Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Oona Mtima M’dziko la Anthu Osaona Mtima

Khalanibe Oona Mtima M’dziko la Anthu Osaona Mtima

Khalanibe Oona Mtima M’dziko la Anthu Osaona Mtima

MASIKU ano, chinyengo chili paliponse ngati mpweya. Anthu amanama, kudulitsa malonda, kuba, kusabweza ngongole ndiponso kudzitamandira chifukwa chochita zinthu mochenjera pa bizinezi. Chifukwa cha zimenezi, zimakhala zovuta kwambiri kuti tikhalebe oona mtima. Kodi tingatani kuti tipitirize kupewa mtima wofuna kuchita chinyengo? Tiyeni tione zinthu zitatu zimene zingatithandize. Zinthu zake ndi izi: Kuopa Yehova, chikumbumtima chophunzitsidwa bwino ndiponso kukhutira ndi zimene tili nazo.

Kuopa Yehova Moyenera

Mneneri Yesaya analemba kuti: “Yehova ndiye Woweruza wathu. Yehova ndiye Wotipatsa Malamulo. Yehova ndiye Mfumu yathu.” (Yes. 33:22) Tikamazindikira udindo wa Yehova umenewu timamuopa ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tiziyesetsa kukhala oona mtima nthawi zonse. Lemba la Miyambo 16:6 limati: “Chifukwa choopa Yehova munthu amapatuka pa choipa.” Apa sizikutanthauza kuti tizichita mantha poganiza kuti Mulungu ndi wankhanza ayi, koma kukhala ndi mtima wosafuna kukhumudwitsa Atate wathu wakumwamba amene amatikonda kwambiri.​—1 Pet. 3:12.

Zimene zinachitikira banja lina zimasonyeza ubwino wa kuopa Mulungu m’njira imeneyi. Ricardo ndi mkazi wake Fernanda anakatenga ndalama zawo kubanki zokwana madola 700 a ku United States. * Fernanda anangotenga ndalamazo n’kuziika m’chikwama osaziwerenga. Atachoka kubankiko, analipira zinthu zina ndi zina. Koma atafika kunyumba anadabwa kupeza kuti pafupifupi ndalama zonse zilipobe. Iwo anazindikira kuti kubankiko anawapatsa ndalama zambiri. Poyamba anaganiza zongogwiritsa ntchito ndalamazo chifukwa anali ndi ngongole zambiri. Ricardo anati: “Tinapempha Yehova kuti atipatse mphamvu kuti tikabweze ndalamazo. Tinkafuna kubweza ndalamazo pofuna kumukondweretsa mogwirizana ndi pempho lake pa Miyambo 27:11.”

Chikumbumtima Chophunzitsidwa Baibulo

Chikumbumtima chathu chikhoza kukhala chothandiza ngati timaphunzira Baibulo ndiponso kuyesetsa kuchita zimene timaphunzirazo. Tikamatero, ‘mawu a Mulungu omwe ndi amoyo ndi amphamvu’ adzafikanso mumtima mwathu osati m’maganizo mokha. Izi zingatithandize “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheb. 4:12; 13:18.

Taganizirani zimene zinachitikira João. Iye anakongola ndalama zokwana madola 5,000 a ku United States. Ndiyeno asanabweze ndalamazo, anasamukira kutauni ina. Patapita zaka 8, João anaphunzira choonadi ndipo chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo chinamulimbikitsa kubweza ngongoleyo. Popeza João amasamalira mkazi ndi ana anayi, ndipo amalandira ndalama zochepa, eni ndalamazo anamulola kuti azibweza ngongoleyo mwapang’onopang’ono mwezi uliwonse.

Muzikhala Okhutira ndi Zimene Muli Nazo

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu. . . . Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:6-8) Kutsatira malangizo anzeru amenewa kungatithandize kuti tisayambe dyera n’kumachita mabizinezi achinyengo kapena okayikitsa pofuna kulemera msanga. (Miy. 28:20) Kutsatira malangizo a Paulo amenewa kungatithandizenso kuti tiziika Ufumu wa Mulungu pa malo oyamba tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatipatsa zinthu zonse zofunika.​—Mat. 6:25-34.

Tiyenera kusamala kuti “chinyengo champhamvu cha chuma” chisatichititse kukhala adyera kapena osirira mwansanje. (Mat. 13:22) Kumbukirani zimene zinachitikira Akani. Iye anaona Aisiraeli akuwoloka mtsinje wa Yorodano m’njira yozizwitsa. Ngakhale kuti anaona zimenezi, iye anayamba kukhala ndi mtima wadyera n’kuba siliva, golide ndi chovala chamtengo wapatali pa katundu amene anatsala mumzinda wa Yeriko. Izi zinachititsa kuti aphedwe. (Yos. 7:1, 20-26) N’chifukwa chake patapita zaka zambiri, Yesu anapereka chenjezo lakuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.”​—Luka 12:15.

Muzikhala Oona Mtima Kuntchito

Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhala oona mtima m’zinthu zonse. Ngati ndife oona mtima kuntchito sitingabe ngakhale pamene aliyense kuntchitoko amaba. (Tito 2:9, 10) M’bale wina dzina lake Jurandir amagwira ntchito m’boma ndipo ankalemba moona mtima ndalama zimene wagwiritsa ntchito pa maulendo ake okagwira ntchito kumalo ena. Koma anzake ankalemba ndalama zambiri kuposa zimene agwiritsa ntchito pa maulendo awo. Ankachita zimenezi chifukwa chakuti bwana wawo ankawaikira kumbuyo. Ndipo bwanayu anakalipira Jurandir chifukwa chochita zinthu moona mtima mpaka anasiya kumutumiza kumalo ena kukagwira ntchito. Koma kenako, kunabwera akuluakulu odzafufuza mmene akugwiritsira ntchito ndalama. Iwo anayamikira kwambiri Jurandir chifukwa chochita zinthu moona mtima ndipo anamukweza pa ntchito.

André amagwira ntchito yogulitsa katundu ndipo tsiku lina anauzidwa ndi bwana wake kuti achite chinyengo mwa kuwonjezera ndalama zoti makasitomala alipire. M’baleyu anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima n’kutsatira mfundo za m’Baibulo. (Sal. 145:18-20) Iye anafotokozera bwanayo chifukwa chimene sangachitire zimenezo koma sizinathandize. Choncho André anasankha kusiya ntchito ya ndalama zambiriyi. Koma patangotha pafupifupi chaka chimodzi, bwanayo anamupempha kuti abwerere kuntchitoko n’kumutsimikizira kuti wasiya chinyengo chowonjezera ndalama zoti makasitomala alipire. André anakwezedwa pa ntchito n’kukhala woyang’anira.

Muzibweza Ngongole

Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense.” (Aroma 13:8) Mwina sitibweza ngongole poganiza kuti mwini wake wa ndalamazo ndi wolemera ndipo sakufunikira kwenikweni ndalamazo. Tisaiwale kuti Baibulo limanena kuti: “Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza.”​—Sal. 37:21.

Koma bwanji ngati tikulephera kubweza ngongole chifukwa cha “zinthu zosayembekezereka”? (Mlal. 9:11) Francisco anabwereka kwa Alfredo ndalama zokwana madola 7,000 a ku United States kuti amalize kulipira ngongole ya nyumba yake. Koma chifukwa cha zovuta zina, Francisco analephera kubweza ndalamazo pa nthawi yake. Choncho iye anapita kwa Alfredo kukakambirana za nkhaniyi ndipo Alfredo anavomera kuti azibweza ngongoleyo pang’onopang’ono.

Muzipewa Kuchita Zinthu Mwachiphamaso

Taganizirani zimene zinachitikira Hananiya ndi mkazi wake Safira, amene anali mu mpingo wachikhristu m’nthawi ya atumwi. Iwo atagulitsa munda wawo, anapereka ndalama zochepa kwa atumwi n’kumanena kuti apereka ndalama zonse zimene anapeza. Iwo ankafuna kuti aoneke ngati owolowa manja kwambiri. Koma mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, mtumwi Petulo anatulukira chinyengo chawo ndipo Yehova anawapha.​—Mac. 5:1-11.

Mosiyana ndi Hananiya ndi Safira, anthu amene ankalemba Baibulo anali oona mtima ndipo sankabisa chilichonse. Mose anafotokoza moona mtima kuti anapsa mtima ndipo izi zinachititsa kuti asaloledwe kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:7-13) Nayenso Yona sanabise zolakwa zake zimene anachita asanalalikire kwa anthu a ku Nineve ndiponso pambuyo pake. Iye analemba zonse.​—Yona 1:1-3; 4:1-3

Pamafunika kulimba mtima kuti munthu anene zoona, makamaka ngati kuchita zimenezi kungamubweretsere mavuto ena. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mtsikana wa zaka 14 dzina lake Nathalia. Iye ataona pepala lake la mayeso, anapeza kuti aphunzitsi anamuchongera yankho lolakwika. Ngakhale kuti ankadziwa kuti aphunzitsiwo akazindikira amuchotsera malikisi, Nathalia anawauzabe. Iye anati: “Makolo anga amandiphunzitsa kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Yehova ndiyenera kukhala woona mtima. Chikumbumtima changa chikanandivutitsa kwambiri ndikanapanda kuwauza aphunzitsi anga.” Aphunzitsiwo anamuyamikira kwambiri chifukwa cha kuona mtima kwake.

Kuona Mtima Kumalemekeza Yehova

Mlongo wina wa zaka 17, dzina lake Giselle, anatola chikwama mmene munali mapepala ofunika ndiponso ndalama zokwana madola 35 a ku United States. Iye anapereka chikwamacho kwa akuluakulu a pasukulupo kuti achibweze kwa mwiniwake. Patatha mwezi umodzi, wachiwiri kwa ahedimasitala anawerengera kalasi yonse kalata yoyamikira Giselle chifukwa cha kuona mtima kwake. Anayamikiranso banja lake chifukwa chomuphunzitsa makhalidwe abwino ndiponso mawu a Mulungu. ‘Ntchito zake zabwino’ zinalemekeza Yehova.​—Mat. 5:14-16.

Pamafunika khama kuti tikhale oona mtima pakati pa anthu ‘odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, ndiponso osakhulupirika.’ (2 Tim. 3:2) Ngakhale zili choncho, kuopa Yehova moyenera, chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo ndiponso kukhutira ndi zimene tili nazo zingatithandize kukhalabe oona mtima m’dziko la anthu osaona mtimali. Tikatero timalimbitsanso kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova, yemwe ndi ‘wolungama ndiponso wokonda ntchito zolungama.’​—Sal. 11:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mayina ena tawasintha.

[Zithunzi patsamba 7]

Kuopa Yehova moyenera kumatithandiza kuti tizikhala oona mtima nthawi zonse

[Chithunzi patsamba 8]

Tikamakhala oona mtima timalemekeza Yehova