Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani Mose anakwiyira ana a Aroni, Eleazara ndi Itamara, abale awo Nadabu ndi Abihu atafa, ndipo kodi chinamukhazika mtima pansi n’chiyani?—Lev. 10:16-20.
Atangokhazikitsa kumene dongosolo la ansembe Yehova anapha Nadabu ndi Abihu, omwe anali ana a Aroni, chifukwa chopereka kwa Mulungu zofukiza pamoto wosaloledwa. (Lev. 10:1, 2) Mose anauza ana a Aroni amene anatsala kuti asalire maliro a abale awo. Pasanapite nthawi yaitali, Mose anakwiyira Eleazara ndi Itamara chifukwa chakuti sanadye mbuzi imene inaperekedwa monga nsembe ya machimo. (Lev. 9:3) N’chifukwa chiyani Mose anakwiya?
Malamulo amene Yehova anapereka kwa Mose anatchula mwachindunji kuti wansembe amene wapereka nsembe ya machimo ankayenera kudyako nsembeyo ali m’bwalo la chihema chokumanako. Akachita zimenezi ankaona kuti akunyamula kapena kuti kuchotsa machimo a anthu amene apereka nsembeyo. Koma sankafunika kudya nsembe ngati ena mwa magazi a nsembeyo awatenga n’kupita nawo ku Malo Oyera, omwe anali chipinda choyamba cha malo opatulika. Ndipo nyama ya nsembe imeneyi ankaitentha ndi moto.—Lev. 6:24-26, 30.
Zikuoneka kuti nkhani yomvetsa chisoniyi itachitika, Mose anaona kuti m’pofunika kuonetsetsa kuti malamulo onse a Yehova atsatiridwa bwinobwino. Atazindikira kuti mbuzi imene inaperekedwa monga nsembe ya machimo yatenthedwa, iye anakwiya. Kenako anafunsa Eleazara ndi Itamara chifukwa chimene iwo sanadyere mbuziyo, popeza magazi a mbuziyi sanaperekedwe kwa Yehova m’Malo Oyera. Izi zinali zosemphana ndi malangizo amene anapatsidwa.—Lev. 10:17, 18.
Aroni anayankha funso la Mose chifukwa chakuti Aroniyo ndi amene analoleza kuti ansembewo achite zimenezo. Poganizira za imfa ya ana ake awiriwo, mwina Aroni anakayikira zoti pangakhale wansembe wina yemwe chikumbumtima chake chingamulole kudya nsembe ya uchimo pa tsikulo. Mwina iye anaganiza kuti Yehova sangasangalale iwo akadya nsembeyo ngakhale kuti tchimo la Nadabu ndi Abihu silinkawakhudza.—Lev. 10:19.
N’kutheka kuti Aroni anaganiza kuti makamaka pa tsiku limene anthu a m’banja lake anayamba kutumikira ngati ansembe anafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. Anafunika kuchita zimenezi ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono n’cholinga choti asangalatse Mulungu. Koma dzina la Yehova linadetsedwa ndi Nadabu ndi Abihu ndipo mkwiyo wa Mulungu unawayakira. Choncho mwina Aroni anaganiza kuti popeza anthu a m’banja lake la ansembe anali atachimwa, abale awo si oyenerera kudya chopereka chopatulika.
Zikuoneka kuti Mose anamvetsa zimene m’bale wakeyu ananena chifukwa chakuti nkhaniyi imatha ndi mawu akuti: “Mose atamva zimenezi, zinam’khutiritsa.” (Lev. 10:20) Nayenso Yehova ayenera kuti anakhutiritsidwa ndi yankho limene Aroni anapereka.