Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwira Nawo Mokwanira Ntchito Yokolola Mwauzimu

Muzigwira Nawo Mokwanira Ntchito Yokolola Mwauzimu

Muzigwira Nawo Mokwanira Ntchito Yokolola Mwauzimu

‘Khalani ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.’​—1 AKOR. 15: 58.

1. Kodi Yesu anauza ophunzira ake kuti achite chiyani?

CHAKUMAPETO kwa chaka cha 30 C. E., pamene Yesu ankadutsa m’dera la Samariya anaima pachitsime cha mumzinda wa Sukari kuti apume. Pamenepo anauza ophunzira ake kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Apa Yesu sankanena za kukolola kwenikweni koma za kusonkhanitsa anthu a mtima wabwino amene angakhale otsatira ake. Mawu akewa akusonyeza kuti iye ankafuna kuti ophunzirawo achitepo kanthu. Panali ntchito yambiri yoti agwire koma nthawi inali yochepa kwambiri.

2, 3. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti tikukhala m’nthawi yokolola? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

2 Mawu a Yesu onena za kukolola ali ndi tanthauzo lapadera masiku ano. Tikukhala mu nthawi imene munda wa padziko lonse ‘n’ngofunika kukolola.’ Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amapatsidwa mwayi wophunzira choonadi chopatsa moyo ndipo anthu masauzande ambiri amabatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu. Ifeyo tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yokolola imene ikugwiridwa kwambiri masiku ano, yomwe ikuyang’aniridwa ndi Yehova Mulungu amene ndi Mwini zokolola. Kodi inuyo ‘mukuchita zochuluka’ pa ntchito yokololayi?​—1 Akor. 15:58.

3 Pa zaka zitatu ndi theka zimene Yesu anachita utumiki wake padziko lapansi, anakonzekeretsa ophunzira ake kugwira ntchito yokolola. M’nkhani ino tikambirana mfundo zitatu mwa mfundo zambiri zofunika zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake. Mfundo iliyonse ikusonyeza khalidwe lofunika kwambiri kwa ife pamene tikugwira ntchito yosonkhanitsa ophunzira a Yesu masiku ano. Tiyeni tikambirane makhalidwe amenewa limodzi ndi limodzi.

Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri

4. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chiti posonyeza ubwino wa kukhala wodzichepetsa?

4 Taganizirani izi: Ophunzira a Yesu angomaliza kumene kukangana kuti wamkulu ndani pakati pawo. Nkhope zawo zikuchita kuonekeratu kuti akangana ndiponso kuti akukayikirana. Ndiyeno Yesu akuitana mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo. Akuyang’ana mwana wamng’onoyo, ananena kuti: “Aliyense amene adzichepetsa ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu koposa mu ufumu wa kumwamba.” (Werengani Mateyo 18:1-4.) Mosiyana ndi dzikoli limene limaona kuti munthu ndi wofunika ngati ali ndi mphamvu, chuma ndiponso udindo, ophunzira a Yesu anafunika kudziwa kuti munthu amakhala wamkulu ngati ali ‘wodzichepetsa’ pamaso pa ena. Yehova akanawadalitsa ndiponso kuwagwiritsa ntchito ngati akanasonyeza kuti ndi odzichepetsadi.

5, 6. Kuti mugwire nawo mokwanira ntchito yokolola, n’chifukwa chiyani muyenera kukhala odzichepetsa? Perekani chitsanzo.

5 Masiku ano, anthu ambiri amatanganidwa kuti akhale olamulira, apeze chuma ndiponso udindo winawake. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amangokhala ndi nthawi yochepa yochita zinthu zauzimu ndipo ena sakhala nayo n’komwe. (Mat. 13:22) Mosiyana ndi anthu amenewa, anthu a Yehova ‘amadzichepetsa’ pamaso pa ena kuti Mwini zokolola aziwadalitsa ndiponso azisangalala nawo.​—Mat. 6:24; 2 Akor. 11:7; Afil. 3:8.

6 Taganizirani chitsanzo cha Francisco yemwe ndi mkulu ku South America. Ali mnyamata anasiya maphunziro a ku yunivesite n’cholinga choti azichita upainiya. Iye anati: “Nditatsala pang’ono kukwatira, ndikanatha kupeza ntchito yomwe ikanathandiza kuti banja lathu lizikhala ndi ndalama zambiri. Koma tinasankha zokhala moyo wosalira zambiri kuti tipitirize kuchita utumiki wa nthawi zonse. Patapita nthawi tinakhala ndi ana ndipo udindo wathu unakula. Koma Yehova anatithandiza kuti tipitirizebe kukhala moyo wosalira zambiri.” Pomaliza Francisco anati: “Kwa zaka zoposa 30, ndakhala ndi mwayi wotumikira monga mkulu kuwonjezera pa maudindo ena apadera. Sitidandaula ngakhale pang’ono kuti tinasankha moyo wosalira zambiri.”

7. Fotokozani zimene munachita potsatira mfundo ya pa Aroma 12:16.

7 Mukamapewa ‘kudzikweza’ m’dzikoli koma n’kumakhala ndi mtima wodzichepetsa, nanunso mungayembekezere kudalitsidwa kwambiri ndiponso kuchita utumiki wosiyanasiyana pa ntchito yokololayi.​—Aroma 12:16; Mat. 4:19, 20; Luka 18:28-30.

Khama Limabweretsa Madalitso

8, 9. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu la matalente. (b) Kodi fanizo limeneli ndi lolimbikitsa kwenikweni kwa anthu ati?

8 Khama ndi lofunikanso kuti tigwire nawo mokwanira ntchito yokololayi. Yesu anasonyeza kuti zimenezi n’zoona m’fanizo la matalente. * Fanizo limeneli ndi lonena za munthu wina yemwe anapita kudziko lina koma anasiyira akapolo ake chuma chake. Kapolo woyamba anamupatsa matalente asanu, wachiwiri matalente awiri ndipo wachitatu anamupatsa talente imodzi. Munthuyo atapita, kapolo woyamba ndi wachiwiri uja anagwira ntchito mwakhama moti nthawi yomweyo ‘anachita malonda’ ndi matalente amene anapatsidwawo. Koma kapolo wachitatu uja anali “waulesi.” Iye anakwirira pansi talente yake. Munthu uja atabwera anapereka mphoto kwa kapolo woyamba ndi wachiwiri uja mwa kuwapatsa udindo woyang’anira “zinthu zochuluka.” Koma analanda talente imene anapatsa kapolo wachitatu uja ndipo anamuthamangitsa.​—Mat. 25:14-30.

9 Mosakayikira, inuyo muli ndi cholinga chotsanzira akapolo awiri akhama a m’fanizo la Yesu ndipo mukufuna kugwira nawo mokwanira ntchito yopanga ophunzira. Koma kodi mungatani ngati panopa mukungochita zochepa chifukwa cha mmene zinthu ziliri pa moyo wanu? Mwina chifukwa cha mavuto a zachuma, mumafunika kugwira ntchito maola ambiri kuti mupeze zofunika za banja lanu. Mwinanso ndinu wokalamba ndipo thupi lanu ndi lofooka. Ngati umu ndi mmene zinthu ziliri pa moyo wanu, ndiye kuti mfundo za m’fanizo la matalente zingakulimbikitseni zedi.

10. Kodi munthu wa m’fanizo la matalente uja anasonyeza bwanji kuti ankadziwa zimene kapolo aliyense angakwanitse, ndipo kodi zimenezi zikukulimbikitsani bwanji?

10 Onani kuti m’fanizoli, munthu uja ankadziwa zimene kapolo aliyense angakwanitse kuchita. Umboni wake ndi wakuti, popereka matalentewo “aliyense anam’patsa malinga ndi luso lake.” (Mat. 25:15) Kapolo woyamba anapindula ndalama zambiri kuposa wachiwiri, ndipo izi n’zimene munthu uja ankayembekezera. Koma munthuyo anadziwa kuti akapolo awiri onsewa anachita khama ndipo anawayamikira pouza aliyense kuti ndi kapolo “wabwino ndi wokhulupirika” komanso anawapatsa mphoto zofanana. (Mat. 25:21, 23) Mofanana ndi zimenezi Yehova Mulungu, yemwe ndi Mwini zokolola, amadziwa kuti zimene mungathe kuchita pomutumikira, zimadalira mmene zinthu ziliri pa moyo wanu. Iye nthawi zonse amaona khama lanu lochokera pansi pa mtima limene mumasonyeza pomutukira ndipo adzakupatsani mphoto yoyenerera.​—Maliko 14:3-9; werengani Luka 21:1-4.

11. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuchita khama ngakhale pamene zinthu pa moyo sizili bwino, kumakhala ndi zotsatira zabwino.

11 Chitsanzo cha mlongo wina dzina lake Selmira yemwe amakhala ku Brazil, chikusonyeza kuti kukhala wa khama potumikira Mulungu sikudalira kuti zinthu zikhale bwino pa moyo wathu. Zaka 20 zapitazo mwamuna wa Selmira anawomberedwa ndi mbava n’kumwalira ndipo anamusiyira ana atatu. Selmira ankagwira ntchito ya pakhomo kwa munthu wina kwa maola ambiri ndipo ankayenda movutikira chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, iye anaganiza zosintha zinthu zina ndi zina pa moyo wake kuti achite upainiya. Kenako ana ake awiri anayambanso upainiya. Selmira anati: “Pa zaka zimene zapitazi ndaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 20 ndipo panopa anthu amenewa ali ngati anthu a m’banja lathu. Ndimasangalala kwambiri chifukwa chakuti anthu amenewa amandikonda ndiponso ndi anzanga. Zimenezi ndi zinthu za mtengo wapatali kwambiri moti sungazigule ndi ndalama.” Apatu Mwini wa zokolola wadalitsa khama la Selmira.

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife akhama pa ntchito yolalikira?

12 Ngati mukulephera kuthera nthawi yambiri mu utumiki chifukwa cha mmene zinthu ziliri pa moyo wanu, mukhoza kuwonjezera zimene mumachita pa ntchito yotuta mwa kuyesetsa kuti utumiki wanu uzikhala wobala zipatso. Mukamatsatiradi mfundo zothandiza zimene timaphunzira pa Msonkhano wa Utumiki mudzakulitsa luso lanu lophunzitsa ndiponso mudzapeza njira zatsopano zolalikirira. (2 Tim. 2:15) Komanso ngati n’zotheka, mungasinthe nthawi imene mumachitira zinthu zina kapenanso kusiya kuchita zinthu zina zosafunika kwenikweni, n’cholinga chakuti nthawi zonse muzilalikira ndi mpingo.​—Akol. 4:5.

13. Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti tikhalebe akhama?

13 Kumbukirani kuti munthu amachita khama chifukwa chokonda ndiponso kuyamikira Mulungu. (Sal. 40:8) M’fanizo la Yesu lija, kapolo wachitatu ankaopa kwambiri mbuye wake ndipo ankamuona ngati ndi wofuna zambiri ndiponso wosaganizira ena. Chifukwa cha zimenezi kapoloyu anakumbira pansi talente yake m’malo moigwiritsa ntchito kuti awonjezere chuma cha mbuye wake. Kuti ifeyo tipewe mtima wamphwayi ndiponso wosayamikira umene kapolo wachitatuyu anali nawo, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova yemwe ndi Mwini zokolola. Choncho muzipatula nthawi yophunzira ndiponso kusinkhasinkha makhalidwe abwino a Yehova monga chikondi, kuleza mtima ndi chifundo. Mukamachita zimenezi, mudzachita zonse zimene mungathe pomutumikira ndi mtima wanu wonse.​—Luka 6:45; Afil. 1:9-11.

“Mukhale Oyera”

14. Kodi amene akufuna kugwira nawo ntchito yokolola ayenera kukhala otani?

14 Pogwira mawu Malemba achiheberi, mtumwi Petulo anafotokoza zimene Mulungu amafuna kwa atumiki ake a padziko lapansi kuti: “Motsanzira Woyerayo amene anakuitanani; inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse, chifukwa malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Pet. 1:15, 16; Lev. 19:2; Deut. 18:13) Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti anthu ogwira ntchito yokolola ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso oyera mwauzimu. Tikhoza kukwaniritsa zimenezi mwa kuchita zinthu zimene zingatichititse kukhala oyera. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingachite zimenezi mothandizidwa ndi mawu a Mulungu amene ndi choonadi.

15. Kodi choonadi cha m’Mawu a Mulungu chili ndi mphamvu yotani pamoyo wathu?

15 Mawu a Mulungu omwe ndi choonadi amayerekezedwa ndi madzi amene amayeretsa. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti, mpingo wa Akhristu odzozedwa ndi woyera pamaso pa Mulungu ngati mkwatibwi woyera wa Khristu. Khristuyo anausambitsa “ndi madzi mwa mawuwo. Anatero . . . , kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.” (Aef. 5:25-27) Pa nthawi ina, Yesu ananena kuti mawu a Mulungu amene ankalalikira ali ndi mphamvu yoyeretsa. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndalankhula kwa inu.” (Yoh. 15:3) Choncho, choonadi cha m’Mawu a Mulungu chili ndi mphamvu yotithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso oyera mwauzimu. Ngati tilola choonadi cha Mulungu kutiyeretsa m’njira imeneyi, kulambira kwathu kudzakhala kovomerezeka pamaso pake.

16. Kodi tingatani kuti tikhale ndi makhalidwe abwino ndiponso tisadetsedwe mwauzimu?

16 Choncho, kuti tiloledwe kugwira nawo ntchito yokolola, poyamba tiyenera kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kusiya kuchita zinthu zonse zimene zingatidetse mwauzimu. Kuti tikhalebe oyenera kugwira nawo ntchito imeneyi, tiyenera kupereka chitsanzo chabwino potsatira mfundo zapamwamba za Yehova. (Werengani 1 Petulo 1:14-16.) Anthufe nthawi zonse timayesetsa kukhala aukhondo, choncho tiyeneranso kulola choonadi cha m’Mawu a Mulungu kutiyeretsa. Tingachite zimenezi mwa kuwerenga Baibulo ndiponso kupezeka pa misonkhano. Timafunikanso kuchita khama kugwiritsa ntchito malangizo ochokera kwa Mulungu. Kuchita zimenezi, kudzatithandiza kulimbana ndi chibadwa chathu chofuna kuchimwa ndiponso zinthu zodetsa za m’dzikoli. (Sal. 119:9; Yak. 1:21-25) N’zolimbikitsa kudziwa kuti mawu a Mulungu omwe ndi choonadi ‘angatisambitse kukhala oyera’ ngakhale titachita tchimo lalikulu.​—1 Akor. 6:9-11.

17. Kuti tikhalebe oyera, kodi tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo ati?

17 Kodi mumalola kuti mawu a Mulungu omwe ndi choonadi azikuyeretsani? Mwachitsanzo, kodi mumatani mukalandira malangizo okhudza kuopsa kwa zosangalatsa zoipa zimene zafala m’dzikoli? (Sal. 101:3) Kodi mumapewa kucheza kwambiri ndi anzanu a kusukulu kapena a kuntchito omwe si Akhristu? (1 Akor. 15:33) Kodi mukuyesetsa ndi mtima wonse kulimbana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kukhala oyera pa maso pa Yehova? (Akol. 3:5) Kodi mumapewa kulowerera ndale za m’dzikoli ndiponso masewera amene amalimbikitsa mpikisano komanso kukonda dziko lako?​—Yak. 4:4.

18. Kodi kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kukhala oyera mwauzimu kungatithandize bwanji kubala zipatso pa ntchito yathu yokolola?

18 Mukamamvera mokhulupirika pa nkhani ngati zimenezi, mudzadalitsidwa kwambiri. Yesu anayerekezera ophunzira ake odzozedwa ndi nthambi za mpesa. Iye anati: “Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso [Atate wanga] amaichotsa, ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira, kuti ibale zipatso zambiri.” (Yoh. 15:2) Mukamalola kuyeretsedwa ndi choonadi cha m’Baibulo, mudzabala zipatso zambiri.

Madalitso Amene Mungapeze Panopa Ndiponso M’tsogolo

19. Kodi ophunzira a Yesu anadalitsidwa bwanji chifukwa cha khama lawo pa ntchito yokolola?

19 Ophunzira okhulupirika amene anatsatira malangizo a Yesu, analimbikitsidwa ndi mzimu woyera pa Pentekosite mu 33 C.E. kuti akhale mboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Ena mwa ophunzirawa ankatumikira m’bungwe lolamulira. Ena ankatumikira ngati amishonale, oyang’anira oyendayenda, ndipo onsewa anathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Anthu amenewa anadalitsidwa kwambiri ndipo anathandiza anthu ambiri kukhala osangalala.

20. (a) Kodi inuyo mwapeza madalitso otani chifukwa chogwira nawo mokwanira ntchito yokolola mwauzimu? (b) Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Tikamakhala odzichepetsa, kuchita khama ndiponso kutsatira mfundo zapamwamba za m’Mawu a Mulungu, tidzapitiriza kugwira nawo mokwanira ndiponso ndi mtima wathu wonse ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika panopa. Anthu ena amavutika ndiponso kukhumudwa chifukwa chofuna chuma ndi moyo wofuna zinthu zosangalatsa m’dzikoli, koma atumiki a Mulungufe timakhala osangalaladi ndiponso okhutira. (Sal. 126:6) Komanso chofunika kwambiri n’chakuti, ‘kugwiritsa ntchito kwathu sikupita pachabe mwa Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Yehova Mulungu yemwe ndi Mwini zokolola adzatipatsa madalitso osatha chifukwa cha ‘ntchito yathu ndi chikondi chimene timasonyeza pa dzina lake.’​—Aheb. 6:10-12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Fanizo la matalenteli kwenikweni limanena za mmene Yesu amachitira zinthu ndi Akhristu odzozedwa, koma lilinso ndi mfundo zimene zingathandize Akhristu onse.

Kodi Mukukumbukira?

Mukamayesetsa kugwira nawo mokwanira ntchito yokolola . . .

• n’chifukwa chiyani kukhala wodzichepetsa n’kofunika?

• kodi mungatani kuti muzichita khama?

• n’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso oyera mwauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Kudzichepetsa kungatithandize kukhala ndi moyo wosalira zambiri n’kumaika patsogolo zinthu zokhudza Ufumu