Pezani Madalitso Kudzera mwa Mfumu Yotsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu
Pezani Madalitso Kudzera mwa Mfumu Yotsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu
“Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye.”—YES. 11:2.
1. Kodi anthu ena anena zotani pa nkhani ya mavuto a padziko lonse?
M’CHAKA cha 2006, katswiri wina wa zakuthambo, dzina lake Stephen Hawking, anafunsa kuti: “M’dziko limene ndale sizikuyenda bwino, komanso limene chikhalidwe ndiponso chilengedwe chasokonekera, kodi zingatheke bwanji kuti anthu akhalenso ndi moyo zaka zina 100?” Nkhani ya m’magazini ina inati: “Talephera kuthetsa umphawi ndiponso kubweretsa mtendere padziko lonse. M’malomwake, zikuoneka kuti takwanitsa kuwonjezera umphawi ndiponso kusokoneza mtendere. Zili ngati kuti palibe chimene tachita. Tayesa maboma osiyanasiyana. Tayesanso kuthetsa nkhondo mwa kukhazikitsa bungwe la League of Nations ndiponso kupanga zida zanyukiliya zambirimbiri, poopseza mayiko kuti asachite nkhondo. Tamenya nkhondo zambiri pofuna kuthetsa nkhondo koma taona kuti mwina n’zosatheka.”—New Statesman.
2. Kodi posachedwapa Yehova adzasonyeza bwanji kuti ndi woyenera kulamulira dziko lapansi?
2 Atumiki a Yehova sadabwa ndi mawu amenewa. Baibulo limatiuza kuti anthu sanalengedwe kuti azidzilamulira okha. (Yer. 10:23) Yehova yekha ndiye woyenera kutilamulira. Choncho iye ali ndi udindo wotipatsa mfundo zoti tiziyendera pa moyo wathu, kutifotokozera cholinga cha moyo wathu ndiponso kutithandiza kukwaniritsa cholingacho. Posachedwapa Mulungu adzasonyeza mphamvu zake mwa kuthetsa maboma olephera amene anthu ayesapo. Pa nthawi imeneyi, iye adzawononga onse amene amakana ulamuliro wake womwe ndi woyenera. Mwa kukana ulamuliro wake, amenewa amachititsa anthu kukhalabe akapolo a uchimo, a kupanda ungwiro ndiponso a “mulungu wa nthawi ino,” amene ndi Satana Mdyerekezi.—2 Akor. 4:4.
3. Kodi Yesaya ananeneratu zinthu ziti zokhudza Mesiya?
3 M’dziko lapansi la Paradaiso, Yehova adzalamulira anthu mwachikondi kudzera mu Ufumu wa Mesiya. (Dan. 7:13, 14) Ponena za Mfumu imeneyi Yesaya analosera kuti: “Nthambi idzatuluka pachitsa cha Jese, ndipo mphukira yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso. Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziwa zinthu ndi woopa Yehova.” (Yes. 11:1, 2) Kodi mzimu woyera wa Mulungu wathandiza bwanji Yesu Khristu, yemwe ndi ‘nthambi yotuluka pachitsa cha Jese,’ kukhala woyenera kulamulira anthu? Kodi ndi madalitso ati amene anthu angapeze mu ulamuliro wake? Nanga kodi tingatani kuti tipeze madalitso amenewa?
Mulungu Anasankha Yesu Kukhala Wolamulira
4-6. N’chiyani chikuchititsa Yesu kukhala woyenera kutumikira ngati Mfumu yanzeru ndi yachifundo, Mkulu wa Ansembe ndiponso Woweruza?
4 Cholinga cha Yehova n’chakuti anthu ake akhale angwiro motsogoleredwa ndi Mfumu yanzeru ndi yachifundo, yomwe ndi Mkulu wa Ansembe komanso Woweruza. N’chifukwa chake Mulungu anasankha Yesu Khristu, amene anamuthandiza ndi mzimu woyera, kuti akhale woyenera kukwaniritsa maudindo ofunika kwambiri amenewa. Tiyeni tione zifukwa zina zotsimikizira kuti Yesu adzakwaniritsadi bwinobwino maudindo amene Mulungu anamupatsa.
5 Yesu amadziwa bwino kwambiri Mulungu. Akol. 1:15) Izi n’zimene zinachititsa Yesu kunena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yoh. 14:9.
Mwana wobadwa yekha ameneyu wakhala ndi Mulungu kwa zaka zankhaninkhani ndipo amawadziwa bwino Atate akewa kuposa wina aliyense. Pa nthawi imeneyi, Yesu anatengera kwambiri makhalidwe a Yehova moti mpake kutchedwa “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (6 Yesu ndi wachiwiri kwa Yehova ndipo amadziwa kwambiri zinthu zonse za m’chilengedwe kuphatikizapo anthu. Pa Akolose 1:16, 17 timawerenga kuti: “Kudzera mwa iye [Mwana wa Mulungu] zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka . . . Iye ali patsogolo pa zinthu zina zonse, ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye.” Ndiye tangoganizani. Yesu monga “mmisiri waluso” wa Mulungu, anathandiza kulenga zinthu zina zonse. Choncho iye amadziwa bwino chilichonse kuyambira pa tinthu tosaoneka ndi maso mpaka kufika pa zinthu zogometsa monga ubongo wa munthu. Mpake kuti Khristu amatchedwa kuti nzeru.—Miy. 8:12, 22, 30, 31.
7, 8. Kodi mzimu wa Mulungu unathandiza bwanji Yesu pa utumiki wake?
7 Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Yesu anati: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu, ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.” (Luka 4:18, 19) Zikuoneka kuti Yesu atabatizidwa, mzimu woyera unamukumbutsa zinthu zimene anaphunzira asanabwere padzikoli. Unamukumbutsanso zimene Mulungu anafuna kuti akwaniritse monga Mesiya pa utumiki wake padziko lapansi.—Werengani Yesaya 42:1; Luka 3:21, 22; Yohane 12:50.
8 Yesu anali munthu woposa onse amene anakhalako komanso anali Mphunzitsi waluso. Zili choncho chifukwa chakuti mzimu woyera unamupatsa mphamvu ndiponso chifukwa chakuti thupi ndi maganizo ake zinali zangwiro. Ndipotu anthu amene ankamumvetsera ‘anadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.’ (Mat. 7:28) Chinthu china n’chakuti, Yesu ankathana ndi zinthu zimene zimayambitsa mavuto a anthu zomwe ndi uchimo, kupanda ungwiro ndi kusadziwa bwino Mulungu. Komanso ankatha kuona zinthu zimene zinali mu mtima mwa anthu n’kuwathandiza moyenera.—Mat. 9:4; Yoh. 1:47.
9. Kodi kudziwa zimene Yesu anachita ali padziko lapansi kwakuthandizani bwanji kuti muzikhulupirira kuti iye ndi Wolamulira wabwino?
9 Yesu anakhalapo munthu. Zimene Yesu anakumana nazo ali munthu komanso zimene anadziwa chifukwa chokhala ndi anthu opanda ungwiro zinamuthandiza kuti akhale Mfumu yabwino. Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Yesu] anayenera ndithu kukhala ngati ‘abale’ ake m’zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu. Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu. Popeza kuti iye mwini anavutika pamene anali kuyesedwa, amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” (Aheb. 2:17, 18) Popeza Yesu ‘anayesedwa,’ iye amamvera chisoni anthu amene akukumana ndi mayesero. Yesu anasonyeza kuti ndi wachifundo pa nthawi imene anali kuchita utumiki padziko lapansi. Anthu odwala, olumala, oponderezedwa ngakhalenso ana ankamasuka naye. (Maliko 5:22-24, 38-42; 10:14-16) Anthu odzichepetsa ndiponso anjala yauzimu ankakopeka nayenso. Koma anthu onyada, odzikuza ndi ‘osakonda Mulungu’ ankamukana, kudana naye ndiponso kumutsutsa.—Yoh. 5:40-42; 11:47-53.
10. Tchulani umboni waukulu wosonyeza kuti Yesu amatikonda kwambiri.
10 Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Umboni waukulu wosonyeza kuti Yesu ndi woyeneradi kukhala Wolamulira ndi wakuti iye anali wokonzeka kutifera. (Werengani Masalimo 40:6-10.) Khristu ananena kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Mosiyana ndi olamulira opanda ungwiro amene amadyera masuku pamutu anthu awo, Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha anthu.—Mat. 20:28.
Anapatsidwa Mphamvu Yothandiza Anthu Kupindula ndi Dipo
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Yesu ndi Wotiwombola?
11 Ndi nkhani yosangalatsa kudziwa kuti Yesu ndi Mkulu wa Ansembe amene adzatsogolera pothandiza anthu kupindula ndi nsembe ya dipo. Ndipotu ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza zimene adzachite monga Wotiwombola mu ulamuliro wake wa zaka 1,000. Tikakhalabe okhulupirika tidzasangalala ndi madalitso amenewa. Iye anachiritsa odwala ndi olumala, anaukitsa akufa, anadyetsa anthu ambirimbiri ndipo ankatha kulamulira zinthu monga mphepo ndi nyanja. (Mat. 8:26; 14:14-21; Luka 7:14, 15) Sikuti ankachita zimenezi kuti anthu amutamande poona mphamvu zake koma ankachita izi chifukwa cha chifundo ndiponso chikondi. Munthu wina wakhate atamupempha kuti amuchiritse, iye anayankha kuti: “Ndikufuna.” (Maliko 1:40, 41) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu adzasonyezanso chifundo choterechi kwa anthu padziko lonse lapansi.
12. Kodi mawu a pa Yesaya 11:9 adzakwaniritsidwa bwanji?
12 Khristu pamodzi ndi anzake amene adzalamulire naye, adzapitirizabe kugwira ntchito yophunzitsa anthu imene Yesu anaiyambitsa zaka 2,000 zapitazo. Choncho, mawu a pa Yesaya 11:9 adzakwaniritsidwa. Lembali limati: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” Mosakayikira maphunziro ochokera kwa Mulungu amenewa adzaphatikizapo zimene tingachite posamalira dzikoli ndi zolengedwa zonse ngati mmene Adamu anayenera kuchitira. Tikamadzafika kumapeto kwa zaka 1,000, cholinga choyambirira cha Mulungu chomwe chili pa Genesis 1:28 chidzakhala chitakwaniritsidwa. Nsembe ya dipo idzakhalanso itagwira ntchito yake yonse.
Yesu Wapatsidwa Mphamvu Zoweruza
13. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda chilungamo?
13 Khristu “ndi amene Mulungu anamuika kukhala woweruza anthu amoyo ndi akufa.” (Mac. 10:42) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yesu sangafe ndipo chilungamo ndi kukhulupirika zidzakhala lamba wa m’chiuno mwake. (Yes. 11:5) Iye anasonyeza kuti amadana ndi dyera, chinyengo ndi zinthu zina zoipa. Anadzudzulanso anthu amene amachitira nkhanza anthu ovutika. (Mat. 23:1-8, 25-28; Maliko 3:5) Kuwonjezera pamenepa, Yesu sankapusitsidwa ndi maonekedwe a munthu “chifukwa payekha anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.”—Yoh. 2:25.
14. Kodi Yesu akusonyeza bwanji kuti amakonda chilungamo masiku ano, nanga ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa?
14 Yesu amakondabe chilungamo ndipo umboni wake ndi wakuti akuyang’anira ntchito yaikulu yolalikira ndi kuphunzitsa yomwe ikuchitika padziko lonse lapansi kusiyana ndi kale lonse. Palibe munthu, boma ngakhale mzimu woipa umene ungaletse ntchito imeneyi kuti ichitike mmene Mulungu akufunira. Choncho, tisakayikire ngakhale pang’ono kuti Armagedo ikadzatha, chilungamo cha Mulungu chidzakhala ponseponse. (Werengani Yesaya 11:4; Mateyu 16:27.) Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikakhala mu utumiki, ndimaona anthu mmene Yesu ankawaonera? Kodi ndimatumikira Yehova ndi mtima wonse ngakhale pa nthawi imene thanzi langa silili bwino kapena pamene ndili ndi mavuto ena?’
15. Kodi tiyenera kukumbukira mfundo iti ngati tikufuna kutumikira Mulungu ndi mtima wonse?
15 Tidzathandizidwa kuti tizitumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse ngati tikumbukira nthawi zonse kuti ntchito yolalikira ndi ya Mulungu. Iye ndi amene watilamula kuti tizigwira ntchitoyi ndipo amaiyang’anira kudzera mwa Mwana wake komanso amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti alimbitse anthu amene amagwira ntchitoyi. Kodi inu mumaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kutumikira monga antchito anzake a Mulungu limodzi ndi Mwana wake, yemwe amatsogoleredwa ndi mzimu? Ndi Yehova yekha amene angalimbikitse anthu oposa 7 miliyoni, ooneka ngati “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” kuti azilalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu m’mayiko 236.—Mac. 4:13.
Pezani Madalitso Kudzera mwa Khristu
16. Kodi lemba la Genesis 22:18 limafotokoza zotani pa nkhani ya madalitso ochokera kwa Mulungu?
16 Yehova anauza Abulahamu kuti: “Kudzera mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu chifukwa chakuti wamvera mawu anga.” (Gen. 22:18) Izi zikutanthauza kuti anthu onse amene amayamikira zimene Mulungu amawachitira adzalandira madalitso kudzera mwa Mesiya, yemwe ndi mbewu yolonjezedwa. Iwo amatumikira mwakhama ndipo saiwala za madalitso amenewa.
17, 18. Kodi Yehova analonjeza chiyani pa Deuteronomo 28:2, ndipo kodi tikuphunzirapo chiyani?
17 Mulungu anauza mtundu wa Isiraeli, womwe unali mbewu ya Abulahamu, kuti: “Madalitso onsewa [amene atchulidwa m’pangano la Chilamulo] adzakutsata ndi kukupeza chifukwa ukumvera mawu a Yehova Mulungu wako.” (Deut. 28:2) Mfundo imeneyi ikugwiranso ntchito kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Ngati inuyo mukufuna kudalitsidwa ndi Yehova, nthawi zonse muyenera ‘kumvera’ mawu ake. Mukatero ‘madalitso onsewa adzakutsatani ndi kukupezani.’ Koma kodi ‘kumvera’ kumatanthauza chiyani?
18 Mawu akuti kumvera amaphatikizapo kusunga mu mtima Mawu a Mulungu ndi chakudya chauzimu chimene iye amapereka. (Mat. 24:45) Kumvera kumatanthauzanso kutsatira zonena za Mulungu ndi Mwana wake. Yesu ananena kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” (Mat. 7:21) Kumvera Mulungu kumatanthauzanso kugonjera dongosolo lakuti mpingo wachikhristu uzikhala ndi akulu oikidwa omwe ndi “mphatso za amuna.”—Aef. 4:8.
19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilandire madalitso?
19 M’gulu la “mphatso za amuna” limeneli muli abale a m’Bungwe Lolamulira omwe amaimira mpingo wonse wachikhristu. (Mac. 15:2, 6) Ndipo pa chisautso chachikulu tidzaweruzidwa mogwirizana ndi zimene timachitira abale a Khristu amenewa. (Mat. 25:34-40) Motero, chinthu china chimene chingachititse kuti tipeze madalitso ndi kumvera ndiponso kuthandiza odzozedwa a Mulungu.
20. (a) Kodi ntchito yaikulu ya “mphatso za amuna” ndi yotani? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira abale amenewa?
20 M’gulu la “mphatso za amuna” limeneli mulinso abale a m’Makomiti a Nthambi, oyang’anira oyendayenda ndiponso akulu m’mipingo. Anthu onsewa amaikidwa pa udindo ndi mzimu woyera. (Mac. 20:28) Ntchito yaikulu ya abale amenewa ndi kulimbikitsa anthu a Mulungufe “kufikira tonse tidzafike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira tidzakhale munthu wachikulire, wofika pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.” (Aef. 4:13) Tikudziwa kuti abale amenewa nawonso ndi opanda ungwiro ngati ife. Komabe timapeza madalitso tikamamvera pamene akutithandiza monga abusa achikondi.—Aheb. 13:7, 17.
21. N’chifukwa chiyani kumvera Mwana wa Mulungu n’kofunika kwambiri panopa?
21 Posachedwapa Khristu adzawononga dongosolo loipa la Satanali. Izi zikadzachitika moyo wathu udzakhala m’manja mwa Yesu. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu wamupatsa udindo wotsogolera “khamu lalikulu la anthu” ku “akasupe a madzi a moyo.” (Chiv. 7:9, 16, 17) Choncho tiyeni tiyesetse mmene tingathere kumvera ndiponso kuyamikira Mfumu yotsogoleredwa ndi mzimu imene Yehova wakhazikitsa.
Kodi Mwaphunzira Chiyani pa . . .
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Yesu anasonyeza kuti ndi wachifundo pamene anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo
[Zithunzi patsamba 18]
Yesu Khristu akuyang’anira ntchito yaikulu yolalikira imene ikuchitika kuposa kale lonse