Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Dipo Limatipulumutsira

Mmene Dipo Limatipulumutsira

Mmene Dipo Limatipulumutsira

“Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha; wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.”​—YOH. 3:36.

1, 2. Tchulani chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti magazini ya Zion’s Watch Tower, iyambe kufalitsidwa.

“MAGAZINI yachinayi ya Nsanja ya Olonda imene inatuluka mu October 1879 inafotokoza kuti palibe munthu aliyense amene amaphunzira Baibulo mosamala yemwe sangaone kufunika kwa imfa ya Yesu. Nkhaniyi inamaliza ndi mawu amphamvu akuti: “Tiyeni tikhale osamala ndi chilichonse chimene chimapeputsa kapena kunyalanyaza mfundo yakuti imfa ya Khristu ndi nsembe ya dipo yotiwombola ku uchimo.”​—Werengani 1 Yohane 2:1, 2.

2 Chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe pa nthawiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower, iyambe kufalitsidwa mu 1879, chinali kuteteza chiphunzitso cha m’Baibulo chokhudza dipo. Mfundo za m’nkhani imeneyi zinalidi ‘chakudya cha panthawi yoyenera’ chifukwa chakuti cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1800 anthu ena omwe ankadzitcha Akhristu ankakayikira zoti imfa ya Yesu ingakhale dipo lotiwombola ku uchimo. (Mat. 24:45) Pa nthawi imeneyi anthu ambiri ankakhulupirira kuti anthu anachita kusanduka kuchokera ku nyama. Mfundo imeneyi imatsutsana ndi mfundo yakuti poyamba anthu anali angwiro koma zinthu zinasintha chifukwa cha uchimo. Anthu amene amakhulupirira zoti anthu anachita kusanduka kuchokera ku nyama amanena kuti anthu akupita patsogolo mwa pang’onopang’ono ndipo safunikira dipo. Choncho malangizo amene mtumwi Paulo anauza Timoteyo ndi ofunika kwambiri. Iye anati: “Sunga bwino chimene unaikizidwa. Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiko “kudziwa zinthu.” Pakuti podzionetsera kudziwa zinthu kotero, ena apatuka pa chikhulupiriro.”​—1 Tim. 6:20, 21.

3. Kodi tsopano tikambirana mafunso ati?

3 Tikukhulupirira kuti nanunso simukufuna ‘kupatuka pa chikhulupiriro.’ Kuti mukhalebe ndi chikhulupiriro champhamvu muyenera kudzifunsa mafunso awa: N’chifukwa chiyani ndikufunika dipo? Kodi panafunika chiyani kuti dipo liperekedwe? Kodi ndingatani kuti ndipindule ndi mphatso yamtengo wapatali imeneyi, yomwe ingandipulumutse ku mkwiyo wa Mulungu?

Tikhoza Kupulumutsidwa ku Mkwiyo wa Mulungu

4, 5. N’chiyani chikusonyeza kuti mkwiyo wa Mulungu wakhala uli pa dongosolo lino la zinthu lomwe ndi loipa?

4 Baibulo ndiponso zimene zakhala zikuchitika zimasonyezeratu kuti kuchokera pa nthawi imene Adamu anachimwa, mkwiyo wa Mulungu ‘wakhala’ uli pa anthu. (Yoh. 3:36) Umboni wa zimenezi ndi wakuti palibe munthu amene safa. Ulamuliro wa Satana wotsutsana ndi Mulungu, walephera kuteteza anthu ku mavuto amene akuwonjezeka, ndipo palibe boma la anthu limene lakwanitsa kupereka zinthu zofunika pa moyo wa nzika zake. (1 Yoh. 5:19) N’chifukwa chake anthu akuvutikabe ndi nkhondo, chiwawa ndi umphawi.

5 Apa zikuonekeratu kuti Yehova sakudalitsa dongosolo lino la zinthu. Paulo anati: “Mkwiyo wa Mulungu ukusonyezedwa kuchokera kumwamba pa anthu onse osaopa Mulungu.” (Aroma 1:18-20) Choncho anthu amene amachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo ndipo salapa sadzapulumuka zotsatira za khalidwe lawo. Masiku ano, anthu akuuzidwa za mkwiyo wa Mulungu kudzera m’mauthenga amene akufalitsidwa ngati miliri pa dziko la Satanali, ndipo mauthenga amenewa akupezeka m’mabuku athu ofotokoza Baibulo.​—Chiv. 16:1.

6, 7. Kodi Akhristu odzozedwa akutsogolera pa ntchito iti, ndipo kodi ndi mwayi uti umene udakalipo kwa anthu amene ali ku mbali ya dziko la Satana?

6 Kodi zimenezi zikusonyeza kuti panopa n’zosatheka kuti munthu achoke mu ulamuliro wa Satana n’kuyanjana ndi Mulungu? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti mwayi woyanjanitsidwa ndi Yehova ukadalipo. Akhristu odzozedwa amene ndi “akazembe m’malo mwa Khristu” amatsogolera pa ntchito yolalikira ndipo akuchonderera anthu a mitundu yonse kuti ‘ayanjanenso ndi Mulungu.’​—2 Akor. 5:20, 21.

7 Mtumwi Paulo ananena kuti Yesu “akutipulumutsa ife ku mkwiyo ukubwerawo.” (1 Ates. 1:10) Pamapeto pake, Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake mwa kuwonongeratu anthu osalapa. (2 Ates. 1:6-9) Kodi ndani adzapulumuke? Baibulo limati: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha; wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Inde, anthu onse a moyo amene amakhulupirira Yesu ndiponso dipo adzapulumuka pa tsiku lomaliza limene Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake mwa kuwononga dongosolo lino la zinthu.

Mmene Dipo Limatipulumutsira

8. (a) Kodi Adamu ndi Hava akanakhala ndi tsogolo lotani? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi Mulungu wachilungamo?

8 Adamu ndi Hava analengedwa angwiro. Ngati iwo akanakhala okhulupirika kwa Mulungu, akanakhala mosangalala limodzi ndi mbadwa zawo m’Paradaiso padziko lapansi. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, makolo athu oyambawo anaphwanya dala lamulo la Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, iwo anaweruzidwa kuti afa ndipo anathamangitsidwa m’Paradaiso woyambayo. Pamene Adamu ndi Hava ankabereka ana, uchimo unali utalowa kale mwa anthu ndipo patapita nthawi mwamuna ndi mkazi oyambawo anakalamba n’kufa. Izi zinasonyeza kuti mawu a Yehova sapita pachabe, komanso kuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Yehova anachenjeza Adamu kuti akadzadya chipatso choletsedwa adzafa, ndipo izi n’zimene zinachitika.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani mbadwa za Adamu zimafa? (b) Kodi tingatani kuti tipulumuke imfa yosatha?

9 Popeza ndife mbadwa za Adamu, tinatengera uchimo ndipo matupi athu ndi opanda ungwiro, choncho timafa. Tinganene kuti pamene Adamu ankachimwa ife tinali m’chiuno mwake, choncho chiweruzo cha imfa chinaphatikizapo ifeyo. Yehova akanasintha chiweruzo chake kuti tisamafe ndiponso akanapanda kupereka dipo ndiye kuti mawu ake sakanakwaniritsidwa. N’chifukwa chake Paulo ananena mawu otsatirawa ponena za ife kuti: “Tikudziwa kuti Chilamulo n’chauzimu, koma ine ndine wa kuthupi, wogulitsidwa ku uchimo. Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutsa ku thupi limene likufa imfa imeneyi?”​—Aroma 7:14, 24.

10 Ndi Yehova yekha amene akanapereka zinthu zimene zikanathandiza kuti machimo athu akhululukidwe n’kutipulumutsa ku chilango cha imfa. Iye anachita zimenezi mwa kutumiza Mwana wake wokondedwa kuchokera kumwamba, kudzabadwa ngati munthu wangwiro, kenako n’kupereka moyo wake monga dipo lotiwombola. Mosiyana ndi Adamu, Yesu anakhalabe wangwiro. Iye “sanachite tchimo” lililonse. (1 Pet. 2:22) Yesu akanakwatira akanatha kubereka ana angwiro. Koma iye sanachite zimenezi, m’malomwake analola kuti adani a Mulungu amuphe n’cholinga chakuti apulumutse mbadwa za Adamu zomwe ndi zochimwa. Izi zinathandiza kuti anthu amene amamukhulupirira apeze moyo wosatha. Malemba amati: “Pali Mulungu mmodzi, ndi mkhalapakati mmodzi, pakati pa Mulungu ndi anthu, ameneyo ndiye munthuyo Khristu Yesu, amene anadzipereka yekha dipo lolinganiza m’malo mwa onse.”​—1 Tim. 2:5, 6.

11. (a) Kodi mmene dipo limatithandizira tingaziyerekezere ndi chiyani? (b) Kodi dipo likupindulitsanso anthu ati?

11 Tingayerekezere mmene dipo limagwirira ntchito ndi zimene zingachitike ngati ogwira ntchito m’banki aba ndalama zonse zimene anthu anasungitsa kubankiyo ndipo anthu oberedwawo ayamba kuvutika. Ndiyeno anthu akubawo agwidwa ndipo alamulidwa kuti akhale kundende zaka zambiri. Nanga bwanji anthu amene aberedwa ndalamawo? Iwo ali pa umphawi ndipo palibe chilichonse chimene angachite. Kenako munthu wina wachifundo komanso wachuma akutenga bankiyo n’kubwezera ndalama zonse za anthu amene anaberedwawo. Mofanana ndi zimenezi, Yehova Mulungu ndi Mwana wake wokondedwa anagula mbadwa za Adamu n’kufafaniza ngongole yawo ya uchimo kudzera m’magazi amene Yesu anakhetsa. N’chifukwa chake ponena za Yesu, Yohane M’batizi ananena kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Dziko limene akulichotsera uchimo likuimira anthu amene ali moyo ndiponso omwe anafa.

Kodi Panafunika Chiyani Kuti Dipo Liperekedwe?

12, 13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Abulahamu polola kupereka Isake nsembe?

12 N’zovuta kumvetsa mmene Atate wathu wakumwamba ndiponso Mwana wake wokondedwa anamvera popereka dipo. Koma m’Baibulo muli nkhani ina imene ingatithandize kumvetsa zimenezi. Mwachitsanzo, kodi mukuganiza kuti Abulahamu anamva bwanji pamene ananyamuka ulendo wa masiku atatu wopita kuphiri la Moriya pomvera lamulo la Mulungu lakuti: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; num’pereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.”​—Gen. 22:2-4.

13 Abulahamu anafikadi pamalo amene amayenera kupereka nsembeyi. Kodi mukuganiza kuti Abulahamu anamva bwanji mumtima mwake pamene ankamanga manja ndi miyendo ya Isake kenako n’kumugoneka paguwa la nsembe limene anakonza? Zinalitu zopweteka kwambiri pamene Abulahamu ankatenga mpeni kuti aphe mwana wake. Ndiyeno taganizirani mmene Isake anamvera pamene anagonekedwa paguwalo, n’kumadikira ululu umene angamve podulidwa pakhosi ndi mpeni wakuthwa. Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova analetsa Abulahamu kuti asaphe mwana wake. Zimene Abulahamu ndi Isake anachita pa nthawi imeneyi zikutithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvera polola kuti anthu olamulidwa ndi Satana aphe Mwana Wake. Zimene Isake anachita polola zimene Abulahamu ankafuna kuchita zikusonyezanso mmene Yesu anadziperekera kuti avutike kenako n’kutifera.​—Aheb. 11:17-19.

14. Fotokozani zimene zinachitikira Yakobo, zomwe zingatithandize kumvetsa nkhani ya dipo.

14 Zimene zinachitikira Yakobo zingatithandizenso kumvetsa nkhani ya dipo. Pa ana ake onse, Yakobo ankakonda kwambiri Yosefe. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti abale ake a Yosefe ankadana naye. Koma Yosefe analola pamene bambo ake anamutuma kuti akaone abale ake. Pa nthawiyi abale akewo ankadyetsa nkhosa za Yakobo kumpoto kwa Hebroni, pa mtunda wa makilomita 100. Kodi mukuganiza kuti Yakobo anamva bwanji pamene ana ake anabwera ndi chovala cha Yosefe chili magazi okhaokha. Iye anafuula kuti: “Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chirombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.” Yakobo anamva chisoni kwambiri ndipo analira mwana wake kwa masiku ambiri. (Gen. 37:33, 34) Zimene Yehova amachita pakakhala vuto linalake ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu opanda ungwiro amachita. Komabe kuganizira zimene zinachitikira Yakobo zingatithandize kumvetsako pang’ono mmene Mulungu anamvera pamene Mwana wake wokondedwa ankazunzidwa padziko lapansi kenako n’kuphedwa mwankhanza.

Mmene Timapindulira ndi Dipo

15, 16. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti walandira dipo? (b) Kodi inuyo mwapindula bwanji ndi dipo?

15 Yehova Mulungu anaukitsa Mwana wake wokhulupirika ndi thupi lauzimu, langwiro ndiponso laulemerero. (1 Pet. 3:18) Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa ophunzira ake masiku 40, ndipo analimbitsa chikhulupiriro chawo komanso kuwakonzekeretsa ntchito yolalikira imene anayenera kuigwira. Kenako iye anapita kumwamba kumene anakapereka nsembe ya magazi ake kwa Mulungu m’malo mwa otsatira ake amene amakhulupirira nsembe yake ya dipo. Yehova anasonyeza kuti walandira dipo la Khristu pouza Yesu kuti apereke mzimu woyera kwa ophunzira ake amene anasonkhana ku Yerusalemu pa Pentekoste mu 33 C.E.​—Mac. 2:33.

16 Akhristu odzozedwa amenewa nthawi yomweyo anayamba kuuza anthu ena kuti athawe mkwiyo wa Mulungu pobatizidwa m’dzina la Yesu Khristu kuti akhululukidwe machimo awo. (Werengani Machitidwe 2:38-40.) Kuchokera pa tsiku losaiwalika limeneli, anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse akhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 6:44) Malinga ndi zimene takambiranazi, tiyenera kuganizira mafunso awiri awa: Kodi pali munthu amene anapatsidwa chiyembekezo cha moyo wosatha chifukwa cha ntchito zake zabwino? Kodi n’zotheka kutaya chiyembekezo chimene tili nachochi?

17. Kodi muyenera kuuona motani mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

17 Anthufe sindife oyenera dipo. Koma chifukwa chokhulupirira dipoli, anthu mamiliyoni ambiri ali pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Koma sikuti munthu akangokhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndiye kuti ubwenziwo sungathe. Kuti tidzapulumuke pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu tiyenera kusonyeza kuti timayamikira kwambiri “dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.”​—Aroma 3:24; werengani Afilipi 2:12.

Pitirizani Kukhulupirira Dipo

18. Kodi kukhulupirira dipo kumafunanso kuti tizichita chiyani?

18 Lemba la Yohane 3:36, limene lili kumayambiriro kwa nkhani ino likusonyeza kuti kukhulupirira Ambuye Yesu Khristu kumafunanso kuti tizimumvera. Chifukwa choyamikira dipo tiyenera kutsatira zinthu zosiyanasiyana zimene Yesu anaphunzitsa kuphatikizapo zokhudza makhalidwe abwino. (Maliko 7:21-23) “Mkwiyo wa Mulungu udzafika” pa anthu onse amene mosalapa amachita zinthu monga dama, nthabwala zotukwana ndiponso “chonyansa cha mtundu uliwonse” kuphatikizapo kukonda kuonera zolaula.​—Aef. 5:3-6.

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira dipo?

19 Kuyamikira kwathu dipo kuyenera kutilimbikitsa kuchita khama kwambiri pa ‘ntchito za kudzipereka kwathu kwa Mulungu.’ (2 Pet. 3:11) Tiyeni tizipatula nthawi yokwanira yopemphera kuchokera pansi pa mtima, kuphunzira Baibulo patokha, kupezeka pa misonkhano, kuchita kulambira kwa pabanja, ndiponso kuchita khama pa ntchito yolalikira za Ufumu. Ndipo ‘tisaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.’​—Aheb. 13:15, 16.

20. Kodi anthu onse amene amakhulupirira dipo angayembekezere madalitso otani?

20 Mkwiyo wa Mulungu ukamadzafika pa dongosolo loipali la zinthu, tidzakhala osangalala kwambiri chifukwa chokhulupirira dipo ndiponso chifukwa chochita zinthu zoyamikira dipolo. Ndipo m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza, tidzayamikira kwa moyo wathu wonse mphatso yapadera imeneyi yomwe ikutipulumutsa ku mkwiyo wa Mulungu.​—Werengani Yohane 3:16; Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tikufunikira dipo?

• Kodi n’chiyani chinafunika kuti dipo liperekedwe?

• Kodi anthu akupindula bwanji ndi dipo?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Mwayi woyanjananso ndi Yehova ukadalipo

[Zithunzi patsamba 15]

Kuganizira nkhani zokhudza Abulahamu, Isake ndi Yakobo kungatithandize kuyamikira zimene zinafunika kuti dipo liperekedwe