Ukalamba Sungatilepheretse Kutumikira Mulungu
Ukalamba Sungatilepheretse Kutumikira Mulungu
Kum’mwera kwa dziko la Spain, mumzinda wotchedwa Málaga, mayi wina dzina lake Ana ndi mwana wake, yemwenso dzina lake ndi Ana, anabatizidwa pa December 19, 2009. Iwo anali m’gulu la anthu 2,352 amene anabatizidwa ku Spain m’chaka cha 2009. Koma chochititsa chidwi ndi anthu awiriwa ndi zaka zawo. Mayiwo anali ndi zaka 107 ndipo mwana wawo anali ndi zaka 83.
Kodi chinawachititsa n’chiyani kuti abatizidwe posonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova? M’zaka za m’ma 1970 munthu wina amene ankakhala m’nyumba yoyandikana ndi nyumba yawo ankaitana Ana wamng’onoyo kuti azichita nawo Phunziro la Buku la Mpingo ku nyumba ya wa Mboni wina. Ana ankapita ku phunziroli mwa apa ndi apo. Koma chifukwa cha ntchito imene ankagwira Ana sanapite patsogolo.
Patapita zaka pafupifupi 10, ana a Ana wamng’onoyo anayamba kuphunzira Baibulo ndipo kenako anakhala atumiki a Yehova. Mmodzi mwa ana akewa dzina lake Mari Carmen anathandiza mayi ake kuti ayambenso kukonda choonadi cha m’Baibulo ndiponso kuphunzira. Kenako agogo ake a Mari Carmen omwe ndi Ana wamkulu, anayambanso kukhala ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi anthu 10 m’banja lawo anabatizidwa.
Pa tsiku la ubatizo wawo, a Ana onse awiri, mayi ndi mwana wake, anali osangalala kwambiri. Ana wa zaka 107 anati: “Yehova wandikomera mtima kwambiri, pondilola kuti ndimudziwe.” Mwana wake anawonjezera kuti: “Paradaiso asanabwere ndikufuna kutumikira Yehova, kuchita chifuniro chake ndiponso kulalikira uthenga wabwino mmene ndingathere.”
Chimene chimachititsa akazi awiri amasiyewa kukhala osangalala kwambiri ndi kupezeka pa misonkhano. Mkulu wina wa mu mpingo wawo anati: “Iwo saphonya msonkhano uliwonse. Nthawi zonse amakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda.”
Chitsanzo chawo pa nkhani ya kukhulupirika chikutikumbutsa mayi wina wamasiye dzina lake Ana, amene “sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku, anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.” Izi zinachititsa kuti akhale ndi mwayi woona Yesu ali mwana. (Luka 2:36-38) Pa nthawi imene anali ndi zaka 84, ukalamba sunalepheretse Ana kutumikira Yehova. Ndi mmenenso zili ndi a Ana awiri amene tatchulawa.
Kodi inu muli ndi achibale amene angakonde kumva uthenga wa m’Baibulo? Kapena kodi munakumanapo ndi munthu wachikulire amene anachita chidwi pamene munamupeza panyumba yake? Anthu amenewa akhoza kukhala ngati a Ana amene tawafotokoza m’nkhani ino ndipo ukalamba sungawalepheretse kutumikira Mulungu woona, Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Yehova wandikomera mtima kwambiri”
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Paradaiso asanabwere ndikufuna kutumikira Yehova”