Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumadana Ndi Kusamvera Malamulo?

Kodi Mumadana Ndi Kusamvera Malamulo?

Kodi Mumadana Ndi Kusamvera Malamulo?

‘[Yesu] anadana ndi kusamvera malamulo.’​—AHEB. 1:9.

1. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani pa nkhani ya chikondi?

POFUNA kutsindika kufunika kwa chikondi, Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Yesu analamula otsatira ake kuti azisonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Iye anati anthu adzawadziwa chifukwa cha chikondi chimenechi. Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.”​—Mat. 5:44.

2. Kodi otsatira a Khristu ayenera kudana ndi chiyani?

2 Sikuti Yesu anangophunzitsa ophunzira ake za chikondi, iye anawaphunzitsanso zimene ayenera kudana nazo. Ponena za Yesu, Malemba amanena kuti: “Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo [kapena kuti zoipa].” (Aheb. 1:9; Sal. 45:7) Zimenezi zikusonyeza kuti tiyenera kukonda chilungamo komanso kudana ndi tchimo, kapena kuti kusamvera malamulo. N’chifukwa chake mtumwi Yohane ananena mosapita m’mbali kuti: “Aliyense amene amachita tchimo samvera malamulo, choncho tchimo ndilo kusamvera malamulo.”​—1 Yoh. 3:4.

3. Pa nkhani yodana ndi zoipa, kodi tikambirana mfundo ziti mu nkhani ino?

3 Choncho popeza ndife Akhristu, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimadana ndi zoipa?’ Tiyeni tione mmene tingasonyezere kuti timadana ndi zoipa pa mbali zinayi izi: (1) Kumwa mowa, (2) kukhulupirira zamizimu, (3) chiwerewere ndiponso (4) mmene timaonera anthu amene amakonda kuchita zoipa.

Musakhale Kapolo wa Mowa

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anali ndi ufulu wolankhula pamene ankachenjeza za kuopsa kwa kumwa mowa kwambiri?

4 Nthawi zina Yesu ankamwa vinyo ndipo ankadziwa kuti vinyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Sal. 104:14, 15) Komabe iye sankamwa mopitirira muyezo ndiponso sankaledzera. (Miy. 23:29-33) Choncho, Yesu anali ndi ufulu wolankhula pamene ankalangiza ena za kuopsa kwa kumwa mowa kwambiri. (Werengani Luka 21:34.) Kuledzera kungapangitse munthu kuchitanso machimo ena akuluakulu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa, koma khalanibe odzaza ndi mzimu.” (Aef. 5:18) Mtumwiyu analangizanso akazi achikulire mu mpingo kuti asakhale “akapolo a vinyo wambiri.”​—Tito 2:3.

5. Kodi anthu amene amamwa mowa ayenera kudzifunsa mafunso ati?

5 Ngati mumamwa mowa, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona nkhani ya kumwa mowa mmene Yesu amaionera? Nditakhala kuti ndikufuna kulangiza anthu ena pa nkhani imeneyi, kodi ndingakhale ndi ufulu wolankhula? Kodi ndimamwa mowa n’cholinga chofuna kuiwala mavuto ndiponso kuchepetsa nkhawa? Kodi pa mlungu ndimamwa mowa wochuluka bwanji? Munthu wina akandiuza kuti ndikumwa mowa kwambiri, kodi ndimatani? Kodi ndimadziikira kumbuyo mwinanso kukhumudwa kumene?’ Tikakhala akapolo a vinyo wambiri tingamalephere kuganiza bwino ndiponso kusankha zinthu mwanzeru. Anthu amene amatsatira Khristu, nthawi zonse amayesetsa kupewa zinthu zimene zingawachititse kuti asamaganize bwino.​—Miy. 3:21, 22.

Muzipewa Zamizimu

6, 7. (a) Kodi Yesu anachita bwanji ndi Satana komanso ziwanda? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amachita zamizimu?

6 Pamene Yesu anali padziko lapansi anatsutsa mwamphamvu Satana ndiponso ziwanda. Iye sanagonje pamene Satana ankamuyesa mwachindunji kuti asakhale wokhulupirika. (Luka 4:1-13) Pamene Satana ankamuyesa mwakabisira kuti asinthe maganizo ndiponso zochita zake, Yesu anazindikira zimenezi ndipo sanagonje. (Mat. 16:21-23) Yesu anathandiza anthu kuti amasuke ku ulamuliro wankhanza wa ziwanda.​—Maliko 5:2, 8, 12-15; 9:20, 25-27.

7 Yesu atakhala Mfumu mu 1914, anayeretsa kumwamba mwa kuchotsako Satana ndi ziwanda zake. Chifukwa cha zimenezi, Satana akuyesetsa ‘kusocheretsa dziko lonse lapansi’ kuposa kale. (Chiv. 12:9, 10) Choncho sitiyenera kudabwa kuti anthu ambiri masiku ano amakopeka ndi zamizimu ndipo zimenezi zikuchulukirachulukira. Kodi tingatani kuti tidziteteze?

8. Pa nkhani ya zosangalatsa zimene timasankha, kodi aliyense ayenera kudzifunsa mafunso ati?

8 Baibulo limanena mosapita m’mbali kuopsa kochita zinthu zokhudzana ndi mizimu. (Werengani Deuteronomo 18:10-12.) Masiku ano Satana ndi ziwanda akusokoneza maganizo a anthu kudzera m’mafilimu, m’mabuku ndiponso masewera a pakompyuta amene ali ndi zinthu zokhudza zamizimu. Choncho tikamasankha zosangalatsa tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Pa miyezi ingapo yapitayi, kodi ndinkakonda mafilimu, mapulogalamu a pa TV, masewera a pa kompyuta kapena mabuku okhala ndi nkhani zamizimu? Kodi ndimadziwadi kufunika kopewa zamizimu kapena ndimaona kuti nkhani imeneyi ndi yaing’ono? Ndikafuna kusankha zosangalatsa, kodi ndimaganizira mmene Yehova angazionere? Ngati ndayamba kusangalala ndi nkhani zokhudza zamizimu, kodi kukonda Yehova ndiponso mfundo zake zolungama kungandichititse kuchitapo kanthu mwamsanga n’kuyamba kuzipewa?’​—Mac. 19:19, 20.

Tizimvera Chenjezo la Yesu pa Nkhani ya Chiwerewere

9. Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti wayamba kukonda zoipa?

9 Yesu ankalimbikitsa kwambiri anthu kuti azitsatira mfundo za Yehova zokhudza kugonana. Iye anati: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:4-6) Yesu ankadziwa kuti zimene timaona ndi maso athu zimakhazikika mumtima mwathu. Choncho pa ulaliki wake wa paphiri iye anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:27, 28) Anthu amene amanyalanyaza machenjezo a Yesu amenewa, ndiye kuti ayamba kukonda zoipa.

10. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti n’zotheka kusiya kukonda zolaula.

10 Satana amagwiritsa ntchito zinthu zolaula pofuna kulimbikitsa anthu kuti azichita zachiwerewere. Masiku ano m’dzikoli zinthu zolaula zili ponseponse. Anthu amene amaonera zolaula, amavutika kuiwala zimene anaonerazo. Iwo amavutikanso kwambiri kuti asiye kuonera zinthu zimenezi. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina. Iye anati: “Ndinkaonera zolaula mobisa. Ndinkaganiza kuti zimene ndinkachitazo sizingakhudze utumiki wanga kwa Yehova. Ndinkadziwa kuti zimenezi n’zolakwika koma ndinkaganiza kuti Mulungu akusangalalabe ndi utumiki wanga.” Kodi n’chiyani chinathandiza m’baleyu? Iye anati: “Ndinauza akulu za vuto langali ngakhale kuti zimenezi zinali zovuta kwambiri.” Patapita nthawi m’baleyu anasiya khalidwe lonyansali. Ndiyeno iye anati: “Nditasiya tchimo limeneli, ndinayamba kuona kuti ndilidi ndi chikumbumtima choyera.” Anthu amene amadana ndi zoipa ayenera kudananso ndi zinthu zolaula.

11, 12. Pa nkhani ya nyimbo, kodi tingasonyeze bwanji kuti timadana ndi zoipa?

11 Nyimbo ndiponso mawu a nyimbozo zimakhudza maganizo athu, choncho zingakhudzenso mtima wathu wophiphiritsa. Nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo anthu akhala akugwiritsa ntchito nyimbo kwa nthawi yaitali pa kulambira koona. (Eks. 15:20, 21; Aef. 5:19) Koma dziko loipa la Satanali limachititsa anthu kuti azikonda nyimbo zimene zimalimbikitsa chiwerewere. (1 Yoh. 5:19) Ndiye kodi mungadziwe bwanji ngati nyimbo zimene mumakonda kumvetsera zikuipitsa mtima wanu kapena ayi?

12 Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nyimbo zimene ndimamvetsera zimalimbikitsa kupha anthu, chigololo, dama ndiponso kunyoza Mulungu? Ngati nditawerengera munthu wina mawu a nyimbo zimene ndimakonda, kodi munthuyo angaone kuti ndimadana ndi zoipa kapena angaganize kuti mtima wanga waipitsidwa?’ Sitinganene kuti timadana ndi zoipa za m’dzikoli pamene timakonda nyimbo zimene zimalimbikitsa zinthu zoipazo? Yesu anati: “Zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima, ndipo zimenezo zimaipitsa munthu. Mwachitsanzo, maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu, zimachokera mumtima.”​—Mat. 15:18, 19; yerekezerani ndi Yakobo 3:10, 11.

Muziona Anthu Okonda Kusamvera Malamulo Mmene Yesu Amawaonera

13. Kodi Yesu ankawaona bwanji anthu amene sankafuna kusiya machimo awo?

13 Yesu ananena kuti anabwera padziko lapansi kudzaitana anthu ochimwa, kapena kuti osamvera malamulo, kuti alape. (Luka 5:30-32) Koma kodi ankawaona bwanji anthu amene sanafune kusiya zochita zawo zoipa? Yesu anachenjeza anthu mwamphamvu kuti asamatsatire zochita za anthu oterewa. (Mat. 23:15, 23-26) Iye ananenanso momveka bwino kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo [limene Mulungu adzapereke chiweruzo], ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’” Koma Yesu adzakana anthu amene amangopitirizabe kusamvera malamulo. Iye adzawauza kuti: “Chokani pamaso panga.” (Mat. 7:21-23) N’chifukwa chiyani adzawaweruza chonchi? Chifukwa chakuti anthu amenewa salemekeza Mulungu ndipo amavutitsa anthu ena chifukwa cha zochita zawo zoipa.

14. N’chifukwa chiyani anthu ochimwa osalapa amachotsedwa mu mpingo?

14 Mawu a Mulungu amanena kuti anthu ochimwa osalapa ayenera kuchotsedwa mu mpingo. (Werengani 1 Akorinto 5:9-13.) Zimenezi ndi zoyenera pa zifukwa monga izi: (1) kuti dzina la Yehova lisanyozedwe, (2) kuteteza mpingo kuti usaipitsidwe ndiponso (3) kuthandiza munthu wochimwa kuti mwina alape.

15. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati ngati tikufuna kukhalabe okhulupirika kwa Yehova?

15 Kodi nafenso timaona anthu amene akupitirizabe kusamvera malamulo ngati mmene Yesu amawaonera? Tiyenera kuganizira mafunso awa: ‘Kodi ndimakonda kucheza ndi munthu wochotsedwa kapena amene wadzilekanitsa ndi mpingo wachikhristu? Nanga bwanji munthu wotereyu atakhala wachibale amene sindikukhala nayenso nyumba imodzi?’ Zimene tingachite pa nkhani imeneyi zingasonyeze ngati timakondadi chilungamo ndiponso ngati tilidi okhulupirika kwa Mulungu. *

16, 17. Kodi mlongo wina anakumana ndi vuto lotani, ndipo n’chiyani chinamuthandiza kutsatira dongosolo lokhudza anthu ochotsedwa mu mpingo?

16 Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina. Mwana wake wamwamuna wamkulu ankakonda Yehova koma pa nthawi ina anayamba kuchita zinthu zoipa mosalapa. Chifukwa cha zimenezi, mwana wakeyu anachotsedwa mu mpingo. Mlongoyu ankakonda Yehova komanso ankakonda mwana wakeyu. Choncho zinali zovuta kwambiri kwa iye kutsatira lamulo la m’Malemba loti asamachezenso ndi mwana wakeyo.

17 Kodi inuyo mukanam’patsa malangizo otani mlongo ameneyu? M’bale wina amene ndi mkulu anathandiza mlongoyo kuzindikira kuti Yehova akumvetsa mmene akumvera mumtima mwake. M’baleyu anamulimbikitsa kuganizira mmene Yehova zinamupwetekera pamene ana ake ena auzimu amupandukira. Ndiyeno anamuthandizanso kuona mfundo yakuti, ngakhale kuti Yehova amadziwa mmene zinthu ngati zimenezi zimapwetekera zikachitika, iye amanenabe kuti anthu osalapa azichotsedwa mu mpingo. Mlongoyo anamvera malangizo amenewa ndipo mokhulupirika anatsatira dongosolo lokhudza anthu osalapa amene achotsedwa mu mpingo. * Kuchita zinthu mokhulupirika chonchi kumakondweretsa mtima wa Yehova.​—Miy. 27:11.

18, 19. (a) Kodi tikasiya kucheza ndi munthu amene amachita zoipa, timasonyeza kuti tikudana ndi chiyani? (b) Kodi chingachitike n’chiyani tikakhala okhulupirika kwa Mulungu ndiponso dongosolo lake?

18 Ngati nanunso muli ndi vuto ngati limeneli, musaiwale kuti Yehova akumvetsa mmene mukumvera mumtima mwanu. Mukasiya kucheza ndi munthu amene wachotsedwa kapena amene wadzilekanitsa ndi mpingo, mumasonyeza kuti mukudana ndi zinthu zoipa zimene munthuyo anachita. Komanso mumasonyeza kuti mumakonda kwambiri wochimwayo ndipo mukumufunira zabwino. Mukakhala wokhulupirika kwa Yehova mungathandize munthu amene walandira chilangoyo kuti alape ndiponso abwerere kwa Yehova.

19 Mlongo wina amene anachotsedwa koma anabwezeretsedwa ananena kuti: “Ndikusangalala kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake moti amaonetsetsa kuti gulu lake likhalebe loyera. Zimene anthu omwe sali m’gulu la Yehova angaone kuti ndi nkhanza, si nkhanza koma ndi zofunika ndiponso zimasonyeza chikondi.” Kodi mukuganiza kuti mlongo ameneyu akananena zimenezi zikanakhala kuti anthu mu mpingo ndiponso abale ake ankapitirizabe kucheza naye atachotsedwa? Tikamatsatira dongosolo la m’Malemba lokhudza anthu ochotsedwa, timasonyeza kuti timakonda chilungamo. Timasonyezanso kuti timazindikira kuti Yehova ndi woyenera kutiuza makhalidwe amene tiyenera kukhala nawo.

“Danani Nacho Choipa”

20, 21. N’chifukwa chiyani kudana ndi zoipa n’kofunika kwambiri?

20 Mtumwi Petulo anachenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.” Kodi n’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Iye ananena kuti chifukwa “mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) Kodi angameze inuyo? Ngati simukufuna kuti zimenezi zikuchitikireni, muyenera kupitiriza kudana ndi zoipa.

21 Kukhala ndi mtima wodana ndi zinthu zoipa si nkhani yapafupi. Anthufe tinabadwa ochimwa ndipo dziko limene tikukhalamoli limalimbikitsa kuti tizitsatira zilakolako za thupi. (1 Yoh. 2:15-17) Koma kutsanzira Yesu Khristu ndiponso kukonda kwambiri Yehova Mulungu, kungatithandize kuti tizidana ndi zoipa. Choncho tiyeni tiziyesetsa ‘kudana nacho choipa’ ndiponso tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova “amateteza . . . okhulupirika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.”​—Sal. 97:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani imeneyi, werengani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1988, tsamba 26 mpaka 31 komanso Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2002, tsamba 3 mpaka 5.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kudziwa mmene timaonera kumwa mowa?

• Kodi tingachite chiyani kuti tidziteteze ku zinthu zamizimu?

• N’chifukwa chiyani zinthu zolaula ndi zoopsa?

• Munthu amene timamukonda akachotsedwa, kodi tingasonyeze bwanji kuti timadana ndi zoipa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Ngati mumamwa mowa, kodi mufunika kuganizira mfundo ziti?

[Chithunzi patsamba 30]

Samalani ndi zosangalatsa zimene zingakhale ndi zinthu zokhudza kukhulupirira mizimu

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi munthu amene amaonera zolaula ndiye kuti wayamba kukonda chiyani?