Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Kodi ndani anayambitsa chiphunzitso chakuti Mulungu anakonzeratu zinthu zonse zimene zimachitika?
John Calvin (Jean Cauvin) ndi amene anayambitsa chiphunzitso chakuti Mulungu anakonzeratu zinthu zonse zimene zimachitika. Ziphunzitso zake zimapezeka m’matchalitchi monga Reformed, Presbyterian, Congregational, ndi Puritan.—9/1, masamba 18-21.
• Kodi mkazi amene Kaini anakwatira anachokera kuti?
Hava anabereka “ana ena aamuna ndi aakazi.” (Gen. 5:4) Choncho mkazi wa Kaini ayenera kuti anali mbadwa ya Havayo.—9/1, tsamba 25.
• Kodi Mulungu anatumiza mngelo uti kuti atsogolere Aisiraeli pamene ankawatulutsa ku Iguputo? (Eks. 23:20, 21)
N’zosakayikitsa kuti mngelo ‘amene anali ndi dzina la Yehova,’ anali Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu. Patapita nthawi mwana ameneyu anadziwika kuti ndi Yesu.—9/15, tsamba 21.
• N’chifukwa chiyani buku la 1 Akorinto limanena za nyama zoperekedwa nsembe ku mafano?
Nyama zinkaperekedwa nsembe mu akachisi a Agiriki ndiponso Aroma, komabe nyama imene sinkadyedwa pamwambowu ankaigulitsa m’misika. Akhristu sankachita nawo miyambo yachipembedzo yachikunja, koma nyama yotsala popereka nsembe imene inkagulitsidwa m’misika sankayenera kuiona monga yodetsedwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muzidya popanda kufunsa mafunso, poopera chikumbumtima chanu, chifukwa ‘dziko lapansi ndi zonse za mmenemo ndi za Yehova.’” (1 Akor. 10:25, 26)—10/1, tsamba 12.
• Polambira Yehova, kodi ndi zifukwa ziti zimene tingapereke pofuna kudzikhululukira zimene Mulungu amaona kuti n’zosamveka?
‘N’zovuta kwambiri. Sindifuna. Ndine wotanganidwa. Sindingathe. Wina wake anandikhumudwitsa.’ Zifukwa zimenezi siziyenera kutilepheretsa kumvera malamulo a Mulungu.—10/15, masamba 12-15.
• Kodi mungatani kuti misonkhano yachikhristu izikhala yolimbikitsa kwa inuyo ndiponso kwa anthu ena?
Muzikonzekera. Muzipezekapo nthawi zonse. Muzifika pa nthawi yabwino. Muzitenga zonse zofunika. Muzipewa zododometsa. Muziyankha pa misonkhano. Ndemanga zanu zizikhala zazifupi. Muzikwaniritsa mbali imene mwapatsidwa. Muziyamikira anthu amene atenga nawo mbali. Muzicheza ndi anthu amene afika pa misonkhano.—10/15, tsamba 22.
• Aroni analephera kukana kuchita zimene anzake ankafuna. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhaniyi?
Mose atachoka, Aisiraeli anakakamiza Aroni kuti awapangire mulungu ndipo Aroni analolera n’kuwapangira. Izi zikusonyeza kuti si achinyamata okha amene amangotsatira zofuna za anzawo. Vutoli limakhudzanso anthu akuluakulu amene amafuna kuchita zabwino. Tiyeni tiziyesetsa kupewa kutsatira zoipa zimene anzathu akufuna.11/15, tsamba 8.
• Kodi mfundo izi ndi zoona kapena zabodza?
Satana alipodi: zoona. (2 Akor. 11:14) Munthu akafa mzimu wake umapita kwinakwake: zabodza. (Mlal. 9:5) Angelo okhulupirika amatisamalira: zoona. (Sal. 34:7) Yesu ndi wofanana mphamvu ndi Mulungu: zabodza. (1 Akor. 11:3.)—12/1, masamba 8-9.