Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzilemekeza Ukwati Monga Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Muzilemekeza Ukwati Monga Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Muzilemekeza Ukwati Monga Mphatso Yochokera kwa Mulungu

“Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.”​—GEN. 2:24.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza Yehova?

YEHOVA MULUNGU ndi amene anayambitsa ukwati ndipo tiyenera kumulemekeza. Popeza iye ndi Mlengi, Mfumu ndiponso Atate wathu wakumwamba, Iye ndi Wopereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17; Chiv. 4:11) Potipatsa mphatsozi, iye wasonyeza chikondi chake chachikulu. (1 Yoh. 4:8) Mulungu akamatipatsa zinthu, akamatiphunzitsa ndiponso akamatipempha kuti tichite zinazake, cholinga chake nthawi zonse ndi chakuti zinthu zitiyendere bwino.​—Yes. 48:17.

2. Kodi ndi malangizo ati amene Yehova anapatsa banja loyambirira?

2 Baibulo limasonyeza kuti ukwati ndi imodzi mwa mphatso ‘zabwino’ zimene Mulungu watipatsa. (Rute 1:9; 2:12) Pomangitsa ukwati woyamba, womwe unali wa Adamu ndi Hava, Yehova anawapatsa malangizo amene akanathandiza kuti ukwati wawo uyende bwino. (Werengani Mateyu 19:4-6.) Iwo akanatsatira malangizo a Mulungu amenewa akanakhala osangalala nthawi zonse. Koma iwo sanamvere lamulo la Mulungu ndipo uku kunali kupanda nzeru chifukwa zotsatira zake zinali zopweteka kwambiri.​—Gen. 3:6-13, 16-19, 23.

3, 4. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano amasonyeza bwanji kuti salemekeza ukwati komanso Yehova Mulungu? (b) Kodi tikambirana zitsanzo ziti m’nkhani ino?

3 Mofanana ndi banja loyambirirali, anthu ambiri masiku ano amasankha zochita m’banja popanda kuganizira bwinobwino malangizo a Yehova. Ena safuna kukhala m’banja mwa lamulo, pamene ena amalowa m’banja koma mongotsatira maganizo ndi zofuna zawo. (Aroma 1:24-32; 2 Tim. 3:1-5) Iwo amanyalanyaza mfundo yakuti ukwati ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo mwa kusalemekeza mphatsoyi, amanyoza Yehova Mulungu amene anaipereka.

4 Ngakhale anthu a Mulungu nthawi zina amaiwala mmene Yehova amaonera ukwati. Akhristu ena amapatukana kapena kusudzulana popanda zifukwa za m’Malemba. Kodi tingapewe bwanji zimenezi? Kodi malangizo a Mulungu pa Genesis 2:24 angathandize bwanji Akhristu kulimbitsa ukwati wawo? Nanga kodi amene akufuna kulowa m’banja angakonzekere bwanji? Tiyeni tikambirane za mabanja atatu otchulidwa m’Baibulo amene amasonyeza kuti kulemekeza Yehova n’kofunika kwambiri kuti banja likhale lolimba.

Khalani Okhulupirika

5, 6. Kodi Zekariya ndi Elizabeti anakumana ndi mayesero otani ndipo anadalitsidwa bwanji chifukwa cha kukhulupirika kwawo?

5 Zekariya ndi Elizabeti anachita zinthu zonse zofunika m’banja. Polowa m’banja aliyense anasankha munthu wokonda Yehova. Zekariya ankatumikira mokhulupirika pa udindo wake monga wansembe ndipo onse ankayesetsa mmene angathere kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Iwo anali ndi zinthu zambiri zowachititsa kuyamikira. Koma mukanafika kunyumba kwawo ku Yuda mukanaona kuti iwo analibe ana. Elizabeti anali wosabereka ndipo onse anali okalamba.​—Luka 1:5-7.

6 Aisiraeli akale ankaona kuti kubereka ana n’kofunika kwambiri choncho mabanja ambiri anali aakulu. (1 Sam. 1:2, 6, 10; Sal. 128:3, 4) M’nthawi ya Zekariya, amuna ena a ku Isiraeli ankachita chinyengo n’kusudzula akazi awo chifukwa chosabereka. Koma Zekariya anali wokhulupirika ndipo ankakhalabe ndi Elizabeti. Iye sanaganizire njira zothetsera banja lakelo ndipo mkazi wakenso sanachite zimenezi. Ngakhale kuti kusabereka kunkawapweteka kwambiri mumtima, iwo anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Ndiyeno patapita nthawi, Yehova anawadalitsa m’njira yozizwitsa moti anabereka mwana wamwamuna atakalamba.​—Luka 1:8-14.

7. Kodi Elizabeti anachita chinthu chinanso chiti chosonyeza kuti anali wokhulupirika kwa mwamuna wake?

7 Elizabeti anachita chinthu chinanso chosonyeza kuti anali wokhulupirika kwambiri. Pa nthawi imene mwana wake Yohane anabadwa, Zekariya anali asakulankhula. Mulungu ndi amene anachititsa zimenezi chifukwa chakuti Zekariya anakayikira mngelo wake. Koma zikuoneka kuti Zekariya anapeza njira yodziwitsira mkazi wake kuti mngelo wa Yehova ananena kuti dzina la mwanayo likhale “Yohane.” Achibale komanso anthu oyandikana nawo anafuna kuti mwanayo apatsidwe dzina la bambo ake. Koma Elizabeti anasonyeza kukhulupirika mwa kunena motsimikiza zimene mwamuna wake anamuuza. Iye anati: “Limenelo iyayi! Dzina lake akhala Yohane.”​—Luka 1:59-63.

8, 9. (a) Kodi kukhulupirika kumathandiza bwanji kuti banja likhale lolimba? (b) Kodi mwamuna kapena mkazi angasonyeze kukhulupirika kwa mnzake m’njira ziti?

8 Mofanana ndi Zekariya ndi Elizabeti, mabanja masiku ano amakumananso ndi mavuto komanso zinthu zokhumudwitsa. Banja la anthu osakhulupirika silingalimbe. Kukopana, kuonera zolaula, chigololo ndiponso zinthu zina zimene zimasokoneza mabanja zimachititsa kuti anthu asiye kukhulupirirana. Anthu akasiya kukhulupirirana m’banja, chikondi chimayamba kuzirala. Tingayerekezere kukhulupirika ndi mpanda waukulu umene umateteza banja kuti anthu ena kapena zinthu zina zisasokoneze banjalo. Mwamuna ndi mkazi wake akakhala okhulupirika, banja lawo limakhala lamtendere. Iwo amatha kukambirana zinthu momasuka ndipo amakondana kwambiri. Apa zikuonekeratu kuti kukhulupirika n’kofunika kwambiri.

9 Yehova anauza Adamu kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Gen. 2:24) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Munthu akalowa m’banja amafunika kusintha mmene ankachitira zinthu ndi anzake komanso achibale ake. Mwamuna kapena mkazi ayenera kupeza nthawi yokwanira yokhala ndi mnzakeyo kuposa wina aliyense. Sayenera kunyalanyaza mnzakeyo pofuna kuti achite zinthu zina ndi anzake ena kapena achibale ake. Sayenera kulola makolo kulowerera pa zosankha zawo kapena pa mavuto a m’banja lawo. Malangizo a Mulungu ndi akuti mwamuna kapena mkazi azikhala wokhulupirika kwa mnzake.

10. N’chiyani chingathandize anthu okwatirana kukhala okhulupirika?

10 Kukhulupirika n’kothandizanso ngakhale m’banja limene wina si Mkhristu. Mlongo wina amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira ananena kuti: “Ndikuyamikira kwambiri kuti Yehova wandiphunzitsa kugonjera ndiponso kulemekeza kwambiri mwamuna wanga. Kukhala wokhulupirika kwathandiza kuti tizikondana komanso kulemekezana m’banja kwa zaka 47.” (1 Akor. 7:10, 11; 1 Pet. 3:1, 2) Choncho yesetsani kusonyeza mnzanuyo kuti mumam’konda kwambiri. Mawu anu ndiponso zochita zanu zizisonyeza kuti mumaona kuti mwamuna kapena mkazi wanuyo ndi munthu wofunika kwambiri padziko lonse. Yesetsani mmene mungathere kuti pasakhale wina aliyense kapena china chilichonse chosokoneza mgwirizano wanu. (Werengani Miyambo 5:15-20.) Ron ndi Jeannette akhala m’banja mosangalala kwa zaka zoposa 35 ndipo ananena kuti, “Tili ndi banja losangalala chifukwa chakuti timatsatira mokhulupirika zimene Mulungu amafuna.”

Banja Logwirizana Limakhala Lolimba

11, 12. Kodi Akula ndi Purisikila ankasonyeza bwanji kugwirizana (a) kunyumba kwawo (b) pa ntchito yawo (c) pa utumiki wachikhristu?

11 Pamene Paulo ankafotokoza za Akula ndi Purisikila, omwe anali anzake apamtima, sankatchula munthu mmodzi payekha. Banja logwirizana limeneli ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha zimene Mulungu ankatanthauza ponena kuti mwamuna ndi mkazi adzakhala “thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Iwo ankachita limodzi zinthu zapakhomo, pa ntchito yawo ndiponso mu utumiki wachikhristu. Mwachitsanzo, Paulo atangofika kumene ku Korinto, Akula ndi Purisikila anamukomera mtima n’kumuitanira kunyumba kwawo ndipo zikuoneka kuti iye anakhalabe kumeneku kwa kanthawi pochita utumiki wake. Atapita ku Efeso, Akula ndi Purisikila ankagwiritsa ntchito nyumba yawo pochita misonkhano ya mpingo ndipo ankagwira ntchito limodzi pothandiza anthu atsopano monga Apolo kuti apite patsogolo mwauzimu. (Mac. 18:2, 18-26) Kenako banja lakhamali linasamukira ku Roma kumene linalolanso kuti nyumba yawo izigwiritsidwa ntchito pochita misonkhano ya mpingo. Patapita nthawi, banjali linabwerera ku Efeso ndipo linkalimbikitsa abale kumeneko.​—Aroma 16:3-5.

12 Kwa kanthawi Akula ndi Purisikila ankapanga mahema limodzi ndi Paulo popeza iyi ndi ntchito imene onsewa ankaidziwa. Apanso tikuona kuti banjali linkagwira ntchito limodzi popanda kupikisana kapena kukangana. (Mac. 18:3) N’zachidziwikire kuti kuchitira limodzi zinthu potumikira Mulungu n’kumene kunawathandiza kuti banja lawo likhale lolimba mwauzimu. Abale a ku Korinto, ku Efeso ndi ku Roma, ankawaona kuti iwo ankagwira ntchito limodzi mwa Khristu Yesu. (Aroma 16:3) Kulikonse kumene anapita, iwo ankagwira limodzi ntchito zokhudza kulalikira Ufumu.

13, 14. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze mgwirizano m’banja? (b) Kodi okwatirana angachite chiyani kuti akhaledi ngati “thupi limodzi”?

13 Kukhala ndi zolinga zofanana ndiponso kuchitira limodzi zinthu kumathandiza kuti banja likhale lolimba. (Mlal. 4:9, 10) Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri okwatirana sachitira limodzi zinthu zambiri. Aliyense amapita kuntchito yake komwe amakakhala nthawi yaitali. Ena amagwira ntchito yomwe imawachititsa kuyendayenda ndipo ena amapita kumayiko akunja kukagwira ntchito n’kumangotumiza ndalama kunyumba kwawo. M’mabanja ena, mwamuna ndi mkazi salankhulana chifukwa chotanganidwa ndi zinthu monga kuonera TV, kuchita masewera kapena kugwiritsa ntchito kompyuta. Kodi umu ndi mmene zilili m’banja lanu? Ngati ndi choncho kodi mungasinthe zinthu ziti kuti muzikhala ndi nthawi yocheza? Mwina mungamathandizane kuphika chakudya, kutsuka mbale, kukonza pakhomo kapena kulima. Mwinanso mungamathandizane kusamalira ana kapena kuthandiza makolo anu okalamba.

14 Koma chofunika kwambiri ndi kuchitira limodzi nthawi zonse zinthu zokhudza kulambira Yehova. Kukambirana limodzi lemba la tsiku ndiponso kulambira kwa pabanja zimathandiza kuti banja lonse lizikhala ndi maganizo komanso zolinga zofanana. Ndi bwinonso kuyenda limodzi mu utumiki. Ngati n’zotheka mungachite bwino kuchitira limodzi upainiya kaya kwa mwezi umodzi kapena chaka chimodzi basi. (Werengani 1 Akorinto 15:58.) Mlongo wina amene anachita upainiya limodzi ndi mwamuna wake anati: “Utumiki unatithandiza kuchitira limodzi zinthu ndiponso kukambirana momasuka. Tonse tinali ndi cholinga chothandiza anthu mwauzimu ndipo izi zinandichititsa kumva kuti ndife amodzi. Ndinayamba kumukonda kwambiri osati kokha monga mwamuna wanga komanso monga mnzanga wapamtima.” Mukamachitira limodzi zinthu zofunika mudzayamba kukonda zinthu zofanana ndipo zochita zanu komanso zimene aliyense amaona kuti ndi zofunika zidzafanananso. Mukatero mudzakhala ngati Akula ndi Purisikila amene ankaganiza, kuona zinthu ndiponso kuchita zinthu ngati “thupi limodzi.”

Muziika Mulungu Pamalo Oyamba

15. Kodi chofunika n’chiyani kuti banja likhale losangalala? Fotokozani.

15 Yesu ankadziwa kufunika koika Mulungu pamalo oyamba m’banja. Iye ankaona pamene Yehova ankamangitsa banja loyamba. Iye anaonanso Adamu ndi Hava akusangalala pamene ankatsatira malangizo a Mulungu. Anaonanso mavuto amene anakumana nawo chifukwa chonyalanyaza malangizowo. Choncho pamene Yesu ankaphunzitsa anthu, anagwira mawu a Atate wake opezeka pa Genesis 2:24. Kenako anawonjezera kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:6) Motero, kulemekeza kwambiri Yehova n’kofunikabe kuti banja likhale losangalala. Pa nkhani imeneyi Yosefe ndi Mariya, omwe anali makolo a Yesu a padziko lapansi, anapereka chitsanzo chabwino kwambiri.

16. Kodi Yosefe ndi Mariya anasonyeza bwanji kuti ankaika Mulungu pamalo oyamba m’banja lawo?

16 Yosefe ankachita zinthu ndi Mariya mokoma mtima ndiponso mwaulemu. Iye atamva zoti Mariya ndi woyembekezera, anafuna kuchita zinthu mwachifundo ngakhale kuti pa nthawiyi mngelo wa Mulungu anali asanamuuze zimene zinachitikira Mariya. (Mat. 1:18-20) Monga banja, iwo anamvera lamulo la Kaisara komanso ankatsatira bwino Chilamulo cha Mose. (Luka 2:1-5, 21, 22) Ngakhale kuti amuna okha ndi amene ankayenera kupita ku zikondwerero zikuluzikulu za ku Yerusalemu, Yosefe ndi Mariya ankapita limodzi ndi achibale awo chaka chilichonse. (Deut. 16:16; Luka 2:41) Pochita izi ndiponso zinthu zina, banja loopa Mulunguli linkayesetsa kusangalatsa Yehova ndipo linkalemekeza kwambiri zinthu zauzimu. Mpake kuti Yehova anawasankha kuti alere Yesu, yemwe ndi Mwana wake, pamene anali wamng’ono padziko lapansi.

17, 18. (a) Kodi anthu okwatirana angaike bwanji Mulungu patsogolo m’banja lawo? (b) Kodi zimenezi zingathandize bwanji banja lawo?

17 Kodi inu mumaikanso Mulungu patsogolo m’banja lanu? Mwachitsanzo, mukamasankha zochita pa nkhani zofunika kodi mumafufuza mfundo za m’Baibulo, kupempherera nkhanizo ndiponso kupempha malangizo kwa Mkhristu wokhwima mwauzimu? Kapena kodi mumangothetsa nkhanizo potsatira maganizo anuanu, a achibale anu kapena a anzanu? Kodi mumayesetsa kutsatira malangizo othandiza pa nkhani za banja amene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amapereka? Kapena kodi mumangotsatira miyambo ya kwanu ndi mfundo zimene anthu amayendera m’dzikoli? Kodi nthawi zonse mumapemphera limodzi, kuphunzira limodzi, ndiponso kukambirana zolinga zauzimu kapena zoyenera kuika pamalo oyamba m’banja lanu?

18 Ponena za zaka 50 zimene akhala m’banja losangalala, Ray anati, “Palibe vuto lililonse limene talephera kulithetsa chifukwa chakuti nthawi zonse timalola Yehova kukhala ‘chingwe chachitatu’ m’banja lathu.” (Werengani Mlaliki 4:12.) Danny ndi Trina ananenanso kuti, “Kutumikira Mulungu limodzi kwathandiza kuti banja lathu likhale lolimba.” Iwo akhala m’banja mosangalala kwa zaka zoposa 34. Nanunso mukamaika Yehova pamalo oyamba m’banja lanu, iye adzakuthandizani kuti banja lanu likhale losangalala ndipo adzakudalitsani kwambiri.​—Sal. 127:1.

Pitirizani Kulemekeza Mphatso Yochokera kwa Mulungu

19. N’chifukwa chiyani Mulungu anapereka mphatso ya ukwati?

19 Anthu ambiri masiku ano amangofuna zinthu zowakomera iwowo m’banja. Koma awa si maganizo amene atumiki a Yehova amayendera. Iwo amadziwa kuti Mulungu anapereka mphatso ya ukwati pofuna kukwaniritsa cholinga Chake. (Gen. 1:26-28) Adamu ndi Hava akanalemekeza mphatso imeneyi, dziko lonse likanakhala paradaiso wodzaza ndi anthu osangalala komanso olungama amene amatumikira Mulungu.

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti ukwati ndi wopatulika? (b) Kodi tidzakambirana za mphatso iti mlungu wamawa?

20 Koposa zonse, atumiki a Mulungu amaona kuti ukwati umawapatsa mwayi wolemekeza Yehova. (Werengani 1 Akorinto 10:31.) Monga taonera, kukhulupirika, kugwirizana ndiponso kuika Yehova pamalo oyamba kumathandiza kuti banja likhale lolimba. Choncho kaya tikukonzekera banja, tikulimbitsa banja lathu kapena tikuyesa kulipulumutsa, chofunika kwambiri ndi kuona kuti ukwati ndi wopatulika ndipo Mulungu ndi amene anauyambitsa. Kukumbukira mfundo imeneyi kudzatithandiza kuti posankha zinthu zokhudza banja tiziyesetsa kutsatira Mawu a Mulungu. Tikatero, tidzasonyeza kuti timalemekeza mphatso ya ukwati komanso Yehova Mulungu amene anapereka mphatsoyi.

21 Komabe pali mphatso inanso imene Yehova watipatsa. Nayonso ingatithandize kukhala osangalala. Mphatso imeneyi ndi kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa. Mu nkhani yotsatira tidzakambirana mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu imeneyi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Akhristu angasonyeze bwanji kukhulupirika m’banja?

• Kodi kugwira ntchito limodzi mogwirizana kungalimbitse bwanji banja?

• Kodi anthu okwatirana angaike bwanji Mulungu pamalo oyamba m’banja lawo?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Yehova amene anayambitsa ukwati?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 15]

Kugwira ntchito pamodzi kumathandiza kuti mabanja azikhala ogwirizana