Musamadzinyenge ndi Maganizo Onama
Musamadzinyenge ndi Maganizo Onama
HAVA atadya chipatso cha mumtengo woletsedwa, Mulungu anamufunsa kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Poyankha Hava anati: “Njoka ndi imene inandinyenga, ndipo ine ndadya.” (Gen. 3:13) Satana, njoka yochenjera imene inamuchititsa kuti asamvere Mulungu, anadzatchedwa “njoka yakale ija, . . . amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Chiv. 12:9.
Nkhani ya m’buku la Genesis imeneyi imasonyeza kuti Satana ndi wochenjera ndipo amanena mabodza n’cholinga choti anyenge anthu amene sali tcheru. Hava ananyengedwadi ndi Satana. Komabe tisaganize kuti ndi Satana yekha amene angatisocheretse. Baibulo limachenjezanso za kuopsa ‘kodzinyenga tokha ndi maganizo onama.’—Yak. 1:22.
Mwina tingaganize kuti n’zosatheka kudzinyenga tokha. Koma Mulungu anali ndi chifukwa chabwino popereka chenjezo limeneli. Choncho tingachite bwino kuganizira mmene tingadzinyengere tokha ndiponso maganizo onama amene angatisocheretse. Chitsanzo cha m’Malemba chingatithandize pa nkhani imeneyi.
Anthu Amene Anadzinyenga
Cha m’ma 537 B.C.E., Koresi Wamkulu wa ku Perisiya anapereka lamulo lolola Ayuda okhala ku Babulo kubwerera ku Yerusalemu kuti akamangenso kachisi. (Ezara 1:1, 2) Mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova, chaka chotsatira Ayuda anayala maziko a kachisi watsopano. Ayudawo anasangalala ndiponso anatamanda Yehova chifukwa chodalitsa ntchito yofunika imeneyi. (Ezara 3:8, 10, 11) Koma pasanapite nthawi, ena anayamba kutsutsa ntchito yomanganso kachisiyi ndipo Ayudawo anagwa ulesi. (Ezara 4:4) Patapita zaka 15 kuchokera pamene Ayudawo anabwerera kwawo, akuluakulu a Perisiya anapereka lamulo loletsa ntchito yomanga ku Yerusalemu. Chifukwa cha zimenezi, akuluakulu a zigawo anapita ku Yerusalemu “n’kukawaletsa [Ayuda] ntchitoyo mwankhondo.”—Ezara 4:21-24.
Chifukwa cha mavuto amenewa, Ayuda anadzinyenga ndi maganizo onama. Iwo anaganiza kuti: “Nthawi yomanga nyumba ya Yehova sinakwane.” (Hag. 1:2) Anaganiza kuti Mulungu sankafuna kuti amange kachisi pa nthawi imeneyo. M’malo moyesa kupeza njira zina zochitira chifuniro cha Yehova, iwo anasiya ntchito yawo yopatulika ndipo anayamba kutanganidwa ndi kukongoletsa nyumba zawo. Mneneri wa Mulungu, Hagai, anawafunsa mosapita m’mbali kuti: “Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala m’nyumba zokongoletsedwa ndi matabwa, nyumba iyi [kachisi wa Yehova] ili bwinja?”—Hag. 1:4.
Kodi mwaona zimene tingaphunzire pa chitsanzo chimenechi? Tikamaona molakwa nthawi imene Mulungu adzakwaniritse chifuniro chake, tingayambe kuganiza kuti kuchita zinthu zauzimu si kofunika kwenikweni ndipo tingayambe kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zathu. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuyembekezera alendo. Mungatanganidwe kwambiri ndi ntchito zapakhomo pokonzekera kubwera kwawo. Koma ngati mutalandira uthenga woti alendo anuwo afika mochedwa, kodi mungasiye zimene munali kuchita powakonzekera?
Kumbukirani kuti Hagai ndi Zekariya anathandiza Ayuda kuzindikira kuti Yehova ankafunabe kuti kachisi amangidwe nthawi yomweyo. Hagai analimbikitsa anthuwo kuti: “Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito.” (Hag. 2:4) Iwo anafunikira kupitirizabe ntchitoyo ali ndi chikhulupiriro choti mzimu wa Mulungu uwathandiza. (Zek. 4:6, 7) Kodi chitsanzo chimenechi sichikutithandiza kupewa kukhala ndi maganizo olakwika ponena za tsiku la Yehova?—1 Akor. 10:11.
Anayenera Kuyamba Kuganiza Bwino
Mu kalata yake yachiwiri, mtumwi Petulo anafotokoza za nthawi imene Yehova adzakhazikitsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (2 Pet. 3:13) Iye ananena kuti anthu ena onyodola ankatsutsa zoti Mulungu adzalowerera pa zochita za anthu. Anthu onyodolawa ankaumirira kunena kuti “zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.” (2 Pet. 3:4) Petulo anafuna kutsutsa maganizo olakwika amenewa. Iye analemba kuti: “Ndikulimbikitsa mphamvu zanu zotha kuganiza bwino mwa kukukumbutsani.” Iye anakumbutsa Akhristu anzakewo kuti anthu onyodolawo ankalakwitsa. M’mbuyomu, Mulungu analowererapo pa zochita za anthu ndipo anabweretsa chigumula padziko lonse.—2 Pet. 3:1, 5-7.
Mu 520 B.C.E., Hagai anaperekanso malangizo ofanana ndi amenewa kwa Ayuda amene anagwa ulesi ndi kusiya ntchito ya Mulungu. Iye anawalimbikitsa kuti: “Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.” (Hag. 1:5) Pothandiza olambira anzake kuti aziganiza bwino, anawakumbutsa za zolinga ndiponso malonjezo a Mulungu okhudza anthu Ake. (Hag. 1:8; 2:4, 5) Hagai atangowalimbikitsa choncho, iwo anayambanso ntchito yomanga ngakhale kuti panali lamulo lowaletsa. Zitatere, adani awo anayesanso kuwasokoneza pa ntchito yawo koma sizinaphule kanthu. Kenako lamulo loletsa ntchitoyi linachotsedwa ndipo pasanathe zaka zisanu anamaliza kumanga kachisi.—Ezara 6:14, 15; Hag. 1:14, 15.
Tiziganizira Mofatsa Zimene Tikuchita
Kodi mukuganiza kuti mofanana ndi Ayuda a m’nthawi ya Hagai, tikhoza kukhumudwa kwambiri patabuka mavuto? Ngati zimenezi zitachitika, zingakhale zovuta kuti tipitirizebe kukhala akhama pa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino. Koma kodi n’chiyani chingatichititse kukhumudwa kapena kugwa ulesi? Tikhoza kukumana ndi mavuto chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika m’dzikoli. Ganizirani za Habakuku amene anafunsa kuti: “Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti?” (Hab. 1:2) Mkhristu akayamba kuganiza kuti tsiku la Yehova likuchedwa, angasiye kuchita khama pa zinthu zauzimu n’kuyamba kufunafuna moyo wawofuwofu. Kodi zimenezi sizingakuchitikireni inuyo? Kungakhale kudzinyenga ngati titamaganiza kuti tsiku la Yehova likuchedwa. Ndiyetu n’zofunika kwambiri kutsatira malangizo a m’Malemba akuti ‘tiziganizira mofatsa zimene tikuchita’ ndiponso ‘tizilimbikitsa mphamvu zathu zotha kuganiza bwino.’ Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kudabwa kuona kuti dongosolo loipa la zinthuli lakhalapobe kwa nthawi yaitali kuposa mmene ndinkaganizira?’
Nthawi Imene Baibulo Linaneneratu
Taganizirani zimene Yesu ananena za mapeto a nthawi ino. Uthenga wa Maliko umasonyeza Maliko 13:33-37) Timapezanso chenjezo lofanana ndi limeneli pa ulosi wonena za zimene zidzachitike pa Aramagedo pa tsiku lalikulu la Yehova. (Chiv. 16:14-16) N’chifukwa chiyani pali machenjezo obwerezabwereza chonchi? Machenjezo amenewa ndi ofunika kwambiri chifukwa anthu ena akhoza kusiya kuchita khama ndiponso kukhala atcheru chifukwa choona kuti adikira nthawi yaitali kuposa mmene ankaganizira.
kuti pamene Yesu anafotokoza ulosi wonena za masiku otsiriza anatichenjeza mobwerezabwereza kuti tizikhala atcheru. (Yesu anapereka fanizo lotithandiza kuona kufunika kopitirizabe kukhala atcheru nthawi zonse pamene tikuyembekezera mapeto a nthawi ino. Iye anatchula za munthu amene nyumba yake inathyoledwa. Kodi munthuyu akanachita chiyani kuti asaberedwe? Anafunika kukhala maso usiku wonse. Yesu anamaliza fanizoli ndi mawu otilangiza akuti: “Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.”—Mat. 24:43, 44.
Fanizoli limasonyeza kuti tiyenera kukhala okonzeka kudikira ngakhale kwa nthawi yaitali. Komanso sitiyenera kudera nkhawa kwambiri ngati tikuona kuti dziko loipali lakhalapo kwa nthawi yaitali kuposa mmene tinkaganizira. Tisadzinyenge ndi maganizo onama akuti ‘nthawi ya Yehova sinakwane.’ Maganizo amenewa angatigwetse ulesi pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Aroma 12:11.
Chotsani Maganizo Onama
Mfundo imene ili palemba la Agalatiya 6:7 ingathandize munthu amene akudzinyenga ndi maganizo onama. Lembali limati: “Musanyengedwe . . . Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” Munda umene wangolimidwa koma osabzalamo kanthu umangomera udzu. Mofanana ndi zimenezi, ngati sitigwiritsa ntchito mphamvu zathu zotha kuganiza bwino, maganizo onama angakhazikike mumtima mwathu. Mwachitsanzo, tingamaganize kuti, ‘Tsiku la Yehova lidzafika ndithu, koma osati panopa.’ Maganizo olakwika amenewa angachititse kuti tiziona zinthu zauzimu mopepuka. Kenako tingagwe ulesi n’kusiya kuchita zinthu zauzimu. Zikatere, tsiku la Yehova lingadzatifikire modzidzimutsa.—2 Pet. 3:10.
Koma maganizo onama sangakhazikike mumtima mwathu ngati nthawi zonse timazindikira “chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Kuwerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse kungatithandize kwambiri pa nkhani imeneyi. Malemba angalimbitse chikhulupiriro chathu chakuti nthawi zonse Yehova amachita zinthu pa nthawi yake.—Hab. 2:3.
Zinthu monga kuphunzira Baibulo, kupemphera, kusonkhana nthawi zonse, kulalikira ndiponso kuchitira ena zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi zingatithandize “kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Pet. 3:11, 12) Yehova amaona ndiponso amayamikira kukhulupirika kwathu. Mtumwi Paulo anatikumbutsa kuti: “Tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”—Agal. 6:9.
Inoyi si nthawi yoti tizidzinyenga ndi maganizo onama akuti tsiku la Yehova likuchedwa. Koma ndi nthawi yolimbitsa mitima yathu chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.
[Chithunzi patsamba 4]
Hagai ndi Zekariya analimbikitsa Ayuda pa ntchito yomanga
[Chithunzi patsamba 5]
Kodi anthuwa akanadziwa nthawi yobwera mbala akanachita chiyani?