Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ali Wosakhulupirika

Zimene Mungachite Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ali Wosakhulupirika

Zimene Mungachite Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ali Wosakhulupirika

MARGARITA ndi mwamuna wake Raúl anatumikirapo Yehova mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka zambiri. * Koma mwana wawo woyamba atangobadwa, Raúl anayamba kusiya kutumikira Yehova. Kenako iye anayamba moyo wachiwerewere ndipo anachotsedwa mumpingo. Margarita anati: “Pamene zonsezi zinkachitika ndinkangoona ngati ndifa. Zinandikhumudwitsa kwambiri ndipo sindinkadziwa kuti ndigwira mtengo wanji.”

Jane atangokwatiwa, zochita za mwamuna wake zinachititsa kuti iye asamakhulupirire mwamuna wakeyo ndiponso kumukonda ngati poyamba. Mwamuna wakeyu anayamba kumuzunza. Jane anati: “Tsiku lina anandimenya mbama. Ndinadabwa kwambiri ndi zimenezi ndipo zinandichititsa manyazi. Kenako ichi chinangokhala chizolowezi chake ndipo akandimenya ankanena kuti ndimukhululukire. Ndinkaganiza kuti popeza ndine Mkhristu, ndiyenera kumamukhululukira n’kuiwala za nkhaniyo. Ndinkaonanso kuti kuuza aliyense mavuto athu, ngakhale akulu mumpingo kukanakhala kusakhulupirika. Mavuto amenewa anapitirira kwa zaka zambiri ndipo zaka zonsezo ndinkamukhululukira. Komabe, ndinkaganiza kuti panali zimene ndikanachita kuti mwamuna wangayo azindikonda. Atandisiya ndi mwana wathu wamkazi ndinkangodziona kuti ndine wolephera. Ndinkaonanso kuti pali zinazake zimene ndikanachita kapena kunena zimene zikanathandiza kuti ukwati wathu usathe.”

Mofanana ndi Margarita ndi Jane, mwina nanunso mukuvutika maganizo, mukukumana ndi mavuto a zachuma ndiponso mavuto okhudza moyo wanu wauzimu chifukwa cha kusakhulupirika kwa mwamuna wanu. Kapena ndinu mwamuna amene mukuvutika maganizo chifukwa cha kusakhulupirika kwa mkazi wanu. Malinga ndi ulosi wa m’Baibulo, panopa tikukhaladi “nthawi yovuta.” Ulosiwu umanena kuti “m’masiku otsiriza” mabanja adzakhala pamavuto chifukwa chakuti anthu adzakhala opanda chikondi chachibadwa. Zochita za anthu ena sizigwirizana ndi zimene amanena kuti amalambira Mulungu. (2 Tim. 3:1-5) Nawonso Akhristu oona amavutika chifukwa cha zinthu zimenezi. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupirire ngati mwamuna kapena mkazi wanu si wokhulupirika?

Muzidziona Mmene Yehova Amakuonerani

Poyamba zingakuvuteni kukhulupirira kuti munthu amene mumam’konda angakukhumudwitseni kwambiri. Mwina mungayambe kudziimba mlandu chifukwa cha khalidwe lake loipalo.

Koma musaiwale kuti nayenso Yesu, yemwe anali wangwiro anakhumudwitsidwapo ndi munthu amene ankamudalira ndiponso kumukonda. Yesu anapemphera kwambiri asanasankhe atumwi ake omwe anali anzake a pamtima. Choncho, atumwi 12 onsewa anali atumiki a Yehova odalirika. Ndiyetu n’zosachita kufunsa kuti Yesu anakhumudwa kwambiri pamene Yudasi anasintha ‘n’kumupereka.’ (Luka 6:12-16) Koma Yehova sanaimbe mlandu Yesu chifukwa cha zimene Yudasi anachita.

N’zoona kuti palibe mwamuna kapena mkazi yemwe ndi wangwiro. Aliyense amalakwitsa zinthu. M’pake kuti wamasalmo anauziridwa kulemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Sal. 130:3) Choncho amuna ndi akazi ayenera kutsanzira Yehova mwa kukhululukirana.​—1 Pet. 4:8.

Komabe, “aliyense wa ife adzadziyankhira yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi chizolowezi cholankhula mosaganizira kapena kuchitira nkhanza mnzake, iyeyo ndi amene ali ndi mlandu kwa Yehova. Yehova amadana ndi nkhanza komanso mawu achipongwe, choncho palibe chifukwa chomveka chakuti munthu azichita zimenezi kwa mwamuna kapena mkazi wake. Kuchita zimenezi, kumangosonyeza kuti munthuyo alibe chikondi ndiponso ulemu. (Sal. 11:5; Aef. 5:33; Akol. 3:6-8) Ndipotu ngati Mkhristu mobwerezabwereza ndiponso mosalapa amapsa mtima ndipo sakufuna kusintha, ayenera kuchotsedwa mumpingo wachikhristu. (Agal. 5:19-21; 2 Yoh. 9, 10) Mwamuna kapena mkazi sayenera kudziimba mlandu ngati wakanena za khalidwe loipali kwa akulu. Yehova amachitira chifundo amuna ndi akazi amene akuzunzidwa.

Mwamuna kapena mkazi akachita chigololo, sikuti amangochimwira mnzake yekhayo koma amachimwiranso Yehova. (Mat. 19:4-9; Aheb. 13:4) Ngati mwamuna kapena mkazi wochimwiridwayo akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, palibe chifukwa chodziimbira mlandu chifukwa cha khalidwe lachiwerewere la mnzakeyo.

Kumbukirani kuti Yehova amadziwa mmene mukumvera mumtima mwanu. Iye amadzifotokoza kuti anali mwamuna wa mtundu wa Isiraeli, ndipo m’Mawu ake muli nkhani zambiri zokhudza mtima zimene zimasonyeza kuti iye anamva chisoni kwambiri pamene mtunduwo unakhala wosakhulupirika kwa iye. (Yes. 54:5, 6; Yer. 3:1, 6-10) Musakayike kuti Yehova amamva kulira kwanu chifukwa cha kusakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wanu. (Mal. 2:13, 14) Iye amadziwa kuti mukufunika kutonthozedwa ndi kulimbikitsidwa.

Mmene Yehova Amatithandizira

Njira ina imene Yehova amathandizira anthu ndi kudzera mumpingo wachikhristu. Jane anathandizidwa mwa njira imeneyi. Iye anati: “Pa nthawi imene woyang’anira dera ankabwera ndinali nditafookeratu ndi nkhawa. Iye anazindikira vuto langa chifukwa choti pa nthawiyi mwamuna wanga anali atatsimikiza kuti tisudzulane. Woyang’anira derayo anapatula nthawi n’kundilimbikitsa ndi malemba monga 1 Akorinto 7:15. Mavesi amene anawerenga ndiponso mawu ake okoma mtima anandithandiza kuti ndisiye kudziimba mlandu ndipo ndinapezako mtendere wamumtima.” *

Margarita amene tam’tchula poyamba uja anazindikiranso kuti Yehova amathandiza anthu kudzera mumpingo wachikhristu. Iye anati: “Zitaonekeratu kuti mwamuna wanga sakufuna kulapa, ndinatenga ana anga n’kusamukira kumzinda wina. Nditafika kumeneko ndinapeza nyumba ya lendi ya zipinda ziwiri. Tsiku lotsatira ndinali wokhumudwa kwambiri ndipo ndikuchotsa katundu m’zikwama ndinamva kugogoda pachitseko. Poyamba ndinkaganiza kuti ndi mayi amene anali mwini wake wa nyumbayi. Iwo ankakhala khomo loyandikana ndi lathu. Koma ndinadabwa kuona kuti anali mlongo wina amene anaphunzirapo Baibulo ndi mayi anga ndipo ndi amene anathandiza banja lathu lonse kuphunzira choonadi. Mlongoyu anali atabwera kudzaphunzira Baibulo ndi mayi amene anali mwini wake wa nyumbayi ndipo sankadziwa kuti ndasamukira kumeneko. Nditangomuona ndinalephera kuugwira mtima moti ndinamufotokozera mavuto anga onse mpaka tonse tinalira. Tsiku lomwelo anakonza zoti tipite kumisonkhano. Mpingo unatilandira bwino kwambiri ndipo akulu anakonza zoti ndithandizidwe kuti ndithe kusamalira banja langa mwauzimu.”

Mmene Ena Angathandizire

Anthu a mumpingo angathandize m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Margarita tsopano anafunika kupeza ntchito. Banja lina mumpingo linadzipereka kuti lizisamalira ana ake akaweruka kusukulu.

Margarita anati: “Ndimayamikira kwambiri abale ndi alongo akamadzipereka kuti ayende nane kapena kuti ayende ndi ana anga mu utumiki wa kumunda.” Mwa kuchita zimenezi, anthu a mumpingo amathandizana “kunyamula mtolo wa wina ndi mnzake” ndipo mwakutero amakwaniritsa “chilamulo cha Khristu.”​—Agal. 6:2.

Anthu amene akuvutika chifukwa cha machimo a ena amayamikira kwambiri akathandizidwa motere. Monique, amene mwamuna wake anamusiyira ana anayi, ndiponso ngongole ya ndalama zokwana madola 15,000, anati: “Abale ndi alongo anga auzimu anandisonyeza chikondi kwambiri. Sindikudziwa kuti zinthu zikanayenda bwanji popanda thandizo lawo. Ndikuona kuti Yehova anandipatsa abale abwino kwambiri amene anadzipereka kuthandiza ana anga. Ndinasangalala kwambiri kuona ana anga akukula mwauzimu chifukwa cha thandizo limeneli. Pa nthawi imene ndinkafunikira malangizo, akulu ankandithandiza. Ndipo ndikakhala ndi vuto loti ndiwafotokozere ankandimvetsera.”​—Maliko 10:29, 30.

Koma bwenzi lachikondi limadziwa kuti si bwino kuyambitsa nkhani yokhudza zinthu zoipa zimene zinachitikira mnzake. (Mlal. 3:7) Margarita anati: “Nthawi zambiri ndinkasangalala kucheza ndi alongo a mumpingo nkhani zokhudza ntchito yolalikira, anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo, ana athu ndiponso zinthu zina zonse koma osati za mavuto anga. Ndimayamikira kuti ankandithandiza kuiwala zakale, ndi kuyamba moyo watsopano.”

Pewani Mtima Wofuna Kubwezera

Nthawi zina, simungaone kuti ndinu amene munachititsa kuti mwamuna kapena mkazi wanu achimwe, koma mungamawawidwe mtima poganiza kuti mukuvutika kwambiri chifukwa cha zoipa zimene mnzanuyo anachita. Ngati mulola maganizo amenewa kukula, zingakulepheretseni kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, mungayambe kufufuza njira yoti mubwezere zoipa zimene mwamuna kapena mkazi wanu wosakhulupirikayo anachita.

Mukazindikira kuti mwayamba kukhala ndi maganizo ofuna kubwezera, mungachite bwino kuganizira chitsanzo cha Yoswa ndi Kalebi. Amuna okhulupirika amenewa anaika moyo wawo pa chiswe kuti akazonde Dziko Lolonjezedwa. Azondi ena analibe chikhulupiriro ndipo anachititsa kuti anthu asamvere Yehova. Ndipo Aisiraeli ena ankafuna kuponya miyala Yoswa ndi Kalebi chifukwa cholimbikitsa Aisiraeli kukhalabe okhulupirika. (Num. 13:25–14:10) Zochita za Aisiraeli zinapangitsa kuti Yoswa ndi Kalebi ayende m’chipululu kwa zaka 40, osati chifukwa cha zolakwa zawo koma za ena.

Ngakhale kuti Yoswa ndi Kalebi anakhumudwa ndi zimenezi, iwo sanakhalebe okwiya chifukwa cha zolakwa za abale awo. Iwo anaika maganizo awo pa kutumikira Yehova mokhulupirika. Zaka 40 zimene anakhala m’chipululu zitatha, iwo limodzi ndi Alevi anapulumuka ndipo analowa m’Dziko Lolonjezedwa.​—Num. 14:28-30; Yos. 14:6-12.

Zochita za mnzanu wosakhulupirika zingachititse kuti muvutike kwa nthawi yaitali. Ukwati ungathe, ndipo izi zingachititse kuti muvutike maganizo ndiponso mukumane ndi mavuto a zachuma. M’malo mokhumudwa kwambiri, kumbukirani kuti Yehova amadziwa zoyenera kuchita ndi anthu amene amaswa mfundo zake mwadala, ngati mmene chitsanzo cha zimene zinachitikira Aisiraeli osakhulupirika m’chipululu chikusonyezera.​—Aheb. 10:30, 31; 13:4.

Mungathe Kupirira

M’malo mongoganiza kwambiri za mavuto anuwo, ganizirani kwambiri zimene Yehova amafuna. Jane anati: “Ndinaona kuti kumvetsera matepi a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kunandithandiza kwambiri kupirira. Misonkhano inandithandizanso kwambiri. Kutenga nawo mbali mokwanira pa misonkhano kunandichititsa kuti ndisamangoganiza za mavuto anga. Ntchito yolalikira nayonso inandilimbikitsa kwabasi. Mwa kuthandiza ena kukhulupirira Yehova, inenso ndinalimbitsa chikhulupiriro changa. Ndipo kuthandiza m’njira zosiyanasiyana anthu amene ndinkaphunzira nawo Baibulo, kunandithandiza kuti ndiziganizira zinthu zofunika.”

Monique, amene tam’tchula poyamba uja, anati: “Kupezeka pamisonkhano nthawi zonse ndiponso kugwira ntchito yolalikira nthawi zambiri, n’kumene kwandithandiza kupirira. Tsopano pabanja lathu timagwirizana kwambiri ndiponso timagwirizana ndi anthu mumpingo. Mavuto anga andithandiza kuzindikira zinthu zimene sindichita bwino. Ndakumana ndi mayesero ambiri, koma Yehova akundithandiza kupirira.”

Inunso mungathe kupirira ngati mukukumana ndi mavuto ngati amenewa. Ngakhale kuti mukuvutika maganizo chifukwa cha kusakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wanu, yesetsani kutsatira malangizo ouziridwa a Paulo akuti: “Tisaleke kuchita zabwino, pakuti panyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”​—Agal. 6:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena.

^ ndime 13 Kuti mudziwe zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kupatukana ndi kusudzulana, werengani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” pa tsamba 125 mpaka 130 ndiponso tsamba 219 mpaka 221.

[Chithunzi patsamba 31]

Mkazi kapena mwamuna amene wasiyidwa amayamikira anthu amene amamuthandiza mu utumiki wa kumunda