Zabwino ‘Zimene Anachita Zapita Naye Limodzi’
Zabwino ‘Zimene Anachita Zapita Naye Limodzi’
THEODORE JARACZ, yemwe anali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anamaliza utumiki wake wa padziko lapansi Lachitatu m’mawa pa June 9, 2010. Iye anali ndi zaka 84 ndipo anasiya mkazi, amene anakhala naye m’banja zaka 53, dzina lake Melita. Anasiyanso mchemwali wake mmodzi yemwe ali ndi mwana wamwamuna mmodzi ndi aakazi awiri.
M’bale Jaracz anabadwa pa September 28, 1925, ku Pike County ku Kentucky, m’dziko la United States. Iye anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwa Yehova ali ndi zaka 15 pa August 10, 1941. Patapita zaka ziwiri, ali ndi zaka 17, anayamba upainiya wokhazikika. Kuyambira pamenepa anakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka pafupifupi 67.
Mu 1946, ali ndi zaka 20, m’bale Jaracz analowa nawo kalasi la nambala 7 la Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Atamaliza maphunzirowa iye anatumizidwa kukatumikira monga woyang’anira woyendayenda ku Cleveland, Ohio ku United States. Mu 1951 anatumizidwa kukatumikira monga woyang’anira nthambi ya ku Australia. Buku la 1983 Yearbook of Jehovah’s Witnesses linanena kuti, M’bale Jaracz “analimbikitsa kwambiri abale m’dziko lonse la Australia. Iye anali wakhama poyendetsa zinthu mwadongosolo m’gulu la Mulungu ndiponso pa ntchito yolalikira.”
Atabwerera ku United States, M’bale Jaracz anakwatira Melita Lasko pa December 10, 1956. Atakwatirana anayamba kutumikira monga oyendayenda ndipo anatumikira mwakhama m’madera ndiponso zigawo zambiri za ku United States. Chakumapeto kwa chaka cha 1974 M’bale Jaracz anaitanidwa kukakhala m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.
Anthu ambiri adzakumbukira M’bale Jaracz monga mtumiki wodzipereka ndiponso wokhulupirika wa Yehova amene ankaika maganizo ake onse potumikira Mulungu. Iye ankakonda ndiponso kusamalira mkazi wake komanso ankaika zofuna za ena patsogolo. (1 Akor. 13:4, 5) M’bale Jaracz anasonyeza kuti ankaganizira anthu chifukwa ankafunitsitsa kuti munthu aliyense azichitiridwa zinthu mwachilungamo ndiponso mwachifundo. Kuwonjezera pamenepa, iye anasonyezanso kuti ankakonda ndiponso kuganizira ena pochita khama mu utumiki wakumunda.
Tikumva chisoni chifukwa cha imfa ya munthu wolimbikira ntchito ndiponso amene ankakondedwa ndi banja la Beteli komanso abale padziko lonse. Ngakhale zili choncho, ndife osangalala kuti M’bale Jaracz anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Tili ndi chikhulupiriro kuti iye ‘anasonyeza kukhulupirika kwake mpaka imfa, ndipo wapatsidwa mphoto ya moyo.’ (Chiv. 2:10) Sitikukayikanso kuti zabwino ‘zimene anachita zapita naye limodzi.’—Chiv. 14:13.