Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Pamene Yesu Khristu ankatumiza atumwi 12 kukalalikira, kodi anawauza kuti atenge ndodo n’kuvala nsapato?

Anthu ena amanena kuti zimene zinalembedwa m’Mauthenga Abwino atatu pa nkhaniyi zimatsutsana. Koma tikayerekezera zimene zinalembedwa m’mauthenga atatuwa tikhoza kuzindikira mfundo ina yochititsa chidwi. Poyamba tiyeni tione zimene Maliko ndi Luka analemba. Maliko analemba kuti: “[Yesu] anawalangiza kuti asatenge mkate, thumba la chakudya, kapena ndalama m’zikwama zawo, koma kuti avale nsapato, ndi kuti asavale malaya awiri amkati.” (Maliko 6:7-9) Koma Luka analemba kuti: “Musanyamule kanthu pa ulendowu, musatenge ndodo, kapena thumba la chakudya, kapena mkate, kapena ndalama zasiliva, kapena kutenga malaya awiri amkati.” (Luka 9:1-3) Malemba awiriwa amaoneka ngati akutsutsana. Malinga ndi zimene Maliko analemba, atumwiwo anauzidwa kuti atenge ndodo ndiponso kuti avale nsapato. Koma Luka analemba kuti iwo sanayenere kutenga chilichonse ngakhale ndodo. Mosiyana ndi Maliko, Luka sananene chilichonse pa nkhani ya nsapato.

Koma kuti timvetse zimene Yesu ankatanthauza pa nthawiyi tiyeni tione mawu amene akupezeka m’Mauthenga Abwino atatu onsewa. M’malemba awiri amene tatchula pamwambawa ndiponso pa Mateyu 10:5-10, atumwiwa anauzidwa kuti asavale kapena kutenga “malaya awiri amkati.” N’zosachita kufunsa kuti mtumwi aliyense ankavala chovala chimodzi chamkati. Choncho iwo sanayenere kutenga chovala china pa ulendowu. N’zodziwikiratunso kuti iwo anali atavala nsapato ndipo Maliko anangolemba kuti “avale nsapato” koma sanalembe kuti atenge zina zapadera. Nanga bwanji za ndodo? Buku lina limati: “Zikuoneka kuti kalelo Aheberi ankakonda kuyenda ndi ndodo.” (The Jewish Encyclopedia; Gen. 32:10) Maliko analemba kuti atumwiwo “asanyamule kanthu pa ulendowo” kupatulapo ndodo imene anali atatenga kale pa nthawi imene Yesu ankapereka malangizowa. Olemba Mauthenga Abwino onse anatsindika malangizo a Yesu akuti atumwi sanayenere kupita kukatenga zinthu zina za pa ulendowu.

Mateyu anatsimikizira mfundo imeneyi. Iye analipo pamene Yesu ankapereka malangizowa ndipo mu uthenga wake analemba mawu a Yesuyo kuti: “Musatenge golide, siliva kapena mkuwa m’zikwama zanu za ndalama. Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo, kapena malaya awiri amkati, nsapato kapena ndodo, chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.” (Mat. 10:9, 10) Nanga bwanji za nsapato zimene atumwiwo anali atavala ndiponso ndodo zimene anali atatenga? Yesu sananene kuti ataye zimene anali atatenga kale koma anawauza kuti asakatenge zina. N’chifukwa chiyani anapereka malangizo amenewa? Chifukwa chakuti “wantchito ayenera kulandira chakudya chake.” Izi n’zimene Yesu ankatanthauza popereka malangizowa ndipo n’zogwirizana ndi zimene ananena pa ulaliki wa paphiri zakuti iwo sayenera kudera nkhawa zimene adzadya, kumwa kapena kuvala.​—Mat. 6:25-32.

Ngakhale kuti poyamba nkhani za m’Mauthenga Abwinowa zingaoneke ngati zikutsutsana, zonse zimanena mfundo yofanana. Mfundo yake ndi yakuti, atumwiwo anayenera kungonyamuka popanda kudodometsedwa ndi kutenga zinthu zina zowonjezera. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yehova ndi amene akanawapatsa zinthu zonse zofunikira.

Kodi “akazi ambiri” amene Solomo anawatchula anali ndani?​—Mlal. 2:8.

Sitikudziwa kwenikweni kuti anali ndani, koma n’kutheka kuti anali akazi otchuka amene Solomo anakumana nawo kunyumba yake yachifumu.

Mu chaputala 2 cha buku la Mlaliki, Solomo ananena za zinthu zosiyanasiyana zimene iye anachita kuphatikizapo zinthu zambirimbiri zimene anamanga. Iye ananena kuti: “Ndinapezanso siliva ndi golide wambiri, ndi chuma chimene chimakhala ndi mafumu ndiponso chimene chimapezeka m’zigawo za dziko. Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi. Ndinalinso ndi akazi ambiri, omwe amasangalatsa mtima wa amuna.”​—Mlal. 2:8.

Akatswiri ambiri amanena kuti “akazi” amene Solomo anawatchula palembali ndi akazi achilendo ndiponso akazi apambali, kapena kuti adzakazi, amene Solomo anadzakhala nawo atakula. Akazi amene anadzakhala nawo atakulawo ndi amene anamuchititsa kuti ayambe kulambira konyenga. (1 Maf. 11:1-4) Koma zimene akatswiriwa amanena sizingakhale zoona. Pamene Solomo ankalemba mawu amenewa n’kuti akudziwana kale ndi “akazi ambiri” amene anawatchulawa. Komanso pa nthawi imeneyi n’kuti Yehova akusangalalabe naye. Tikutero chifukwa nthawi imeneyo, Mulungu anali kumugwiritsa ntchito kulemba mabuku ena a m’Baibulo. Zimenezi sizikanatheka pa nthawi imene Solomo anali ndi akazi achilendo ndiponso akazi apambali ambirimbiri chifukwa nthawi imeneyo iye anasiya kulambira koona.

M’buku la Mlaliki, Solomo ananena kuti “anafufuza mawu okoma ndipo analemba mawu olondola a choonadi.” (Mlal. 12:10) N’zoonekeratu kuti iye ankadziwa mawu akuti “mfumukazi” ndiponso “mdzakazi” chifukwa anagwiritsa ntchito mawu amenewa polemba mabuku ena a m’Baibulo. (Nyimbo 6:8, 9) Koma palemba la Mlaliki 2:8, iye sanagwiritse ntchito mawu amenewa omwe anali kuwadziwa bwino.

Solomo anali wotchuka kwambiri moti mpaka mfumukazi yochokera ku Sheba, womwe unali ufumu wolemera kwambiri, inamva za iye ndipo inapita kukamuona. Mfumukaziyi inagoma kwambiri chifukwa cha zimene inamva ndiponso kuona. (1 Maf. 10:1, 2) Zimenezi zingatithandize kudziwa zimene Solomo ankatanthauza pamene anatchula “akazi ambiri.” N’kutheka kuti iye anali kunena za akazi otchuka amene anakumana nawo kunyumba yake yachifumu pa zaka zambiri zimene iye anakhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu.