Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziganizira Zimene Yehova Wakuchitirani Kale

Muziganizira Zimene Yehova Wakuchitirani Kale

Muziganizira Zimene Yehova Wakuchitirani Kale

YESU atangoukitsidwa, ophunzira ake awiri anali pa ulendo wochokera ku Yerusalemu kupita ku Emau. Ponena za nkhaniyi, Uthenga Wabwino wa Luka umati: “[Ophunzirawo] ali mkati mokambirana ndi kufunsana, Yesu anafika ndi kuyamba kuyenda nawo limodzi. Koma m’maso mwawo sanathe kumuzindikira.” Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “‘Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?’ Iwo anangoima chilili ndi nkhope zachisoni.” N’chifukwa chiyani anali ndi nkhope zachisoni? Chifukwa chakuti ophunzirawo ankaganiza kuti pa nthawiyo Yesu akanapulumutsa mtundu wa Isiraeli ku ulamuliro wopondereza wa anthu a mitundu ina koma izi sizinachitike. M’malo mwake Yesu anaphedwa.​—Luka 24:13-21; Mac. 1:6.

Yesu anayamba kukambirana ndi ophunzirawo. Iye “anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose ndi za aneneri zonse.” Panali zinthu zambiri zofunika ndiponso zolimbitsa chikhulupiriro zimene zinachitika pa utumiki wa Yesu. Ophunzira atamva zimene Yesu ankafotokoza, chisoni chawo chinatha n’kuyamba kusangalala. Madzulo a tsiku lomwelo iwo anati: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” (Luka 24:27, 32) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene ophunzira a Yesu anachita?

Kodi Timamva Bwanji Ngati Zimene Tinkayembekezera Sizikuchitika?

Ophunzira awiri amene ankapita ku Emau anali achisoni chifukwa chakuti zimene ankayembekezera sizinachitike. Zomwe zinawachitikirazo n’zimene zafotokozedwa pa Miyambo 13:12 kuti: “Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.” Izi ndi zimene zachitikiranso ena a ife amene tatumikira Yehova kwa zaka zambiri. Enafe tinkaganiza kuti pofika pano “chisautso chachikulu” chikhala chitachitika kale. (Mat. 24:21; Chiv. 7:14) M’pomveka kuti panopa tikhoza kukhumudwa chifukwa chakuti zimene tinkayembekezera sizinachitike.

Koma kumbukirani kuti ophunzira awiriwa anayambanso kusangalala Yesu atawathandiza kuganizira za maulosi amene anali atakwaniritsidwa ngakhale pa nthawi yawo. Nafenso n’zotheka kukhala osangalala ndiponso kuthana ndi zinthu zimene zimatikhumudwitsa. M’bale wina dzina lake Michael, yemwe wakhala mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Si bwino kumangoganizira zimene Yehova sanachite. Tiziganizira zimene iye wachita kale.” Malangizo amenewa ndi abwino kwabasi.

Zimene Yehova Wachita Kale

Taganizirani zinthu zina zochititsa chidwi zimene Yehova wachita kale. Yesu anati: “Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi.” (Yoh. 14:12) Masiku ano atumiki a Mulungu akugwira ntchito yaikulu kwambiri kuposa imene Akhristu m’mbuyomu anagwira. Anthu oposa 7 miliyoni akuyembekeza kupulumuka pa chisautso chachikulu. Tangoganizani, m’mbuyomu sizinachitikepo kuti atumiki okhulupirika a Yehova ochuluka chonchi azigwira ntchito yolalikira m’mayiko ambiri padziko lonse lapansi. Yehova wakwaniritsa mawu aulosi a Yesu akuti “ntchito zazikulu kuposa zimenezi” zidzachitika.

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Yehova watichitira? Iye wachititsa kuti anthu ofuna kuphunzira choonadi achoke m’dziko loipali n’kulowa m’paradaiso wauzimu amene iye wakonza. (2 Akor. 12:1-4) Taganizirani zinthu zina zokhudza paradaiso ameneyu zimene titha kuziona mosavuta. Mwachitsanzo, taonani mabuku amene muli nawo kunyumba kwanu kapena amene amasungidwa ku Nyumba ya Ufumu. Taonaninso mlozera nkhani amene amapezeka m’magazini athu a December ndiponso m’buku la Watch Tower Publications Index, kapena CD ya Watchtower Library. Ndiyeno mvetserani sewero la nkhani ya m’Baibulo pa CD kapena tepi. Yesaninso kukumbukira zinthu zimene munaona ndiponso kumva pa msonkhano wachigawo wa posachedwapa. Ganiziraninso za ubwenzi umene tili nawo ndi abale ndi alongo athu achikhristu. Zonsezi ndi umboni wakuti Yehova ndi wowolowa manja chifukwa amatipatsa chakudya chauzimu cha mwanaalirenji ndiponso ubale wa padziko lonse. Kunena zoona tilidi m’paradaiso wauzimu.

Wamasalimo Davide ananena kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa, ndipo mumatiganizira.” (Sal. 40:5) Choncho tiyeni tiziganizira zinthu zodabwitsa zimene Yehova watichitira kale ndiponso mmene amatikondera. Tikatero tidzapeza mphamvu zotithandiza kupirira ndiponso kukhala okhulupirika potumikira ndi mtima wathu wonse Atate wathu wakumwamba Yehova.​—Mat. 24:13.

[Chithunzi patsamba 31]

Yesu anathandiza ophunzira ake kuganizira zimene Yehova anali atawachitira kale

[Chithunzi patsamba 32]

Yesani kukumbukira zinthu zimene munaona ndiponso kumva pa msonkhano wachigawo wa posachedwapa