Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Lingalirani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala”

“Lingalirani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala”

“Lingalirani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenera Kukhala”

“Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu.”​—2 PET. 3:11.

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malangizo a Petulo a m’kalata yake yachiwiri, anali ofunika kwambiri kwa Akhristu pa nthawiyo?

PA NTHAWI imene mtumwi Petulo ankalemba kalata yake yachiwiri youziridwa, n’kuti mpingo wachikhristu utakumana kale ndi chizunzo chachikulu. Koma chizunzo chimenechi sichinafooketse mpingowu kapena kuulepheretsa kukula. Choncho Mdyerekezi anagwiritsa ntchito njira ina ndipo njirayi anali ataigwiritsapo ntchito kufooketsera anthu ena. Malinga ndi zimene Petulo ananena, Satana pofuna kusokoneza anthu a Mulungu, anagwiritsa ntchito aphunzitsi onyenga amene anali ndi “maso odzala chigololo” ndiponso “mtima wophunzitsidwa kusirira kwa nsanje.” (2 Pet. 2:1-3, 14; Yuda 4) Masiku anonso, kalata yachiwiri ya Petulo ili ndi malangizo ogwira mtima otithandiza kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu.

2. Kodi chaputala 3 cha kalata yachiwiri ya Petulo chimanena za chiyani makamaka, ndipo tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

2 Petulo analemba kuti: “Ndikuona kuti n’koyenera kumakugalamutsani mwa kukukumbutsani pamene ndikali mumsasa uno, popeza ndikudziwa kuti ndatsala pang’ono kutuluka mumsasa wangawu . . . Choncho nthawi zonse ndidzachita chilichonse chotheka, kuti ndikadzachoka, mudzathe kukumbukira zinthu zimenezi.” (2 Pet. 1:13-15) Petulo ankadziwa kuti watsala pang’ono kumwalira koma ankafuna kuti anthuwo azidzakumbukirabe malangizo ake. Ndipotu malangizowa ndi mbali ya Baibulo moti tonsefe tikhoza kuwawerenga. Chaputala 3 cha kalata yachiwiri ya Petulo n’chothandiza kwambiri kwa ifeyo chifukwa chakuti chimanena za “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu lilipoli komanso za kuwonongedwa kwa miyamba ndi dziko lapansi zophiphiritsira. (2 Pet. 3:3, 7, 10) Kodi mu chaputala chimenechi Petulo akutipatsa malangizo otani? Kodi kutsatira malangizo amenewa kungatithandize bwanji kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?

3, 4. (a) Tchulani mawu amene Petulo ananena ndipo kodi iye anapereka chenjezo lotani? (b) Kodi tikambirana mfundo zitatu ziti?

3 Atafotokoza za kuwonongeka kwa dziko la Satana, Petulo anati: “Lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu.” (2 Pet. 3:11, 12) Ndi mawu amenewa, Petulo anafotokoza momveka bwino kuti anthu okhawo amene amachita chifuniro cha Yehova ndiponso kusonyeza makhalidwe abwino, ndi amene adzapulumutsidwa pa “tsiku lakubwezera.” (Yes. 61:2) N’chifukwa chake mtumwi Petulo ananenanso kuti: “Choncho inu okondedwa, pokhala odziwiratu zimenezi, chenjerani kuti musasochere [ndi aphunzitsi onyenga] pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulo, kutinso musagwe polephera kuchirimika kwanu.”​—2 Pet. 3:17.

4 Popeza Petulo anali mmodzi mwa “odziwiratu”zinthu, iye ankadziwa kuti m’masiku otsiriza Akhristu adzayenera kukhala tcheru kuti akhalebe ndi mtima wosagawanika. Kenako mtumwi Yohane anafotokoza chifukwa chake. Iye anaona m’masomphenya Satana atagwetsedwa kuchokera kumwamba ndipo anali ndi “mkwiyo waukulu” pa “osunga malamulo a Mulungu, ndi amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (Chiv. 12:9, 12, 17) Atumiki odzozedwa okhulupirika a Mulungu pamodzi ndi anzawo a “nkhosa zina” adzapambana. (Yoh. 10:16) Koma bwanji ifeyo aliyense payekha? Kodi tidzapitirizabe kukhala ndi mtima wosagawanika? Izi zikhoza kutheka ngati titayesetsa (1) kukhala ndi makhalidwe abwino (2) kukhalabe opanda thotho ndi opanda chilema mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu, (3) kukhala ndi maganizo oyenera tikakumana ndi mayesero. Tiyeni tikambirane mfundo zimenezi.

Khalani ndi Makhalidwe Abwino

5, 6. Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe ati, ndipo n’chifukwa chiyani pamafunika ‘kuyesetsa mwakhama’ kuti tikhale ndi makhalidwe amenewa?

5 Kumayambiriro kwa kalata yake yachiwiri, Petulo analemba kuti: “Inunso yesetsani mwakhama kuwonjezera pa chikhulupiriro chanu makhalidwe abwino, pa makhalidwe anu abwino muwonjezepo kudziwa zinthu, pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa chipiriro, pa chipiriro kudzipereka kwanu kwa Mulungu, pa kudzipereka kwanu kwa Mulungu chikondi cha pa abale, pa chikondi cha pa abale chikondi. Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo zisefukira, zidzakutetezani kuti musakhale ozirala kapena osabala zipatso pa kum’dziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.”​—2 Pet. 1:5-8.

6 Kunena zoona pamafunika ‘kuyesetsa mwakhama’ kuti tizichita zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, pamafunika khama kuti tizipezeka pa misonkhano yonse yampingo, kuti tiziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso kuti tiziphunzira patokha nthawi zonse. Pamafunikanso khama ndiponso kugawa bwino nthawi kuti Kulambira kwa Pabanja kuzichitika nthawi zonse ndiponso kuzikhala kosangalatsa komanso kopindulitsa. Koma ngati tili ndi chizolowezi chabwino pa nkhaniyi, kuchita zimenezi sikukhala kovuta makamaka ngati taona phindu lake.

7, 8. (a) Kodi anthu ena anena zotani pa nkhani ya Kulambira kwa Pabanja? (b) Kodi inuyo mukupindula bwanji ndi kulambira kwa pabanja?

7 Pa nkhani ya kulambira kwa pabanja mlongo wina analemba kuti: “Kulambira kwa pabanja kumatithandiza kuphunzira nkhani zosiyanasiyana.” Mlongo winanso ananena kuti: “Kunena zoona, sindinkafuna kuti phunziro la buku lithe. Ndinkalikonda kwambiri. Koma tsopano pamene tinayamba Kulambira kwa Pabanja, ndazindikira kuti Yehova amadziwa zimene timafunikira ndiponso nthawi yake.” M’bale wina, yemwe ndi mutu wa banja, anati: “Kulambira kwa pabanja kumatithandiza kwambiri. Timakhala ndi mwayi wophunzira zinthu zogwirizana ndi banja lathu ndipo zimenezi n’zosangalatsa kwambiri. Ine ndi mkazi wanga tikuona kuti panopa tikuyesetsa kusonyeza zipatso za mzimu kuposa kale ndipo tikusangalala kwambiri mu utumiki.” M’bale winanso anati: “Ana athu amafufuza nkhani zosiyanasiyana paokha, amaphunzira zambiri ndipo amasangalala kwambiri. Dongosolo limeneli latichititsa kukhulupirira kwambiri kuti Yehova amadziwa mavuto athu ndipo amayankha mapemphero athu.” Kodi umu ndi mmene inunso mumamvera pa nkhani ya kulambira kwa pabanja?

8 Musamalole zinthu zing’onozing’ono kukulepheretsani kuchita kulambira kwa pabanja. Mwamuna wina ndi mkazi wake anati: “Milungu inayi yapitayi, Lachinayi lililonse pankachitika kanthu kena komwe kankangotsala pang’ono kutilepheretsa kuchita phunziro koma sitinkalola kuti katilepheretse.” N’zoona kuti nthawi zina pangafunike kusintha tsiku limene mumachita Kulambira kwa Pabanja. Komabe muzionetsetsa kuti musachite kulephereratu mlungu wonse osachita Kulambira kwa Pabanja.

9. Kodi Yehova anathandiza bwanji Yeremiya ndipo kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chake?

9 Zimene zinachitikira mneneri Yeremiya ndi chitsanzo chabwino. Iye ankafunika kuthandizidwa mwauzimu ndi Yehova ndipo atathandizidwa anayamikira kwambiri. Thandizo limeneli linamulimbikitsa kuti apitirizebe kulalikira kwa anthu opanda chidwi. Iye anati: ‘Mawu a Mulungu ali ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga.’ (Yer. 20:8, 9) Zimenezi zinamuthandizanso kuti apirire mavuto amene anakumana nawo pa nthawi yovuta kwambiri pamene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa. Masiku ano tili ndi Baibulo lonse lathunthu. Tikamaliphunzira mwakhama ndiponso kuona zinthu mmene Mulungu amazionera, ifeyo mofanana ndi Yeremiya tidzatha kupirira polalikira, kukhala okhulupirika pamene tikukumana ndi mayesero ndiponso kukhala oyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu.​—Yak. 5:10.

Khalanibe ‘Opanda Thotho Ndiponso Opanda Chilema’

10, 11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhalebe ‘opanda thotho ndiponso opanda chilema,’ ndipo kodi zimenezi zimafuna chiyani?

10 Akhristufe tikudziwa kuti tili m’masiku otsiriza. Choncho sitidabwa tikamaona anthu m’dzikoli akutanganidwa ndi zinthu zimene Yehova amanyansidwa nazo monga dyera, chiwerewere ndiponso chiwawa. Mfundo imene Satana amayendera tingaifotokoze mwachidule kuti: ‘Ngati atumiki a Mulungu sangagonje chifukwa choopsezedwa, ndiye kuti mwina akhoza kugonja akasokonezedwa.’ (Chiv. 2:13, 14) Choncho, tiyenera kutsatira malangizo a Petulo akuti: “Chitani chilichonse chotheka kuti [Mulungu] adzakupezeni opanda thotho, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.”​—2 Pet. 3:14.

11 Mawu akuti “chitani chilichonse chotheka” akufanana ndi malangizo oyamba a Petulo akuti “yesetsani mwakhama.” N’zodziwikiratu kuti Yehova amene anauzira mtumwi Petulo kunena mawu amenewa amadziwa kuti timafunika kuchita khama kuti tikhalebe ‘opanda thotho ndiponso opanda chilema’ osadetsedwa ndi zonyansa za dziko la Satanali. Kuchita khama kumaphatikizapo kuteteza mtima wathu kuti usamatengeke ndi zilakolako zoipa. (Werengani Miyambo 4:23; Yakobe 1:14, 15.) Kumaphatikizaponso kukhalabe olimba potsutsidwa ndi anthu amene amadabwa ndi moyo wathu wachikhristu ndiponso amene ‘amatinyoza.’​—1 Pet. 4:4.

12. Kodi lemba la Luka 11:13 limatilimbikitsa bwanji?

12 Popeza ndife opanda ungwiro, zimativuta kwambiri kuchita zinthu zabwino. (Aroma 7:21-25) Komabe timadziwa kuti zinthu zingatiyendere bwino ngati titapempha kwa Yehova, amene amapereka mzimu wake woyera mowolowa manja kwa anthu amene amamupempha ndi mtima wonse. (Luka 11:13) Mzimu woyera umenewu amatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene amachititsa kuti Mulungu azitiyanja. Zimenezi zimatithandiza kuti tizipirira mayesero ndiponso mavuto amene timakumana nawo, omwe akupitiriza kuwonjezeka pamene tsiku la Yehova likuyandikira.

Mayesero Azikulimbikitsani

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto?

13 Popeza tili m’dziko loipali, tipitirizabe kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Koma m’malo moti tizikhumudwa ndi mavuto, ndi bwino tiziona kuti mavutowo akutipatsa mwayi wosonyeza kuti timakonda Mulungu. Tizionanso kuti ndi mwayi woti tilimbitse chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndiponso m’Mawu ake. Yakobe amene anali wophunzira wa Yesu analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwa kuti chikhulupiriro chanu choyesedwacho, chimabala chipiriro.” (Yak. 1:2-4) Tisaiwalenso kuti: “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero.”​—2 Pet. 2:9.

14. Kodi chitsanzo cha Yosefe chikukulimbikitsani bwanji inuyo?

14 Taganizirani za Yosefe mwana wa Yakobo amene anagulitsidwa ndi azichimwene ake enieni. (Gen. 37:23-28; 42:21) Kodi chikhulupiriro cha Yosefe chinafooka chifukwa cha nkhanza zimene anamuchitirazi? Kodi iye anakwiyira Mulungu chifukwa cholola kuti zimenezi zimuchitikire? Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Yosefe sanachite zimenezi. Komabe sikuti mavuto a Yosefe anathera pomwepa. Patapita nthawi, anamunamizira kuti ankafuna kugwirira mkazi ndipo anaikidwa m’ndende. Koma apanso, Yosefe sanasiye kukhala wodzipereka kwa Mulungu. (Gen. 39:9-21) M’malo mwake, iye analola mayeserowa kumulimbikitsa ndipo anadalitsidwa kwambiri.

15. Kodi chitsanzo cha Naomi chikutiphunzitsa chiyani?

15 Mwachibadwa, tikakumana ndi mavuto timakhumudwa kapenanso kuda nkhawa. N’kutheka kuti Yosefe anamvaponso choncho nthawi zina. Ndipo ndi mmenenso atumiki ena a Mulungu anamvera. Taganizirani za Naomi amene mwamuna wake ndiponso ana ake aamuna awiri anamwalira. Iye anati: “Musanditcha Naomi, munditche Mara; [kutanthauza “kuwawa”] pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.” (Rute 1:20, 21) Mpake kuti Naomi ankamva chonchi. Koma mofanana ndi Yosefe, iye sanafooke mwauzimu komanso anakhalabe ndi mtima wosagawanika. Ndipotu Yehova anadalitsa mayi wokhulupirikayu. (Rute 4:13-17, 22) Kuwonjezera pamenepa, m’Paradaiso amene akubwera, Mulungu adzathetsa mavuto onse obwera chifukwa cha Satana ndi dziko lake loipali. Pa nthawi imeneyo, “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”​—Yes. 65:17.

16. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya pemphero ndipo chifukwa chiyani?

16 Kaya tikumane ndi mavuto otani, kudziwa kuti Mulungu amatikonda nthawi zonse kumatithandiza kupirira. (Werengani Aroma 8:35-39.) Satana sangasiye kutifooketsa, koma adzalephera ngati tikhalabe “oganiza bwino,” ndiponso ngati ‘tikhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera.’ (1 Pet. 4:7) Yesu anati: “Khalani maso, muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:36) Onani kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “mopembedzera” limene ndi pemphero lochonderera modzichepetsa. Yesu anatilangiza kuti tiyenera kupemphera mopembedzera pofuna kutsindika mfundo yakuti, ino si nthawi yotayirira pa nkhani ya kukhala wovomerezeka kwa iyeyo ndi Atate wake. Anthu amene adzapulumuke pa tsiku la Yehova ndi okhawo amene ali ovomerezeka kwa iye.

Pitirizani Kutumikira Yehova Mwachangu

17. Ngati mumalalikira m’gawo lovuta kodi chitsanzo chabwino cha aneneri akale chingakuthandizeni bwanji?

17 Kuchita nawo zinthu zauzimu kumatitsitsimula. Izi zikutikumbutsa mawu a Petulo akuti: “Lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu.” (2 Pet. 3:11) Ina mwa ntchito zimenezi, ndi kulalikira uthenga wabwino ndipo imeneyi ndi ntchito yofunika kwambiri. (Mat. 24:14) N’zoona kuti m’madera ena ntchito yolalikira ingakhale yovuta mwina chifukwa chakuti anthu alibe chidwi kapena amatsutsa, kapenanso chifukwa chakuti amakhala otanganidwa ndi zochitika za tsiku ndi tsiku. Atumiki a Yehova akale ankakumananso ndi mavuto ngati amenewa. Koma iwo sanasiye utumiki wawo, m’malomwake ankalalikira uthenga wochokera kwa Mulungu “tsiku ndi tsiku.” (2 Mbiri 36:15, 16; werengani Yeremiya 7:24-26.) Kodi n’chiyani chinawathandiza kupirira? Iwo ankaona utumiki wawo mmene Yehova ankauonera osati mmene anthu ankauonera. Ankaonanso kuti ndi mwayi waukulu kutchedwa ndi dzina la Mulungu.​—Yer. 15:16.

18. Kodi ntchito yolalikira Ufumu idzalemekeza bwanji dzina la Mulungu mtsogolo?

18 Ifenso tili ndi mwayi wolengeza dzina la Yehova ndi cholinga chake. Taganizirani izi: Chifukwa cha ntchito yathu yolalikira, pa tsiku lalikulu la Yehova, adani a Mulungu sadzanena kuti sanamve za iye ndiponso za cholinga chake. Mofanana ndi Farao iwo adzadziwa kuti Yehova walowererapo. (Eks. 8:1, 20; 14:25) Pa nthawi imeneyinso, Yehova adzalemekeza atumiki ake chifukwa adzaonetsetsa kuti anthu onse adziwa kuti atumikiwo analidi kuimira iyeyo.​—Werengani Ezekieli 2:5; 33:33.

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufunitsitsa kugwiritsa ntchito bwino nthawi imene Yehova akuleza mtimayi?

19 Chakumapeto kwa kalata yake yachiwiri, Petulo analembera okhulupirira anzake kuti: “Muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.” (2 Pet. 3:15) Motero, tiyeni tipitirizebe kugwiritsa ntchito bwino nthawi imene Yehova akuleza mtimayi. Kodi tingachite zimenezi motani? Mwa kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu, kukhalabe ‘opanda thotho ndi opanda chilema,’ kukhala ndi maganizo abwino pa mavuto amene tikukumana nawo ndiponso mwa kukhala achangu pa ntchito za Ufumu. Tikamachita zimenezi, timakhala m’gulu la anthu amene adzalandira madalitso osatha amene “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zidzabweretse.​—2 Pet. 3:13.

Kodi mukukumbukira?

• Kodi tingatani kuti tikhale ndi makhalidwe abwino?

• Kodi tingatani kuti tikhalebe ‘opanda thotho ndiponso opanda chilema’?

• Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yosefe ndi Naomi?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti kugwira nawo ntchito yolalikira, ndi mwayi waukulu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni amunanu kuti inuyo ndiponso banja lanu mukhale ndi makhalidwe abwino?

[Zithunzi patsamba 10]

Kodi zimene Yosefe anachita pamene ankakumana ndi mavuto, zikutiphunzitsa chiyani?