 N’zachidziwikire kuti Maliko sanataye mtima chifukwa chokanidwa ndi Paulo. Iye anapitirizabe ntchito yake yaumishonale ndipo anakatumikira kudera lina limodzi ndi Baranaba. (Mac. 15:39) Umboni wakuti anali wokhulupirika ndiponso wodalirika umaoneka m’mawu onena za iye amene Paulo analemba m’zaka zotsatira. Pa nthawiyi n’kuti Paulo ali m’ndende ku Roma ndipo analembera Timoteyo kalata. M’kalatayi Paulo anati: “Pobwera utengenso Maliko, pakuti iye ndi wofunika ponditumikira.” (2 Tim. 4:11) Pa nthawiyi Paulo anaona kuti Maliko anali atasintha.

18 Nkhaniyi ikutiphunzitsa kanthu kena. Maliko anali ndi makhalidwe abwino oyenera mmishonale. Iye sanakhumudwe chifukwa chakuti Paulo anamukana poyamba paja. Maliko ndi Paulo anali anthu auzimu ndipo sanasungirane chakukhosi. Paulo anazindikira kuti Maliko ndi wofunika kuti amutumikire. Choncho abale akasemphana maganizo n’kukambirana nkhaniyo, ndi bwino kuiwala zakale n’kuyamba kuthandiza ena kuti apite patsogolo mwauzimu. Tikamaona mbali zimene abale athu amachita bwino, tingalimbikitse mpingo.

Muzilimbikitsana Mumpingo

19. Kodi anthu mumpingo wachikhristu angathandizane bwanji?

19 “Nthawi yovuta” ino, mumafunika thandizo la abale ndi alongo anu mumpingo ndipo nawonso amafuna thandizo lanu. (2 Tim. 3:1) Nthawi zina Mkhristu sangadziwe zoyenera kuchita akakumana ndi vuto linalake, koma Yehova amadziwa. Iye angagwiritse ntchito abale osiyanasiyana mumpingo kuphatikizapo inuyo, kuthandiza ena kusankha zochita mwanzeru. (Yes. 30:20, 21; 32:1, 2) Choncho yesetsani kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti pitirizani “kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake, monga mmene mukuchitiradi.”​—1 Ates. 5:11.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikitsa ena mumpingo wachikhristu?

• Kodi inuyo mungathandize anthu ena pa mavuto ati?

• N’chifukwa chiyani ifeyo timafunika thandizo la anzathu mumpingo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Ngati Mkhristu mnzathu akuvutika, tiyenera kumuthandiza

[Chithunzi patsamba 12]

Achinyamata ambiri mumpingo wachikhristu angathe kuchita bwino zinthu zambiri