Thandizani Ana Anu Kuti Azikonda Kuwerenga ndi Kuphunzira
Thandizani Ana Anu Kuti Azikonda Kuwerenga ndi Kuphunzira
KUTHANDIZA ana anu kuti azikonda kuwerenga ndiponso kuphunzira, ndi njira imodzi yofunika kwambiri powathandiza kuti akhale ndi tsogolo labwino. Ndipotu kuwerenga ndiponso kuphunzira n’kosangalatsa kwambiri. Anthu ambiri amakumbukira kuti ali ana, makolo awo ankawawerengera. Munthu akamawerenga amasangalala ndipo zotsatira zakenso zimakhala zosangalatsa. Zimenezi ndi zoona makamaka kwa atumiki a Mulungu chifukwa kukula mwauzimu kumadalira kuphunzira Baibulo. Bambo wina yemwe ndi Mkhristu anati: “Zinthu zimene timakonda kwambiri, ndi zokhudza kuwerenga ndi kuphunzira.”
Ana anu akakhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira akhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Sal. 1:1-3, 6) Ngakhale kuti kuwerenga si kofunika kuti munthu adzapulumuke, Baibulo limati kuwerenga kungatithandize kwambiri kuti tidalitsidwe mwauzimu. Mwachitsanzo, lemba la Chivumbulutso 1:3 limati: “Wosangalala ali iye amene awerenga mokweza, ndi iwo amene akumva mawu a ulosi umenewu.” Mtumwi Paulo mouziridwa analangiza Timoteyo kufunika koika maganizo pa zimene akuphunzira. Iye anati: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo.” N’chifukwa chiyani Timoteyo anafunika kuchita zimenezi? ‘Kuti kupita kwake patsogolo kuonekere kwa anthu onse.’—1 Tim. 4:15.
Komabe, kuwerenga ndi kuphunzira pazokha sizingapindulitse munthu. Anthu ambiri amene ali ndi luso limeneli amakonda kuchita zinthu zina zosapindulitsa kwenikweni. Ndiyeno kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azikonda kuphunzira zinthu zopindulitsa?
Asonyezeni Chikondi Ndipo Muzikhala Chitsanzo
Ana amasangalala kwambiri ndi kuphunzira ngati akusonyezedwa chikondi pophunzirapo. Owen ndi mkazi wake Claudia, omwe ndi Akhristu anafotokoza za ana awo kuti: “Iwo ankayembekezera mwachidwi nthawi yophunzira. Ankaona kuti ndi otetezeka ndipo ankakhala omasuka kwambiri. Iwo ankaona kuti nthawi ya phunziro ndi imene amasonyezedwa chikondi kwambiri.” Ngakhale anawo atafika zaka za pakati pa 13 ndi 19, zomwe zimakhala zaka zovuta kwambiri, chikondi chimene amasonyezedwa pophunzira chimawathandiza kuti azikonda kuphunzira. Ana a Owen ndi Claudia panopa akuchita upainiya ndipo akusangalala kwambiri chifukwa choti anathandizidwa kukonda kuwerenga ndi kulemba.
Kuwonjezera pa chikondi chinthu china chofunika kwambiri, ndi chitsanzo cha makolo. Ana amene nthawi zambiri amaona makolo awo akuwerenga ndi kuphunzira, nawonso amayamba kuchita zinthu zimenezi ndipo amaona kuti n’zofunika pa moyo wawo. Koma kodi inuyo monga kholo mungakhale bwanji chitsanzo ngati mwachibadwa simukonda kuwerenga? Mungafunike kusintha mmene mumaonera kuwerenga, n’kuyamba kuona kuti ndi kofunika. (Aroma 2:21) Ngati kuwerenga kuli mbali yaikulu pa zochita zanu za tsiku ndi tsiku, ndiye kuti ana anu azikondanso kuwerenga. Mukamachita khama makamaka pa kuwerenga Baibulo, kukonzekera misonkhano ndiponso kuchita phunziro la banja, ana anu adzaona kuti zinthu zimenezi n’zofunika.
Choncho, chikondi ndiponso chitsanzo chanu n’zofunika kwambiri pamene mukulimbikitsa ana anu kuti azikonda kuwerenga. Koma, kodi ndi njira ziti zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezi?
Thandizani Ana Anu Kuti Azikonda Kuwerenga
Kodi ndi zinthu ziti zofunika zimene zingathandize ana anu kuti azikonda kuwerenga? Apezereni mabuku adakali ang’ono. M’bale wina yemwe ndi mkulu mumpingo, amene makolo ake anamuthandiza kuti azikonda kuwerenga, anati: “Muzionetsetsa kuti ana anu ali ndi mabuku awoawo kuyambira adakali ang’ono. Mukamachita zimenezi, anawo azikonda kwambiri kuwerenga pamoyo wawo.” Ana ambiri asanadziwe kuwerenga, amakhala atayamba kale kukonda mabuku ofotokoza Baibulo monga lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Mukamawawerengera ana anu mabuku amenewa, mumawathandiza kudziwa chilankhulo ndiponso “zochitika zauzimu ndi mawu auzimu.”—1 Akor. 2:13.
Muziwawerengera mokweza nthawi zonse. Khalani ndi chizolowezi chowerengera ana anu tsiku ndi tsiku. Kuchita zimenezi kumawaphunzitsa kutchula bwino mawu ndiponso kumawathandiza kukhala ndi chizolowezi chowerenga. Chinthu china chofunikanso, ndi mmene mumawerengera. Mukamawerenga mwaumoyo, ana anu aziwerenganso mwaumoyo. Mukamachita zimenezi, ana anu azikupemphani kuti muwawerengere nkhani imodzimodziyo mobwerezabwereza. Akakupemphani muziwawerengera. Kenako, azifuna kuti muwawerengere nkhani zina zatsopano. Koma samalani kuti musawerengere ana anuwo pamene sakufuna. Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Iye ankaphunzitsa anthu mogwirizana ndi “mmene anakhozera kumva.” (Maliko 4:33) Ngati simukukakamiza ana anu kuwerenga, aziyembekezera mwachidwi nthawi yowerengayo ndipo mudzakwanitsa cholinga chanu chowathandiza kuti azikonda kuwerenga.
Muziwalimbikitsa kutengapo mbali ndiponso muzikambirana zimene mukuwerenga. Mudzasangalala kwambiri kuona kuti pasanapite nthawi yaitali ana anu adzayamba kudziwa mawu ambiri, kuwatchula bwino ndiponso kumvetsa matanthauzo ake. Kukambirana zimene mwawerenga kungawathandize kupita patsogolo mofulumira. Buku lina lofotokoza mmene mungathandizire ana kuti aziwerenga bwino linati, kukambirana ndi ana kumathandiza kuti “aphunzire mawu amene akadzayamba kuwerenga, azidzawazindikira ndiponso kuwamvetsa.” Bukuli linatinso: “Kwa ana ang’ono amene ubongo wawo ukuphunzira kuwerenga, kulankhulana n’kofunika kwambiri ndipo mukamalankhula nawo zinthu zofunika kwambiri . . . ubongowo umaphunzira msanga.”
Muziuza ana anu kuti akuwerengereni, ndipo muziwalimbikitsa kufunsa mafunso. Mukhoza kuwafunsa funso linalake n’kupereka mayankho angapo kuti anawo asankhepo lolondola. Mukamatero, iwo amadziwa kuti mabuku angawathandize kuphunzira zambiri ndiponso kuti mawu amene akuwerenga amakhala ndi matanthauzo. Kuphunzitsa ana mwa njira imeneyi n’kofunika kwambiri makamaka ngati zimene mukuwerengazo ndi zochokera m’Baibulo lomwe ndi buku lofunika kwambiri kuposa buku lililonse.—Aheb. 4:12.
Komabe, musaiwale kuti kuwerenga n’kovuta. Kuti munthu adziwe kuwerenga bwinobwino, pamatenga nthawi ndithu ndiponso pamafunika kuwerenga pafupipafupi. * Choncho kuti mulimbikitse ana anu kudziwa kuwerenga, muyenera kumawayamikira nthawi zonse. Kuchita zimenezi, kudzawathandiza kuti azikonda kuwerenga.
Kuwerenga N’kofunika Ndipo Kumasangalatsa
Kuthandiza ana anu kaphunziridwe koyenera, kumawathandiza kuti azikhala ndi cholinga powerenga. Kuphunzira kumaphatikizapo kudziwa mfundo ndiponso kuona kugwirizana kwake ndi mfundo zina. Kumafunanso kuti munthu azisanja bwino mfundo m’maganizo, kuzikumbukira ndiponso kuzigwiritsa ntchito. Mwana akadziwa kaphunziridwe koyenera n’kuzindikiranso ubwino wa kuphunzira, amaona kuti kuphunzirako n’kofunika ndiponso kosangalatsa.—Mlal. 10:10.
Aphunzitseni zinthu zimene zingawathandize kuphunzira. Kuchita zinthu monga Kulambira kwa Pabanja, kukambirana lemba la tsiku ndiponso
zinthu zina, kumathandiza kuti ana anu akhale ndi luso lophunzira. Kukhazikika pamalo amodzi ndiponso kuganizira kwambiri nkhani inayake kwa kanthawi, kungathandize ana kuti aziika maganizo awo pa zimene akuphunzira ndipo izi n’zofunika kwambiri kuti aphunzire zinthu. Kuwonjezera pamenepo, mungauze mwana wanu kuti akufotokozereni mmene nkhani imene waphunzira ikugwirizanirana ndi zimene akudziwa kale. Izi zingamuthandize kuti azitha kuyerekezera zinthu. Apo ayi, mungapemphe mwana wanuyo kuti afotokoze mwachidule mfundo zazikulu za nkhani imene wawerenga m’mawu akeake. Zimenezi zingamuthandize kumvetsa bwino tanthauzo la zimene wawerengazo ndi kuzikumbukira. Mungawaphunzitsenso kuti akamaliza kuwerenga nkhani ina yake, azibwereza mfundo zazikulu. Imeneyi ndi njira inanso yothandiza kuti azikumbukira zimene awerengazo. Ngakhale ana angaphunzitsidwenso kuti azilemba manotsi achidule paphunziro kapena kumisonkhano ya mpingo. Zimenezi zingathandize kuti maganizo awo asamayendeyende akamaphunzira. Njira zophunzirira zimenezi, zingathandize kuti kuphunzira kukhale kosangalatsa ndiponso kwaphindu kwa inuyo komanso ana anu.Muzionetsetsa kuti malo ophunzirira ndi abwino. Munthu savutika kuika maganizo pa zimene akuphunzira ngati chipinda chimene akuphunzirira chili ndi mpweya wabwino, n’chowala bwino, chopanda phokoso ndiponso ngati zinthu zaikidwa bwino m’chipindacho. Chinthu china chofunika kwambiri ndi mmene makolo amaonera nkhani ya kuphunzira. Mayi wina anati: “Nthawi zonse makolo afunika kumapeza nthawi yowerenga ndiponso kuphunzira ndipo asamaphonye kuchita zimenezi. Zimenezi zimathandiza kuti ana awo azidziwa nthawi yoyenera kuchita zinthu. Amadziwa kuti zinthu izi ndiyenera kuzichita pa nthawi yakutiyakuti.” Makolo ambiri salola kuti zinthu zina zizichitika pa nthawi yophunzira. Munthu wina anena kuti kuchita zimenezi kumathandiza ana kukhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira.
Sonyezani kufunika kwa zimene akuphunzira. Muyeneranso kuthandiza ana anu kuti aziona ubwino wa zimene akuphunzira. Ana akamagwiritsa ntchito zinthu zimene aphunzira amaona kuti kuphunzira n’kopindulitsa. M’bale wina wachinyamata anati: “Kuwerenga zinthu zimene sindikuona phindu lake, kumandivuta. Koma ndikaona kuti mfundo zake zingandithandize, ndimayesetsa kuti ndimvetse bwino nkhaniyo.” Achinyamata akaona kuti kuphunzira kungawathandize, amaika maganizo pa zimene akuphunzirazo. Iwo amayembekezera mwachidwi nthawi yophunzira ngati mmene amachitira ndi kuwerenga.
Madalitso Osaneneka
Kuthandiza ana anu kuti azikonda kuwerenga, kumabweretsa madalitso osaneneka moti n’zosatheka kutchula onse m’nkhani ino. Ena mwa madalitso ake ndi akuti ana amakhoza bwino kusukulu, amagwira bwino ntchito, amagwirizana ndi anzawo, amamvetsa bwino mmene zinthu zikuyendera m’dzikoli, amakondana kwambiri ndi makolo awo ndiponso amasangalala akamawerenga ndi kuphunzira zinthu.
Koposa zonse, kukonda kuphunzira kungachititse kuti ana anu akhale anthu oopa Mulungu. Kungatsegulenso maganizo ndi mitima yawo kuti adziwe “bwino lomwe m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama” kwa choonadi cha m’Baibulo. (Aef. 3:18) Kunena zoona, pali zinthu zambiri zimene makolo achikhristu ayenera kuphunzitsa ana awo. Makolo akamapatula nthawi kusamalira ana awo ndiponso akamachita zonse zimene angathe kuwathandiza kuyambira ali ana, amayembekezera kuti anawo akadzakula adzasankha kukhala olambira Yehova. Kuthandiza ana kuti azikonda kuphunzira, kumathandiza kuti anawo akule mwauzimu ndiponso kuti akhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Choncho, mulimonsemo pempherani kwa Yehova kuti adalitse khama lanu pamene mukuyesetsa kuphunzitsa ana anu kuti azikonda kuwerenga ndiponso kuphunzira.—Miy. 22:6.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 14 Pali ana ena amene ali ndi vuto lolephera kugwira zinthu msanga. Ana oterewa amavutika kuwerenga ndiponso kuphunzira. Kuti mudziwe mmene makolo angawathandizire, onani Galamukani! ya March 8, 1997, tsamba 25.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 26]
Kuti Ana Anu Azikonda Kuwerenga . . .
• Apezereni mabuku
• Muziwawerengera mokweza
• Muziwalimbikitsa kutengapo mbali
• Muzikambirana zimene mukuwerenga
• Muziuza ana anu kuti akuwerengereni
• Muzilimbikitsa ana anu kufunsa mafunso
Kuti Ana Azikonda Kuphunzira . . .
• Mukhale chitsanzo chabwino
• Aphunzitseni zinthu monga:
○ kuika maganizo pa zimene akuphunzira
○ kuyerekezera zinthu
○ kufotokoza mwachidule mfundo zikuluzikulu
○ kubwereza mfundo zazikulu
○ kulemba manotsi achidule
• Muzionetsetsa kuti malo ophunzirira ndi abwino
• Muziwasonyeza kufunika kwa zimene akuphunzira