Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa” mwa Kupewa Kupsa Mtima

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa” mwa Kupewa Kupsa Mtima

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa” mwa Kupewa Kupsa Mtima

“Okondedwa, musabwezere choipa . . . koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”​—AROMA 12:19, 21.

1, 2. Kodi abale ndi alongo amene anali paulendo anapereka chitsanzo chotani?

GULU la abale ndi alongo 34 linali paulendo wopita ku msonkhano wopatulira ofesi ya nthambi. Ndege imene anakwera inawonongeka ndipo izi zinachititsa kuti achedwe paulendo wawowu. Poyamba iwo ankayembekezera kuti aima kwa ola limodzi lokha kuti athire mafuta koma anatha maola 44 ali pa bwalo lina la ndege pomwe panalibe chakudya chokwanira, madzi ndiponso zimbudzi. Anthu ambiri amene anakwera nawo ndegeyo anakwiya ndipo anayamba kuopseza anthu ogwira ntchito pabwalo la ndegeli. Koma abale ndi alongowo anangokhala phee.

2 Abale ndi alongowa anafika ku msonkhanowu mochedwa moti anangomvera nawo chigawo chomaliza cha pulogalamuyo. Ngakhale kuti anali otopa, pulogalamu itatha iwo sanabwerere kwawo mwamsanga n’cholinga chakuti acheze ndi abale ndi alongo akumeneko. Pambuyo pake anazindikira kuti anthu ena anaona kuti iwo anali oleza mtima ndiponso odziletsa. Munthu wina anauza anthu ogwira ntchito pabwalo la ndegelo kuti: “Pakanapanda Akhristu 34 paulendowu, pabwalo la ndege pakanachitika chipolowe.”

Tikukhala M’dziko la Anthu Okwiya

3, 4. (a) Kodi kupsa mtima kwabweretsa mavuto otani pakati pa anthu, ndipo kodi zimenezi zinayamba liti? (b) Kodi Kaini akathana kudziletsa? Fotokozani.

3 Anthu m’dzikoli amakhala okwiya chifukwa chopanikizika ndi mavuto. (Mlal. 7:7) Nthawi zambiri zimenezi zimapangitsa kuti anthu azidana ndiponso kuchita chiwawa. M’mayiko ambiri mukuchitika nkhondo. Mavuto a m’banja amachititsa kuti anthu a m’banjamo azikangana. Zinthu zoterezi zinayamba kalekale. Kaini, yemwe anali mwana woyamba wa Adamu ndi Hava, anapha mng’ono wake Abele chifukwa cha kupsa mtima ndiponso nsanje. Kaini anachita zimenezi ngakhale kuti Yehova anali atamuchenjeza kuti asiye kukhala ndi maganizo olakwikawo ndipo anamulonjeza kuti amudalitsa akamvera.​—Werengani Genesis 4:6-8.

4 Ngakhale kuti Kaini anali wopanda ungwiro, anali ndi ufulu wosankha pa nkhaniyi. Iye akanatha kupewa kukwiya kwambiri. N’chifukwa chake iye anali ndi mlandu pa chiwembu chimene anachitira m’bale wakechi. Popeza ifenso ndife opanda ungwiro, zimakhala zovuta kuti tipewe kupsa mtima ndiponso kuchita zinthu chifukwa chopsa mtima. Mavuto amene timakumana nawo “nthawi yovuta” ino, amachititsanso kuti tizipanikizika. (2 Tim. 3:1) Mwachitsanzo, mavuto a zachuma amatisowetsa mtendere. Apolisi ndiponso mabungwe amene amathandiza mabanja amanena kuti mavuto a zachuma akuchuluka m’mabanja chifukwa cha kulalatirana ndiponso kuchitirana nkhanza.

5, 6. Kodi mzimu wa dzikoli ungatikhudze bwanji pa nkhani ya kupsa mtima?

5 Anthu ambiri amene timachita nawo zinthu ndi “odzikonda,” “odzikweza” ndiponso “owopsa.” (2 Tim. 3:2-5) N’zosavuta kuti titengere makhalidwe amenewa n’kumakhala anthu okwiya. (2 Tim. 3:2-5) Ndipotu mafilimu ndiponso mapulogalamu a pa TV amachititsa anthu kuganiza kuti munthu akaputidwa choyenera kuchita ndi kubwerezera basi. Amakonzedwa m’njira yoti anthu aziyembekezera kuona munthu wotchuka wa m’filimuyo akubwezera mwa kupha mwankhanza munthu amene anachita zoipa.

6 Zimenezi zimalimbikitsa anthu kukhala ndi “mzimu wa dziko” ndiponso wa Satana yemwe ndi wolamulira wokwiya. Iwo saona zinthu mmene Yehova amazionera. (1 Akor. 2:12; Aef. 2:2; Chiv. 12:12) Mzimu umenewu umachititsa anthu opanda ungwiro kuti azingochita zofuna zawo ndipo ndi wotsutsana ndi mzimu wa Mulungu ndiponso zipatso zake. Akhristu amaphunzitsidwa kuti asamabwezere ena akawachitira zoipa. (Werengani Mateyo 5:39, 44, 45.) Ndiyeno kodi tingatani kuti tizitsatira kwambiri zimene Yesu anaphunzitsa?

Zitsanzo Zabwino Ndiponso Zoipa

7. Kodi n’chiyani chinachitika Simeoni ndi Levi atapsa mtima?

7 M’Baibulo muli malangizo ambirimbiri okhudza kudziletsa pa nkhani ya kupsa mtima. Mulinso zitsanzo zosonyeza zotsatira za kupsa mtima ndiponso ubwino wa kupewa kupsa mtima. Taganizirani zimene zinachitika Simeoni ndi Levi, omwe anali ana a Yakobo, atabwezera zimene Sekemu anachita. Sekemu anagwirira mlongo wawo dzina lake Dina. Izi zitachitika iwo “anapwetekedwa mtima, nakwiya kwambiri.” (Gen. 34:7) Kenako ana ena a Yakobo anaukira mzinda wa Sekemu n’kutenga katundu yense. Anatenganso akazi ndi ana kuti akhale akapolo. Sikuti iwo anachita zimenezi chifukwa chongomvera chisoni Dina, koma ayenera kuti anali odzikuza ndipo ankaona kuti Sekemu wawachotsera ulemu. Ankaonanso kuti Sekemu wawalakwira ndiponso walakwira Yakobo bambo awo. Koma kodi Yakobo anaona bwanji zimene ana ake anachitazi?

8. Kodi nkhani ya Simeoni ndi Levi ikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yobwezera?

8 Yakobo ayenera kuti anamva chisoni kwambiri ndi zimene zinachitikira Dina, komabe anadzudzula ana akewa chifukwa chobwezera. Koma Simeoni ndi Levi anapereka zifukwa zodzikhululukira ponena kuti: “Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?” (Gen. 34:31) Koma nkhaniyi sinathere pompo chifukwa Yehova nayenso sanasangalale nazo. N’chifukwa chake patapita zaka zambiri, Yakobo analosera kuti mbadwa za Simeoni ndi Levi zidzamwazikana m’mafuko ena a Isiraeli. (Werengani Genesis 49:5-7.) Chifukwa cholephera kulamulira mkwiyo wawo, iwo anakhumudwitsa Mulungu ndiponso bambo awo.

9. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Davide atsale pang’ono kubwezera chifukwa chopsa mtima?

9 Izi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Mfumu Davide anachita. Panali nthawi zambiri pamene iye akanatha kubwezera koma anadziletsa. (1 Sam. 24:3-7) Koma pa nthawi ina Davide anangotsala pang’ono kubwezera chifukwa chopsa mtima. Munthu wina wolemera dzina lake Nabala anakalipira anyamata a Davide ngakhale kuti iwo anateteza abusa ndi ziweto zake. Davide anakwiya ndi zimene zinachitikira anyamata ake ndipo anafuna kukabwezera moti ananyamuka ndi anyamata akewa kuti akaphe Nabala ndi anthu onse a m’banja mwake. Ali m’njira, munthu wina anadziwitsa Abigayeli mkazi wa Nabala za nkhaniyi ndipo anamulimbikitsa kuti achitepo kanthu. Abigayeli anali mkazi wanzeru moti nthawi yomweyo, anatenga mphatso zambiri ndipo anapita kukakumana ndi Davide. Iye modzichepetsa anapepesa kwambiri chifukwa cha chipongwe chimene Nabala anachita ndipo anapempha Davide kuti amukhululukire popeza Davideyo anali woopa Yehova. Mtima wa Davide unakhala m’malo ndipo anati: ‘Udalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi.’​—1 Sam. 25:2-35.

Zimene Akhristu Ayenera Kuchita

10. Kodi Akhristu ayenera kuiona bwanji nkhani yobwezera?

10 Nkhani ya Simeoni ndi Levi komanso ya Davide ndi Abigayeli imasonyeza kuti Yehova sasangalala ndi kukwiya mosadziletsa ndiponso kuchita chiwawa. Nkhanizi zikusonyezanso kuti iye amatidalitsa tikamayesetsa kukhazikitsa mtendere. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’ Koma, ‘ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse chakudya; ngati ali ndi ludzu, m’patse chakumwa; pakuti mwakutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.’ Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”​—Aroma 12:18-21. *

11. Kodi mlongo wina anaphunzira bwanji zoyenera kuchita akakwiya?

11 N’zotheka ndithu kutsatira malangizo amenewa. Mwachitsanzo, mlongo wina anadandaulira mkulu wina za bwana wake watsopano. Iye anafotokoza kuti bwanayo anali wovuta ndiponso woipa mtima. Mlongoyo anakwiya kwambiri chifukwa cha bwana wakeyo moti ankafuna kusiya ntchito. Mkuluyo anamulangiza kuti asachite zinthu mopupuluma. Iye anaona kuti kukwiya kwa mlongoyu kunachititsa kuti zinthu ziipe kwambiri ngakhale kuti bwanayo ankamuchitiradi zoipa. (Tito 3:1-3) Mkuluyo ananena kuti kaya asiya ntchitoyo kapena ayi, mlongoyo ayenera kusintha mmene amachitira zinthu munthu akamuchitira zoipa. Anamulangizanso kuti ayenera kuchitira bwana wakeyo zinthu zimene iyenso angafune kuchitiridwa ngati mmene Yesu ananenera. (Werengani Luka 6:31.) Mlongoyu anavomera kuti ayesetsa. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Patapita nthawi, bwana uja anasintha moti tsiku lina anayamikira mlongoyo chifukwa cholimbikira ntchito.

12. N’chifukwa chiyani zimakhala zopweteka kwambiri akakhala kuti amene watilakwira ndi Mkhristu mnzathu?

12 Nthawi zambiri sizitidabwitsa kwenikweni akakhala kuti amene watilakwirayo si Mkhristu mnzathu. Timadziwa kuti moyo m’dziko la Satanali ndi wovuta ndipo timafunika kudziletsa kuti tisamapse mtima ndi zochita za anthu oipa. (Sal. 37:1-11; Mlal. 8:12, 13; 12:13, 14) Koma akakhala kuti amene watipsetsa mtima ndi m’bale kapena mlongo, zimakhala zopweteka kwambiri. Mlongo wina anati: “Nditangophunzira kumene choonadi, zinkandivuta kwambiri kuvomereza kuti anthu m’gulu la Yehova ndi opanda ungwiro.” Tinachoka m’dziko loipali ndi maganizo akuti Akhristu onse mumpingo azichitirana zinthu mokoma mtima. Choncho ngati Mkhristu wina makamaka amene ali ndi udindo mumpingo, wanena kapena kuchita zinthu zosayenera Mkhristu, zimatipweteka kwambiri kapena kutipsetsa mtima. Timadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zikuchitika m’gulu la Yehova?’ Komatu zinthu ngati zimenezi zinkachitikanso pakati pa Akhristu odzozedwa m’nthawi ya atumwi. (Agal. 2:11-14; 5:15; Yak. 3:14, 15) Kodi tiyenera kuchita chiyani zimenezi zikachitika?

13. Kodi tiyenera kuchita chiyani pakakhala kusemphana maganizo, ndipo n’chifukwa chiyani?

13 Mlongo amene tam’tchula poyamba uja anati: “Ndaphunzira kupempherera anthu amene andipsetsa mtima ndipo zimenezi n’zothandiza nthawi zonse.” Pajatu Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera anthu amene akutizunza. (Mat. 5:44) Ndiye ngati tiyenera kupempherera otizunza kuli bwanji abale ndi alongo athu? Mofanana ndi bambo amene amafuna kuti ana ake azikondana, Yehova amafunanso kuti atumiki ake padziko lapansi azikondana. Tikuyembekezera nthawi imene tidzakhale limodzi kosatha mwamtendere komanso mosangalala ndipo Yehova panopa akutiphunzitsiratu mmene tingachitire zimenezi. Iye amafuna kuti tizikhala ogwirizana pogwira ntchito yofunika kwambiri imene watipatsa. Choncho tiyeni tizithetsa msanga kusiyana maganizo kapena ‘kungokhululuka’ zimene munthu wina watichitira n’kuziiwala. (Werengani Miyambo 19:11.) M’malo mopewa abale athu pakakhala mavuto, tiyenera kuthandizana kuti tikhalebe m’gulu la anthu a Mulungu n’kukhala otetezeka m’manja a Yehova amene adzakhalapo mpaka kalekale.​—Deut. 33:27.

Kuchita Zinthu Modekha Kumathandiza

14. Popeza Satana amafuna kuti tigawanike, kodi tingalimbane naye bwanji?

14 Satana ndi ziwanda zake akuyesetsa kusokoneza mabanja ndiponso mipingo kuti isakhale yogwirizana. Iwo akuchita zimenezi n’cholinga choti atilepheretse kulalikira uthenga wabwino. Satana ndi ziwanda zake amafuna kuti tigawanike podziwa kuti mutu umodzi susenza denga. (Mat. 12:25) Kuti tithe kulimbana ndi Satana ndi ziwanda zake, tiyenera kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.” (2 Tim. 2:24) Kumbukirani kuti nkhondo yathu “sitikulimbana ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi . . . makamu a mizimu yoipa.” Kuti tipambane pa nkhondoyi tiyenera kuvala zida zonse za zauzimu kuphatikizapo “nsapato zokonzekera uthenga wabwino wa mtendere.”​—Aef. 6:12-18.

15. Kodi tiyenera kutani anthu omwe si mboni akatichitira zoipa?

15 Adani a Yehova amakonzera ziwembu zoopsa Mboni za Yehova zomwe ndi anthu amtendere. Ena mwa adani amenewa amazunza Mbonizi. Ena amalemba nkhani zabodza zokhudza ifeyo m’nyuzipepala, pomwe ena amatinamizira m’makhoti. Yesu anauza ophunzira ake kuti adzakumana ndi zimenezi. (Mat. 5:11, 12) Kodi zimenezi zikachitika tiyenera kutani? Sitiyenera kubwezera “choipa pa choipa” mwa zolankhula kapena zochita zathu.​—Aroma 12:17; werengani 1 Petulo 3:16.

16, 17. Kodi mpingo wina unakumana ndi vuto lotani?

16 Kaya Satana atichitire zotani, “kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino” kungathandize kuti tichitire umboni. Mwachitsanzo, abale a mumpingo wina ku chilumba china cha ku Pacific anachita lendi holo inayake kuti achitiremo Chikumbutso. Akuluakulu a tchalitchi china atamva zimenezi, anauza anthu awo kuti akasonkhane muholoyo kuti achite mapemphero awo pa nthawi imene abalewo anakonza zoti mwambowo uchitike. Koma mkulu wa apolisi analamula akuluakulu a tchalitchiwo kuti apereke mwayi kwa abalewo kuti agwiritse ntchito holoyo. Nthawi ya mwambowo itakwana anthu a tchalitchiwo anali atadzaza muholoyo n’kuyamba mapemphero awo.

17 Pamene apolisi ankakonza zoti atulutse anthuwa muholoyo, pulezidenti wa tchalitchicho anapita kwa akulu ena n’kuwafunsa kuti: “Kodi pali zimene mukufuna kuchita madzulo ano?” M’bale wina atamuuza za Chikumbutso iye anayankha kuti, “Kuteroko eti? Sindimadziwa.” Atatero wapolisi uja anati, “Paja tinakuuzanitu m’mawa uja.” Kenako pulezidentiyo anayang’ana mkuluyo akumwetulira mwachinyengo n’kunena kuti: “Ndiye mutani? Panopa muholoyi mwadzaza kale anthu. Kapena muuza apolisi kuti atithamangitse?” Iye anachita dala zimenezi n’cholinga choti zioneke ngati abalewo ndi amene akufuna kuyambitsa chisokonezo. Kodi abale athu anatani pamenepa?

18. Kodi abale anatani pulogalamu yawo itasokonezedwa, ndipo kodi zotsatira zake zinali zotani?

18 Abalewo analola kuti anthuwo achite mapemphero awo kwa mphindi 30 kuti akatha iwo achite Chikumbutso. Mapemphero awowo anapitirira nthawi imene anapangana, komabe atamaliza n’kutuluka, abalewo anachita Chikumbutso. Tsiku lotsatira akuluakulu aboma analamula kuti pakhale bungwe lofufuza zimene zinachitika. Bungwelo litafufuza, linalamula a tchalitchiwo kuti alengeze kuti amene anayambitsa vuto si Mboni za Yehova koma pulezidenti wa tchalitchi chawo. Bungwelo linayamikiranso Mboni za Yehova chifukwa chochita zinthu moleza mtima. Abalewo anayesetsa “kukhala mwa mtendere ndi anthu onse” ndipo zotsatira zake zinali zabwino.

19. Kodi chinthu china chimene chingathandize kuti tizikhala mwamtendere ndi anthu n’chiyani?

19 Chinthu china chimene chingatithandize kukhala mwamtendere ndi anthu ndi kulankhula mwaulemu. Nkhani yotsatira ifotokoza tanthauzo la kulankhula mwaulemu komanso mmene tingachitire zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mawu akuti “makala a moto” amanena za njira imene anthu ankagwiritsa ntchito poyenga zitsulo. Anthuwo ankaika makala a moto pamwamba ndi pansi pa chitsulo chimene akufuna kuyengacho. Tikamakomera mtima anthu amene atichitira zoipa, timafewetsa mtima wawo n’kuwathandiza kuti azisonyeza makhalidwe awo abwino.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani anthu m’dzikoli ali okwiya kwambiri?

• Fotokozani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza zotsatira za kupsa mtima ndiponso ubwino wa kupewa kupsa mtima.

• Kodi tiyenera kuchita chiyani Mkhristu mnzathu akatikhumudwitsa?

• Kodi tiyenera kutani anthu omwe si Mboni akatichitira zoipa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Simeoni ndi Levi akubwerera kwawo atachita zinthu chifukwa cha kupsa mtima

[Zithunzi patsamba 18]

Kuchita zinthu mokoma mtima kungathandize kuti anthu ena asinthe maganizo awo oipa