Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Kugwirizana

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Kugwirizana

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Kugwirizana

“Ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa [m’khola].”​—MIKA 2:12.

1. Kodi chilengedwe chimasonyeza bwanji nzeru za Mulungu?

WAMASALMO ananena kuti: “Nchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” (Sal. 104:24) Nzeru za Mulungu zimaoneka bwino tikaganizira mmene mitundu yosiyanasiyana ya zomera, tizilombo, nyama ndiponso mabakiteliya zimakhalira ndi moyo mogwirizana komanso tikaona zimene zimachitika m’matupi athu. M’matupi athuwa mumachitika zinthu zosiyanasiyana kuyambira ndi ziwalo zikuluzikulu mpaka kukafika mu timaselo ting’onoting’ono. Zonsezi zimagwira ntchito mogwirizana ndipo zimachititsa kuti tikhale athanzi.

2. Malinga ndi chithunzi chimene chili patsamba 13, n’chifukwa chiyani tinganene kuti mgwirizano umene unali mu mpingo wachikhristu unali wodabwitsa kwambiri?

2 Yehova analenga anthu kuti azikhala modalirana. Anthu amaoneka mosiyanasiyana, ali ndi makhalidwe osiyanasiyana ndiponso maluso osiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepa, Mulungu analenga anthu oyambirira ndi makhalidwe amene iyenso ali nawo ndipo makhalidwe amenewa akanawathandiza kukhala mogwirizana ndiponso modalirana. (Gen. 1:27; 2:18) Komabe, si anthu onse amene ali pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo ambiri alephera kuchita zinthu mogwirizana. (1 Yoh. 5:19) Choncho, mgwirizano umene unali mu mpingo wachikhristu mu nthawi ya atumwi unali wodabwitsa kwambiri. Tikutero chifukwa munali anthu osiyanasiyana, ena anali akapolo a ku Efeso, azimayi otchuka achigiriki, amuna ophunzira achiyuda ndiponso anthu amene poyamba ankapembedza mafano.​—Mac. 13:1; 17:4; 1 Ates. 1:9; 1 Tim. 6:1.

3. Kodi Baibulo limayerekezera m’gwirizano wa Akhristu ndi chiyani, ndipo mu nkhani ino tikambirana chiyani?

3 Kulambira koona kumachititsa anthu kukhala ogwirizana ngati ziwalo za thupi limodzi. (Werengani 1 Akorinto 12:12, 13.) Mu nkhani ino tikambirana zinthu izi: Kodi kulambira koona kumagwirizanitsa bwanji anthu? N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene angagwirizanitse anthu amitundu yonse? Kodi ndi mavuto ati amene Yehova amatithandiza kuthanana nawo kuti tikhale ogwirizana? Ndipo pa nkhani ya m’gwirizano, Akhristu oona amasiyana bwanji ndi anthu amene ali m’Matchalitchi Achikhristu?

Kodi Kulambira Koona Kumagwirizanitsa Bwanji Anthu?

4. Kodi kulambira koona kumagwirizanitsa bwanji anthu?

4 Anthu amene amalambira moona amazindikiza kuti popeza Yehova analenga zinthu zonse, iye ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Chiv. 4:11) Choncho ngakhale kuti Akhristu oona amakhala m’madera osiyanasiyana ndiponso zochitika pa moyo wawo zimakhala zosiyanasiyana, onse amamvera malamulo a Mulungu ndipo amayendera mfundo zofanana za m’Baibulo. Akhristu oona onse amaona kuti Yehova ndi “Atate” wawo ndipo ndi mmene zililidi. (Yes. 64:8; Mat. 6:9) Motero Akhristu oona onse ndi abale mwauzimu ndipo amakhala mogwirizana. Pofotokoza mgwirizano umenewu, wamasalmo anati: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!”​—Sal. 133:1.

5. Kodi ndi khalidwe liti limene limathandiza kuti Akhristu oona azigwirizana?

5 Ngakhale kuti Akhristu oona ndi opanda ungwiro, amalambira Mulungu chifukwa anaphunzira kukondana. Yehova amawaphunzitsa kukondana kuposa mmene wina aliyense angawaphunzitsire. (Werengani 1 Yohane 4:7, 8.) Mawu ake amati: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso. Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.” (Akol. 3:12-14) Chikondi chimenechi, chomwe ndi chomangira umodzi changwiro, ndi chimene chimadziwikitsa Akhristu oona. Kodi inuyo panokha, simunaone kuti Akhristu oona amadziwika chifukwa cha kugwirizana?​—Yoh. 13:35.

6. Kodi kuyembekezera Ufumu kumatithandiza bwanji kukhala ogwirizana?

6 Akhristu oona amakhalanso ogwirizana chifukwa chakuti amayembekeza kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse a anthu. Iwo amadziwanso kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maulamuliro a anthu ndipo udzabweretsa mtendere weniweni ndiponso wosatha kwa anthu omvera. (Yes. 11:4-9; Dan. 2:44) N’chifukwa chake Akhristu amamvera mawu amene Yesu ananena okhudza otsatira ake. Iye anati: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yoh. 17:16) Akhristu oona salowerera nawo mikangano ya dzikoli, choncho amakhala ogwirizana ngakhale pa nthawi imene anthu ena akumenyana.

Pali Dongosolo Limodzi Limene Timalandirira Malangizo

7, 8. Kodi malangizo a m’Baibulo amatithandiza bwanji kukhala ogwirizana?

7 M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankagwirizana chifukwa panali dongosolo limodzi limene ankalandirira malangizo. Iwo ankadziwa kuti Yesu ankaphunzitsa ndiponso kutsogolera mpingo kudzera m’bungwe lolamulira lomwe linapangidwa ndi atumwi ndiponso akulu a ku Yerusalemu. Amuna odzipereka amenewa, ankasankha zinthu mogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndipo ankagwiritsa ntchito oyang’anira oyendayenda kupereka malangizowo ku mipingo yosiyanasiyana. Ponena za oyang’anira amenewa, Baibulo limati: “Popitiriza ulendo wawo m’mizinda, anali kuwapatsira okhulupirira kumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.”​—Mac. 15:6, 19-22; 16:4.

8 Masiku anonso, Bungwe Lolamulira lomwe lapangidwa ndi Akhristu odzozedwa limathandiza kuti mpingo wa padziko lonse ukhale wogwirizana. Bungwe Lolamulira limafalitsa m’zinenero zambiri mabuku amene amakhala olimbikitsa mwauzimu. Chakudya chauzimu chimenechi chimachokera m’Mawu a Mulungu. Choncho zimene amaphunzitsa sizochokera kwa anthu koma kwa Yehova.​—Yes. 54:13.

9. Kodi ntchito imene Mulungu watipatsa imatithandiza bwanji kukhala ogwirizana?

9 Nawonso oyang’anira achikhristu amalimbikitsa mgwirizano potsogolera pa ntchito yolalikira. Mzimu umene umagwirizanitsa anthu amene amatumikira limodzi Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa mzimu umene umagwirizanitsa anthu m’dzikoli amene amangogwirizana chifukwa chakuti amachitira zinthu limodzi. Mpingo wachikhristu sunakhazikitsidwe kuti uzingogwira ntchito ngati malo ochezerako. Unakhazikitsidwa kuti uzilemekeza Yehova, kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira, ndiponso kuti uzichita zinthu zimene zingachititse kuti Akhristu azilimbikitsana. (Aroma 1:11, 12; 1 Ates. 5:11; Aheb. 10:24, 25) N’chifukwa chake mtumwi Paulo anauza Akhristu kuti: “Mukuchirimika mu mzimu umodzi. Ndipo ndi mtima umodzi, mukulimbika pamodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha uthenga wabwino.”​—Afil. 1:27.

10. Kodi anthu a Mulungufe ndife ogwirizana m’njira ziti?

10 Ndiponso, anthu a Yehovafe ndife ogwirizana chifukwa timavomereza ulamuliro wa Yehova, timakonda abale athu, timayembekezera Ufumu wa Mulungu ndiponso timalemekeza anthu amene Mulungu akuwagwiritsa ntchito kutiyang’anira. Yehova amatithandiza kuthana ndi makhalidwe amene chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu angasokoneze umodzi wathu.​—Aroma 12:2.

Gonjetsani Kunyada ndi Nsanje

11. N’chifukwa chiyani kunyada sikugwirizanitsa anthu ndipo Yehova amatithandiza bwanji kuthetsa khalidwe limeneli?

11 Kunyada kumadanitsa anthu. Munthu amene amadziona kuti ndi wapamwamba nthawi zambiri amachita zinthu modzitama chifukwa chonyada. Koma zimenezi zimasokoneza mgwirizano chifukwa zimachititsa anthu ena kuyamba kuchita nsanje. Yakobo yemwe anali mtumwi, analemba mosapita m’mbali kuti: “Kunyada konse kotero ndi koipa.” (Yak. 4:16) Munthu amene amaona kuti anthu ena ndi otsika alibe chikondi. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzichepetsa chifukwa amachita zinthu ndi anthu opanda ungwirofe. Ponena za Mulungu, Davide alemba kuti: “Kufatsa [kudzichepetsa NW] kwanu kunandikulitsa.” (2 Sam. 22:36) Mawu a Mulungu amatithandiza kuthana ndi kunyada mwa kutiphunzitsa kukhala ndi maganizo oyenerera. Paulo analemba mouziridwa kuti: “Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndani? Inde, uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira? Ndiye ngati unachita kulandira zinthu zimenezo, n’chifukwa chiyani ukudzitama ngati kuti sunachite kulandira?”​—1 Akor. 4:7.

12, 13. N’chifukwa chiyani n’zosavuta kuyamba kuchita nsanje? (b) Tikamaona anthu mmene Yehova amawaonera, kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

12 Nsanje ndi chinthu chinanso chimene chimalepheretsa anthu kukhala ogwirizana. Chifukwa cha kupanda ungwiro kumene tinatengera, tonsefe tili ndi “chizolowezi cholakalaka kuchita kaduka.” Ngakhale Akhristu amene atumikira kwa nthawi yaitali, nthawi zina amachitira nsanje anthu ena chifukwa cha mmene zinthu ziliri pa moyo wawo, zinthu zimene ali nazo, utumiki umene akuchita ndiponso maluso awo. (Yak. 4:5) Mwachitsanzo, m’bale amene ali ndi banja akhoza kumachitira nsanje m’bale wina amene ali mu utumiki wanthawi zonse chifukwa cha maudindo amene ali nawo, osadziwa kuti nayenso m’baleyo akumuchitira nsanje iyeyo chifukwa chakuti ali ndi banja ndiponso ana. Kodi tingatani kuti nsanje yotereyi isasokoneze mgwirizano wathu?

13 Kuti tipewe nsanje, tiyenera kukumbukira kuti Baibulo limayerekezera mpingo wa Akhristu odzozedwa, ndi ziwalo za thupi la munthu. (Werengani 1 Akorinto 12:14-18.) Mwachitsanzo, ngakhale kuti diso lanu lili pa malo oonekera kwambiri kuposa mtima wanu, kodi zonsezi si zofunika kwa inu? N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye amaona kuti munthu aliyense mu mpingo ndi wofunika ngakhale kuti ena nthawi zina angakhale odziwika kwambiri kuposa ena. Choncho, tiziona abale athu mmene Yehova amawaonera. M’malo mochitira nsanje abale athu, ndi bwino kuti tiziwadera nkhawa ndiponso kuwaganizira. Tikamachita zimenezi, timathandiza kuti Akhristu oona azisiyana ndi anthu amene ali m’Matchalitchi Achikhristu.

Matchalitchi Achikhristu Amadziwika Chifukwa Chosagwirizana

14, 15. Kodi zinatani kuti Matchalitchi Achikhristu ampatuko ayambe kusagwirizana?

14 Kugwirizana kwa Akhristu oona kumawasiyanitsa ndi anthu amene ali m’Matchalitchi Achikhristu amene amangokhalira kukangana. Mwachitsanzo, cha m’ma 300 C.E., Chikhristu champatuko chinafala kwambiri moti mfumu ya ku Roma inayamba kulamulira Chikhristu ndipo izi zinachititsa kuti Matchalitchi Achikhristu afalikire. Kenako tchalitchi cha ku Roma chitayamba kugawanika, maufumu ambiri amene ankachitsatira, anachoka mu ulamuliro wa Roma ndipo anayambitsa matchalitchi awo.

15 Ambiri mwa maufumu amenewa anamenyana kwa nthawi yaitali. M’zaka za m’ma 1600 ndi 1700 anthu ku Britain, France ndi ku United States analimbikitsa mzimu wokonda dziko lako moti kukonda dziko lako kunangokhala ngati chipembedzo. Pofika cha m’ma 1800 ndi 1900, anthu ambiri anayamba kukhala ndi mzimu wokonda dziko lawo. Patapita nthawi, Matchalitchi Achikhristu anagawanika m’magulu ambiri ndipo ambiri ankalimbikitsa mzimu wokonda dziko lako. Zimenezi zachititsa kuti anthu amene amapita kutchalitchi afike mpaka pochita nkhondo ndi Akhristu achipembedzo chawo a m’dziko lina. Masiku ano anthu a m’Matchalitchi Achikhristu sagwirizana chifukwa cha zikhulupiriro zawo ndiponso chifukwa chokonda dziko lawo.

16. Kodi ndi nkhani ziti zimene zimasiyanitsa anthu a m’Matchalitchi Achikhristu?

16 M’zaka za m’ma 1900, magulu ena a Matchalitchi Achikhristu anayambitsa zoti pakhale mgwirizano wa matchalitchi. Koma atayesetsa kwa zaka zambiri, ndi matchalitchi ochepa okha amene anagwirizana ndipo anthu ambiri opita kutchalitchi akusiyanabe maganizo pa nkhani zoti anthu anachokera ku nyama, kuchotsa mimba, kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndiponso kulola kuti akazi azitsogolera mu mpingo. M’madera ena, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ayesa kugwirizanitsa anthu mwa kufewetsa ziphunzitso zina zimene zinkawachititsa kuti asamagwirizane. Komabe, kufewetsa ziphunzitso sikunagwirizanitse anthu a m’Matchalitchi Achikhristu koma kwangochititsa anthu kukhala ndi chikhulupiriro chosalimba.

Kulambira Koona Kumathetsa Mzimu Wokonda Dziko Lako

17. Pa nkhani ya kugwirizana kwa Akhristu oona, kodi Baibulo linalosera kuti chidzachitike ndi chiyani “masiku otsiriza”?

17 Ngakhale kuti anthu masiku ano ndi ogawanika kwambiri kuposa ndi kale lonse, Akhristu oona ndi osiyana chifukwa iwo ndi ogwirizana. Mika yemwe anali mneneri wa Mulungu, analosera kuti: “Ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa [m’khola].” (Mika 2:12) Mika analosera kuti kulambira koona kudzakwezeka kuposa mitundu ina yonse ya kulambira kaya ndi milungu yonyenga kapena mayiko amene amalambiridwa ngati milungu. Iye analemba kuti: “Kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako. Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu.”​—Mika 4:1, 5.

18. Kodi kulambira koona kwatithandiza kusintha zinthu ziti?

18 Mika analoseranso kuti kulambira kuona kudzagwirizanitsa anthu amene poyamba ankadana. Iye anati: “[Anthu] amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake; . . . ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.” (Mika 4:2, 3) Anthu amene anasiya kulambira milungu yopangidwa ndi anthu kapena kulambira mayiko awo, n’kuyamba kulambira Yehova, amasangalala ndi mgwirizano wa padziko lonse. Mulungu amawaphunzitsa kukondana.

19. Kodi mfundo yakuti kulambira koona kukugwirizanitsa anthu mamiliyoni ambiri, ndi umboni wachiyani?

19 Mgwirizano wa Akhristu oona padziko lonse ndi wapadera kwambiri ndipo ndi umboni wakuti Yehova akutsogolerabe anthu ake ndi mzimu woyera. Anthu a m’mitundu yonse akugwirizanitsidwa kwambiri kuposa ndi kale lonse. Apa zikuonekeratu kuti lemba la Chivumbulutso 7:9, 14 likukwaniritsidwa mochititsa chidwi. Izi zikusonyeza kuti posachedwapa angelo a Mulungu adzasiya kugwira “mphepo” zimene zidzawononge dongosolo la zinthu lilipoli. (Werengani Chivumbulutso 7:1-4, 9, 10, 14.) Ndi mwayitu waukulu kukhala nawo m’gulu la abale ogwirizana padziko lonse lapansi. Koma kodi aliyense payekha angatani kuti athandize kuti mgwirizano umenewu upitirire? Funso limeneli liyankhidwa m’nkhani yotsatira.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kulambira koona kumagwirizanitsa bwanji anthu?

• Kodi tingatani kuti nsanje isasokoneze mgwirizano wathu?

• N’chifukwa chiyani mzimu wokonda dziko lako sugawanitsa Akhristu oona?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Akhristu oyambirira anachokera ku zikhalidwe zosiyanasiyana

[Zithunzi patsamba 15]

N’chifukwa chiyani tinganene kuti mukamagwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu mumathandizira kuti tizikhala ogwirizana?