Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu

Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu

Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu

“Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova, ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.”​—SAL. 33:6.

1, 2. (a) Kodi zimene anthu akudziwa zokhudza zinthu zakuthambo ndi zapadziko lapansi zawonjezeka bwanji? (b) Kodi tifunika kuyankha funso liti?

ZAKA zoposa 100 zapitazo, asayansi ambiri ankaganiza kuti m’chilengedwechi muli mlalang’amba umodzi wokha wotchedwa Milky Way. Komatu kumeneku kunali kulakwitsa kwambiri. Panopa anthu apeza kuti m’chilengedwechi muli milalang’amba yoposa 100 biliyoni ndipo ina ili ndi nyenyezi mabiliyoni ambirimbiri. Masiku ano anthu akugwiritsa ntchito zipangizo zamphamvu kwambiri zoonera zinthu zakuthambo ndipo chifukwa cha zimenezi akutulukira milalang’amba inanso.

2 Pa nthawi imeneyo, anthu sankadziwa zambiri pa nkhani ya zinthu zakuthambo komanso zokhudza dzikoli. N’zoona kuti zimene ankadziwa pa nthawiyo zinali zambiri tikayerekezera ndi zimene anthu ankadziwa nthawiyi isanafike. Koma masiku ano anthu akudziwa bwino za kukongola ndi kudabwitsa kwa zamoyo ndiponso mmene dziko limathandizira kuti zinthuzo zikhalebe ndi moyo. N’zosakayikitsa kuti zaka zikubwerazi tiphunziranso zinthu zambiri za m’dzikoli ndi zakuthambo. Koma ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi zinthu zonsezi zinakhalako bwanji? Yankho la funso limeneli tingalidziwe chifukwa chakuti Mlengi watiululira m’Malemba Opatulika.

Chilengedwe N’chodabwitsa

3, 4.  Kodi Mulungu analenga bwanji chilengedwechi ndipo kodi zimene analenga zimamupatsa bwanji ulemerero?

3 Mawu oyamba a m’Baibulo amafotokoza zimene zinachitika kuti chilengedwechi chikhalepo. Mawuwo amati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Gen. 1:1) Poyamba panalibe chinthu china chilichonse ndipo Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, kuti alenge zinthu zakumwamba, dziko lapansi ndiponso zinthu zonse m’chilengedwechi. Anthu aluso amagwiritsa ntchito manja ndi zipangizo kuti apange zinthu, koma Mulungu akafuna kugwira ntchito zodabwitsa amagwiritsa ntchito mzimu woyera.

4 Malemba amanena mophiphiritsira kuti mzimu woyera ndi “chala” cha Mulungu. (Luka 11:20; Mat. 12:28) Ndipo “ntchito za manja ake,” kapena kuti zinthu zimene Yehova analenga pogwiritsa ntchito mzimu woyera, zimam’patsa ulemerero waukulu. Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.” (Sal. 19:1) Kunena zoona chilengedwechi chimasonyeza kuti mzimu woyera wa Mulungu ndi wamphamvu kwambiri. (Aroma 1:20) Kodi chimasonyeza bwanji zimenezi?

Mulungu Ali ndi Mphamvu Zopanda Malire

5. Perekani chitsanzo cha m’chilengedwe chosonyeza kuti mzimu woyera wa Yehova ndi wamphamvu.

5 Chilengedwe chachikulu kwambirichi chimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire. (Werengani Yesaya 40:26.) Tangoganizirani za dzuwa. Dzuwa, lomwe lili m’gulu la nyenyezi, lili pamtunda wa makilomita oposa 150 biliyoni kuchokera padzikoli ndipo ndi lotentha pafupifupi madigiri seshasi 15 miliyoni. Ngakhale kuti ndi lotentha chonchi, mtundawu ndi wabwino kwambiri moti izi zimathandiza kuti zamoyo zikhalebe ndi moyo padzikoli. N’zosachita kufunsa kuti panafunika mphamvu zambiri kuti dzuwa ndiponso nyenyezi zina mabiliyoni ambirimbiri zilengedwe. Yehova ali ndi mphamvu zotha kuchita zonsezi.

6, 7. (a) Perekani umboni wosonyeza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera mwadongosolo. (b) N’chiyani chikusonyeza kuti chilengedwechi sichinangokhalapo chokha?

6 Pali maumboni ambirimbiri osonyeza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera mwadongosolo kwambiri polenga zinthu. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti muli ndi timipira tamitundu yosiyanasiyana m’bokosi linalake. Kenako mukukhutchumula bokosilo kuti mipirayo isakanikirane, n’kukhuthulira pansi mipira yonseyo nthawi imodzi. Kodi zingatheke kuti mipira ya mitundu yofanana ipezeka pamalo amodzi, mwina ya buluu payokha, yachikasu payokha? Sizingatheke. Nthawi zonse zinthu zimene zimangochitika pa zokha sizichitika mwadongosolo, ndipo imeneyi ndi mfundo yosatsutsika m’chilengedwechi.

7 Koma kodi tikayang’ana m’mwamba pogwiritsa ntchito zipangizo zoonera zinthu zakuthambo tikhoza kuona chiyani? Titha kuona zinthu zambiri zosanjidwa bwino monga milalang’amba, nyenyezi ndiponso mapulaneti. Zonsezi zimayenda mwadongosolo kwambiri. N’zosatheka kuti zinthu zimenezi zinangokhalapo pazokha, popanda winawake wozisanja bwinobwino. Ndiyeno tingafunse kuti, Kodi pachiyambipo ndi mphamvu iti imene inagwiritsidwa ntchito polenga zinthu mwadongosolo chonchi? Sitingadziwe bwino za mphamvu imene inagwiritsidwa ntchito polenga zinthu mwa kungophunzira zimene asayansi amaona kapena kutulukira. Koma Baibulo limasonyeza kuti mzimu woyera wa Mulungu ndi umene unagwiritsidwa ntchito ndipo ndi wamphamvu kuposa mphamvu ina iliyonse m’chilengedwechi. Wamasalimo anaimba kuti: “Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova, ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.” (Sal. 33:6) Tikayang’ana kumwamba usiku popanda zipangizo zoonera kuthambo, timangoona kambali kochepa chabe ka “makamu” a nyenyezi amenewa.

Ntchito ya Mzimu Woyera Polenga Dziko

8. Pa zinthu zimene Yehova analenga, kodi timadziwa zochuluka bwanji?

8 Zinthu za m’chilengedwe zimene tikuzidziwa panopa n’zochepa kwambiri tikayerekezera ndi zimene sitikuzidziwa. Potsimikizira mfundo imeneyi, munthu wokhulupirika Yobu ananena kuti: “Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake, ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Patapita zaka zambirimbiri, Mfumu Solomo amene ankayang’anitsitsa mwachidwi zimene Yehova analenga, ananena kuti: “Chilichonse [Mulungu] anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.”​—Mlal. 3:11; 8:17.

9, 10. Kodi Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu iti polenga dzikoli ndipo ndi zinthu ziti zimene zinachitika pa masiku atatu oyambirira olenga zinthu?

9 Koma Yehova wafotokoza mfundo zofunika kwambiri pa nkhani ya zinthu zimene analenga. Mwachitsanzo, Malemba amatiuza kuti mzimu wa Mulungu unali kugwira ntchito padzikoli zaka zosawerengeka m’mbuyomu. (Werengani Genesis 1:2.) Pa nthawi imeneyi kunalibe mtunda, kuwala ndiponso mpweya woti anthu angapume.

10 Baibulo limafotokozanso zimene Mulungu anachita pa masiku a kulenga zinthu. Awatu sanali masiku enieni a maola 24 koma nyengo yaitali ndithu. Pa tsiku loyamba, Yehova anachititsa kuti kuwala kuonekere padziko lapansi. Kuwalaku kunakwanira bwinobwino pamene dzuwa ndi mwezi zinayamba kuonekera padzikoli. (Gen. 1:3, 14) Pa tsiku lachiwiri, Mulungu anapanga mlengalenga. (Gen. 1:6) Ndiyeno padzikoli panali madzi, kuwala ndi mpweya koma panalibe mtunda. Chakumayambiriro kwa tsiku lachitatu la kulenga, Yehova anapanga mtunda pogwiritsa ntchito mzimu woyera. Kuti zimenezi zitheke, mwina iye anachititsa kuti mphamvu za m’chilengedwe za pansi pa nthaka zichititse kuti madzi asiyane ndi mtunda. (Gen. 1:9) Koma panalinso zinthu zina zogometsa zimene zinalengedwa pa tsiku lachitatuli kapena pa nyengo zina zolenga zinthu.

Ntchito ya Mzimu Woyera Polenga Zamoyo

11. Kodi zinthu zamoyo zokongola ndiponso zodabwitsa zimene zili m’chilengedwechi zimasonyeza chiyani?

11 Mzimu wa Mulungu unagwiranso ntchito zina mwadongosolo kwambiri polenga zinthu zamoyo. Kudzera mwa mzimu woyera, Mulungu analenga zomera ndi zinyama zosiyanasiyana zodabwitsa kuchokera pa tsiku lachitatu lolenga zinthu mpaka tsiku la 6. (Gen. 1:11, 20-25) Choncho zinthu zamoyo, zomwe ndi zokongola, zodabwitsa ndiponso zosanjidwa mwadongosolo, zimasonyeza kuti pali winawake wanzeru kwambiri amene anazilenga.

12. (a) Kodi DNA imagwira ntchito yotani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zimachitika chifukwa cha ntchito imene DNA imagwira?

12 Taganizaninso za DNA yomwe imakhala ndi malangizo othandiza kuti mwana azibadwa ndi maonekedwe a makolo ake. Zamoyo zonse padziko lapansi, kuphatikizapo tizilombo tosaoneka ndi maso, udzu, njovu, anangumi ndiponso anthu, zili ndi DNA. Ngakhale kuti zinthu zimene zimapezeka padzikoli ndi zosiyanasiyana, DNA ya zonsezi ndi imene imachititsa kuti zinthu zimene zili m’gulu limodzi zisasinthe n’kufanana ndi zinthu za m’gulu lina. Choncho mogwirizana ndi cholinga cha Yehova Mulungu, zinthu zamoyo zimapitiriza kuchita zinthu mmene Mulungu anazilengera. (Sal. 139:16) Dongosolo limeneli limasonyezanso kuti “chala” cha Mulungu, kapena kuti mzimu woyera, ndi umene unagwira ntchito polenga zinthu.

Cholengedwa Chapadera Padziko Lapansi

13. Kodi Mulungu analenga bwanji munthu?

13 Patapita zaka zambiri ndiponso Mulungu atalenga zinthu zamoyo ndi zopanda moyo, dzikoli silinalinso “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu.” Koma pa nthawiyi, Yehova anali asanamalize kugwiritsa ntchito mzimu wake polenga zinthu. Anali atatsala pang’ono kulenga chinthu chapadera kwambiri padziko lapansi. Chakumapeto kwa tsiku la 6 lolenga zinthu, Mulungu analenga munthu. Kodi anamulenga bwanji? Iye anagwiritsa ntchito mzimu woyera ndi zinthu za m’nthaka.​—Gen. 2:7.

14. Kodi anthu ndi osiyana kwambiri ndi nyama m’njira yapadera iti?

14 Pa Genesis 1:27 pali mawu akuti: “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.” Mawu akuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu amatanthauza kuti Yehova anatilenga m’njira yakuti tingathe kusonyeza chikondi, kusankha tokha zochita ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wathu. Choncho ubongo wathu ndi wosiyana kwambiri ndi wa nyama. Yehova analenga ubongo wa munthu makamaka n’cholinga choti tizitha kuphunzira mosangalala za iyeyo ndiponso ntchito zake mpaka kalekale.

15. Kodi Adamu ndi Hava anali ndi tsogolo lotani?

15 Pa chiyambi, Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava dziko lapansi ndi zinthu zonse zochititsa chidwi zopezeka m’dzikoli kuti aziphunzire n’kumasangalala nazo. (Gen. 1:28) Yehova anawapatsa chakudya chamwanaalirenji ndiponso paradaiso wokongola woti azikhalamo. Iwo anali ndi mwayi wokhala ndi moyo kosatha ndiponso wokhala makolo okondedwa a ana angwiro mabiliyoni ambirimbiri. Koma zinthu zinasokonekera.

Kuzindikira Ntchito ya Mzimu Woyera

16. Kodi tili ndi chiyembekezo chotani ngakhale kuti anthu awiri oyambirira anapandukira Mulungu?

16 M’malo moyamikira ndiponso kumvera Mlengi wawo, Adamu ndi Hava anachita zinthu modzikonda ndipo anapandukira Yehova. Izi zachititsa kuti ana awo, amene ndi anthu onse opanda ungwiro, azivutika. Koma Baibulo limafotokoza mmene Mulungu adzachotsere mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kuchimwa kwa makolo athu oyambawa. Malemba amasonyezanso kuti Yehova adzakwaniritsa cholinga chimene anali nacho poyamba. Dzikoli lidzakhala paradaiso moti anthu onse m’dzikolo adzakhala osangalala, athanzi ndipo sadzafanso. (Gen. 3:15) Mzimu woyera wa Mulungu ukhoza kutithandiza kuti tizikhulupirirabe lonjezo lolimbikitsa limeneli.

17. Kodi tiyenera kukana maganizo ati?

17 Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera. (Luka 11:13) Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. Masiku ano ziphunzitso zakuti kulibe Mulungu ndiponso kuti zinthu sizinachite kulengedwa koma zinangosintha kuchokera ku zinthu zina zikuchulukirachulukira. Anthu amakhulupirira zimenezi chifukwa chakuti amatsatira mfundo zolakwika ndiponso zopanda maziko. Tisalole kuti maganizo olakwikawa atisokoneze kapena kutichititsa mantha. Akhristu onse ayenera kukhala okonzeka kukana maganizo amenewa ndiponso kukana kumangotsatira anzawo amene amakhala ndi maganizo amenewa.​—Werengani Akolose 2:8.

18. Tikamaganizira za chiyambi cha chilengedwe ndiponso anthu, n’chifukwa chiyani tinganene kuti maganizo akuti kulibe Mlengi wanzeru ndi osamveka?

18 Ngati munthu ataona bwinobwino umboni wakuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse, akhoza kumakhulupirira kwambiri Baibulo ndiponso Mulunguyo. Anthu ambiri akaganizira za chiyambi cha chilengedwechi ndiponso anthu, safuna kuvomereza zoti pali wina wake wamphamvu amene anazilenga. Ngati titaona zinthu mwa njira imeneyi ndiye kuti tikusiya maumboni ena. Tikhoza kusiyanso kuganizira za dongosolo loonekeratu limene lilipo pa zinthu “zosawerengeka” zimene zili m’chilengedwechi. (Yobu 9:10; Sal. 104:25) Koma Akhristufe sitikayikira zoti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse mwanzeru pogwiritsa ntchito mzimu woyera.

Mzimu Woyera Ndi Wofunika Kuti Tizikhulupirira Mulungu

19. Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti Mulungu alikodi ndiponso kuti mzimu wake woyera ukugwira ntchito?

19 Sikuti timafunika kudziwa chinthu china chilichonse cholengedwa kuti tizikhulupirira Mulungu, kuti tizimukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Zimenezi n’zofanana ndi maubwenzi a anthu. Anthufe sitikhala pa ubwenzi ndi munthu wina chifukwa chongodziwa zinthu zinazake za munthuyo. Komabe kuti ubwenzi wa anthu ulimbe, anthuwo amafunika kudziwana bwino. N’chimodzimodzinso ndi kukhulupirira Mulungu. Munthu amayamba kukhulupirira kwambiri Mulungu akamaphunzira zambiri zokhudza Mulunguyo. Umu ndi mmenenso zimakhalira ndi anthu amene akudziwana bwino. Timakhala ndi umboni wakuti Mulungu alikodi tikamaona kuti akuyankha mapemphero athu ndiponso tikamaona ubwino wotsatira mfundo zake. Timayandikira kwambiri Yehova tikamaona umboni wowonjezereka wakuti akutitsogolera, akutiteteza, akutidalitsa pomutumikira ndiponso akutipatsa zinthu zimene timafunikira. Zonsezi ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mulungu aliko ndiponso wakuti mzimu wake woyera ukugwira ntchito.

20. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu analenga chilengedwechi ndiponso anthu? (b) Kodi chidzachitike n’chiyani ngati tipitiriza kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu?

20 Kulembedwa kwa Baibulo ndi umboni wina waukulu wakuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera. Tikutero chifukwa chakuti anthu amene analilemba “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Pet. 1:21) Kuphunzira Malemba mosamala kungatithandize kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. (Chiv. 4:11) Khalidwe lalikulu la Yehova la chikondi ndi limene linamuchititsa kuti alenge zinthu zonse. (1 Yoh. 4:8) Choncho tiyeni tiyesetse mmene tingathere kuti tithandize anthu ena kudziwa bwino Atate wathu wachikondi wakumwamba, yemwenso ndi Mnzathu wapamtima. Ngati tipitiriza kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, tidzakhala ndi mwayi wophunzira za iye kwamuyaya. (Agal. 5:16, 25) Yehova anasonyeza chikondi chosaneneka pamene anagwiritsa ntchito mzimu woyera polenga zinthu zakumwamba, dziko lapansi ndiponso anthu. Choncho, tiyeni tonse tipitirize kuphunzira za Yehova ndi ntchito zake zazikulu komanso tizitsanzira chikondi chake chosanenekachi.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi kukhalapo kwa zinthu zakumwamba ndiponso zapadziko lapansi kumatiuza chiyani za mmene Mulungu anagwiritsira ntchito mzimu woyera?

• Kodi kulengedwa kwathu m’chifaniziro cha Mulungu kumatipatsa mwayi wochita zinthu zotani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuona bwinobwino umboni wakuti zinthu zinachita kulengedwa?

• Kodi tingalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi tingaphunzire chiyani tikaona dongosolo limene lili m’chilengedwechi?

[Mawu a Chithunzi]

Stars: Anglo-Australian Observatory/​David Malin Images

[Zithunzi patsamba 8]

Kodi DNA imagwira ntchito yotani pa zinthu izi?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi ndinu wokonzeka kufotokoza bwino zimene mumakhulupirira?