Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu Ndi Ndani?

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu Ndi Ndani?

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu Ndi Ndani?

“Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—SAL. 83:18.

1, 2. Ngakhale kuti kudziwa dzina la Yehova n’kofunika, kodi tiyeneranso kuchita chiyani?

MWINA nthawi yoyamba imene munaona dzina la Yehova inali pamene wina anakuwerengerani lemba la Salimo 83:18. N’kutheka kuti munadabwa kuwerenga mawu awa: “Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Sitikukayikira kuti kuchokera nthawi imeneyo nanunso mwakhala mukugwiritsa ntchito lemba limeneli kuthandiza anthu ena kuti adziwe Yehova, Mulungu wathu wachikondi.​—Aroma 10:12, 13.

2 Kudziwa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri, komabe kungodziwa dzinali si kokwanira. Mawu a wamasalimo angatithandize kuzindikira mfundo inanso yofunika kuti tipulumuke. Iye ananena kuti: “Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Zoonadi, Yehova ndi wofunika kwambiri m’chilengedwe chonse. Popeza Yehova ndi Mlengi wa zinthu zonse, amayembekezera kuti zolengedwa zonse zizimugonjera. (Chiv. 4:11) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthu wofunika kwambiri pa moyo wanga ndi ndani?’ Ndi bwino kuti tiganizire mmene tingayankhire funso limeneli.

Nkhani Imene Inayamba M’munda wa Edeni

3, 4. Kodi Satana anakwanitsa bwanji kunyengerera Hava ndipo zotsatira zake zinali zotani?

3 Zimene zinachitika m’munda wa Edeni kalelo zimasonyeza bwinobwino kuti funso limeneli ndi lofunika kwambiri. M’mundamu, mngelo wopanduka amene anadzakhala Satana Mdyerekezi ananyengerera Hava kuti azingoganizira zofuna zake m’malo moganizira lamulo la Yehova lakuti asadye chipatso cha mtengo winawake. (Gen. 2:17; 2 Akor. 11:3) Hava anakopeka ndi zimenezi ndipo anasonyeza kuti salemekeza ulamuliro wa Yehova. Iye sanasonyeze kuti Yehova ndi wofunika kwambiri kwa iye. Koma kodi Satana anakwanitsa bwanji kumunyengerera Hava?

4 Pokambirana ndi Hava, Satana anagwiritsa ntchito njira zambiri zochenjera. (Werengani Genesis 3:1-5.) Choyamba, Satana sanagwiritse ntchito dzina la Yehova. Iye ankangoti “Mulungu.” Mosiyana ndi Satana, wolemba buku la Genesis anagwiritsa ntchito dzina la Yehova pa vesi loyamba la chaputala chimenechi. Chachiwiri, m’malo monena za “lamulo” la Mulungu, Satana anangofunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati . . . ?” (Gen. 2:16) Zikuoneka kuti ponena kuti “anati,” Satana anayesetsa kuchepetsa mphamvu ya lamulo limene Mulungu anapereka. Chachitatu, ngakhale kuti ankalankhula ndi Hava yekha, iye anagwiritsa ntchito dala mawu olemekeza monga akuti “musadye” ngati kuti akulankhula ndi anthu awiri. Pochita zimenezi, iye anamukopa kuti ayambe kudziona ngati wofunika kwambiri ndiponso kuti akhoza kudziyankhira komanso kulankhula m’malo mwa mwamuna wake. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Hava anaona kuti ndi woyeneradi kudziyankhira ndiponso kulankhula m’malo mwa mwamuna wake moti anauza njokayo kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya.”

5. (a) Kodi Satana anachititsa Hava kuganizira kwambiri zinthu ziti? (b) Kodi Hava anasonyeza chiyani pamene anadya chipatso choletsedwa?

5 Satana anapotozanso mfundo zina. Iye anasonyeza kuti Mulungu sanachite chilungamo pouza Adamu ndi Hava kuti ‘asadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamo.’ Kenako Satana anachititsa Hava kudziganizira kwambiri ndiponso kuganiza kuti moyo umene anali nawo sunali wabwino ndipo akhoza kusintha zinthu ‘n’kufanana ndi Mulungu.’ Kenako anamuchititsa kuti aziganizira kwambiri za mtengowo ndi zipatso zake osati za ubwenzi wake ndi Mulungu, yemwe anamupatsa zinthu zonse. (Werengani Genesis 3:6.) Chomvetsa chisoni n’chakuti pamene anadya chipatsocho, Hava anasonyeza kuti Yehova sanali wofunika kwambiri kwa iye.

Nkhani Imene Inayamba M’nthawi ya Yobu

6. Pa nkhani ya kukhulupirika kwa Yobu, kodi Satana anakayikira chiyani, ndipo Yobu anapatsidwa mwayi wotani?

6 Patapita zaka zambiri, munthu wokhulupirika Yobu analinso ndi mwayi wosonyeza kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wake. Yehova atauza Satana kuti Yobu anali munthu wokhulupirika, Satanayo anati: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?” (Werengani Yobu 1:7-10.) Sikuti Satana anatsutsa zoti Yobu ankamvera Mulungu koma anakayikira zolinga zake. Iye ananamizira Yobu kuti sankatumikira Yehova chifukwa chomukonda koma chifukwa cha zolinga zadyera. Yobu yekha ndi amene akanayankha nkhaniyi ndipo anapatsidwa mwayi woti achite zimenezi.

7, 8. Kodi Yobu anakumana ndi mavuto ati nanga kukhulupirika ndiponso kupirira kwake kunasonyeza chiyani?

7 Yehova analola kuti Satana amubweretsere Yobu mavuto otsatizanatsatizana. (Yobu 1:12-19) Kodi Yobu anatani zinthu zitasintha kwambiri pa moyo wake? Baibulo limanena kuti iye “sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.” (Yobu 1:22) Koma Satana sanalekere pomwepo. Iye ananenanso kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” * (Yobu 2:4) Satana ankatanthauza kuti ngati Yobu atazunzika kwambiri ndi matenda sangaonenso kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wake.

8 Yobu anadwala matenda amene anawononga kwambiri thupi lake ndipo kenako mkazi wake anamuuza kuti atukwane Mulungu n’cholinga choti afe. Nawonso anthu atatu amene anabwera kudzatonthoza Yobu anamunena kuti anachimwira Mulungu. (Yobu 2:11-13; 8:2-6; 22:2, 3) Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, Yobu anakhalabe wokhulupirika. (Werengani Yobu 2:9, 10.) Kukhulupirika ndiponso kupirira kwake kunasonyeza kuti iye ankaona Yehova kukhala wofunika kwambiri pa moyo wake. Yobu anasonyezanso kuti ngakhale munthu wopanda ungwiro akhoza kuyesetsa kuyankha mabodza amene Mdyerekezi amanena.​—Yerekezerani ndi Miyambo 27:11.

Yankho Labwino Kwambiri Limene Yesu Anapereka

9. (a) Kodi poyamba Satana anayesa bwanji Yesu? (b) Kodi Yesu anachita chiyani atayesedwa?

9 Yesu atangobatizidwa, Satana anayesa kumukopa kuti akhale wodzikonda n’kutsatira zofuna zake m’malo mopitiriza kuona kuti Yehova ndiye wofunika kwambiri pa moyo wake. Mdyerekezi anayesa Yesu m’njira zitatu. Poyamba anayesa kumukopa kuti athetse njala yake pomuuza kuti asandutse miyala kukhala mitanda ya mkate. (Mat. 4:2, 3) Yesu anali atasala kudya masiku 40 choncho ankamva njala kwambiri. Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti agwiritse ntchito mphamvu zake zochita zozizwitsa pofuna kuthetsa njala yakeyo. Kodi Yesu anatani? Mosiyana ndi Hava, Yesu ankaganizira kwambiri Mawu a Yehova ndipo nthawi yomweyo anakana zimene Satana anamuuza.​—Werengani Mateyu 4:4.

10. N’chifukwa chiyani Satana anauza Yesu kuti adziponye pansi kuchokera pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi?

10 Satana anayesanso kukopa Yesu kuti ayambe kudziona kuti ndi wofunika kwambiri. Anamuuza kuti adziponye pansi kuchokera pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi. (Mat. 4:5, 6) Kodi cholinga cha Satana chinali chiyani? Satana ananena kuti ngati Yesu savulala akadziponya pansi zikanatsimikizira kuti iye anali “mwana wa Mulungu.” Apatu Mdyerekezi ankafuna kuti Yesu aziganizira kwambiri za mmene anthu ankamuonera mpaka kufika pochita zinthu zodzionetsera. Satana ankadziwa kuti munthu akhoza kulolera kuchita zinthu zoopsa kwambiri chifukwa cha kunyada kapena kuopa kuti achita manyazi pa maso pa anthu ena. Satana anapotoza lemba koma Yesu anasonyeza kuti ankamvetsa bwino Mawu a Yehova. (Werengani Mateyu 4:7.) Yesu anakana zimenezi ndipo apanso anasonyeza kuti ankaona Yehova kukhala wofunika kwambiri pa moyo wake.

11. N’chifukwa chiyani Yesu anakana pamene Mdyerekezi anamuuza kuti amupatsa maufumu onse a padziko?

11 Satana atathedwa nzeru ndi Yesu, anamuyesa komaliza pomuuza kuti amupatsa maufumu onse a padziko. (Mat. 4:8, 9) Yesu anakana nthawi yomweyo. Iye anazindikira kuti akachita zimene Satana ankafunazo ndiye kuti wakana zoti Yehova ndi Wam’mwambamwamba kapena kuti woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Werengani Mateyu 4:10.) Pa mayesero onsewa, Yesu ankayankha Satana pogwiritsira ntchito malemba okhala ndi dzina la Yehova.

12. Kodi Yesu atatsala pang’ono kumaliza ntchito yake ya padziko lapansi, anavutika maganizo ndi nkhani iti, nanga tikuphunzira chiyani pa zimene anachita?

12 Yesu atatsala pang’ono kumaliza ntchito yake ya padziko lapansi, anafunika kusankha zochita pa nkhani yovuta kwambiri. Pa nthawi yonse ya utumiki wake iye anasonyeza kuti ankafunitsitsa kupereka moyo wake nsembe. (Mat. 20:17-19, 28; Luka 12:50; Yoh. 16:28) Koma Yesu anazindikiranso kuti adzazengedwa mlandu wabodza m’khoti la Ayuda n’kuphedwa ngati munthu wonyoza Mulungu. Kuganizira zoti aphedwa mwa njira imeneyi kunamuvutitsa maganizo kwambiri. Iye anapemphera kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka, kapu iyi indipitirire.” Kenako anati: “Koma osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” (Mat. 26:39) Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa ndipo izi zinapereka umboni wosatsutsika wakuti iye ankaona kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wake.

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri kwa Ifeyo Ndi Ndani?

13. Kodi taphunzira chiyani pa nkhani ya Hava, Yobu ndi Yesu Khristu?

13 Kodi taphunzira chiyani? Nkhani ya Hava ikutiphunzitsa kuti anthu amene amatengeka ndi zofuna zawo kapena mtima wodzikuza amasonyeza kuti Yehova si wofunika kwambiri kwa iwo. Koma kukhulupirika kwa Yobu kukutiphunzitsa kuti ngakhale anthu opanda ungwiro akhoza kusonyeza kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wawo ngati atakhalabe okhulupirika pokumana ndi mavuto. Iwo angachite zimenezi ngakhale pamene sakudziwa chimene chikuchititsa mavuto awowo. (Yak. 5:11) Pomaliza, chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa kuti tisamade nkhawa ngati zinthu zochititsa manyazi zikutichitikira ndipo tisamaganizire kwambiri mmene anthu amationera. (Aheb. 12:2) Koma kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimenezi?

14, 15. Kodi zimene Yesu anachita poyesedwa zikusiyana bwanji ndi zimene Hava anachita, ndipo tingatsanzire bwanji Yesu? (Perekani ndemanga pa chithunzi chimene chili patsamba 18.)

14 Tisalole kuti mayesero amene timakumana nawo atichititse kuiwala Yehova. Hava analola kuti maganizo ake onse akhale pa zipatso za mtengo woletsedwa. Iye anaona kuti zipatsozo “n’zokoma kudya, zokhumbirika ndi zosiririka.” (Gen. 3:6) Izitu n’zosiyana kwambiri ndi zimene Yesu anachita atayesedwa katatu. Poyesedwa, iye ankaganizira kwambiri zotsatira zake osati mayeserowo. Iye ankadalira Mawu a Mulungu ndipo ankagwiritsa ntchito dzina la Yehova.

15 Tikamayesedwa kuti tichite zinthu zimene Yehova amadana nazo, kodi timaganizira kwambiri chiyani? Tikamaganizira kwambiri mayeserowo m’pamenenso timalakalaka kwambiri kuchita zoipazo. (Yak. 1:14, 15) Tiyenera kuchotsa mwamsanga maganizo amenewo mumtima mwathu ngakhale kuti kuchita zimenezi kungafanane ndi kuchotsa mbali ina ya thupi lathu. (Mat. 5:29, 30) Mofanana ndi Yesu, tiyenera kuganizira kwambiri zotsatira za zimene tikufuna kuchita, makamaka mmene zingakhudzire ubwenzi wathu ndi Yehova. Tiyenera kuganiziranso zimene Mawu a Mulungu amanena. Tikamachita zimenezi m’pamene timasonyeza kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu.

16-18. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kukhumudwa kwambiri? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira mavuto?

16 Tisalole kuti mavuto amene timakumana nawo atichititse kukwiyira Yehova. (Miy. 19:3) Pamene tikuyandikira kwambiri mapeto a dziko loipali, anthu ambiri a Yehova akukumana ndi masoka ndiponso mavuto. Masiku ano sitiyembekezera kutetezedwa mozizwitsa ku zinthu zimenezi. Komabe mofanana ndi Yobu, anthu amene timawakonda akamwalira ndiponso tikakumana ndi mavuto tingakhumudwe kwambiri.

17 Yobu sankadziwa chifukwa chimene Yehova analolera kuti zinthu zoipa zimuchitikire. Ifenso nthawi zina sitingadziwe chifukwa chimene zinthu zoipa zikuchitikira. Mwina tinamvapo za abale ena okhulupirika amene anaphedwa ndi chivomezi ngati chimene chinachitika ku Haiti, kapena amene anaphedwa ndi masoka ena achilengedwe. Mwina tikudziwanso za munthu wokhulupirika amene anaphedwa ndi anthu ena kapena amene anafa pa ngozi. N’kutheka kuti ifeyo tikuvutika ndi mavuto enaake kapena tikuchitiridwa zinthu zina zimene tikuona kuti n’zopanda chilungamo. Chifukwa cha kupwetekedwa mtima, tikhoza kumadzifunsa kuti: ‘Yehova, n’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira? Ndalakwa chiyani ine?’ (Hab. 1:2, 3) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira zoterezi zikatichitikira?

18 Si bwino kuthamangira kuganiza kuti zinthu ngati zimenezi zikatichitikira ndiye kuti Yehova sakusangalala nafe. Yesu anapereka chitsanzo cha zimenezi pamene anafotokoza za anthu ena amene anaphedwa mu nthawi yake. (Werengani Luka 13:1-5.) Mavuto ambiri amachitika chifukwa cha “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka.” (Mlal. 9:11) Kaya tikuvutika chifukwa chiyani, tikhoza kupirira ngati tiganizira kwambiri za “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse” n’kumulola kuti atithandize. Iye adzatipatsa mphamvu kuti tipitirize kumutumikira mokhulupirika.​—2 Akor. 1:3-6.

19, 20. Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kupirira zinthu zochititsa manyazi ndipo n’chiyani chingatithandize kutengera chitsanzo chake?

19 Tisalole kuti kunyada kapena kuopa kuchita manyazi kukhale nkhani yaikulu pa moyo wathu. Chifukwa cha kudzichepetsa, Yesu “anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo.” (Afil. 2:5-8) Iye anapirira zinthu zambiri zochititsa manyazi chifukwa chodalira Yehova. (1 Pet. 2:23, 24) Pochita zimenezi, Yesu anaika chifuniro cha Yehova patsogolo. Choncho Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. (Afil. 2:9) Yesu analimbikitsa ophunzira ake kutengera chitsanzo chake.​—Mat. 23:11, 12; Luka 9:26.

20 Nthawi zina, mayesero amene timakumana nawo amakhala ochititsa manyazi. Komabe tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro ngati cha mtumwi Paulo. Iye anati: “N’chifukwa chake ndikuvutika chonchi, koma sindikuchita manyazi. Pakuti ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo ndikukhulupirira kuti adzasunga chimene ndachiika m’manja mwake kufikira tsikulo.”​—2 Tim. 1:12.

21. Ngakhale kuti anthu m’dzikoli ndi odzikonda, kodi ifeyo tiziyesetsa kuchita chiyani?

21 Baibulo linaneneratu kuti m’masiku athu ano “anthu adzakhala odzikonda.” (2 Tim. 3:2) Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri ali ndi mtima wofuna kukhala patsogolo nthawi zonse. Tisalole kutengera mtima umenewu. M’malomwake, tonsefe tikakumana ndi mayesero, masoka kapena zinthu zochititsa manyazi tiyenera kuyesetsa kusonyeza kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti mawu akuti “khungu kusinthanitsa ndi khungu” amatanthauza kuti chifukwa cha kudzikonda, Yobu akanalolera kuti khungu kapena moyo wa ana ake ndiponso ziweto zake ziwonongeke pofuna kuteteza khungu kapena moyo wake. Ena amanena kuti mawuwa amatanthauza kuti munthu angalolere kuti khungu lake liwonongeke pofuna kupulumutsa moyo wake. Mwachitsanzo, munthu amatha kupherera chibakera ndi mkono mpaka mkonowo kuvulala n’cholinga choti asamenyedwe mutu. Kaya mawu okuluwikawa ankatanthauza chiyani, mfundo yake ndi yakuti Yobu akanalolera kupereka chilichonse kuti ateteze moyo wake.

Kodi Taphunzira Chiyani pa . . .

• mmene Satana ananyengera Hava?

• zimene Yobu anachita atakumana ndi mavuto?

• zimene Yesu ankaganizira kwambiri?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Hava sanaganizire za ubwenzi wake ndi Yehova

[Chithunzi patsamba 18]

Yesu anakana mayesero a Satana ndipo ankaganizira kwambiri za kuchita chifuniro cha Yehova

[Zithunzi patsamba 20]

Kulalikira m’matenti pambuyo pa chivomezi ku Haiti

Tikakumana ndi mavuto tiyenera kuganizira kwambiri za “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse”