Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Pezani Chitetezo M’dzina la Yehova’

‘Pezani Chitetezo M’dzina la Yehova’

‘Pezani Chitetezo M’dzina la Yehova’

“Ndidzasiyamo anthu . . . odzichepetsa ndi ofatsa, ndipo amenewa adzapeza chitetezo m’dzina la Yehova.”​—ZEF. 3:12.

1, 2. Kodi ndi mphepo yamkuntho yophiphiritsira iti imene idzafika posachedwapa?

KODI tsiku lina muli pa ulendo munabisalapo pansi pa mtengo kukugwa mvula? Koma mvulayo ikakhala yamkuntho simungabisale pansi pa mtengo basi. Koma mungafunefune malo abwino kumene mungatetezeke.

2 Koma pali mtundu wina wa mkuntho umene ukubwera. Mkuntho umenewu ukhoza kuwononga anthu onse. “Tsiku la mphepo yamkuntho” limeneli ndi lophiphiritsira. Tsikuli ndi “tsiku lalikulu la Yehova” limene lidzakhudza munthu aliyense. Koma n’zotheka kupeza chitetezo. (Werengani Zefaniya 1:14-18.) Kodi tingadzapeze bwanji chitetezo posachedwapa, “tsiku la mkwiyo wa Yehova” likadzayamba?

Masiku a Mphepo Yamkuntho M’nthawi za M’Baibulo

3. Kodi ndi “mvula yamabingu” iti imene inafikira mafuko 10 a Isiraeli?

3 Tsiku la Yehova lidzayamba zipembedzo zonyenga zonse padziko lapansi zikamadzawonongedwa. Kuti tidziwe mmene tingapezere chitetezo pa nthawiyo, tiyenera kuona zimene zinachitikira anthu a Mulungu m’mbuyomu. Yesaya, amene anakhalapo m’zaka za m’ma 700 B.C.E., anayerekezera chiweruzo cha Yehova pa mafuko 10 ampatuko a ufumu wa Isiraeli ndi “mvula yamabingu,” imene anthu sakanatha kuipewa. (Werengani Yesaya 28:1, 2.) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa mu 740 B.C.E., pamene Asuri anawononga mafuko amenewa. Fuko la Efulaimu linali lalikulu kwambiri ndipo linkaimira mafuko 10 onsewa.

4. Kodi “tsiku lalikulu la Yehova” linafika bwanji pa Yerusalemu mu 607 B.C.E?

4 Mafuko 10 a Isiraeli atawonongedwa, “tsiku lalikulu la Yehova” linafikanso pa Yerusalemu ndi ufumu wa Yuda mu 607 B.C.E. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti nawonso anthu a ku Yuda anali ampatuko. Motsogoleredwa ndi Nebukadinezara, Ababulo anaopseza Yuda ndi likulu lake, Yerusalemu. Pa nthawiyi anthu a ku Yudeya anapempha thandizo ku “malo othawirapo abodza,” omwe anali mgwirizano wandale umene anachita ndi Iguputo. Komabe mofanana ndi mphepo ya mkuntho yowononga, Ababulo anawononga “malo othawirapo” amenewo.​—Yes. 28:14, 17.

5. Kodi zinthu zidzawayendera bwanji anthu a Mulungu, monga gulu, pamene zipembedzo zonyenga zizidzawonongedwa?

5 Tsiku lalikulu la Yehova limene linafika pa Yerusalemu limasonyeza zimene zidzachitikire Matchalitchi Achikhristu mu nthawi yathu. Zipembedzo zinanso zomwe zikupanga “Babulo Wamkulu,” amene akuimira ulamuliro wa padziko lonse wa chipembedzo chonyenga, zidzafafanizidwa. Kenako mbali zotsala za dongosolo loipa la Satanali zidzawonongedwanso. Koma anthu a Mulungu, monga gulu, adzapulumuka chifukwa akupeza chitetezo mwa Yehova.​—Chiv. 7:14; 18:2, 8; 19:19-21.

Kupeza Chitetezo Chauzimu Ndiponso Chakuthupi

6. Kodi anthu a Yehova angapeze bwanji chitetezo?

6 Kodi anthu a Mulungu angapeze bwanji chitetezo m’nthawi yamapeto ino? Tikhoza kupeza chitetezo chauzimu mwa kulemekeza ndi “kuganizira za dzina” la Mulungu ndiponso mwa kumutumikira mwakhama. (Werengani Malaki 3:16-18.) Koma kungoganizira chabe dzina la Mulungu si kokwanira. Tikutero chifukwa Malemba amati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Aroma 10:13) Pali kugwirizana pakati pa kuitanira pa dzina la Yehova ndi kupulumutsidwa ndi iye. Ndipotu anthu a mtima wabwino akhoza kuona kusiyana pakati pa anthu amene sakutumikira Mulungu ndi Akhristu oona, amene amalemekeza ndi “kuganizira za dzina lake” ndiponso kumutumikira monga Mboni zake.

7, 8. Kodi Akhristu oyambirira anapulumutsidwa bwanji mwakuthupi ndipo izi zidzafanana ndi chiyani masiku ano?

7 Komabe chitetezo chimene tingapeze si chauzimu chokha. Mulungu walonjezanso anthu ake za chitetezo chakuthupi. Timapeza umboni wa zimenezi pa zimene zinachitika mu 66 C.E. pamene asilikali achiroma motsogoleredwa ndi Cestius Gallus anaukira mzinda wa Yerusalemu. Yesu analosera kuti masiku a chisautso chimenecho ‘adzafupikitsidwa.’ (Mat. 24:15, 16, 21, 22) Zimenezi zinachitika pamene asilikali achiromawo mosayembekezeka anabwerera osaukira mzindawo ndipo zinapereka mpata woti Akhristu oona ‘apulumuke.’ Iwo anapeza mwayi wothawa mumzindawo ndiponso m’madera a pafupi ndi mzindawo. Ena anawoloka mtsinje wa Yorodano ndipo anakapeza chitetezo kumapiri a kum’mawa kwa mtsinjewo.

8 Pali kufanana pakati pa Akhristu a m’nthawi imeneyo ndi anthu a Mulungu a masiku ano. Kale, Akhristu oyambirira anafufuza malo a chitetezo ndipo izi n’zimene atumiki a Mulungu a masiku ano adzachita. Koma masiku ano Akhristu sadzathawira kumalo amodzi enieni chifukwa Akhristu oona amapezeka padziko lonse lapansi. Ngakhale zili choncho, monga gulu, anthu “osankhidwawo” pamodzi ndi anzawo okhulupirika adzapulumuka mwakuthupi pamene Matchalitchi Achikhristu azidzawonongedwa. Izi zidzatheka chifukwa chopeza chitetezo mwa Yehova ndi gulu lake, lomwe lili ngati phiri.

9. Kodi ndani akufuna kuti anthu asadziwe dzina la Yehova? Perekani chitsanzo.

9 Koma Matchalitchi Achikhristu ndi oyeneradi kuwonongedwa chifukwa chakuti ndi amene achititsa kuti anthu amene amapita kumatchalitchi awo asadziwe Baibulo ndiponso chifukwa chakuti amadana ndi dzina la Mulungu. Zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500, dzina lenileni la Mulungu linkadziwika kwambiri ku Ulaya. Dzinali linkalembedwa ndi zilembo zinayi zachiheberi zimene zimaimira YHWH (kapena JHVH), ndipo zilembozo zinkapezeka pandalama, pamakoma a nyumba, m’mabuku, m’Mabaibulo ambiri ndiponso m’matchalitchi achikatolika ndi a zipembedzo zina. Koma masiku ano anthu ayamba kuchotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo ndipo asiya kuligwiritsa ntchito. Umboni wa zimenezi ndi kalata ya pa June 29, 2008, yonena za dzina la Mulungu, imene inapita kwa mabishopu. Kalatayi inalembedwa ndi bungwe la akuluakulu a Katolika loona za kulambira ndiponso loika malamulo a kayendetsedwe ka Misa. M’kalatayi, tchalitchi cha Katolika chinanena kuti dzina la Mulungu, kaya lalembedwa motani, siliyenera kugwiritsidwa ntchito ndipo m’malo mwake azigwiritsa ntchito mawu akuti “Ambuye.” Akuluakulu a ku Vatican, komwe ndi likulu la tchalitchi cha Katolika, ananena kuti dzina la Mulungu siliyenera kugwiritsidwa ntchito kapena kutchulidwa poimba nyimbo kapena popemphera pa misonkhano yachikatolika. Nawonso atsogoleri a matchalitchi ena achikhristu komanso zipembedzo zina asokoneza anthu ambirimbiri opembedza kuti asadziwe Mulungu woona.

Chitetezo kwa Anthu Amene Akuyeretsa Dzina la Mulungu

10. Kodi dzina la Mulungu likulemekezedwa bwanji masiku ano?

10 Mosiyana ndi zimene zipembedzo zina zikuchita, a Mboni za Yehova amalemekeza kwambiri dzina la Mulungu. Amayeretsa dzinali mwa kuligwiritsa ntchito mwaulemu. Yehova amasangalala ndi anthu amene amamukhulupirira ndipo iye amakhala aliyense amene angafunike kuti adalitse ndi kuteteza anthu ake. Mulungu “amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.”​—Nah. 1:7; Mac. 15:14.

11, 12. Kodi ndani anakhalabe okhulupirika kwa Yehova ku Yuda, nanga ndani akuchita zimenezi masiku ano?

11 Ngakhale kuti anthu ambiri ku Yuda kalelo anali ampatuko, panali ena amene anapeza “chitetezo m’dzina la Yehova.” (Werengani Zefaniya 3:12, 13.) Pamene Mulungu analanga Ayuda osakhulupirika polola kuti Ababulo aukire dziko lawo n’kutenga ukapolo anthu ake, anthu ena monga Yeremiya, Baruki ndi Ebedi-meleki anapulumutsidwa. Iwo ankakhala pakati pa mtundu wampatuko koma anakhalabe okhulupirika. Enanso anakhalabe okhulupirika pamene anali ku ukapolo. Mu 539 B.C.E., Amedi ndi Aperisi motsogoleredwa ndi Koresi anagonjetsa Ababulo. Pasanapite nthawi yaitali Koresi anapereka lamulo lolola Ayuda amene anatsala kuti abwerere kudziko lawo.

12 Ponena za anthu okabwezeretsa kulambira koona, Zefaniya analosera kuti Yehova adzawapulumutsa ndipo adzakondwera nawo. (Werengani Zefaniya 3:14-17.) Izi ndi zimene zachitikanso masiku ano. Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa kumwamba, Yehova anapulumutsa odzozedwa okhulupirika amene anatsala n’kuwachotsa ku ukapolo wauzimu wa Babulo Wamkulu. Ndipo iye amakondwera nawo mpaka pano.

13. Kodi anthu a mitundu yonse akumasulidwa ku chiyani masiku ano?

13 Anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi anatulukanso mu Babulo Wamkulu ndipo anamasulidwa ku ziphunzitso zonyenga za zipembedzo. (Chiv. 18:4) Choncho, mawu a pa Zefaniya 2:3 akukwaniritsidwa masiku ano kuposa m’mbuyomu. Lembali limati: “Bwerani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi.” Anthu ofatsa ochokera m’mitundu yonse, okhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padziko lapansi, akupeza chitetezo mu dzina la Yehova.

Dzina la Mulungu Si Chithumwa

14, 15. (a) Kodi anthu ena agwiritsa ntchito zinthu ziti ngati chithumwa? (b) Kodi sitiyenera kugwiritsa ntchito chiyani ngati chithumwa?

14 Aisiraeli ena ankaganiza kuti kachisi ali ngati chithumwa chowateteza kwa adani awo. (Yer. 7:1-4) Kachisi asanamangidwe, Aisiraeli ankaganizanso kuti likasa la pangano linali ngati chithumwa chowateteza pa nkhondo. (1 Sam. 4:3, 10, 11) Constantine Wamkulu analemba zilembo ziwiri zoyambirira za dzina lakuti “Khristu,” zomwe m’Chigiriki ndi X ndi P, pazishango za asilikali ake. Anachita zimenezi pokhulupirira kuti asilikaliwo adzatetezedwa pa nkhondo. Ndiponso anthu amanena kuti Mfumu Gustav Adolph Yachiwiri ya ku Sweden inavala chovala chankhondo chimene chasonyezedwa patsamba 7. Mfumu imeneyi inamenya nawo nkhondo ina ya ku Ulaya imene inatenga zaka 30. Onani kuti dzina lakuti “Iehova” linalembedwa moonekera kwambiri pachovalachi.

15 Anthu a Mulungu ena amene ankavutitsidwa ndi ziwanda anapeza chitetezo chifukwa chotchula mokweza dzina la Yehova. Komabe, zinthu zokhala ndi dzina la Mulungu sitiyenera kuziona ngati chithumwa kapena kuzigwiritsa ntchito ngati kuti zingatiteteze mwamatsenga. Kupeza chitetezo mu dzina la Yehova sikutanthauza zimenezi.

Mmene Tingapezere Chitetezo Masiku Ano

16. Kodi tingapeze bwanji chitetezo chauzimu masiku ano?

16 Tingapeze chitetezo chauzimu masiku ano pakati pa gulu la anthu a Mulungu. (Sal. 91:1) Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” komanso akulu m’mipingo, timachenjezedwa za zinthu za m’dzikoli zimene zingachititse kuti tisakhale ndi chitetezo chimenechi. (Mat. 24:45-47; Yes. 32:1, 2) Mwachitsanzo, takhala tikulandira malangizo mobwerezabwereza pa nkhani yokonda chuma ndipo izi zatiteteza kuti tisakumane ndi tsoka mwauzimu. Timalimbikitsidwanso kupewa mphwayi chifukwa zingachititse kuti tisiye kutumikira Yehova. Mawu a Mulungu amati: “Mphwayi za opusa n’zimene zidzawawononge. Koma munthu wondimvera adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miy. 1:32, 33) Tikamayesetsa kukhala ndi khalidwe loyera timatetezedwa mwauzimu.

17, 18. N’chiyani chikuthandiza anthu mamiliyoni ambiri kupeza chitetezo m’dzina la Yehova masiku ano?

17 Kumbukiraninso kuti kapolo wokhulupirika amatilimbikitsa kutsatira lamulo la Yesu lakuti tilalikire uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Zefaniya ananena za chinthu chimene chidzathandiza anthu kupeza chitetezo m’dzina la Mulungu. Iye analemba kuti: “Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.”​—Zef. 3:9.

18 Kodi chilankhulo choyera n’chiyani? Chilankhulo choyera ndi choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu chonena za Yehova ndi zolinga zake. Mukamauza anthu za choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu ndi mmene Ufumuwu udzayeretsera dzina lake, mumakhala mukulankhula chilankhulo choyera. Mumachitanso zimenezi pamene mukunena motsindika kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse komanso mukamauza anthu mosangalala za madalitso amuyaya amene anthu okhulupirika adzalandira. Chifukwa chakuti anthu ambiri akulankhula chilankhulo chophiphiritsa chimenechi anthu ochuluka ‘akuitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.’ Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse akupeza chitetezo kwa Yehova.​—Sal. 1:1, 3.

19, 20. M’nthawi za Baibulo kodi anthu odalira “malo othawirapo abodza” anagwiritsidwa bwanji mwala?

19 Anthu m’dzikoli akukumana ndi mavuto akuluakulu. Pofuna kuthana ndi mavutowo ambiri amadalira anthu opanda ungwiro. Kapenanso, amaganiza kuti magulu andale angawathandize ndipo izi n’zofanana ndi zimene Aisiraeli akale anachita. Iwo ankadalira mitundu yoyandikana nawo ndipo ankachita nayo mapangano kuti iwathandize. Koma mukudziwa kuti izi sizinathandize Aisiraeliwo. Masiku ano, palibe boma limene lingathetse mavuto a anthu. Ngakhale bungwe la United Nations silingathetse mavutowa. Choncho munthu sangapeze chitetezo m’magulu andale kapena pochita mapangano. Baibulo linalosera kuti amenewa ndi “malo othawirapo abodza.” Mpake kuwaona motere chifukwa anthu onse amene amawadalira adzagwiritsidwa mwala.​—Werengani Yesaya 28:15, 17.

20 Posachedwapa tsiku la Yehova lomwe lili ngati chimvula chamkuntho lidzabwera. Pa nthawi imeneyo, palibe chuma, nyumba zotetezeka kapena zoyesayesa zilizonse za anthu zimene zingapereke chitetezo. Lemba la Yesaya 28:17 limati: “Mvula yamatalala idzakokolola malo othawirapo abodza ndipo madzi adzasefukira pamalo obisalako.”

21. Kodi tidzapindula bwanji mwa kutsatira lemba la chaka cha 2011?

21 Panopo komanso pa tsiku la Yehova, anthu a Mulungu angapeze chitetezo chenicheni kwa Mulungu wawo, Yehova. Dzina lakuti Zefaniya limatanthauza kuti “Yehova Wabisa” ndipo limasonyeza kuti Mulungu ndi amene amapereka malo enieni obisalako. M’pomveka kuti lemba la chaka cha 2011 likupereka malangizo anzeru akuti: ‘Pezani chitetezo m’dzina la Yehova.’ (Zef. 3:12) Ngakhale masiku anowa tingapeze chitetezo m’dzina la Yehova ndipo tiyenera kumukhulupirira ndi mtima wonse. (Sal. 9:10) Choncho tsiku lililonse tizikumbukira mawu olimbikitsa akuti: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.”​—Miy. 18:10.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi tingapeze bwanji chitetezo m’dzina la Yehova masiku ano?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kudalira “malo othawirapo abodza”?

• Kodi tatsimikiziridwa za chitetezo chiti m’tsogolo?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Lemba la chaka cha 2011 ndi lakuti: ‘Pezani chitetezo m’dzina la Yehova.’​—Zefaniya 3:12.

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

Thüringer Landesmuseum Heidecksburg Rudolstadt, Waffensammlung “Schwarzburger Zeughaus”