Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzina la Mulungu M’chigwa cha ku Switzerland

Dzina la Mulungu M’chigwa cha ku Switzerland

Dzina la Mulungu M’chigwa cha ku Switzerland

KODI munamvapo dzina lakuti St. Moritz? Amenewa ndi malo otchuka kwambiri amene anthu ambiri amapitako akakhala pa tchuthi ndipo amapezeka ku chigwa cha Engadine m’dziko la Switzerland. Koma awa ndi malo amodzi okha amene anthu amakonda kukaona akapita kuchigwa chokongolachi m’mphepete mwa mapiri otchedwa Alps, omwe pamwamba pake amakutidwa ndi chipale chofewa. Chigwachi chili kum’mwera cha kum’mawa kwa dziko la Switzerland pafupi ndi dziko la Italy. M’chigwachi mulinso nkhalango yotetezedwa ndi boma kumene kuli mitengo ndi maluwa okongola komanso zinyama. Zonsezi zimalemekeza Mlengi wathu wamkulu Yehova. (Sal. 148:7-10) Koma palinso zinthu zina zokhudza chikhalidwe cha pakatikati pa zaka za m’ma 1600 zomwe zilipobe.

M’chigwachi muli chinthu chinanso chochititsa chidwi chimene chimapezeka panyumba zambiri. Anthu kumeneku ankakonda kulemba dzina la Mulungu pamalo monga pakhomo la nyumba zawo. M’zaka za m’mbuyomu anthu a m’derali ankakongoletsa kunja kwa nyumba zawo mwa kulemba mawu ndi penti kapena mochita kugoba pamakoma ake. M’munsimu mungaone chithunzi cha nyumba ya kumudzi wotchedwa Bever. Panyumbayi analembapo mawu akuti: “Chaka cha 1715. Yehova ndi woyamba ndipo Yehova ndi wotsiriza. Zinthu zonse ndi zotheka ndi Mulungu ndipo popanda iye palibe zimene zingatheke.” Mawu olembedwa kalekale amenewa amatchula dzina la Mulungu kawiri.

Mukhoza kuona zimene zinalembedwa kale kwambiri panyumba ina m’mudzi wotchedwa Madulain. Panyumbayi analembapo mawu akuti: “Masalimo 127. Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe. Lucius Rumedius. Chaka cha 1654.”

N’chifukwa chiyani anthu a m’chigwachi ankalemba dzina la Mulungu pamalo oonekera? Kalelo, pa nthawi imene anthu ambiri anachoka m’tchalitchi cha katolika n’kuyambitsa matchalitchi ena, Baibulo linafalitsidwa mu Chiromansh. Chilankhulochi n’chochokera ku Chilatini ndipo chimalankhulidwa ku Engadine. Ndipotu Baibulo ndi buku loyamba kumasuliridwa m’chilankhulo chimenechi. Chifukwa chochita chidwi ndi zimene anawerenga m’Mawu a Mulungu, anthu akumeneku ankalemba kunja kwa nyumba zawo osati mayina awo okha komanso mawu a m’Baibulo kuphatikizapo dzina lenileni la Mulungu.

Mpaka pano, zolemba zawozi zimalengeza dzina la Yehova ndiponso kumutamanda ngakhale kuti papita zaka zambiri kuchokera pamene anazilemba. Alendo ndiponso anthu okhala m’derali akhoza kuphunzira zambiri za Yehova yemwe ndi Mulungu wabwino. Iwo angaphunzire zimenezi ku Bever mwa kupita kunyumba ina yokhala ndi dzina la Mulungu, yomwe ndi Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

© Stähli Rolf A/​age fotostock