Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu kwa Akhristu Anzanu?

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu kwa Akhristu Anzanu?

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu kwa Akhristu Anzanu?

“Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.”​—AROMA 12:10.

1, 2. (a) Kodi Paulo anapereka malangizo ati m’kalata yake yopita kwa Aroma? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

M’KALATA yake yopita kwa Aroma, mtumwi Paulo anatsindika kufunika koti Akhristufe tizisonyezana chikondi mu mpingo. Iye ananena kuti chikondi chathu sichiyenera kukhala “cha chiphamaso.” Iye ananenanso kuti tiyenera ‘kukonda abale’ ndi “chikondi chenicheni.”​—Aroma 12:9, 10a.

2 Kukonda abale sikumangotanthauza mmene timamvera mumtima mwathu. Tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timawakonda. Ndipotu palibe amene angadziwe zoti timam’konda pokhapokha ngati titachita zinthu zosonyeza chikondi. N’chifukwa chake Paulo anawonjezera kuti: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10b) Kodi kusonyeza ulemu kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala patsogolo posonyeza ulemu kwa Akhristu anzathu? Nanga kodi tingasonyeze bwanji ulemuwu?

Kodi Ulemu Weniweni Umatanthauza Chiyani?

3. Malinga ndi zinenero zoyambirira za Baibulo, kodi mawu akuti “ulemu” amatanthauza chiyani?

3 Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “ulemu” kwenikweni amatanthauza “kulemera.” Munthu amene amalemekezedwa amaonedwa kuti ndi wolemerera kapena kuti wofunika. M’Malemba, mawu achiheberi amenewa amamasuliridwanso kuti “ulemerero” zimene zimasonyeza kulemekeza kwambiri munthu. (Gen. 45:13) M’Baibulo mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “ulemu” amanena za chinthu cholemekezeka, chapamwamba ndiponso cha mtengo wapatali. (Luka 14:10) Choncho, anthu amene timawalemekeza ndi ofunika ndiponso a mtengo wapatali kwa ife.

4, 5. Kodi kulemekeza ena kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

4 Kodi kulemekeza ena kumatanthauza chiyani? Kulemekeza abale athu sikumangotanthauza kuchita zinthu zooneka pamaso pa anthu kuti timawalemekeza. Ngakhale kuti zochita zathu zingasonyeze kuti timalemekeza ena, ulemu kwenikweni umayambira mu mtima.

5 N’zosatheka kuti Mkhristu asonyeze ulemu weniweni kwa Akhristu anzake ngati ulemuwo sukuchokera mu mtima. (3 Yoh. 9, 10) Mofanana ndi mtengo umene umakula bwino ngati mizu yake yazikika m’nthaka yabwino, munthu amasonyeza ulemu weniweni ngati ulemuwo ukuchokera mu mtima. Ngati ulemu wathu si wochokera mu mtima, sukhalitsa. (Mac. 5:1-5) Tsopano tingamvetse chifukwa chake Paulo asanapereke malangizo oti tizilemekezana ananena mawu akuti: “Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso.”​—Aroma 12:9; werengani 1 Petulo 1:22.

Muzilemekeza Anthu Chifukwa Analengedwa “M’chifaniziro cha Mulungu”

6, 7. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza anthu ena?

6 Popeza ulemu weniweni umachokera mu mtima, sitiyenera kuiwala zifukwa za m’Malemba zotichititsa kulemekeza abale athu onse. Tsopano tiyeni tikambirane ziwiri mwa zifukwa zimenezi.

7 Mosiyana ndi zolengedwa zina padzikoli, anthu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Yak. 3:9) N’chifukwa chake anthufe tili ndi makhalidwe amenenso Mulungu ali nawo monga chikondi, nzeru ndi chilungamo. Tiyeni tionenso chinthu china chimene Mlengi wathu anatipatsa. Wamasalmo anati: “Inu Yehova . . . inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba! . . . Munamuchepetsa [munthu] pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu, kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu.” (Sal. 8:1, 4, 5; 104:1) * Mulungu anaveka kapena kuti kupatsa anthu onse ulemu ndi ulemerero. Choncho tikamalemekeza anthu timasonyeza kuti tikudziwa kuti Yehova ndi amene anayambitsa kupereka ulemu kwa anthu. Ndiye ngati anthufe timafunika kulemekeza anthu onse, kuli bwanji Akhristu anzathu.​—Yoh. 3:16; Agal. 6:10.

Tonse Ndife Anthu a Banja Limodzi

8, 9. Kodi Paulo anati tiyenera kulemekeza okhulupirira anzathu chifukwa chiyani?

8 Paulo anatchulanso chifukwa china chimene tiyenera kulemekezana. Asanapereke malangizo akuti tizilemekezana, iye anati: “Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu.” Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chikondi chenicheni” amanena za mgwirizano wa anthu a m’banja lokondana ndiponso lochitira zinthu limodzi. Choncho pogwiritsa ntchito mawu amenewa, Paulo anatsindika mfundo yakuti anthu a mu mpingo ayenera kukhala ngati anthu a m’banja logwirizana. (Aroma 12:5) Kumbukiraninso kuti Paulo ankalembera Akhristu odzozedwa mawu amenewa ndipo onsewo anali ana a Atate mmodzi Yehova. Motero iwo anali a m’banja limodzi. Choncho Akhristu odzozedwa m’nthawi ya Paulo analidi ndi chifukwa chomveka chosonyezana ulemu. N’chimodzimodzinso ndi Akhristu odzozedwa masiku ano.

9 Nanga bwanji a “nkhosa zina”? (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti panopa si ana a Mulungu, amatchulana kuti m’bale kapena mlongo. Ndipo izi n’zoyenera chifukwa chakuti iwo amapanga banja lachikhristu logwirizana la padziko lonse. (1 Pet. 2:17; 5:9) Choncho ngati a nkhosa zina amamvetsa tanthauzo la mawu akuti “m’bale” kapena “mlongo” amene amawagwiritsa ntchito, nawonso ali ndi chifukwa chomveka cholemekezera okhulupirira anzawo.​—Werengani 1 Petulo 3:8.

N’chifukwa Chiyani Kulemekeza Ena N’kofunika?

10, 11. N’chifukwa chiyani kulemekeza ena n’kofunika kwambiri?

10 N’chifukwa chiyani kulemekeza ena n’kofunika kwambiri? Chifukwa chake ndi ichi: Tikamalemekeza abale ndi alongo athu timathandizira kuti zinthu ziziyenda bwino ndiponso kuti mpingo wonse ukhale wogwirizana.

11 N’zoona kuti Akhristu oonafe timakhala olimba chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso chifukwa cha thandizo la mzimu wake. (Sal. 36:7; Yoh. 14:26) Komabe Akhristu anzathu akasonyeza kuti amatiyamikira zimatilimbikitsa kwambiri. (Miy. 25:11) Munthu wina akachita kapena kunena zinthu zosonyeza kuti amatiyamikira ndiponso kutilemekeza zimatilimbikitsa. Izi zimatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe zivute zitani kuyenda mosangalala panjira yopita ku moyo. Mosakayikira, zimenezi ziyenera kuti zinakuchitikiranipo.

12. Kodi aliyense angatani kuti alimbikitse chikondi mu mpingo?

12 Popeza Yehova amadziwa zoti anthufe timafuna kulemekezedwa, iye amatilimbikitsa kudzera m’Mawu ake kuti: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10; werengani Mateyo 7:12.) Akhristu amene amatsatira malangizo amenewa ndi mtima wonse amathandiza kuti anthu onse mu mpingo wachikhristu azikondana. Choncho, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi liti pamene mochokera pansi pa mtima ndinalankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti ndimalemekeza m’bale kapena mlongo wina mu mpingo?’​—Aroma 13:8.

Ndi Udindo wa Aliyense Kulemekeza Ena

13. (a) Kodi ndani ayenera kukhala patsogolo posonyeza anthu ena ulemu? (b) Kodi mawu a Paulo opezeka pa Aroma 1:7 akusonyeza chiyani?

13 Kodi ndani ayenera kukhala patsogolo posonyeza ulemu kwa ena? M’kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anafotokoza kuti akulu achikhristu ndi amene ‘akutsogolera pakati pathu.’ (Aheb. 13:17) N’zoona kuti akulu amakhala patsogolo pa zinthu zosiyanasiyana. Komabe, monga abusa a nkhosa, iwo ayenera kukhala patsogolo polemekeza Akhristu ena kuphatikizapo akulu anzawo. Mwachitsanzo, akulu akakumana kuti akambirane zinthu zauzimu zofunika pa mpingo amalemekezana. Iwo amachita zimenezi mwa kumvetsera mosamala wina akamalankhula. Kuwonjezera pamenepo, akamasankha zochita iwo amasonyezana ulemu mwa kuganizira mfundo za akulu onse. (Mac. 15:6-15) Komabe, tiyenera kukumbukira kuti malangizo a m’kalata ya Paulo kwa Aroma sanali opita kwa akulu okha, koma ku mpingo wonse. (Aroma 1:7) Choncho malangizo akuti tizikhala patsogolo pa nkhani ya kulemekeza ena ndi ofunikanso kwa tonsefe.

14. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kusiyana pakati pa kusonyezana ulemu ndi kukhala patsogolo posonyezana ulemu. (b) Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti?

14 Tiyeni tionenso mbali ina ya malangizo a Paulo amenewa. Iye sanangolimbikitsa Akhristu anzake ku Roma kusonyezana ulemu, koma kuti azikhala patsogolo posonyezana ulemuwo. Kodi pali kusiyana kulikonse pakati pa kusonyezana ulemu ndi kukhala patsogolo posonyezana ulemu? Taganizirani chitsanzo ichi. Kodi mphunzitsi angauze ana amene amadziwa kale kuwerenga kuti aziphunzira kuwerenga? Ayi sangatero. Iwo amadziwa kale kuwerenga. M’malomwake mphunzitsiyo angawathandize kuti aziwerenga bwino kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, chikondi chimene chimatichititsa kuti tizilemekezana ndi chizindikiro cha Akhristu oona. (Yoh. 13:35) Ana amene amadziwa kale kuwerenga akhoza kukulitsa luso lawo la kuwerenga. N’chimodzimodzinso ifeyo, tikhoza kupita patsogolo mwa kukhala patsogolo posonyezana ulemu. (1 Ates. 4:9, 10) Uwu ndi udindo umene aliyense wa ife ali nawo. Choncho tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimakhala patsogolo polemekeza ena mu mpingo?’

Muzilemekeza “Anthu Onyozeka”

15, 16. (a) Kodi sitiyenera kuiwala anthu ati pa nkhani yosonyeza ulemu ndipo chifukwa chiyani? (b) N’chiyani chingasonyeze ngati timalemekeza abale ndi alongo kuchokera mu mtima kapena ayi?

15 Kodi ndi anthu ati amene sitiyenera kuwaiwala pa nkhani yopatsa ena ulemu mu mpingo? Mawu a Mulungu amati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.” (Miy. 19:17) Kodi mfundo ya palembali tingaigwiritse ntchito bwanji pamene tikuyesetsa kukhala patsogolo posonyezana ulemu?

16 Inu mungavomereze kuti anthu ambiri savutika kulemekeza anthu amene amawaona kuti ndi apamwamba koma salemekeza kwenikweni anthu amene amawaona kuti ndi otsika. Koma Yehova satero. Mawu ake amati: “Amene akundilemekeza ndiwalemekeza.” (1 Sam. 2:30; Sal. 113:5-7) Yehova amalemekeza anthu onse amene amamutumikira ndiponso kumulemekeza. Iye sanyalanyaza “anthu onyozeka.” (Werengani Yesaya 57:15; 2 Mbiri 16:9) Ifenso timafuna kutsanzira Yehova. Choncho ngati tikufuna kudziwa ngati timalemekeza anthu ena mochokera pansi pa mtima, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amene si odziwika kwambiri ndiponso alibe udindo mu mpingo ndimachita nawo bwanji zinthu?’ (Yoh. 13:14, 15) Yankho la funso limeneli lingasonyeze bwino ngati timalemekeza anthu ena kuchokera mu mtima kapena ayi.​—Werengani Afilipi 2:3, 4.

Muzisonyeza Ulemu mwa Kupatula Nthawi Yothandiza Ena

17. Tchulani njira imodzi yofunika kwambiri imene tingasonyezere kuti tikukhala patsogolo pa nkhani yosonyeza ulemu, nanga n’chifukwa chiyani njira imeneyi ili yofunika kwambiri?

17 Kodi njira yofunika kwambiri imene tingasonyezere kuti timakhala patsogolo posonyeza ena ulemu mu mpingo ndi iti? Tingachite zimenezi mwa kupatula nthawi kuti tithandize ena. N’chifukwa chiyani tikutero? Akhristufe timakhala otanganidwa ndipo nthawi yathu yambiri timachita zinthu zosiyanasiyana za mpingo. Choncho n’zosadabwitsa kuti timaona kuti nthawi ndi yamtengo wapatali. Ndipo tikudziwa kuti sitiyenera kufuna kuti abale ndi alongo athu azisiya zinthu zawo kwa nthawi yaitali kuti atithandize. Ifenso timayamikira ngati ena mu mpingo amadziwa kuti si bwino nthawi zonse kuyembekezera kuti tiyenera kusiya zinthu zathu kuti tiwathandize pa zinthu zina.

18. Malinga ndi chithunzi chomwe chili patsamba 18, kodi tingasonyeze bwanji kuti timafuna kupatula nthawi kuti tithandize Akhristu anzathu?

18 Ngakhale zili choncho, (makamaka amene timatumikira mu mpingo ngati abusa) tiyenera kudziwa kuti tikamalolera kusiya zinthu zathu n’cholinga chakuti tithandize okhulupirira anzathu, timasonyeza kuti timawalemekeza. N’chifukwa chiyani zili choncho? Tikasiya zimene tikuchita n’cholinga choti tithandize anthu ena zimakhala ngati tikuwauza kuti, ‘Inu ndinu munthu wofunika kwambiri kwa ine moti ndi bwino kukuthandizani kusiyana ndi kupitiriza zimene ndikuchitazi.’ (Maliko 6:30-34) Tikapanda kusiya zinthu zathu, timasonyeza kuti zimene tikuchitazo n’zofunika kwambiri kuposa munthuyo. Izi zingachititse munthuyo kuona kuti si wofunika kwenikweni kwa ifeyo. N’zoona kuti nthawi zina pamakhala zinthu zina zofunika mwamsanga zoti sitingadukize. Komabe zimene tingachite pamenepa, zingasonyeze ngati timalemekeza abale ndi alongo athu kuchokera mu mtima kapena ayi.​—1 Akor. 10:24.

Muziyesetsa Kukhala Patsogolo Posonyeza Ulemu

19. Kodi njira inanso imene tingasonyezere kuti timalemekeza Akhristu anzathu ndi iti?

19 Palinso njira zina zofunika kwambiri zimene tingasonyezere kuti timalemekeza Akhristu anzathu. Mwachitsanzo, tikapatula nthawi yoti tiwathandize, tiyeneranso kuwamvetsera akamalankhula. Pa nkhani imeneyinso Yehova ndi chitsanzo chabwino. Wamasalimo Davide ananena kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” (Sal. 34:15) Timayesetsa kutsanzira Yehova mwa kuyang’ana ndiponso kumvetsera mwatcheru abale athu akatipempha kuti tiwathandize. Tikamatero, timasonyeza kuti timawalemekeza.

20. Pa nkhani yosonyezana ulemu, kodi ndi mfundo ziti zimene tiyenera kuzikumbukira?

20 Monga taonera, nthawi zonse ndi bwino kukumbukira chifukwa chake tiyenera kulemekeza Akhristu anzathu kuchokera pansi pa mtima. Komanso, tiyenera kufufuza mipata yosonyeza kuti tikukhala patsogolo pa nkhani yolemekeza ena kuphatikizapo onyozeka. Tikamachita zimenezi tidzalimbikitsa chikondi ndiponso mgwirizano pakati pathu mu mpingo. Choncho, tiyeni tonsefe tipitirizebe kusonyezana ulemu komanso makamaka kukhala patsogolo pochita zimenezi. Kodi mudzayesetsa kuchita zimenezi?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mawu a Davide a m’Salimo 8 mwaulosi amanenanso za Yesu Khristu yemwe ndi munthu wangwiro.​—Aheb. 2:6-9.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ulemu weniweni umatanthauza chiyani?

• Kodi tiyenera kulemekeza Akhristu anzathu pa zifukwa ziti?

• N’chifukwa chiyani kulemekezana n’kofunika?

• Fotokozani njira zimene tingasonyezere kuti timalemekeza Akhristu anzathu.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi tingasonyeze bwanji ulemu kwa Akhristu anzathu?