Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumasangalala Kuwerenga Mawu a Mulungu?

Kodi Mumasangalala Kuwerenga Mawu a Mulungu?

Kodi Mumasangalala Kuwerenga Mawu a Mulungu?

MLONGO wina dzina lake Lorraine ananena kuti: “Nditangoyamba kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ndinkaona kuti ndi chintchito. Ndinkalephera kutsatira nkhani zake moti ndinkayamba kuganizira zinthu zina.”

Anthu enanso anavomereza kuti kuwerenga Baibulo, poyamba sikukhala kosangalatsa. Koma iwo sanasiye chifukwa chakuti ankadziwa kuti kuwerenga Malemba Opatulika n’kofunika kwambiri. M’bale wina dzina lake Marc anati: “N’zosavuta kuti zinthu zina zisokoneze pulogalamu yowerenga ndi kuphunzira Baibulo. Ndinafunika kupemphera kwambiri komanso kuchita khama kuti ndiziwerenga Baibulo tsiku lililonse.”

Kodi mungatani kuti muzikonda kwambiri Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu? Nanga mungatani kuti muzisangalala poliwerenga? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuchita zimenezi.

Mfundo Zothandiza Powerenga Baibulo

Powerenga Baibulo muzipemphera ndiponso kuikapo maganizo anu onse. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira Mawu ake. Muzimupempha kuti atsegule maganizo anu ndi mtima wanu kuti mumvetse bwino nzeru zake. (Sal. 119:34) Popanda kuchita zimenezi, muzingowerenga Baibulo mwamwambo ndipo chidwi chofuna kuliphunzira chikhoza kutha. Mlongo wina dzina lake Lynn anati: “Nthawi zina ndimawerenga mothamanga kwambiri moti timfundo tina tosangalatsa timangondidutsa. Nthawi zambiri sindimvetsa bwinobwino mfundo zazikulu. Koma ndimapempha Mulungu kuti andithandize kuika maganizo onse pa zimene ndikuwerenga.”

Muziona kufunika kwa zimene mukuwerenga. Kumbukirani kuti kumvetsa choonadi cha m’Baibulo ndiponso kuchitsatira n’kumene kungakuthandizeni kupeza moyo wosatha. Choncho muziyesetsa kuti mupeze mfundo zothandiza n’kumazitsatira. M’bale wina dzina lake Chris anati: “Ndimayang’ana zinthu zimene zingandithandize kuzindikira maganizo ndiponso zolinga zoipa zimene ndili nazo. Ndimasangalala kuona kuti m’Baibulo ndiponso m’mabuku athu muli mfundo zothandiza ineyo ngakhale kuti olemba ake sakundidziwa.”

Khalani ndi zolinga zimene mungakwanitse. Yesani kudziwa mfundo zatsopano zokhudza anthu otchulidwa m’Baibulo. Mukhoza kupeza mfundo zosangalatsa zokhudza anthu amenewa m’mabuku monga Insight on the Scriptures, Watch Tower Publications Index kapena m’mlozera nkhani wa m’magazini a December. Mukamawadziwa bwino amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo, mungamvetse bwino zimene anachita ndipo zingakukhudzeni kwambiri.

Muzifufuza njira zatsopano zofotokozera Malemba. (Mac. 17:2, 3) Sophia amaphunzira Baibulo ndi cholinga chimenechi. Iye ananena kuti: “Pophunzira Baibulo ndimafufuza njira zatsopano zofotokozera Malemba mu utumiki ndiponso pa zochitika zina. Ndimachita zimenezi n’cholinga choti ndizifotokoza choonadi momveka bwino. Nsanja ya Olonda ndi imene imandithandiza kwambiri kupeza mfundo zatsopano zimenezi.”​—2 Tim. 2:15.

Muziona m’maganizo mwanu zimene zinkachitika. Lemba la Aheberi 4:12 limanena kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo.” Kuti Mawu a Mulungu akhale amoyo kwa inu, powerenga muyenera kuona m’maganizo mwanu zimene anthu otchulidwa m’Baibulowo ankaona. Muzitha kumva zimene iwo ankamva ndiponso kuyesa kukhala ndi maganizo amene iwo anali nawo. Muzigwirizanitsa zimene ankakumana nazo pa moyo wawo ndi zimene inuyo mukukumana nazo. Phunzirani pa zimene iwo anachita. Izi zikhoza kukuthandizani kumvetsa ndiponso kukumbukira zimene munawerenga m’Baibulo.

Muzikhala ndi nthawi yokwanira yofufuza malemba ovuta komanso mmene awafotokozera. Muzidzipatsa nthawi yochuluka pophunzira. Mukamawerenga mukhoza kukhala ndi mafunso ochititsa chidwi ofunika kuti mudzafufuze. Muzifufuza mawu ovuta, kuona mawu a m’munsi ndiponso kuona mndandanda umene uli pakati pa tsamba lililonse m’Baibulo wosonyeza mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana ndi zimene mukuwerenga. Mukamamvetsa bwino ndiponso kutsatira zimene mukuwerenga, m’pamenenso mumasangalala kwambiri kuphunzira Mawu a Mulungu. Mukatero, mudzatha kunena mawu a wamasalimo akuti: “Ndatenga zikumbutso zanu [Yehova] kukhala chuma changa mpaka kalekale, pakuti zimakondweretsa mtima wanga.”​—Sal. 119:111.

Musamawerenge mothamanga. Pewani kuphunzira zinthu zambirimbiri pa nthawi yochepa. Muzipezanso nthawi yokonzekera misonkhano ya mpingo. Raquel ananena kuti: “Nthawi zambiri maganizo anga sakhazikika moti sinditha kutsatira zimene ndikuwerenga. Choncho ndimaona kuti kuphunzira zinthu zochepa pa nthawi yochepa kumandithandiza kwambiri. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndizipindula kwambiri ndi zimene ndikuphunzira.” Chris ananena kuti: “Ndikakhala kuti ndilibe nthawi yokwanira ndimawerenga mothamanga ndipo chikumbumtima changa chimandivutitsa chifukwa chakuti ndimakumbukira zochepa. Zimene ndikuwerengazo sizikhazikika mumtima.” Chotero mukamawerenga muzikhala ndi nthawi yokwanira.

Muzilakalaka kwambiri kuwerenga mawu a Mulungu. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Koma monga makanda obadwa kumene, muzilakalaka mkaka wosasukuluka umene uli m’mawu a Mulungu, kuti mwa kumwa mkakawo, mukule ndi kukhala oyenera chipulumutso.” (1 Pet. 2:2) Mwachibadwa, makanda amalakalaka mkaka. Koma Malemba amasonyeza kuti kulakalaka Mawu a Mulungu sikumangochitika mwachibadwa. Ngakhale titamawerenga tsamba limodzi tsiku lililonse tikhoza kuyamba kulakalaka kuwerenga Baibulo. Zimene poyamba zimaoneka kukhala zovuta posapita nthawi zimakhala zosangalatsa.

Muzisinkhasinkha zimene mwawerenga. Mumapindulanso kwambiri ngati musinkhasinkha zimene mwawerenga. Zimenezi zimathandiza kwambiri kuti muzigwirizanitsa nkhani zimene mwapeza pofufuza. Pasanapite nthawi yaitali, mudzakhala ndi nzeru zamtengo wapatali kwambiri.​—Sal. 19:14; Miy. 3:3.

Nthawi Yanu Sipita Pachabe

Pamafunika khama kuti mutsatire mfundo zimenezi pophunzira mawu a Mulungu nthawi zonse koma phindu lake ndi lalikulu. Mudzayamba kumvetsa bwino Malemba. (Aheb. 5:12-14) Kuzindikira ndiponso nzeru zimene mungapeze pophunzira Malemba ouziridwa zingakuthandizeni kukhala osangalala ndiponso amtendere. Anthu amene amadziwa ndiponso kutsatira nzeru zopezeka m’Mawu a Mulungu amakhala ngati apeza “mtengo wa moyo.”​—Miy. 3:13-18.

Kuphunzira mozama Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kukhala ndi mtima womvetsa zinthu. (Miy. 15:14) Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzitha kupereka malangizo ogwira mtima ochokera m’Baibulo. Mukamalola kuti mfundo za m’Malemba ndi za m’mabuku ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” zizikutsogolerani posankha zochita, mudzaona kuti Mawu ouziridwa ndi Yehova akukuthandizani kukhala osangalala ndiponso kukhala ndi moyo wabwino. (Mat. 24:45) Mudzayamba kuganiza bwino ndiponso kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Zinthu zonse zokhudzana ndi ubwenzi wanu ndi Mulungu zidzayenda bwino.​—Sal. 1:2, 3.

Kukonda kwambiri Mulungu kudzakulimbikitsani kuuza ena za chikhulupiriro chanu. Zimenezi n’zosangalatsanso kwambiri. Sophia akuyesetsa kuloweza ndiponso kugwiritsa ntchito malemba osiyanasiyana kuti akope chidwi cha anthu amene amakumana nawo mu utumiki wachikhristu. Zimenezi zathandiza kuti aziphunzitsa anthu mowafika pamtima ndiponso kuti azisangalala kwambiri ndi utumiki. Iye ananena kuti, “Kuona anthu akuyamikira mfundo zochokera m’Baibulo n’kosangalatsa kwambiri.”

Koma chinthu chofunika kwambiri chimene munthu amapeza akamasangalala kuwerenga Mawu a Mulungu ndicho kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kuphunzira Baibulo kumakuthandizani kudziwa mfundo za Mulungu ndipo mumayamba kuyamikira kwambiri chikondi, kuwolowa manja ndiponso chilungamo chake. Palibenso chinthu china chimene ndi chofunika ndiponso chopindulitsa kwambiri kuposa kuwerenga Baibulo. Muziphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse ndipo pophunzira muziikapo maganizo anu onse. Mukamatero, nthawi yanu sidzapita pachabe.​—Sal. 19:7-11.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

MFUNDO ZOTHANDIZA POWERENGA MAWU A MULUNGU

▪ Powerenga Baibulo muzipemphera ndiponso kuikapo maganizo anu onse.

▪ Muziona kufunika kwa zimene mukuwerenga.

▪ Khalani ndi zolinga zimene mungakwanitse.

▪ Muzifufuza njira zatsopano zofotokozera Malemba.

▪ Muziona m’maganizo mwanu zimene zinkachitika.

▪ Muzikhala ndi nthawi yokwanira yofufuza malemba ovuta komanso mmene awafotokozera.

▪ Musamawerenge mothamanga.

▪ Muzilakalaka kwambiri kuwerenga Mawu a Mulungu.

▪ Muzisinkhasinkha zimene mwawerenga.

[Chithunzi patsamba 4]

Yerekezerani kuti muli nawo pa zimene zikuchitika m’nkhani imene mukuwerenga m’Baibulo