Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu

Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu

Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu

“Mawu anu azikhala . . . okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”​—AKOL. 4:6.

1, 2. Kodi achinyamata ambiri amaiona bwanji nkhani yokhala osiyana ndi ena ndipo chifukwa chiyani?

MOSAKAYIKIRA, mwaonapo kuti kupewa kutengera zochita za anzanu n’kovuta kwambiri. N’kutheka kuti pa nthawi ina munthu wina anakukakamizani kuti muchite zinthu zimene munkadziwa kuti si zoyenera. Kodi mumamva bwanji izi zikachitika? Mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Christopher anati: “Nthawi zina ndimangofuna nditalowa pansi kapena kungochita zimene anzanga onse akuchita kuti ndisamaoneke ngati wotsalira.”

2 Kodi inu mumafuna kuchita zoti musangalatse anzanu? Ngati ndi choncho n’chifukwa chiyani? Kodi mwina mumafuna kuti iwo azikukondani? Maganizo amenewa paokha si olakwika. Ngakhale anthu akuluakulu amafunanso kukondedwa ndi anzawo. Palibe amene amasangalala akamasalidwa, kaya akhale wamng’ono kapena wamkulu. Komabe si nthawi zonse pamene anthu amakuyamikirani chifukwa chokana kuchita zoipa. Ngakhalenso Yesu anakumanapo ndi vuto limeneli koma iye ankachitabe zabwino. Anthu ena ankamutsatira ndipo anakhala ophunzira ake pomwe ena ankanyoza Mwana wa Mulunguyu ndipo ‘ankamuona ngati wopanda pake.’​—Yes. 53:3.

Kukhala Osiyana ndi Anzanu N’kovuta

3. N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwitsa kumangotsatira zofuna za anzanu?

3 Nthawi zina mungafune kumangotsatira zofuna za anzanu kuti azikukondani. Koma kumeneku kungakhale kulakwitsa. Akhristu sayenera kukhala ngati ‘tiana, otengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde.’ (Aef. 4:14) Ana aang’ono angatengeke mosavuta ndi zochita za anthu ena. Koma inu monga achinyamata mukukula. Choncho, ngati mumakhulupirira zoti mfundo za Yehova n’zopindulitsadi, muyenera kuchita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chanucho. (Deut. 10:12, 13) Mukapanda kutero, ndiye kuti anthu ena azikusankhirani zochita ndipo mudzangokhala ngati chidole chawo.​—Werengani 2 Petulo 2:19.

4, 5. (a) Kodi Aroni analephera bwanji kukana kuchita zimene anzake ankafuna, ndipo kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi? (b) Kodi anzanu angakukakamizeni kuchita zofuna zawo m’njira ziti?

4 Pa nthawi ina Aroni, yemwe anali m’bale wake wa Mose, anangotsatira zofuna za anzake chifukwa choopa kuwakhumudwitsa. Aisiraeli atamukakamiza kuti awapangire mulungu, iye anamvera. Sikuti Aroni anali munthu wamantha. Izi zisanachitike, anapita ndi Mose kukalankhula ndi Farao, yemwe anali wamphamvu kwambiri ku Iguputo. Aroni anauza Farao molimba mtima uthenga wa Mulungu. Koma pamene Aisiraeli anzake anamukakamiza kuchita zoipa, Aroni analolera. Zimenezi zikusonyeza kuti n’zovuta kukana kuchita zimene anzanu akufuna. Aroni analimba mtima polankhula zimene sizinasangalatse mfumu ya Igupto, koma analephera kuchita zimenezi ndi Aisiraeli anzake.​—Eks. 7:1, 2; 32:1-4.

5 Chitsanzo cha Aroni chikusonyeza kuti si achinyamata okha kapena anthu amene amafuna kuchita zoipa omwe amangotsatira zofuna za anzawo. Vutoli limakhudzanso anthu amene amafuna kuchita zabwino ngati inuyo. Anzanu angakunyengerereni kuti muchite zoipa mwa kukudererani, kukunyozani kapena kukutsutsani. Kaya angakukakamizeni mwa njira iti, kukhala osiyana ndi anzanu n’kovuta. Kuti mupewe kumangotsatira zimene anzanu amafuna, musamakayikire ngakhale pang’ono zimene mumakhulupirira.

“Pitirizani Kudziyesa Kuti Mudziwe Kuti Ndinu Munthu Wotani”

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani si bwino kukayikira zimene mumakhulupirira, ndipo kodi mungatani kuti musamakayikire? (b) Kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati kuti musamakayikire zimene mumakhulupirira?

6 Kuti mupewe kutengera zofuna za anzanu simuyenera kukayikira kuti zimene mumakhulupirira ndiponso mfundo zimene mumayendera ndi zolondola. (Werengani 2 Akorinto 13:5.) Izi zingakuthandizeni kukhala wolimba mtima ngakhale kuti mwina ndinu wamantha mwachibadwa. (2 Tim. 1:7, 8) Koma ngakhale munthu atakhala wolimba mtima, zimakhala zovuta kuti nthawi zonse azitsatira zinthu zimene sazikhulupirira ndi mtima wonse. Choncho, ndi bwino kufufuza umboni wotsimikizira kuti mfundo za m’Baibulo zimene mwaphunzitsidwa ndi zoona. Yambani ndi mfundo zoyambirira za choonadi. Mwachitsanzo, mumakhulupirira kuti kuli Mulungu ndipo mwamvapo anthu ena akunena chifukwa chake nawonso amakhulupirira kuti alipo. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimandichititsa kutsimikizira kuti kuli Mulungu?’ Cholinga cha funso limeneli si kukuchititsani kukayikira koma kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Mofananamo, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikudziwa bwanji kuti Malemba ndi ouziridwa ndi Mulungu?’ (2 Tim. 3:16) ‘N’chifukwa chiyani ndikukhulupirira kuti ano ndi “masiku otsiriza”?’ (2 Tim. 3:1-5) ‘Kodi n’chifukwa chiyani ndimakhulupirira kuti ndikhoza kupindula ndikamatsatira mfundo za Yehova?’​—Yes. 48:17, 18.

7 Mwina simungakonde kudzifunsa mafunso amenewa poopa kuti simupeza mayankho ake. Koma kuchita zimenezi kungafanane ndi kusayang’ana nthawi pa wotchi yanu poopa kuti mupeza nthawi yopita kwinakwake itakwana. Ngati nthawi yonyamuka yakwana muyenera kuchitapo kanthu. Mofanana ndi zimenezi, ngati mwazindikira kuti mukukayikira zinthu zina zimene mumakhulupirira muyenera kuchitapo kanthu.​—Mac. 17:11.

8. Fotokozani zimene mungachite kuti musamakayikire zoti lamulo la Mulungu loletsa dama ndi lanzeru?

8 Taonani chitsanzo ichi. Baibulo limatilimbikitsa kuti “thawani dama.” Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndingachite bwino kutsatira lamulo limeneli?’ Tsopano ganizirani zifukwa zonse zimene anzanu amachitira khalidwe loipali. Ganiziraninso zifukwa zosiyanasiyana zosonyeza kuti munthu amene amachita dama amakhala ‘akuchimwira thupi lake.’ (1 Akor. 6:18) Ndiyeno ganizirani zifukwazo, n’kudzifunsa kuti: ‘Kodi njira yabwino imene ndiyenera kutsatira ndi iti? Kodi ndi nzeru kuchitadi chiwerewere?’ Taganiziraninso nkhani imeneyi n’kudzifunsa kuti, ‘Ngati nditachita chiwerewere, kodi ndidzamva bwanji mu mtima mwanga?’ Anzanu ena akhoza kusangalala nazo, koma kodi mudzamva bwanji mukakhala ndi makolo anu kapena Akhristu anzanu ku Nyumba ya Ufumu? Kodi mungamamve bwanji mukafuna kupemphera kwa Mulungu? Kodi mungalole kuti musakhalenso oyera pamaso pa Mulungu pongofuna kusangalatsa anzanu a kusukulu?

9, 10. Kodi kusakayikira zimene mumakhulupirira kungakuthandizeni bwanji pamene muli ndi anzanu?

9 Ngati ndinu wachinyamata muli pa msinkhu umene mukuyamba kukhala ndi “luntha la kuganiza” kusiyana ndi kale lonse. (Werengani Aroma 12:1, 2.) Gwiritsani ntchito nthawi imeneyi kuganizira zimene kukhala wa Mboni za Yehova kumatanthauza kwa inu. Kusinkhasinkha zimenezi kudzakuthandizani kuti musamakayikire zimene mumakhulupirira. Ndiyeno anzanu akamakukakamizani kuchita zoipa, mudzatha kukana molimba mtima nthawi yomweyo. Maganizo anu adzafanana ndi a mtsikana wina wachikhristu amene anati: “Ndikakana zimene anzanga akufuna, sindichita manyazi chifukwa zimangowathandiza kudziwa zimene ndimakhulupirira. Sikuti ndimachita izi chifukwa cha ‘chipembedzo changa’ basi, koma ndi mfundo zimene ndimayendera pa moyo wanga ndipo zimakhudza maganizo anga ndi zolinga zanga.”

10 Pamafunika khama ndithu kuti mutsatire zimene mukudziwa kuti ndi zolondola. (Luka 13:24) Mwina mungamaone ngati kuchita zimenezi n’kosathandiza. Koma dziwani kuti: Mukamachita zinthu ngati kuti mukufuna kupepesa kapena simukutsimikiza zimene mukufuna kuchita, anthu ena adzazindikira zimenezo ndipo adzapitiriza kukukakamizani. Koma ngati mungalankhule motsimikiza mudzadabwa poona kuti anzanuwo asiya nthawi yomweyo.​—Yerekezerani ndi Luka 4:12, 13.

‘Muziyamba Mwaganiza Musanayankhe’

11. Kodi kukonzekera zimene mungachite kuti musamangotsatira zofuna za anzanu n’kofunika motani?

11 Chinthu china chofunika kwambiri kuti musamangotsatira zofuna za anzanu ndi kukonzekera. (Werengani Miyambo 15:28.) Pokonzekera muziganizira zimene anzanu angakukakamizeni kuti muchite. Nthawi zina kukonzekera kungakuthandizeni kupewa zimenezi. Tiyerekeze kuti mwaona gulu la anzanu likusuta fodya kutsogolo. N’zachidziwikire kuti akhoza kukuuzani kuti musute nawo. Ngati mutadziwa zimenezi, kodi mungatani? Lemba la Miyambo 22:3 limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” Ngati mungasinthe njira mukhoza kupewa kukumana nawo. Kuchita zimenezi si mantha koma ndi nzeru.

12. Kodi mungayankhe bwanji anthu akakufunsani mokupanikizani?

12 Bwanji ngati mwakumana nawo mwachindunji? Tiyerekeze kuti mnzanu wakufunsani modabwa kuti, ‘Kodi iweyo sunagonanepo ndi winawake?’ Chofunika ndi kutsatira malangizo a pa Akolose 4:6 akuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” Monga mmene lemba limeneli likunenera, yankho lanu lidzadalira mmene zinthu zilili. N’kutheka kuti simungafunike kumufotokozera mfundo zambirimbiri za m’Baibulo. Mwina mukhoza kungoyankha mwachidule koma motsimikiza. Mwachitsanzo, poyankha funso lokhudza kugonana lija mungayankhe kuti, “Inde sindinagonanepo ndi munthu wina,” kapena munganene kuti, “Sizikukukhudza zimenezo.”

13. Kodi kuzindikira kungakuthandizeni bwanji kuyankha mnzanu akakunyozani?

13 Nthawi zambiri Yesu ankangoyankha mwachidule akaona kuti kulankhula zambiri sikungathandize. Pa nthawi ina atafunsidwa ndi Herode, Yesu sanayankhe kalikonse. (Luka 23:8, 9) Nthawi zambiri ndi bwino kusayankha mafunso achipongwe. (Miy. 26:4; Mlal. 3:1, 7) Koma nthawi zina mungaone kuti munthu wina akufunadi kudziwa chifukwa chake simukuchita zinthu zina monga kugonana, ngakhale kuti poyamba munthuyo angakhale atakunyozani. (1 Pet. 4:4) Zikatero, mungafunike kumufotokozera bwinobwino mfundo za m’Baibulo zimene mumayendera. Ngati izi zikufunikadi musaope kumufotokozera. Muzikhala “okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani.”​—1 Pet. 3:15.

14. Kodi mungatani kuti mupanikizenso munthu amene akukuvutitsani?

14 Nthawi zina mukhoza kupanikizanso anthu amene akukuvutitsani. Koma muyenera kuchita zimenezi mosamala. Mwachitsanzo, ngati mnzanu akukuuzani kuti musute mukhoza kunena kuti, “Ayi sindikufuna.” Kenako n’kumuuza kuti, “Ndimakuona ngati ndiwe wozindikira ndiye ndikudabwa kukuona ukusuta.” Kodi mwaona mmene nanunso mukhoza kumupanikizira. M’malo moti inuyo mufotokoze chifukwa chimene simusutira, mnzanuyo ndi amene aziganiza zimene zimamuchititsa kusuta. *

15. Kodi ndi pa nthawi iti pamene muyenera kuchoka pamalo amene anzanu akukukakamizani kuchita zoipa, ndipo chifukwa chiyani?

15 Nanga bwanji ngati mutayesetsa kwambiri koma anzanuwo akukuvutitsanibe? Zikatero ndi bwino kungochokapo. Mukakhalabe pamalowo, mukhoza kulolera zofuna za anzanuwo. Choncho ingochokanipo. Mukachoka musaganize kuti mwagonja. Tikutero chifukwa chakuti simunalole kuchita zimene anzanuwo akufuna. Simunakhale ngati chidole cha anzanuwo ndipo mwakondweretsa mtima wa Yehova.​—Miy. 27:11.

Muzikhala ndi ‘Zolinga Zimene Zingakupindulireni’

16. Kodi nthawi zina tingakakamizike bwanji kuchita zinthu zosayenera ndi anthu amene amati ndi Akhristu?

16 Nthawi zina tingakakamizike kuchita zinthu zoipa ndi achinyamata amene amati ndi atumiki a Yehova. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati munthu woteroyo wakuitanani kukacheza kwinakwake koma mutafika kumaloko mwapeza kuti palibe munthu wamkulu amene akuyang’anira zinthu? Nanga bwanji ngati wachinyamata wina amene amati ndi wachikhristu wabweretsa mowa pamene inuyo ndiponso ena amene ali pamalowo sanafike pa msinkhu wololedwa kumwa mowa? Pakhoza kuchitika zinthu zina zofuna kuti mutsatire chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo. Mtsikana wina wachikhristu ananena kuti: “Ine ndi mng’ono wanga tinatuluka m’chipinda chimene tinkaonera filimu imene anthu a mufilimuyo ankatukwana. Anzathu ena anakhalabe n’kumaonera. Makolo athu anatiyamikira kwambiri chifukwa cha zimene tinachita. Koma anzathu amene ankaonerawo anakwiya kwambiri chifukwa chakuti tinawachititsa kuoneka ngati oipa.”

17. Popita kokacheza kodi n’chiyani chimene mungachite n’cholinga chakuti mutsatire mfundo za Mulungu?

17 Chitsanzo chimene takambiranachi chikusonyeza kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo kungakhale kovuta. Koma musasiye kuchita zinthu zimene mukudziwa kuti ndi zolondola. Kuti izi zitheke, muzikhala okonzeka. Mukapita kukacheza kwinakwake, muzikonzeratu njira yochokera ngati patachitika zinthu zimene simumaziyembekezera. Achinyamata ena amakambirana ndi makolo awo kuti akangowaimbira foni abwere kumalo amene akucheza kudzawatenga. (Sal. 26:4, 5) Kuchita zimenezi n’kopindulitsa.​—Miy. 21:5.

‘Sangalalani ndi Unyamata Wanu’

18, 19. (a) Kodi mukudziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti muzisangalala? (b) Kodi Mulungu amamva bwanji akaona anthu amene satengera zochita za anzawo?

18 Yehova anakulengani m’njira yoti muzisangalala ndi moyo ndipo amafunadi kuti muzisangalala. (Werengani Mlaliki 11:9.) Kumbukirani kuti zimene anzanu ambiri amachita ndi “zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” (Aheb. 11:25) Koma Mulungu woona amafuna kuti musangalale kuposa pamenepo. Iye amafuna kuti musangalale kwamuyaya. Choncho mukamayesedwa kuti muchite zinthu zimene Mulungu amadana nazo, muyenera kukumbukira kuti zimene Yehova amakuuzani kuti muchite, nthawi zonse zimakhala zokupindulitsani.

19 Popeza ndinu wachinyamata, muyenera kudziwa kuti mukachita zosangalatsa anzanu, ambiri mwa anzanuwo akhoza kukuiwalani pakapita zaka zambiri. Mosiyana ndi zimenezi, mukapewa kutsatira zofuna za anzanu, Yehova amaona ndipo sadzakuiwalani ndiponso sadzaiwala kukhulupirika kwanu. Iye ‘adzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira.’ (Mal. 3:10) Kuwonjezera pamenepa, iye adzakupatsani mowolowa manja mzimu woyera umene ungakuthandizeni pa zinthu zimene simungakwanitse panokha. Ndithudi, Yehova adzakuthandizani kupewa kutengera zochita za anzanu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani bokosi lakuti, “Mmene Mungakonzekerere” m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, masamba 132 mpaka 133.

Kodi Mukukumbukira?

• Perekani umboni wosonyeza kuti kupewa kutsatira zofuna za anzanu n’kovuta.

• Kodi kusakayikira zimene timakhulupirira kungatithandize bwanji kupewa kutengera zofuna za anzathu?

• Kodi mungakonzekere bwanji kupewa kutengera zofuna za anzanu?

• Kodi mukudziwa bwanji kuti Yehova amayamikira kukhulupirika kwanu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

N’chifukwa chiyani Aroni analolera kupanga fano la mwana wa ng’ombe?

[Chithunzi patsamba 10]

Muzikonzekera zimene mungayankhe