Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyeneradi Kuchita Khama?

Kodi Tiyeneradi Kuchita Khama?

Kodi Tiyeneradi Kuchita Khama?

KULAMBIRA KWA PABANJA ndiponso kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kulera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ngati ndinu kholo, mukudziwa kuti ana sachedwa kutopa pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Kodi mungachite chiyani kuti asamatope msanga? Tiyeni tione zimene makolo ena achitapo.

M’bale wina wa ku California ku United States, dzina lake George, anati: “Pamene ana athu anali aang’ono, ine ndi mkazi wanga tinkachita phunziro la Baibulo la banja m’njira zosiyanasiyana kuti likhale losangalatsa. Nthawi zina tonse tinkavala zovala ngati za nthawi ya m’Baibulo, kenako n’kumayerekezera zimene tikuwerenga mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Tinkagwiritsanso ntchito zinthu zimene tinkapanga tokha monga malupanga, ndodo zachifumu ndiponso mabasiketi. Tinkachitanso masewero monga oti wina aganize za munthu winawake m’Baibulo ndipo enafe tinkamufunsa mafunso mpaka titadziwa amene akumuganizirayo. Tinkachita masewera enanso okhala ndi mafunso osiyanasiyana okhudza Baibulo, ena ovutirapo ndi ena osavuta. Komanso tinkafufuza nkhani ngati ya Nowa ndi chingalawa kenako tinkamanga kachingalawa kofanana ndi cha Nowa ndiponso tinkalemba mzere wosonyeza nthawi imene zinthu za m’Baibulo zinachitika. Nthawi zina tinkajambula anthu ena kapena zochitika zinazake za m’Baibulo. Panopa tikukonzekera kuti tijambule zida zauzimu zimene zili pa lemba la Aefeso 6:11-17 ndiponso aliyense adzafotokoza zimene chida chinachake pa lembali chimaimira. Kuchita zinthu ngati zimenezi kwatithandiza kuti tizisangalala ndi phunziro lathu la banja.”

Mlongo wina wa ku Michigan, ku America, dzina lake Debi, anati: “Pa nthawi imene mwana wathu wamkazi anali ndi zaka pafupifupi zitatu, sankachita chidwi pamene ine ndi mwamuna wanga tinkamuphunzitsa. Koma tsiku lina pamene ndinali kumuwerengera nkhani ya Isaki ndi Rabeka mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndinatenga zidole ziwiri n’kumayerekezera kuti zikulankhulana. Ndipo mwanayo anayamba kumvetsera mwachidwi kwambiri. Pa miyezi yotsatira, tinkagwiritsa ntchito zidole ziwirizo poyerekezera anthu osiyanasiyana a m’Baibulo. Tikawerenga nkhani ina m’Baibulo, mwana wathuyo ankafunafuna zidole kapena zinthu zina m’nyumba zimene tinkagwiritsa ntchito poyerekezera nkhaniyo. Ankasangalala kwambiri pofunafuna zinthuzo ndipo ankakhala ngati akusewera. Mwachitsanzo, anapeza bokosi la nsapato kuti likhale nyumba ya Rahabi ndiponso kansalu kofiira kuti kakhale chingwe chofiira. Nthawi ina, tinakulunga chidole cha njoka yaitali mita imodzi ndi hafu ku ndodo ya tsache lalikulu kuti tiyerekezere njoka yamkuwa ya pa lemba la Numeri 21:4-9. Tinkasunga zinthuzi m’chikwama chachikulu. Mwana wathuyo ankakonda kukhala m’chipinda chochezera n’kumafufuza zinthu m’chikwamachi. Tinkasangalala kwambiri kumuona akuchita zimenezi ndiponso akuyerekezera nkhani zina payekha.”

Kulera ana si nkhani yapafupi. Sikuti kungowaphunzitsa kamodzi pa mlungu pa kulambira kwa pabanja n’kokwanira ayi. Tikutero chifukwa pamafunika kuwaphunzitsa nthawi zonse kuti akhale ndi mtima wofuna kutumikira Yehova. Koma kuchita Kulambira kwa Pabanja ndiponso kuphunzira Baibulo mlungu ndi mlungu n’kofunika kwambiri pophunzitsa ana. Mosakayikira, tiyenera kuchitadi khama.