Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndimayamikira Kutumikira Yehova, Ngakhale pa Nthawi Zovuta

Ndimayamikira Kutumikira Yehova, Ngakhale pa Nthawi Zovuta

Ndimayamikira Kutumikira Yehova, Ngakhale pa Nthawi Zovuta

Yosimbidwa ndi Maatje de Jonge-van den Heuvel

NDILI ndi zaka 98 ndipo ndakhala ndikutumikira Yehova kwa zaka 70. Koma sikuti ndangodutsa mofewa. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndinatsekeredwa m’ndende ndipo ndili kumeneku ndinataya mtima moti ndinachita zinthu zimene ndinadzadandaula nazo kwambiri. Patapita zaka zingapo ndinakumananso ndi vuto lina lalikulu. Komabe, ndimayamikira Yehova kuti ndakhala ndi mwayi womutumikira ngakhale pa nthawi zovuta.

Moyo wanga unasintha mu October 1940. Pa nthawiyi ndinkakhala ku Hilversum, tawuni imene ili pa mtunda wa makilomita 24 kum’mwera cha kum’mawa kwa mzinda wa Amsterdam m’dziko la Netherlands. Dzikoli linkalamulidwa ndi chipani cha Nazi. Ndinakwatiwa ndi mwamuna wachikondi kwambiri dzina lake Jaap de Jonge ndipo tinali titakhala m’banja zaka zisanu. Tinali ndi mwana wamkazi wa zaka zitatu dzina lake Willy ndipo tinkamukonda kwambiri. Tinkakhala pafupi ndi banja lina losauka limene linkavutika kwambiri kuti lipeze chakudya cha ana awo 8. Ngakhale zinali choncho, banjali linkasamaliranso mnyamata wina amene ankakhala nawo. Ndinkadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anthuwa akudzivutitsa posamaliranso munthu ameneyu?’ Pamene ndinapita kukawapatsa chakudya ndinamva kuti munthuyo anali mpainiya. Munthuyo anandiuza za Ufumu wa Mulungu ndiponso madalitso amene Ufumuwo udzabweretse. Zimene ndinamva zinandikhudza kwambiri ndipo ndinayamba kuphunzira choonadi. Chaka chomwecho ndinadzipereka kwa Yehova kenako ndinabatizidwa. Patapita chaka chimodzi kuchokera pamene ndinabatizidwa, mwamuna wanga anabatizidwanso.

Ngakhale kuti pa nthawiyi sindinkalidziwa bwino Baibulo ndinkadziwa kuti ngati ndasankha kukhala wa Mboni ndiye kuti ndalowa m’gulu loletsedwa. Ndinkadziwanso kuti Mboni zambiri zinali zitatsekeredwa m’ndende chifukwa cholalikira uthenga wa Ufumu. Ngakhale zinali choncho, ndinayambapo kulalikira nyumba ndi nyumba ndipo ine ndi mwamuna wanga tinalolera kuti apainiya ndi oyang’anira oyendayenda azifikira m’nyumba yathu. Mabuku ofotokoza Baibulo amene abale ndi alongo a ku Amsterdam ankabweretsa tinkawasunganso m’nyumba yathu. Iwo ankanyamula mabuku ambiri panjinga zawo ndipo ankakutira mabukuwo ndi malona. Apatu anasonyeza chikondi kwambiri ndiponso kulimba mtima. Iwo ankaika moyo wawo pachiswe pofuna kuthandiza abale awo.​—1 Yoh. 3:16.

“Amayi, Mubwera Posachedwapa Eti?”

Patangopita miyezi pafupifupi 6 kuchokera pamene ndinabatizidwa, apolisi atatu anabwera kunyumba kwathu. Iwo anabwera kudzafufuza mabuku. Apolisiwa sanapeze mabuku ambiri amene tinasunga koma anangopeza ochepa chabe amene tinabisa kunsi kwa bedi. Atangowapeza ananditenga kupita nane ku polisi ya ku Hilversum. Pamene ndinkatsanzikana ndi mwana wanga Willy, anandifunsa kuti, “Amayi, mubwera posachedwapa eti?” Ndinamuyankha kuti, “Ee, ndibwera posachedwapa.” Koma panapita miyezi 18 ndisanakumanenso ndi mwana wangayu.

Ndiyeno wapolisi wina ananditenga pa sitima n’kupita nane kuti Amsterdam kuti ndikafunsidwe mafunso. Ofunsawo anandikakamiza kuti ndiulule ngati abale ena atatu a ku Hilversum ndi a Mboni za Yehova. Ndinawayankha kuti: “Enawo sindikuwadziwa. Ndikungodziwapo mmodzi amene amatibweretsera mkaka.” Zomwe ndinanenazi zinali zoona chifukwa m’baleyu ankabweretsadi mkaka. Kenako ndinauza anthuwo kuti: “Zoti ndi wa Mboni za Yehova kapena ayi sindikudziwa. Mungachite bwino kumufunsa iyeyo osati ineyo.” Nditakana kunena chilichonse pa nkhaniyi anandimenya mbama n’kunditsekera muselo imene ndinakhalamo kwa miyezi iwiri. Mwamuna wanga atadziwa kumene ndinali ankandibweretsera zovala ndi chakudya. Ndiyeno mu August 1941, anapita nane ku ndende ya azimayi yoipa kwambiri ya Ravensbrück. Ndendeyi inali pa mtunda wa makilomita 80 kumpoto kwa Berlin, m’dziko la Germany.

“Asisi, Musade Nkhawa”

Titafika kundendeyi, tinauzidwa kuti akhoza kutimasula ngati titasaina chikalata chonena kuti tasiya chikhulupiriro chathu. Koma ine sindinasaine. Zitatero, anandilanda zinthu zanga zonse n’kupita nane kubafa komwe ndinavula zovala zonse n’kuzipereka. Kumeneku ndinapeza alongo ena achikhristu ochokera ku Netherlands. Kenako anatipatsa zovala za kundende zokhala ndi chizindikiro cha kansalu kapepo kamene anasokerera pamalaya. Anatipatsanso mbale, kapu ndi sipuni. Tsiku loyamba tinagonekedwa m’nyumba ina mongoyembekezera. Kuchokera pamene ndinamangidwa, ndinalira kwa nthawi yoyamba nditafika m’nyumbayi. Ndinalira n’kumadzifunsa kuti: “Kodi chindichitikire n’chiyani? Kodi ndikhala kuno kwa nthawi yaitali bwanji?” Kunena zoona, pa nthawiyi ubwenzi wanga ndi Yehova sunali wolimba kwenikweni chifukwa ndinali nditangophunzira choonadi kwa miyezi yochepa chabe. Panali zambiri zimene ndinafunika kuphunzira. Tsiku lotsatira akuitana mayina, mlongo wina wachidatchi ayenera kuti anaona kuti sindikusangalala ndipo ananena kuti: “ Asisi, musade nkhawa. Palibe zimene zingatichitikire.”

Atamaliza kuitana mayina anatitenga kupita kunyumba ina ndipo kumeneku alongo mahandiredi angapo ochokera ku Germany ndi ku Netherlands anatilandira bwino. Ena mwa alongo a ku Germany amenewa anali atakhala m’nyumbayi kwa nthawi yopitirira chaka chimodzi. Ndinalimbikitsidwa kwambiri kukhala ndi alongo amenewa ndipo sindinkada nkhawa. Ndinachita chidwi kuona kuti nyumba imene alongowa ankakhala inali yaukhondo kwambiri kuposa nyumba zina zonse za kundendeyi. Kuwonjezera pamenepa, nyumba yathuyi inkadziwikanso kuti anthu ake sankaberana, kutukwana kapenanso kumenyana. Ngakhale kuti kundendeku ankatizunza, nyumba yathuyi inali ngati chilumba chaukhondo chopezeka panyanja yonyansa.

Moyo wa Kundende

Kundendeku tinkagwira ntchito kwambiri koma sitinkadya mokwanira. Tinkadzuka 5 koloko m’mawa ndipo kenako asilikali ankaitana mayina titaima panja. Izi zinkachitika kwa ola lathunthu ndipo sankasintha zimenezi kaya kukhale mvula kapena dzuwa. Iwo ankaitananso mayina nthawi ya 5 koloko madzulo tikaweruka ku ntchito ya kalavulagaga. Kenako tinkadya supu ndi buledi basi, ndipo tinkapita kukagona titatoperatu.

Tsiku lililonse, kupatulapo Lamlungu, ndinkagwira ntchito kumunda komwe ndinkamweta tirigu, kuchotsa matope ndi zinyalala m’ngalande ndiponso kuyeretsa makola a nkhumba. Ngakhale kuti ntchitoyi inali ya kalavulagaga ndiponso yauve, ndinkaigwira tsiku lililonse chifukwa chakuti ndinali wachinyamata komanso wamphamvu ndithu. Ndinkapezanso mphamvu pogwira ntchito ndikamaimba nyimbo zokhala ndi uthenga wa m’Baibulo. Komabe tsiku lililonse ndinkalakalaka kuonana ndi mwamuna wanga komanso mwana wanga.

Tinkalandira chakudya chochepa kwambiri koma tinkasungako buledi pang’ono tsiku lililonse. Tinkachita izi n’cholinga choti tidzakhale ndi chakudya chokwanira Lamlungu pa nthawi yosonkhana kuti tikambirane nkhani za m’Baibulo. Tinalibe mabuku ofotokoza Baibulo koma ndinkamvetsera mwachidwi alongo achikulire okhulupirika a ku Germany akamafotokoza nkhani za m’Baibulo. Tinkachitanso mwambo wokumbukira imfa ya Khristu.

Kuda Nkhawa, Kunong’oneza Bondo ndi Kulimbikitsidwa

Nthawi zina tinkauzidwa kuti tigwire ntchito yochirikiza nkhondo imene asilikali a Nazi ankamenya. Popeza sitinkalowerera nkhani za ndale, alongo onse anakana kugwira ntchito zoterezi ndipo inenso ndinatsatira kulimba mtima kwawo. Pofuna kutilanga chifukwa cha zimenezi, sanatipatse chakudya kwa masiku angapo ndipo ankatikakamiza kuima panja kwa maola angapo pa nthawi yoitana mayina. Tsiku lina m’nyengo yozizira anatitsekera m’nyumba yopanda zipangizo zilizonse zotenthetsera m’nyumbamo ndipo tinakhalamo kwa masiku 40.

Mboni za Yehovafe tinkauzidwa nthawi ndi nthawi kuti tikasaina chikalata chonena kuti tasiya chikhulupiriro chathu atitulutsa ndipo tizipita kwathu. Nditakhala kundende ya Ravensbrück kwa nthawi yoposa chaka chimodzi, ndinataya mtima kwambiri. Ndinkalakalaka kwambiri kuona mwamuna wanga ndi mwana wanga moti ndinapita kwa asilikali n’kuwauza kuti andipatse chikalata chosonyeza kuti sindidzakhalanso Wophunzira Baibulo ndipo ndinachisaina.

Alongo atamva zimene ndinachitazi, ena anayamba kundipewa. Koma alongo awiri achikulire a ku Germany anandipeza n’kunditsimikizira zoti amandikondabe. Mayina awo anali Hedwig ndi Gertrud. Tsiku lina tikugwira ntchito m’makola a nkhumba alongowa anandifotokozera mokoma mtima kufunika kotumikira Yehova ndi mtima wosagawanika ndiponso mmene tingasonyezere kuti timamukonda mwa kusagonja pa mayesero. Chifukwa chakuti iwo anandilankhula mwachikondi ngati mayi anga zinandikhudza kwambiri. * Ndinazindikira kuti ndinali nditalakwitsa ndipo ndinkafuna kukasintha zimene ndinasainirazo. Tsiku lina madzulo ndinauza mlongo wina maganizo angawa. Msilikali wina ayenera kuti anamva zimene tinkakambiranazi chifukwa madzulo omwewo ndinatulutsidwa m’ndendeyo n’kunditumiza pa sitima kubwerera ku Netherlands. Msilikali wina wamkulu, yemwe ndimakumbukirabe nkhope yake, anati, “Ndiwebe Wophunzira Baibulo ndipo sudzasintha.” Ndinamuyankha kuti, “Inde, ngati Yehova alola.” Koma ndinkaganizabe kuti, ‘Kodi ndingasinthe bwanji zimene ndinasainira zija?’

Mfundo ina imene inali m’chikalata chija inali yakuti: “Ndikutsimikiza kuti sindidzachitanso zinthu mogwirizana ndi gulu la Mboni za Yehova (International Bible Students Society).” Ndinadziwa zoyenera kuchita kuti ndisinthe zimene ndinasainira. Nditangofika kwathu mu January 1943, ndinayambiranso ntchito yolalikira. Ndinkadziwa kuti ngati a chipani cha Nazi akanandigwiranso ndikulalikira za Ufumu wa Mulungu akanandipatsa chilango choopsa kwambiri.

Pofuna kusonyeza Yehova kuti ndikufunadi ndi mtima wonse kumutumikira mokhulupirika, ine ndi mwamuna wanga tinakonza zoti abale onyamula mabuku ndiponso oyang’anira oyendayenda azifikiranso m’nyumba yathu. Ndinayamikira kwambiri kukhalanso ndi mwayi wosonyeza kuti ndimakonda Yehova ndi anthu ake.

Ndinakumana ndi Vuto Lalikulu

Kutangotsala miyezi yochepa kuti nkhondo ithe, ine ndi mwamuna wanga tinakumana ndi vuto lalikulu. Mwana wathu, Willy, anayamba kudwala matenda oopsa amene amachititsa munthu kubanika (diphtheria). Matendawa anayamba mwadzidzidzi mu October 1944 ndipo anakula mwamsanga moti anamwalira patangopita masiku atatu. Pa nthawiyi mwanayu anali ndi zaka 8 zokha.

Tinali ndi mwana mmodzi yekhayu ndipo imfa yake inali yopweteka kwambiri. Mavuto amene ndinakumana nawo kundende ya Ravensbrück sanali opweteka ndikawayerekezera ndi imfa ya mwana wathuyu. Komabe tikamada nkhawa kwambiri tinkalimbikitsidwa ndi mawu a pa Salimo 16:8 akuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” Ine ndi mwamuna wanga tinkakhulupirira kwambiri lonjezo la Yehova lakuti akufa adzauka. Sitinabwerere m’mbuyo mwauzimu ndipo tinkalalikira uthenga wabwino mwakhama. Mwamuna wanga ankandithandiza kuyamikira mwayi wanga wotumikira Yehova mpaka pamene iye anamwalira mu 1969.

Tinadalitsidwa Ndipo Tinkasangalala

Pa zaka zambiri zimene zapitazi, chinthu china chimene chandithandiza kukhala wosangalala ndi kugwirizana ndi atumiki a nthawi zonse. Mofanana ndi nthawi ya nkhondo ija, oyang’anira oyendayenda limodzi ndi akazi awo ankafikira m’nyumba yathu akamachezera mpingo wathu. Banja la Maarten Kaptein ndi mkazi wake Nel, limene linkachita utumiki woyendayenda, linakhala m’nyumba yathu kwa zaka 13. Pamene Nel anayamba kudwala ndinali ndi mwayi womusamalira kwa miyezi itatu mpaka pamene anamwalira. Kucheza ndi anthu amenewa komanso abale ndi alongo a mumpingo wathu kwandithandiza kuti ndizisangalala ndi paradaiso wauzimu amene tilimo masiku ano.

Chinthu china chosangalatsa kwambiri pa moyo wanga ndi kupezeka ku Ravensbrück pa mwambo wokumbukira zochitika kundendeyi mu 1995. Kumeneku ndinaonana ndi alongo amene tinali nawo kundendeyi ndipo tinali tisanaonane kwa zaka zoposa 50. Zinali zosangalatsa kwambiri ndiponso zolimbikitsa kukumana ndi alongo amenewa ndipo tinali ndi mwayi wolimbikitsana kuti tiziyembekezera tsiku limene tidzaona okondedwa athu amene anamwalira akuukitsidwa.

Pa Aroma 15:4 mtumwi Paulo ananena kuti timakhala ndi ‘chiyembekezo chifukwa Malemba amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.’ Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa chiyembekezo chimene chandithandiza kumutumikira ngakhale pa nthawi zovuta.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Pa nthawiyi sitinkatha kukambirana ndi abale a ku likulu lathu ndipo abale ankasamalira nkhani zokhudza kulowerera ndale malinga ndi luso lawo. Choncho anthu ankaona nkhaniyi mosiyanasiyana.

[Chithunzi patsamba 10]

Ndili ndi Jaap mu 1930

[Chithunzi patsamba 10]

Mwana wathu Willy ali ndi zaka 7

[Chithunzi patsamba 12]

Mu 1995 ndinalimbikitsidwa nditakumananso ndi anzanga awa. Ndili pa mzere woyamba ndipo ndine wachiwiri kuchokera kumanzere