Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kumvera Kuposa Nsembe”

“Kumvera Kuposa Nsembe”

“Kumvera Kuposa Nsembe”

SAULI anali mfumu yoyamba ya Isiraeli. Ngakhale kuti anasankhidwa ndi Mulungu woona, iye anadzakhala wosakhulupirika.

Kodi Sauli analakwitsa chiyani? Kodi zikanatheka kupewa zimene analakwitsazo? Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake?

Yehova Anasankha Mfumu

Sauli asanakhale mfumu, mneneri Samueli ndi amene ankaimira Mulungu mu Isiraeli. Koma kenako Samueli anakalamba ndipo ana ake anali osakhulupirika. Pa nthawi imeneyi mtunduwu unali kuopsezedwa ndi adani awo. Pamene akulu onse a mu Isiraeli anapempha Samueli kuti asankhe mfumu yomwe ingawaweruze ndi kuwatsogolera ku nkhondo, Yehova anauza mneneriyo kuti adzoze Sauli. Yehova anati: “Iye adzapulumutsa anthu anga m’manja mwa Afilisiti.”​—1 Sam. 8:4-7, 20; 9:16.

Sauli anali “mnyamata wokongola.” Koma sikuti anasankhidwa chifukwa cha maonekedwe ake okha. Iye analinso wodzichepetsa. Mwachitsanzo, anafunsa Samueli kuti: “Kodi ine si wa m’fuko la Benjamini, fuko laling’ono kwambiri pa mafuko onse a Isiraeli? Ndipo kodi banja langa sindilo laling’ono kwambiri pa mabanja onse a m’fuko la Benjamini? Ndiye n’chifukwa chiyani mwalankhula mawu otere kwa ine?” Sauli anali wodzichepetsa ngakhale kuti bambo wake, dzina lake Kisi, anali “wachuma kwambiri.”​—1 Sam. 9:1, 2, 21.

Taganiziraninso zimene Sauli anachita Samueli atauza anthu kuti Sauliyo ndi amene Yehova wasankha kukhala mfumu ya Isiraeli. Poyamba Samueli anadzoza Sauli mwamseri ndipo anamuuza kuti: “Uchite chilichonse chimene ungathe, chifukwa Mulungu woona ali ndi iwe.” Kenako mneneriyu anasonkhanitsa anthu kuti awauze mfumu imene Yehova anasankha. Koma Sauli atatchulidwa, sanapezeke. Iye anali atabisala chifukwa cha manyazi. Koma Yehova anaulula pamene anabisala ndipo analengezedwa kuti ndi mfumu.​—1 Sam. 10:7, 20-24.

Ku Nkhondo

Pasanapite nthawi, anthu onse amene anali kumukayikira anazindikira kuti Sauli anali mfumu yabwino kwambiri. Pamene Aamoni ankafuna kulanda mzinda wina wa ku Isiraeli, “mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito” pa Sauli. Iye anasonkhanitsa asilikali a Isiraeli n’kuwatsogolera ku nkhondo ndipo anapambana. Koma Sauli anasonyeza kuti Mulungu ndi amene anawathandiza kupambana. Iye anati: “Yehova watipulumutsa mu Isiraeli.”​—1 Sam. 11:1-13.

Sauli anali ndi makhalidwe abwino ndipo Mulungu anamudalitsa. Iye ankadziwanso kuti zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa chothandizidwa ndi mphamvu ya Yehova. Komabe, panali chinthu chimodzi chofunika kwambiri chimene chikanathandiza Aisiraeli ndi mfumu yawo kuti zinthu zipitirize kuwayendera bwino. Samueli anauza anthu a ku Isiraeli kuti: “Ngati mudzaopa Yehova, n’kumutumikiradi ndi kumvera mawu ake, ndipo ngati simudzapandukira malamulo a Yehova, Yehova Mulungu wanu adzakhala nanu, inuyo pamodzi ndi mfumu yokulamuliraniyo.” Kodi Aisiraeli akanakhala okhulupirika kwa Mulungu zinthu zikanawayendera bwanji? Samueli anati: “Chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.”​—1 Sam. 12:14, 22.

Kuti Mulungu asangalale ndi Aisiraeli, iwo anayenera kumumvera ndipo umu ndi mmene zililinso masiku ano. Atumiki a Yehova akamamumvera iye amawadalitsa. Koma nanga chimachitika n’chiyani ngati samvera Yehova?

“Wachita Chinthu Chopusa”

Patapita nthawi, Afilisti anapsa mtima kwambiri ndi zimene Sauli anachita. Asilikali “ochuluka kwambiri ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja” anabwera kuti adzamenyane ndi Sauli. “Amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zawathina, chifukwa anthu onse anali atapanikizika. Anthuwo anapita kukabisala m’mapanga, m’maenje, kumatanthwe, m’zipinda za pansi ndi m’zitsime zopanda madzi.” (1 Sam. 13:5, 6) Kodi Sauli anachita chiyani?

Samueli anauza Sauli kuti akakumane ku Giligala kumene mneneriyu ankafuna kukapereka nsembe. Sauli anayembekezera koma Samueli anachedwa kubwera ndipo asilikali a Sauli anayamba kubalalika. Choncho Sauli anaganiza zoyamba kupereka yekha nsembezo. Iye atangopereka nsembe, Samueli anafika. Samueli atamva zimene Sauli anachita, anamuuza kuti: “Wachita chinthu chopusa. Sunatsatire lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa. Ukanatsatira lamulo limeneli, Yehova akanalimbitsa ufumu wako pa Isiraeli mpaka kalekale. Tsopano ufumu wako sukhalitsa. Yehova apeza munthu wapamtima pake, ndipo Yehova amuika kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa iwe sunasunge zimene Yehova anakulamula.”​—1 Sam. 10:8; 13:8, 13, 14.

Chifukwa chosowa chikhulupiriro, Sauli modzikweza sanafune kumvera lamulo la Mulungu lakuti adikire Samueli kuti adzapereke nsembe. Zimene Sauli anachitazi zinali zosiyana kwambiri ndi zimene Gideoni, yemwe anali mtsogoleri wa asilikali a Isiraeli, anachita. Yehova analamula Gideoni kuti achepetse gulu lake la asilikali kuchoka pa 32,000 kufika pa 300, ndipo iye anamvera. N’chifukwa chiyani anamvera? Chifukwa chakuti ankakhulupirira Yehova. Mulungu anamuthandiza kugonjetsa asilikali okwana 135,000. (Ower. 7:1-7, 17-22; 8:10) Yehova akanathandizanso Sauli koma chifukwa cha kusamvera kwake, Afilisiti analanda katundu wa Isiraeli.​—1 Sam. 13:17, 18.

Nanga ife tikakumana ndi mavuto timasankha bwanji zochita? Anthu opanda chikhulupiriro angaone kuti ndi bwino kunyalanyaza mfundo za Mulungu. N’kutheka kuti Sauli anaganiza kuti zimene iye anachita Samueli atachedwa zinali zanzeru. Koma anthu amene amafuna kusangalatsa Yehova amaona kuti kutsatira mfundo za m’Malemba n’kwanzeru.

Yehova Anakana Sauli

Pa nthawi imene Aisiraeli anali kumenyana ndi Aamaleki, Sauli anachimwanso. Mulungu ankadana ndi anthu a ku Amaleki omwe anaukira Aisiraeli popanda chifukwa, Aisiraeliwo atangochoka ku Iguputo. (Eks. 17:8; Deut. 25:17, 18) Aamaleki anagwirizananso ndi anthu a mitundu ina pomenyana ndi anthu osankhidwa a Mulungu pa nthawi ya Oweruza. (Ower. 3:12, 13; 6:1-3, 33) Choncho Yehova analamula Sauli kuti akawononge Aamalekiwo.​—1 Sam. 15:1-3.

M’malo momvera lamulo la Yehova loti akaphe Aamaleki onse ndiponso kuti akawononge katundu wawo, Sauli anangogwira mfumu yawo komanso sanaphe ziweto zawo zabwino. Kodi Sauli anayankha bwanji Samueli atamufunsa za nkhaniyi? Sauli ananena kuti anthu ena ndi amene anachititsa zimenezi. Iye anati: “[Anthuwa] sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambirizi n’cholinga chofuna kuzipereka nsembe kwa Yehova.” Kaya Sauli ankafunadi kupereka nsembe nyamazo kapena ayi, iye sanamvere Mulungu. Sauli ‘sanali kudzionanso ngati mwana.’ N’chifukwa chake mneneri wa Mulungu anauza Sauli kuti sanamvere Mulungu. Kenako Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera kuposa nsembe . . . Popeza iwe wakana mawu a Yehova, iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”​—1 Sam. 15:15, 17, 22, 23.

Yehova atamuchotsera Sauli mzimu woyera n’kusiyanso kumudalitsa, mfumu yoyamba ya Isiraeli imeneyi inayamba kukhala ndi “maganizo oipa.” Sauli anayamba kukayikira ndiponso kuchitira nsanje Davide, munthu amene Yehova anadzamupatsa ufumu. Baibulo limanena kuti Sauli ataona kuti “Yehova ali ndi Davide, . . . anali kudana ndi Davide nthawi zonse.” Choncho Sauli anayesa kupha Davide maulendo angapo. Iye anali kusakasaka Davide ndipo analamulanso kuti ansembe okwana 85 pamodzi ndi anthu ena aphedwe. M’pake kuti Yehova anakana Sauli.​—1 Sam. 16:14; 18:11, 25, 28, 29; 19:10, 11; 20:32, 33; 22:16-19.

Afilisiti ataukiranso Aisiraeli, Sauli anapita kukafunsira kwa wamizimu poganiza kuti athandizidwa. Tsiku lotsatira, anavulazidwa kwambiri ku nkhondo ndipo anadzipha. (1 Sam. 28:4-8; 31:3, 4) Pofotokoza za mfumu ya Isiraeli yosamverayi, Malemba amati: “Sauli anafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake popeza anachita zosakhulupirika kwa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu. Sauli sanafunse kwa Yehova.”​—1 Mbiri 10:13, 14.

Zimene zinachitikira Saulizi zimasonyeza kuti kumvera Yehova n’kofunika kwambiri kuposa nsembe iliyonse imene tingapereke. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yoh. 5:3) Choncho tisaiwale mfundo yofunika kwambiri yakuti tingakhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu ngati timamumvera.

[Chithunzi patsamba 21]

Poyamba Sauli anali mtsogoleri wodzichepetsa

[Chithunzi patsamba 23]

N’chifukwa chiyani Samueli anauza Sauli kuti “kumvera kuposa nsembe”?