Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa.
• Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kuti adzathe kudziimira paokha?
Muzipereka chitsanzo chabwino kwa mwana wanu. (Yoh. 13:15) Muzidziwa zimene sangakwanitse. Anawo akamakula makolo ayenera kuwaphunzitsa kuchita zinthu zina monga kusamalira thupi lawo, kuchita zinthu pa nthawi yake ndiponso kuchita ntchito za kusukulu. Muziwapatsa malangizo omveka bwino owathandiza kukwaniritsa udindo wawo.—5/1, , masamba 19-20.
• N’chifukwa chiyani Mulungu sanalange Aroni atapanga fano la Mwana wa ng’ombe?
Aroni anaswa lamulo la Mulungu loletsa kulambira mafano. Koma pemphero la Mose linagwira ntchito “mwamphamvu kwambiri” pa nkhani ya Aroni. (Yak. 5:16) Aroni anali wokhulupirika kwanthawi yaitali. Anthu anamukakamiza Aroni kuti awapangire fano koma kenako anasonyeza kuti iye kwenikweni sanagwirizane ndi kulambira fanoli, chifukwa iye limodzi ndi ana a Levi anakhala ku mbali ya Yehova. (Eks. 32:25-29)—5/15, tsamba 21.
• Kodi ku Ofiri kumene Baibulo limanena kuti kunkachokera golide wabwino kwambiri kunali kuti?
Pofuna kubweretsa golide kuchokera ku Ofiri, Solomo anapanga zombo ku Ezioni Geberi. (1 Maf. 9:26-28) Doko limeneli linali mphepete mwa Nyanja Yofiira cha kudera limene masiku ano limatchedwa Aqaba ndi Elat. Choncho doko la Ofiri liyenera kuti linali ku Arabia, pafupi ndi Nyanja Yofiira, apo ayi linali kugombe lina ku Africa kapena ku India.—6/1, tsamba 15.
• Kodi mafuta a Basamu wa ku Gileadi amaimira chiyani? (Yer. 8:22)
Mafuta a Basamu anali onunkhira kwambiri opangidwa kuchokera ku utomoni wa zomera zosiyanasiyana zopezeka m’madera ambiri ku Gileadi, cha kum’mawa kwa mtsinje wa Yordano. Chifukwa chakuti mafutawa ankagwiritsidwanso ntchito ngati mankhwala ankawapaka pa mabala. Aisiraeli akanayenera kuzindikira mmene moyo wawo wauzimu unalili, n’kupeza thandizo koma sanachite zimenezi. (Yer. 8:9)—6/1, masamba 21-22.
• Kodi Mkhristu angatani ngati mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo?
Ngati mwamuna kapena mkazi wochimwiridwayo akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, palibe chifukwa chodziimbira mlandu chifukwa cha khalidwe lachiwerewere la mnzakeyo. Mulungu amamva kulira kwanu chifukwa cha kusakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wanu. Iye amadziwa kuti mukufunika kutonthozedwa ndi kulimbikitsidwa. Iye angakulimbikitseni kudzera mwa Akhristu anzanu.—6/15, masamba 30-31.
• Kodi mungathandize bwanji munthu amene akudwala?
Muzimvetsera akamalankhula. (Mlal. 3:1, 7) Muzimumvera chisoni komanso muzichita zinthu momuganizira. (Aroma 12:15) Muzimulimbikitsa ndiponso muzimuthandiza. (Akol. 4:6; 1 Yoh. 3:18) Musamutaye. (Miy. 17:17)—7/1, masamba 10-13.
• Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu alibe chiyambi?
M’pemphero lake, Mose anasonyeza kuti Mulungu alibe chiyambi. (Sal. 90:2) Choncho, m’pomveka kuti Mulungu yekha ndi amene amadziwika ndi dzina laulemu lakuti “Mfumu yosatha.” (1 Tim. 1:17)—7/1, tsamba 28.
• Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azikonda kuwerenga?
Kuwasonyeza chikondi ndiponso kuwapatsa chitsanzo chabwino kungathandize kuti ana anu azikonda kuwerenga. Komanso muziwapezera mabuku. Muziwawerengera mokweza. Muziwalimbikitsa kutengapo mbali ndiponso muzikambirana zimene mukuwerenga. Muziuza ana anu kuti akuwerengereni ndiponso muziwalimbikitsa kufunsa mafunso.—7/15, tsamba 26.
• N’chifukwa chiyani Yesu atamva kuti Lazaro, yemwe anali mnzake, akudwala sanapite msanga kukamuchiritsa?
Pa nthawi imene Yesu ankafika n’kuti patatha masiku anayi kuchokera pamene Lazaro anamwalira. Chifukwa chodikira, Yesu anapereka mpata wochitira umboni za Atate wake. Izi zinachititsa kuti anthu ambiri akhale okhulupirira. (Yoh. 11:45)—8/1, masamba 14-15
• Kodi “misanje” kapena kuti malo opatulika olambirira inali chiyani?
Nthawi zambiri misanje inali malo a pamwamba paphiri kapena malo ena amene anthu ankalambira milungu yonyenga. Nthawi zina ankamangapo maguwa a nsembe, zipilala zopatulika, mizati ndi zinthu zina kuti azizigwiritsa ntchito pa kupembedza kumene Mulungu sankagwirizana nako. (Num. 33:52)—8/1, tsamba 23.