Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse

Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse

Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse

“Umakonda chilungamo.”​—SAL. 45:7.

1. Kodi n’chiyani chingatithandize kuyenda “m’tinjira tachilungamo”?

YEHOVA akutsogolera anthu ake “m’tinjira tachilungamo” kudzera m’Mawu ake ndiponso mwa mzimu wake woyera. (Sal. 23:3) Komabe popeza anthufe ndife opanda ungwiro, nthawi zina timachoka panjira yachilungamo. Zikatere pamafunika khama kuti tiyambirenso kuchita zinthu zabwino. Kodi chingatithandize n’chiyani? Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukonda kuchita zinthu zolungama.​Werengani Salimo 45:7.

2. Kodi “tinjira tachilungamo” n’chiyani?

2 Kodi palembali “tinjira tachilungamo” n’chiyani? “Tinjira” timeneti ndi moyo umene munthu amakhala chifukwa chotsatira mfundo zolungama za Yehova. Mawu achiheberi ndiponso achigiriki amene amamasuliridwa kuti “chilungamo” amatanthauza “kuwongoka” potsatira kwambiri makhalidwe abwino. Popeza Yehova ndi “malo okhalamo chilungamo,” anthu amene amamulambira amadalira iyeyo kuti awauze njira za makhalidwe abwino zimene iwowo ayenera kutsatira.​—Yer. 50:7.

3. Kodi tingaphunzire bwanji zambiri zokhudza chilungamo cha Mulungu?

3 Kuti tikondweretsedi Mulungu, tiyenera kuyesetsa ndi mtima wathu wonse kutsatira zimene iye amaona kuti ndi zolungama. (Deut. 32:4) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira zambiri za Yehova Mulungu kuchokera m’Mawu ake, Baibulo. Tikamaphunzira zambiri za Mulungu ndiponso kumuyandikira tsiku lililonse, m’pamenenso timakonda kwambiri chilungamo chake. (Yak. 4:8) Komanso tikamasankha zinthu zofunika pa moyo wathu, tiyenera kulola kuti Mawu ouziridwa a Mulungu azititsogolera.

Muzifunafuna Chilungamo cha Mulungu

4. Kodi tingafunefune bwanji chilungamo cha Mulungu?

4 Werengani Mateyu 6:33. Tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu timasonyeza kuti tikufunafuna chilungamo cha Mulungu. Komabe pali zinanso zimene tiyenera kuchita. Kuti Yehova azisangalala ndi utumiki wathu wopatulika, tiyenera kukhala ndi makhalidwe amene iye amaona kuti ndi abwino. Kodi anthu onse amene akufunafuna chilungamo cha Yehova ayenera kuchita chiyani? Ayenera “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.”​—Aef. 4:24.

5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisafooke?

5 Tikamayesetsa kutsatira mfundo zolungama za Mulungu, nthawi zina tingakhumudwe n’kufooka chifukwa cha zolakwa zathu. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisafooke koma tizikonda ndiponso kuchita chilungamo? (Miy. 24:10) Tiyenera kupemphera kwa Yehova nthawi zonse ‘ndi mitima yoona. Tizichita zimenezi tilibe chikayikiro chilichonse komanso tili ndi chikhulupiriro.’ (Aheb 10:19-22) Kaya ndife odzozedwa kapena tikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, timakhulupirira dipo la nsembe ya Yesu Khristu. Timakhulupiriranso kuti iye ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba. (Aroma 5:8; Aheb. 4:14-16) M’magazini yoyamba ya Nsanja ya Olonda munali chitsanzo chosonyeza kuti magazi a Yesu ndi amphamvu kwambiri ndipo angatiyeretsedi. (1 Yoh. 1:6, 7) Magaziniyo inati: “Mukakhala pamalo owala, n’kumayang’ana chinthu chofiira kudzera pagalasi lofiiranso, chinthucho chimaoneka choyera. N’chimodzimodzinso ndi machimo athu. Ngakhale atakhala ofiira kwambiri, Mulungu akawaona pogwiritsa ntchito magazi a Khristu, machimo athuwo amaoneka oyera. Ifenso tiyenera kuwaona mmene Mulungu akuwaonera.” (July 1879, tsamba 6) Ndiyetu n’zoonekeratu kuti Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali kwambiri pamene anapereka dipo la nsembe ya Mwana wake wokondedwa.​—Yes. 1:18.

Nthawi Zonse Muzivala Zida Zauzimu

6. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuvala zida zonse zauzimu nthawi zonse?

6 Nthawi zonse tifunika kuvala “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo” chifukwa ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pa zida zathu zauzimu zankhondo zochokera kwa Mulungu. (Aef. 6:11, 14) Kaya tangodzipereka kumene kwa Yehova kapena takhala tikumutumikira kwa zaka zambiri, timafunika kuonetsetsa kuti tsiku ndi tsiku tavala zida zonse zauzimu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Mdyerekezi ndi ziwanda zake anaponyedwa padziko lapansili. (Chiv. 12:7-12) Satana wakwiya kwambiri ndipo akudziwa kuti watsala ndi nthawi yochepa. Choncho iye akuukira anthu a Mulungu kwambiri kuposa kale. Kodi tsopano tikuona kufunika kovala “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo”?

7. Kodi tidzachita chiyani ngati timamvetsa kufunika kwa “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo”?

7 Chotetezera pachifuwa chimateteza mtima weniweni. Chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro, mtima wathu wophiphiritsa ndi wonyenga ndipo ungatichititse china chilichonse choipa. (Yer. 17:9) Ndiye popeza mtima wathu umafuna kuchita zinthu zoipa, n’kofunika kuti tiziuphunzitsa kuchita zabwino. (Gen. 8:21) Ngati timaona kufunika kwa “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo” sitidzachivula ngakhale kwa kanthawi kochepa pochita zosangalatsa zimene Mulungu amadana nazo. Komanso sitidzaganizira ndiponso kulakalaka kuchita zinthu zoipa. Sitidzawononga nthawi yambiri tikuonera TV. Koma tidzapitirizabe kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingakondweretse Yehova. Ngakhale titagwa kwa nthawi yochepa mwa kuganiza ndiponso kuchita zinthu zosalungama, tikhoza kudzukanso titathandizidwa ndi Yehova.​—Werengani Miyambo 24:16.

8. N’chifukwa chiyani tikufunika “chishango chachikulu chachikhulupiriro”?

8 Chida china chauzimu ndicho “chishango chachikulu chachikhulupiriro.” Chimatithandiza “kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.” (Aef. 6:16) Ndiyeno chikhulupiriro ndiponso kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse zimatithandiza kuchita chilungamo komanso kuyendabe panjira yopita ku moyo wosatha. Tikamakonda kwambiri Yehova m’pamenenso timaona kuti chilungamo chake n’chofunika kwambiri. Nanga kodi chikumbumtima chathu chingatithandize bwanji kuti tizikonda chilungamo?

Pitirizani Kukhala ndi Chikumbumtima Chabwino

9. Kodi kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino kungatithandize bwanji?

9 Pamene tinabatizidwa tinapempha Yehova kuti atipatse “chikumbumtima chabwino.” (1 Pet. 3:21) Popeza kuti timakhulupirira dipo, magazi a Yesu amaphimba machimo athu ndipo timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Komabe kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu tiyenera kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino. Chikumbumtima chathu chikamatitsutsa kapena kutichenjeza tiyenera kuyamikira kuti chikugwira bwino ntchito. Zimenezi zimasonyeza kuti chikumbumtima chathu si chakufa pa nkhani yokhudza njira zolungama za Yehova. (1 Tim. 4:2) Koma pali njira inanso imene chikumbumtima chingathandizire anthu amene amafuna kukonda chilungamo.

10, 11. (a) Fotokozani chitsanzo chosonyeza kufunika komvera chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo. (b) N’chifukwa chiyani kukonda chilungamo kungatithandize kukhala osangalala kwambiri?

10 Ngati titachita zinthu zoipa, chikumbumtima chathu chikhoza kutitsutsa kapena kutivutitsa. Mwachitsanzo, pa nthawi ina mnyamata wina anasiya kuyenda “m’tinjira tachilungamo.” Iye anayamba kukonda kwambiri zinthu zolaula ndiponso kusuta chamba. Akapita ku misonkhano chikumbumtima chake chinkamuvutitsa ndipo akakhala mu utumiki ankadziona kuti ndi munthu wachinyengo. Choncho anasiya kusonkhana ndiponso kulalikira. Iye anati, “Koma sindinkadziwa kuti zimenezi zichititsa kuti chikumbumtima changa chizindivutitsa kwambiri.” Kenako anati, “Ndinakhala moyo wopusawu kwa zaka zinayi.” Patapita nthawi anayamba kuganiza zobwerera m’choonadi. Iye ankaganiza kuti Yehova sangamve pemphero lake, koma anapempherabe kuti amukhululukire. Pasanathe mphindi 10, mayi ake anabwera kudzamuona ndipo anamulimbikitsa kuti ayambenso kusonkhana. Iye anapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo anapempha mkulu wina kuti aziphunzira naye. Patapita nthawi anabatizidwa ndipo amathokoza Yehova chifukwa chomuthandiza.

11 Kodi si zoona kuti anthufe timakhala osangalala tikamachita zinthu zachilungamo? Tikamakonda ndiponso kuchita chilungamo nthawi zonse, timakhala osangalala kwambiri chifukwa chodziwa kuti tikusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Musaiwale kuti idzafika nthawi pamene anthu onse adzakhala osangalala nthawi zonse chifukwa chokhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo adzasonyeza bwinobwino kuti analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Choncho, tiyeni panopa tizikonda kwambiri chilungamo kuchokera pansi pa mtima ndi kusangalatsa Yehova.​—Miy. 23:15, 16.

12, 13. Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu?

12 Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu? Tikamaphunzira Malemba ndiponso mabuku athu ophunzitsa Baibulo tifunika kukumbukira kuti “mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” (Miy. 15:28) Taganizirani mmene kuchita zimenezi kungatithandizire pa nkhani yokhudza ntchito imene tiyenera kugwira. Ngati ntchito inayake ikuonekeratu kuti ndi yosemphana ndi zimene Malemba amanena, ambirife sizitivuta kutsatira malangizo amene timalandira kudzera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Koma pamene sitikudziwa bwinobwino ngati ntchito imene tikufuna kugwira ndi yogwirizana ndi Malemba kapena ayi, tiyenera kupemphera ndiponso kuganizira mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kusankha bwino pa nkhaniyo. * Mfundo ina imene tiyenera kuiganizira ndi yakuti ndi bwino kupewa kukhumudwitsa chikumbumtima cha ena. (1 Akor. 10:31-33) Koma mfundo zofunika kwambiri zimene tiyenera kuganizira ndi zimene zimakhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu. Ngati Yehova ndi weniweni kwa ife, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikagwira ntchito imeneyi ndidzakhumudwitsa Yehova ndi kumumvetsa chisoni?’​—Sal. 78:40, 41.

13 Tikamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo, tiyenera kukumbukira kuti ndi bwino kusinkhasinkha mfundo zimene zili m’nkhaniyo. Kodi timakonda kumangolemba mizere kunsi kwa mayankho kenako n’kupita pandime ina? Kuphunzira mwa njira imeneyi sikungatithandize kwenikweni kukonda kwambiri chilungamo kapena kukhala ndi chikumbumtima chothandiza. Ngati tikufuna kuti tizikonda kwambiri chilungamo tiyenera kuphunzira mwakhama ndiponso kusinkhasinkha zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu. Pamafunikadi khama kuti tizikonda chilungamo ndi mtima wathu wonse.

Tizimva Njala ndi Ludzu la Chilungamo

14. Kodi Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu amafuna kuti tizimva bwanji tikamachita utumiki wathu womwe ndi wopatulika?

14 Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu amafuna kuti tizichita utumiki wathu mosangalala. Kodi tingatani kuti tizisangalala? Tiyenera kukonda chilungamo. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anati: “Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta.” (Mat. 5:6) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani kwa anthu amene akufuna kukonda chilungamo?

15, 16. Kodi njala ndiponso ludzu lauzimu zidzatha bwanji?

15 M’dziko lomwe tikukhalali wolamulira wake ndi woipa. (1 Yoh. 5:19) Tikawerenga nyuzipepala m’dziko lililonse, timamva za zinthu zoipa ndiponso zachiwawa zambirimbiri zimene zikuchitika. Anthu amene amakonda chilungamo amavutika maganizo kwambiri akaona anthu akuchitirana nkhanza. (Mlal. 8:9) Anthu amene timakonda Yehovafe, timadziwa kuti iye yekha ndi amene angathetse njala ndiponso ludzu lauzimu la anthu amene amafuna kuphunzira kuchita chilungamo. Anthu osakonda Mulungu adzawonongedwa ndipo amene amakonda chilungamo sadzavutikanso ndi anthu ophwanya malamulo. (2 Pet. 2:7, 8) Zimenezi zikadzachitika, anthu okonda chilungamo adzakhala pa mtendere.

16 Atumiki a Yehovafe, amenenso tikutsatira Yesu Khristu, timadziwa kuti onse amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo “adzakhuta.” Zimenezi zidzachitika Mulungu akakwaniritsa malonjezo ake okhudza kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene “mudzakhala chilungamo.” (2 Pet. 3:13) Choncho tisamafooke kapena kudabwa tikaona kuti m’dziko la Satanali mulibe chilungamo chifukwa chakuti anthu akuponderezana ndiponso akuchita zachiwawa. (Mlal. 5:8) Yehova Wamwambamwamba akudziwa zimene zikuchitika ndipo posachedwapa adzapulumutsa anthu okonda chilungamo.

Zinthu Zimatiyendera Bwino Tikamakonda Chilungamo

17. Tchulani madalitso amene timapeza chifukwa chokonda chilungamo.

17 Lemba la Salimo 146:8 limanena za madalitso amene timapeza tikamayenda panjira ya chilungamo. Palembali wamasalimo anaimba kuti: “Yehova amakonda anthu olungama.” Taganizirani mfundo imeneyi. Ambuye wa chilengedwe chonse amatikonda chifukwa timakonda chilungamo. Popeza Yehova amatikonda, ndife otsimikiza kuti adzatisamalira tikamaika zinthu za Ufumu patsogolo. (Werengani Salimo 37:25; Miyambo 10:3.) Kutsogoloku, padziko lonse lapansili padzakhala anthu okonda chilungamo okhaokha. (Miy. 13:22) Anthu a Mulungu ambiri adzakhala ndi moyo wosangalala ndiponso wosatha padziko lapansi lokongola kwambiri la paradaiso. Iwo adzalandira madalitso amenewa chifukwa chakuti amachita chilungamo. Koma ngakhale panopa, anthu amene amakonda chilungamo cha Mulungu akulandira madalitso. Iwo ali ndi mtendere wa mumtima ndipo zimenezi zimathandiza kuti azikhala mogwirizana m’banja ndiponso mu mpingo.​—Afil. 4:6, 7.

18. Kodi tizichita zinthu zabwino ziti pamene tikudikira tsiku la Yehova?

18 Pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova, tiyenera kupitirizabe kufunafuna chilungamo chake. (Zef. 2:2, 3) Choncho tiyeni tizikonda njira zolungama za Yehova Mulungu kuchokera pansi pa mtima. Kuti tichite zimenezi timafunika nthawi zonse kuvala “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo.” Izi zingatithandize kuteteza mtima wathu wophiphiritsa. Tiyeneranso kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino chimene chingatithandize kukhala osangalala komanso kukondweretsa mtima wa Mulungu.​—Miy. 27:11.

19. Kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani, ndipo tidzakambirana zotani m’nkhani yotsatira?

19 “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mawu amenewa ndi olimbikitsatu kwambiri kwa ifeyo pamene tikuyesetsa kuchita zabwino m’dzikoli lomwe muli chiwawa, kuipa ndiponso mavuto ena. N’zoona kuti anthu otalikirana ndi Mulungu sangamvetse chifukwa chake ifeyo timayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Koma zinthu zimatiyendera bwino chifukwa chotsatira chilungamo cha Yehova. (Yes. 48:17; 1 Pet. 4:4) Choncho tiyeni tipitirizebe kusangalala mwa kukonda ndiponso kuchita chilungamo ndi mtima wathunthu. Koma kukhala ndi mtima wathunthu potumikira Yehova kumafunanso kuti tizidana ndi kusamvera malamulo. M’nkhani yotsatira tidzakambirana tanthauzo la zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri zimene Baibulo limanena poyankha mafunso okhudza nkhani ya ntchito, werengani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999, tsamba 28 mpaka 30.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kuzindikira kufunika kwa dipo kungatithandize bwanji kuti tizikonda chilungamo?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo”?

• Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chimatithandiza kusankha bwino pa nkhani za ntchito