Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthawi Imene Simuli pa Banja

Muzigwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthawi Imene Simuli pa Banja

Muzigwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthawi Imene Simuli pa Banja

“Amene angathe kuchita zimenezi achite.”​—MAT. 19:12.

1, 2. (a) Kodi Yesu, Paulo ndi Akhristu ena amaona bwanji kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa? (b) N’chifukwa chiyani anthu ena saona kuti kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa ndi mphatso?

UKWATI ndi mphatso ina yamtengo wapatali kwambiri imene Mulungu anapereka kwa anthu. (Miy. 19:14) Koma pali Akhristu ena omwe sali pa banja amene amakhalanso moyo wabwino ndiponso wosangalala. M’bale wina wa zaka 95 dzina lake Harold sanakwatirepo ndipo anati: “Ngakhale kuti ndimasangalala ndikakhala pa gulu komanso ndikamachereza alendo, ndikakhala ndekha sindisungulumwa. Ndikuona kuti ndili ndi mphatso yokhala wosakwatira.”

2 Yesu Khristu ndi mtumwi Paulo ananena kuti kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa nakonso ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Werengani Mateyu 19:11, 12; 1 Akorinto 7:7.) N’zoona kuti pali anthu ena amene sali pa banja koma sanachite kusankha zimenezi. Nthawi zina zimakhala zovuta kuti munthu apeze mwamuna kapena mkazi woyenera. Koma nthawi zina kutha kwa banja kapena imfa zimachititsa kuti munthu amene anali pa banja kwa zaka zambiri atsale yekha. Kodi kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa kungakhale bwanji mphatso? Kodi Akhristu angatani kuti azigwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene sali pa banja?

Mphatso Yapadera

3. Kodi Akhristu amene sali pa banja ali ndi mwayi wotani?

3 Nthawi zambiri munthu amene sali pa banja amakhala ndi nthawi komanso ufulu wochita zambiri kusiyana ndi amene ali pa banja. (1 Akor. 7:32-35) Izi zimamupatsa mwayi wowonjezera utumiki wake, wofutukula mtima wake kuti akonde anthu ambiri komanso woti ayandikire Yehova. Chifukwa cha zimenezi, Akhristu ambiri azindikira kuti kusakhala pa banja kuli ndi ubwino wake ndipo asankha “kuchita zimenezi” pa moyo wawo wonse kapena kwa kanthawi. Pali ena amene poyamba sanasankhe kuti asakhale pa banja koma zinthu zitasintha anaganizira mofatsa za moyo wawo komanso kupemphera ndipo aona kuti Yehova akhoza kuwathandiza kuti akhazikike mumtima mwawo. Iwo aona kuti akhoza kukhalabe osakwatira kapena osakwatiwa.​—1 Akor. 7:37, 38.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu amene sali pa banja angatumikire Mulungu bwinobwino?

4 Akhristu omwe sali pa banja amadziwa kuti ukwati si umene ungachititse kuti akhale ofunika kwa Yehova ndiponso m’gulu lake. Mulungu amakonda munthu aliyense payekha. (Mat. 10:29-31) Palibe munthu kapena chinthu china chilichonse chimene chingatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu. (Aroma 8:38, 39) Kaya tili pa banja kapena ayi tikhoza kutumikira Mulungu bwinobwino.

5. Kodi Akhristu omwe sali pa banja angatani kuti agwiritse ntchito bwino mphatso imeneyi?

5 Anthu okhala ndi luso loimba kapena lochita masewera enaake amayenera kuchita khama kuti zinthu ziwayendere bwino. Nawonso Akhristu osakwatira kapena osakwatiwa ayenera kuchita khama kuti agwiritse ntchito bwino mphatso imeneyi. Kodi Akhristu amenewa angachite bwanji zimenezi, kaya akhale m’bale kapena mlongo, wachinyamata kapena wachikulire, wochita kusankha zimenezi kapena ayi? Tiyeni tikambirane zitsanzo zina zolimbikitsa za Akhristu oyambirira n’kuona zimene tikuphunzirapo.

Achinyamata Osakwatira Kapena Osakwatiwa

6, 7. (a) Kodi ana aakazi a Filipo anapatsidwa mwayi uti wotumikira Mulungu? (b) Kodi Timoteyo anagwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene anali wosakwatira m’njira ziti, ndipo kodi anadalitsidwa bwanji chifukwa cha mtima wofuna kutumikira ali wachinyamata?

6 Mlaliki Filipo anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene ankalalikira nawo mwakhama. (Mac. 21:8, 9) Kunenera inali imodzi mwa mphatso zozizwitsa za mzimu woyera ndipo atsikana amenewa ankagwiritsa ntchito mphatso imeneyi pokwaniritsa lemba la Yoweli 2:28, 29.

7 Timoteyo anali wachinyamata amene ankagwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene anali wosakwatira. Kuyambira ali wakhanda, amayi ake a Yunike ndi agogo ake a Loisi anamuphunzitsa “malemba oyera.” (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) Zikuoneka kuti iwo anakhala Akhristu pamene Paulo anabwera kwawo ku Lusitara pa ulendo wake woyamba cha m’ma 47 C.E. Patapita zaka ziwiri, Paulo anafika kachiwiri ku Lusitara ndipo pa nthawiyi Timoteyo ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 20 kapena kuposerapo. Ngakhale kuti anali wamng’ono komanso anali atangophunzira kumene choonadi, akulu achikhristu a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo “anamuchitira umboni wabwino.” (Mac. 16:1, 2) Ndiyeno Paulo anapempha Timoteyo kuti aziyenda naye. (1 Tim. 1:18; 4:14) Sitikudziwa ngati patapita nthawi Timoteyo anakwatira kapena ayi. Chomwe tikudziwa n’chakuti ali wachinyamata anavomera kuyenda ndi Paulo ndipo kwa zaka zambiri ankatumikira ngati mmishonale komanso woyang’anira wosakwatira.​—Afil. 2:20-22.

8. N’chiyani chinathandiza Yohane Maliko kukwaniritsa zolinga zauzimu ndipo kodi anadalitsidwa bwanji?

8 Yohane Maliko anagwiritsanso ntchito mwanzeru nthawi imene anali wachinyamata wosakwatira. Iye anali mu mpingo wa ku Yerusalemu limodzi ndi amayi ake Mariya komanso msuweni wake Baranaba. Banja la Maliko liyenera kuti linali lochita bwino chifukwa anali ndi nyumba yawoyawo mumzinda komanso anali ndi wantchito. (Mac. 12:12, 13) Ngakhale kuti Maliko ankachokera m’banja lotere ndiponso anali wachinyamata, iye sankafuna kumangochita zinthu zomukomera ndiponso sanali wodzikonda. Analibe mtima wongofuna kukwatira ndi kukhazikika. Mosakayikira kucheza ndi atumwi kuyambira ali wamng’ono kunamuthandiza kuti azifunitsitsa kutumikira ngati mmishonale. Choncho iye mofunitsitsa anatsagana ndi Paulo ndi Baranaba pa ulendo wawo woyamba wa umishonale ndipo ankawatumikira. (Mac. 13:5) Pa nthawi ina, anayenda ndi Baranaba ndipo kenako anatumikira ndi Petulo ku Babulo. (Mac. 15:39; 1 Pet. 5:13) Sitikudziwa kuti Maliko anakhala nthawi yaitali bwanji asanakwatire. Koma iye ankadziwika kuti anali munthu wokonda kutumikira ena ndiponso kuchita zambiri mu utumiki wa Mulungu.

9, 10. Kodi ndi zinthu ziti zimene Akhristu achinyamata omwe sali pa banja angachite potumikira Mulungu? Perekani chitsanzo.

9 Masiku anonso, achinyamata ambiri mu mpingo amagwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene sali pa banja pochita zambiri mu utumiki wa Mulungu. Mofanana ndi Maliko ndi Timoteyo, iwo amaona kuti kusakhala pa banja kumawathandiza kuti ‘atumikire Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.’ (1 Akor. 7:35) Uwu ndi mwayi waukulu kwambiri. Pali zinthu zambiri zimene mungachite monga upainiya, kutumikira kumene kuli ofalitsa Ufumu ochepa, kuphunzira chinenero china, kuthandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi maofesi a nthambi, kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndiponso kutumikira pa Beteli. Ngati ndinu wachinyamata ndiponso simuli pa banja, kodi mukugwiritsa ntchito bwino mwayi umenewu?

10 M’bale wina dzina lake Mark anayamba upainiya asanakwanitse zaka 20 kenako anapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndipo watumikira m’mayiko ambiri. Pofotokoza za utumiki wa nthawi zonse umene wachita kwa zaka 25, iye anati: “Ndakhala ndikuyesetsa kulimbikitsa anthu mwa kuyenda nawo mu utumiki, kuwayendera ulendo waubusa, kuwaitana kunyumba kwathu kudzadya chakudya, ndiponso kukonza mapwando oti abale ndi alongo acheze n’kumalimbikitsana mwauzimu. Zonsezi zandithandiza kukhala wosangalala kwambiri.” Malinga ndi zimene Mark ananena, munthu amasangalala kwambiri chifukwa cha kupatsa ndipo munthu akamachita zambiri potumikira Mulungu amakhala ndi mipata yambiri yopatsa. (Mac. 20:35) Kaya mumakonda zinthu zotani, muli ndi maluso otani kapena mumadziwa zinthu zotani pali zambiri mu ntchito ya Ambuye zimene achinyamatanu masiku ano mungachite.​—1 Akor. 15:58.

11. Fotokozani ubwino wosathamangira kulowa m’banja.

11 Ngakhale kuti achinyamata ambiri amaganiza zodzalowa m’banja ndi bwino kusathamangira kuchita zimenezi. Paulo analimbikitsa achinyamata kudikira kaye mpaka atapitirira “pachimake pa unyamata,” kapena kuti atapitirira nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu. (1 Akor. 7:36) Pamafunika nthawi yokwanira kuti mudzidziwe nokha komanso kuti mudziwe zambiri pa moyo zimene zingakuthandizeni kusankha mwamuna kapena mkazi wabwino. Malumbiro a ukwati si nkhani ya masewera ndipo ndi ofunika kuwatsatira pa moyo wanu wonse.​—Mlal. 5:2-5.

Achikulire Osakwatira Kapena Osakwatiwa

12. (a) Kodi n’chiyani chimene chinathandiza Anna pa nthawi imene anali wamasiye? (b) Kodi iye anali ndi mwayi wotani?

12 Anna, wotchulidwa mu Uthenga Wabwino wa Luka, ayenera kuti anakhumudwa kwambiri mwamuna wake atamwalira mwadzidzidzi atangokhala m’banja zaka 7 zokha. Sitikudziwa ngati iye anali ndi ana ndiponso ngati ankafuna kukwatiwanso. Koma Baibulo limanena kuti pamene anali ndi zaka 84, anali adakali wamasiye. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, tingaone kuti Anna anagwiritsa ntchito nthawi imene anali wosakwatiwa kuyandikira Yehova. Iye “sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku, anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.” (Luka 2:36, 37) Choncho ankaika patsogolo zinthu zauzimu. Kuti achite zimenezi ankafunika kuchita khama ndipo anadalitsidwa kwambiri. Iye anali ndi mwayi woona Yesu ali kamwana ndiponso wouza ena za chipulumutso chobwera kudzera mwa Mesiya.​—Luka 2:38.

13. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Dorika anali wakhama mu mpingo? (b) Kodi Dorika anadalitsidwa bwanji chifukwa cha ntchito zake zabwino komanso zachifundo?

13 Mayi wina dzina lake Dorika, kapena kuti Tabita, ankakhala mumzinda wa m’mphepete mwa nyanja kumpoto chakumadzulo kwa Yerusalemu wotchedwa Yopa. Baibulo silinena chilichonse za mwamuna wake, choncho ayenera kuti pa nthawiyo anali wosakwatiwa. Dorika “anali kuchita ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” Zikuoneka kuti ankasokera zovala akazi amasiye ovutika komanso anthu ena ndipo izi zinachititsa kuti anthu azimukonda. Choncho atadwala ndi kumwalira mwadzidzidzi, mpingo wonse unaitana Petulo n’kumuchonderera kuti adzamuukitse mlongo wawo wokondedwayu. Nkhani ya kuukitsidwa kwake itadziwika mu Yopa monse, anthu ambiri anakhala okhulupirira. (Mac. 9:36-42) N’kutheka kuti Dorika anathandizapo ena mwa anthu amenewa kudzera mu ntchito zake zachifundo chachikulu.

14. N’chifukwa chiyani Akhristu amene sali pa banja amayandikira kwambiri Yehova?

14 Achikulire ambiri m’mipingo masiku ano sali pa banja ndipo ali ngati Anna ndi Dorika. Ena sanapeze munthu woyenera kumanga naye banja koma ena banja lawo linatha kapena mnzawo anamwalira. Popeza Akhristu oterewa sakhala ndi munthu womuuza zakukhosi kwawo, amayamba kudalira kwambiri Yehova. (Miy. 16:3) Mwachitsanzo, Silvia ndi mlongo wosakwatiwa amene watumikira pa Beteli kwa zaka zoposa 38 ndipo amaona kuti kukhala wosakwatiwa ndi dalitso. Iye anati, “Nthawi zina ndimaona kuti ndimangokhalira kulimbikitsa anthu ena ndipo ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi nanga ineyo ndani angandilimbikitse?’” Koma kenako anati: “Kukhulupirira kuti Yehova amadziwa bwino zimene ndikufunikira kumandithandiza kumuyandikira. Ndipo nthawi zina ndimalimbikitsidwa m’njira zosayembekezeka.” Tikamayandikira Yehova, iye amatilimbikitsa ndi kutisonyeza chikondi chachikulu.

15. Kodi Akhristu amene sali pa banja angafutukule bwanji mitima yawo?

15 Munthu amene sanalowe m’banja amakhala ndi mwayi ‘wofutukula mtima wake’ kuti azikonda anthu ambiri. (Werengani 2 Akorinto 6:11-13.) Mwachitsanzo, Jolene ndi mlongo wosakwatiwa amene wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 34. Iye anati: “Ndimachita khama kwambiri kuti ndizicheza ndi anthu osiyanasiyana osati amsinkhu wanga wokha. Kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa kumapereka mpata waukulu kuti munthu atumikire Yehova ndiponso kuti athandize achibale, Akhristu anzake komanso anthu ena. Pamene ndikukula ndi pamene ndikusangalala kwambiri kuti ndine wosakwatiwa.” Anthu okalamba, makolo amene akulera okha ana, achinyamata ndiponso anthu ena mu mpingo amayamikira zimene anthu amene sali pa banja amawachitira modzipereka. Kunena zoona, timasangalala kwambiri tikamakomera mtima anthu ena. Kodi inunso mukhoza ‘kufutukula mtima wanu’ kuti muzikonda anthu ambiri?

Amene Asankha Kusalowa M’banja kwa Moyo Wawo Wonse

16. (a) N’chifukwa chiyani Yesu sanakwatire? (b) Perekani umboni woti Paulo anagwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene sanali pa banja.

16 Yesu sanakwatire chifukwa chofuna kukonzekera ndi kuchita utumiki wake. Iye anayenda maulendo ataliatali, kuchita utumiki kuyambira m’mawa mpaka usiku ndipo kenako anapereka moyo wake nsembe. Kukhala wosakwatira kunamuthandiza kuti achite zonsezi. Nayenso mtumwi Paulo anayenda maulendo ataliatali ndipo pa utumiki wake anakumana ndi mavuto osaneneka. (2 Akor. 11:23-27) Ngakhale kuti mwina Paulo anali atakwatirapo, iye ataikidwa kukhala mtumwi anasankha kukhalabe wosakwatira. (1 Akor. 7:7; 9:5) Pofuna kuthandiza anthu kuchita zambiri mu utumiki, Yesu ndi Paulo analimbikitsa anthu amene angakwanitse kuti atsatire chitsanzo chawo. Koma sikuti anaika lamulo loti munthu amene akufuna kuchita utumiki ayenera kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa.​—1 Tim. 4:1-3.

17. Kodi anthu ena masiku ano atsatira bwanji chitsanzo cha Yesu ndi Paulo, ndipo n’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti Yehova amayamikira mtima wawo wodzimana?

17 Masiku ano, anthu ena asankhanso zosalowa m’banja kwa moyo wonse n’cholinga choti achite zambiri mu utumiki. Harold amene tamutchula poyamba uja watumikira pa Beteli kwa zaka zoposa 56. Iye anati: “Pa zaka 10 zoyambirira zimene ndinakhala pa Beteli ndinaona anthu ambiri apabanja amene ankachoka pa Beteli chifukwa cha matenda kapena pofuna kukathandiza makolo awo okalamba. Ine makolo anga onse anamwalira ndipo ndimakonda kwambiri utumiki wa pa Beteli moti sindinafune kuuika pangozi mwa kukwatira.” Zaka zingapo zapitazo, Margaret amene wakhala akuchita upainiya kwa nthawi yaitali ananenanso kuti: “M’mbuyomu mwayi wokwatiwa ndinali nawo koma ndinkatanganidwa kwambiri ndi utumiki moti sindinkaganizira kwambiri nkhani ya banja. Ndiponso ndinkagwiritsa ntchito ufulu umene ndinali nawo monga wosakwatiwa kuti ndichite zambiri potumikira Yehova ndipo izi zandithandiza kukhala wosangalala.” Yehova sadzaiwala anthu amene amadzimana zinthu zina kuti achite zambiri pomulambira.​—Werengani Yesaya 56:4, 5.

Gwiritsani Ntchito Bwino Mpata Umene Muli Nawo

18. Kodi anthu ena angalimbikitse bwanji Akhristu amene sali pa banja?

18 Tiyenera kuyamikira ndiponso kulimbikitsa anthu amene sali pa banja omwe amayesetsa mmene angathere kutumikira Yehova. Timawakonda ndi kuyamikira zimene aliyense payekha amachita mu mpingo. Tikamayesetsa kukhala ‘abale, alongo, amayi kapena ana’ awo auzimu iwo sadzasungulumwa.​Werengani Maliko 10:28-30.

19. Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene simuli pa banja?

19 Kaya mwasankha kusalowa m’banja kapena zangochitika pa zifukwa zina, zitsanzo za m’Malemba ndiponso za masiku ano zimene takambiranazi zikusonyeza kuti mukhoza kukhala ndi moyo wosangalala. Pali mphatso zina zimene timayembekeza kulandira koma zina timalandira mosayembekezeka. Zina timaziyamikira nthawi yomweyo koma zina timaziyamikira patapita nthawi. Zonsezi zimadalira mmene timaonera zinthu. Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene simuli pa banja? Yandikirani Yehova, khalani ndi zochita zambiri potumikira Mulungu ndipo futukulani mtima wanu kuti muzikonda anthu ambiri. Mofanana ndi ukwati, munthu angaone kuti kusalowa m’banja ndi dalitso ngati akuona mphatsoyi mmene Mulungu amaionera ndiponso ngati akuigwiritsa ntchito mwanzeru.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kusakhala pa banja kungakhale bwanji mphatso?

• Kodi kusakhala pa banja kungapereke mwayi wotani kwa achinyamata?

• Kodi Akhristu amene sali pa banja ali ndi mipata yotani yoyandikira Yehova ndiponso yofutukula mitima yawo?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Kodi mukugwiritsa ntchito bwino mwayi umene muli nawo potumikira Mulungu?