Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Ana Kulidziwa Bwino Gulu la Yehova

Thandizani Ana Kulidziwa Bwino Gulu la Yehova

Thandizani Ana Kulidziwa Bwino Gulu la Yehova

ANA amafuna kuphunzira. Taganizirani za mafunso amene ana a Aisiraeli ayenera kuti anali nawo ku Iguputo, usiku wa Pasika woyamba. Iwo ayenera kuti anafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani apha mwana wa nkhosa?’ ‘N’chifukwa chiyani bambo akupaka magazi pachitseko?’ ‘Kodi tikupita kuti?’ Zimene Yehova anauza mitu ya mabanja ya Isiraeli ndi umboni wosonyeza kuti iye anasangalala ndi mafunso amenewa. Yehova anawauza zimene adzafotokozere ana awo pochita Pasika m’tsogolo. Iye anati: “Ndiyeno ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’ Pamenepo mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya pasika kwa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Isiraeli mu Iguputo pamene anali kupha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’” (Eks. 12:24-27) Kenako Yehova anakumbutsa makolo achiisiraeli kufunika koyankha mafunso amene ana awo angakhale nawo okhudza “malangizo ndi zigamulo” zimene Yehova anawapatsa.​—Deut. 6:20-25.

Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova ankafuna kuti ana azipeza mayankho okhutiritsa a mafunso okhudza kulambira koona. Anawo ankafunika mayankho amene akanawalimbikitsa kukonda kwambiri Yehova monga Mulungu ndiponso Mpulumutsi wawo. Izi n’zimenenso Yehova amafuna masiku ano. Njira imodzi imene makolo angathandizire ana awo kuti azikonda kwambiri Mulungu ndi anthu ake, ndi mwa kuwathandiza kudziwa bwino gulu la Yehova ndiponso kumvetsa mmene anawo amapindulira ndi dongosolo lake. Tiyeni tsopano tikambirane njira zina zimene zingathandize ana kuti aphunzire zambiri zokhudza gulu la Mulungu.

Athandizeni Kudziwa Mpingo Wanu

Ana anu ayenera kudziwa bwino mpingo umene mumasonkhana. Kuti zimenezi zitheke, inuyo makolo muyenera kumawatenga ana anu ku misonkhano yonse ya mpingo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukutsanzira zimene Yehova anauza Aisiraeli. Iye anawalamula kuti: “Sonkhanitsani anthu, amuna, akazi, ana . . . , kuti amvetsere ndi kuphunzira, pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi. Ana awo amene sadziwa chilamulo ichi azimvetsera, ndipo aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu.”​—Deut. 31:12, 13.

Ana akhoza kuphunzira Mawu a Yehova kuyambira ali akhanda. Ponena za Timoteyo, mtumwi Paulo anati: “Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera.” (2 Tim. 3:15) Pa misonkhano m’Nyumba ya Ufumu, ngakhale ana aang’ono amayamba kuphunzira mfundo zimene zikukambidwa ndipo amayamba kuzolowera nyimbo za Ufumu. Iwo amaphunziranso kugwiritsa ntchito ndiponso kulemekeza Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, pa misonkhano yathu ana amaonanso khalidwe la chikondi limene limadziwikitsa Akhristu oona. Yesu anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Anthu mu Nyumba ya Ufumu amakondana ndipo amamva kuti ndi otetezeka. Izi zimathandiza ana kuona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri kwa moyo wawo wonse.

Mukakhala ndi chizolowezi chofika mofulumira pa Nyumba ya Ufumu, n’kukhalanso pang’ono misonkhano ikatha, ana anu amakhala ndi mpata wopeza mabwenzi. Ana anu asamangocheza ndi ana anzawo, ndi bwino kuti muziwadziwikitsanso kwa abale ndi alongo a misinkhu yosiyanasiyana. Ana anu akadziwana ndi anthu akuluakulu, amazindikira kuti anthu oterewa amadziwa zambiri ndipo ali ndi nzeru. Uziya, mfumu yachinyamata ya Yuda, inkachita bwino chifukwa chakuti Zekariya “anali kumulangiza kuti aziopa Mulungu woona.” Masiku anonso, anthu amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri mokhulupirika amathandiza kwambiri achinyamata. (2 Mbiri 26:1, 4, 5) Mukakhala m’Nyumba ya Ufumu, afotokozereni ana anu ntchito ya laibulale, bolodi la chidziwitso ndiponso zinthu zina.

Athandizeni Kudziwa Gulu la Padziko Lonse

Ana ayenera kudziwa kuti mpingo wanu ndi mbali ya gulu la padziko lonse m’mipingo yoposa 100,000. Afotokozereni mbali zosiyanasiyana za gululi, mmene limagwirira ntchito ndiponso zimene angachite kuti athandize nawo pa ntchito ya gululi. Afotokozereni chifukwa chake mumafunitsitsa kupezeka pa misonkhano ya dera ndi yachigawo ndiponso kuchezeredwa ndi woyang’anira dera.​—Onani bokosi lakuti,  “Zimene Mungaphunzire pa kulambira kwa Pabanja,” patsamba 28.

Ngati n’kotheka, muziitana oyang’anira oyendayenda, amishonale, atumiki a pa Beteli ndi anthu ena amene akuchita utumiki wa nthawi zonse kuti mudzadye nawo chakudya kunyumba kwanu. Musaganize kuti anthu amenewa sakhala ndi nthawi yocheza ndi ana. Atumiki a nthawi zonse amenewa, amayesetsa kutsanzira Yesu yemwe nthawi zonse ankalandira ana ndiponso kucheza nawo. (Maliko 10:13-16) Ana anu akamamvetsera atumiki a Yehova amenewa akusimba zimene akumana nazo n’kumaona mmene akusangalalira mu utumiki wawo, iwonso angayambe kukhala ndi cholinga chodzachita utumiki wa nthawi zonse.

Monga banja, mungachitenso chiyani kuti muthandize ana anu kulidziwa bwino gulu la Yehova? Nawa malangizo ena. Konzani zoti banja lanu liziphunzira kabuku kakuti Mboni za Yehova​—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? kapena nkhani zofotokoza mbiri ya moyo wa abale ndi alongo zimene zili m’magazini a Nsanja ya Olonda. Tsindikani makhalidwe amene atumiki a Yehova asonyeza monga kudzipereka, kudzichepetsa ndiponso kukhulupirika. Sonyezani mmene Yehova wawagwiritsira ntchito kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Gwiritsani ntchito mavidiyo amene gulu la Yehova latulutsa kuti muwaphunzitse mfundo zofunika kwambiri zakale ndiponso za masiku ano. Ngati mungakwanitse, konzani zokaona ofesi ya nthambi ndiponso nyumba za Beteli za m’dziko lanu kapena za m’mayiko ena. Ana anu akaona malo amenewa, angachite chidwi kwambiri kudziwa mmene gulu la Yehova limagwirira ntchito. Motsogozedwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, gululi limapereka chakudya chauzimu ndiponso malangizo kwa abale padziko lonse ngati mmene zinalili m’nthawi ya atumwi.​—Mat. 24:45-47; Mac. 15:22-31.

Aphunzitseni Mogwirizana ndi Msinkhu Wawo

Pophunzitsa ana anu, muzikumbukira mmene Yesu ankaphunzitsira atumwi ake. Pa nthawi ina iye anawauza kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” (Yoh. 16:12) Yesu sankaphunzitsa ophunzira ake zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Koma iye ankawaphunzitsa mfundo zofunika za choonadi pang’onopang’ono n’cholinga chakuti amvetse bwinobwino. Inunso musamaphunzitse ana anu zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Mukamawaphunzitsa zinthu zokhudza gulu pang’onopang’ono koma mosalumphalumpha, ana anu azikhala ndi chidwi ndiponso azisangalala kuphunzira za mpingo wachikhristu. Ana anu akamakula muzibwereza zimene munawaphunzitsa n’kuwonjezera mfundo zina.

Mpingo wachikhristu ndi malo abwino kwambiri amene angatithandize kukhala olimba mwauzimu ndipo achinyamata amene amachita zinthu ndi mpingo amakhala okonzeka kulimbana ndi mayesero m’dziko la Satanali. (Aroma 12:2) Sitikukayikira kuti mudzasangalala kuthandiza ana anu kudziwa bwino gulu la Yehova. Mulungu adalitse ana anu kuti akhalabe okhulupirika ku gulu lake ndiponso kwa Mulungu wachikondi amene tikum’tumikira.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 28]

 Zimene Mungaphunzire pa Kulambira kwa Pabanja

M’munsimu muli mfundo zina zokhudza gulu zimene mungakambirane pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja.

▪ Kambiranani mbiri ya mpingo wanu. Kodi mpingowo unakhazikitsidwa liti ndipo unayamba bwanji? Kodi mpingowo unasonkhanapo m’Nyumba za Ufumu ziti? Mukamakambirana zimenezi, mungachite bwino kuitana m’bale kapena mlongo amene wakhala mu mpingowo kwa nthawi yaitali kuti adzayankhe ena mwa mafunso amene ana anu angakhale nawo.

▪ Fotokozani cholinga cha misonkhano ya mpingo yosiyanasiyana ndiponso misonkhano ikuluikulu. Fotokozaninso mmene ana anu angapindulire ndi misonkhano imeneyi.

▪ Kambiranani kufunika kwa masukulu amene gulu la Yehova linakhazikitsa. Kambirananinso zinthu zosangalatsa zimene anthu amene anaphunzira ku masukulu amenewa akuchita.

▪ Thandizani ana anu kudziwa kufunika kokhala ofalitsa okhazikika a uthenga wabwino. Afotokozereni kuti zimene iwowo amachita mu utumiki zimaphatikizidwa mu lipoti la ntchito ya padziko lonse limene limalembedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

▪ Kambiranani mbali zosiyanasiyana za utumiki wa nthawi zonse zimene achinyamata angachite m’gulu la Yehova. Mfundo zambiri mungazipeze m’mutu 10 wa buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova.

▪ Thandizani ana anu kumvetsa mmene zinthu zimayendera mu mpingo ndiponso chifukwa chake. Afotokozereni chifukwa chake sayenera kuchita zinthu zosemphana ndi gulu la Yehova ngakhale zitakhala zazing’ono. Asonyezeni zimene angachite kuti athandize kuti zinthu ziziyenda bwino mu mpingo mwa kutsatira malangizo a akulu.

[Chithunzi]

Ana anu adzapindula akamacheza ndi anthu amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali mu mpingo

[Zithunzi patsamba 26]

Mofanana ndi Aisiraeli akale, makolo ayenera kuyesetsa kupereka mayankho ogwira mtima kwa ana awo akawafunsa mafunso okhudza gulu la Yehova