Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhala Okonzeka’

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhala Okonzeka’

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhala Okonzeka’

“Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.”​—LUKA 12:40.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti ‘tikhale okonzeka’?

KODI n’chiyani chidzachitike kwa inuyo ndi banja lanu pamene ‘Mwana wa munthu adzafika mu ulemerero wake kudzalekanitsa anthu’? (Mat. 25:31, 32) Popeza izi zidzachitika pa ola limene sitikuliganizira, m’pofunika kuti tizitsatira malangizo a Yesu akuti “khalani okonzeka.”​—Luka 12:40.

2 M’nkhani yoyamba ija tinakambirana kuti aliyense m’banja akamakwaniritsa udindo wake, amathandiza kuti banja lonse likhale maso mwauzimu. Tiyeni tione zinthu zina zimene zingathandize kuti moyo wauzimu wa banja lathu uziyenda bwino.

Khalani ndi Diso “Lolunjika pa Chinthu Chimodzi”

3, 4. (a) Kodi mabanja achikhristu ayenera kusamala ndi zinthu ziti? (b) Kodi kukhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi” kumatanthauza chiyani?

3 Kuti anthu m’banja akonzekere kubwera kwa Khristu, ayenera kusamala kuti zinthu zina zisawalepheretse kuchita zinthu zokhudza kulambira koona. Anthu onse m’banja ayenera kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingawasokoneze polambira Yehova. Popeza kukondetsa chuma ndi msampha umene wakola mabanja ambiri, ndi bwino kuti tikambirane mawu a Yesu akuti tikhale ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi.” (Werengani Mateyu 6:22, 23.) Nyali imathandiza pounikira njira kuti munthu asapunthwe poyenda. Mofanana ndi nyali, zinthu zimene timaona ndi “maso a mtima” wathu zingatiunikire n’kutithandiza kuti tisapunthwe mwauzimu.​—Aef. 1:18.

4 Kuti munthu azitha kuona bwino, diso lake liyenera kukhala labwinobwino ndiponso lotha kulunjika pa chinthu chimene akuyang’ana. N’chimodzimodzinso ndi maso a mtima wathu. Kukhala ndi diso lophiphiritsira lomwe ndi lolunjika pa chinthu chimodzi kumatanthauza kuika maganizo pa cholinga chimodzi. M’malo moika maganizo athu pa zinthu zakuthupi ndiponso kusamalira banja lathu mwakuthupi, timaika maganizo athu pa zinthu zauzimu. (Mat. 6:33) Apa tikutanthauza kuti tizikhutira ndi zinthu zakuthupi zimene Mulungu watipatsa komanso kuona kuti kutumikira Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo.​—Aheb. 13:5.

5. Kodi mtsikana wina anasonyeza bwanji kuti anali ndi “diso” lolunjika pa kutumikira Mulungu?

5 Ana akaphunzitsidwa kukhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi, zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri. Taganizirani chitsanzo cha mtsikana wina wa ku Ethiopia. Iye anakhoza bwino kwambiri maphunziro ake a ku sekondale moti anapatsidwa mwayi womulipirira kuti apitirize maphunziro ake. Popeza maganizo ake onse anali pa kutumikira Yehova, iye anakana mwayi umenewu. Kenako anapatsidwa mwayi wa ntchito ya malipiro okwana madola 4,200 a ku United States pa mwezi. Ndalama zimenezitu ndi zambiri kwabasi tikayerekezera ndi malipiro amene anthu amalandira m’dziko lake. Koma “diso” la mtsikanayu linalunjika pa kuchita upainiya basi. Iye anakana ntchitoyi popanda kufunsa makolo ake. Kodi makolo ake anatani atamva zimene iye anachita? Iwo anasangalala n’kumuuza kuti amamunyadira kwambiri.

6, 7. Kodi tiyenera ‘kukhala maso’ ndi zinthu ziti?

6 Mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 6:22, 23 kwenikweni amachenjeza za umbombo. Yesu sanayerekeze ‘diso lolunjika pa chinthu chimodzi’ ndi ‘diso loyang’ana zinthu zambiri’ koma analiyerekezera ndi ‘diso loipa.’ Mawu achigiriki amene anamasulira kuti ‘diso loipa’ angatanthauzenso kuti diso losirira mwansanje kapena laumbombo. Kodi Yehova amaona bwanji kusirira kwa nsanje kapena umbombo? Baibulo limanena kuti: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo [kapena kuti kusirira kwa nsanje] zisatchulidwe n’komwe pakati panu.”​—Aef. 5:3.

7 N’zosavuta kuona kuti munthu wina ndi waumbombo koma zimakhala zovuta kuti munthu adzione yekha kuti ndi waumbombo. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) Kuti tichite zimenezi tiyenera kudzifufuza n’cholinga choti tidziwe zimene timaona kuti ndi zofunika kwambiri mumtima mwathu. Mabanja achikhristu ayenera kuganizira mofatsa za nthawi ndiponso ndalama zimene amagwiritsa ntchito posangalala komanso pogula zinthu.

8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tili maso’ pa nkhani yogula zinthu?

8 Pogula zinthu, si bwino kungoganizira ngati tili ndi ndalama zokwanira kugula zinthuzo. Tiyenera kudzifunsanso mafunso awa: ‘Kodi ndili ndi nthawi yokwanira yogwiritsa ntchito chinthu chimenechi ndiponso kuchisamalira? Kodi zitenga nthawi yaitali bwanji kuti ndiphunzire kuchigwiritsa ntchito bwinobwino?’ Achinyamatanu musamakhulupirire zinthu zonse zimene otsatsa malonda amanena n’kumavutitsa makolo anu kuti akugulireni zovala kapena zinthu zina zodula kwambiri. Muyenera kuphunzira kudziletsa. Anthu onse m’banja ayenera kuonanso ngati kugula zinthu zina kungalepheretse banjalo kukonzekera kubwera kwa Mwana wa munthu. Muzikhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”​—Aheb. 13:5.

Khalani ndi Zolinga Zauzimu

9. Kodi kukhala ndi zolinga zauzimu kungathandize bwanji banja?

9 Chinthu china chimene chingathandize anthu m’banja kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti azikonda kwambiri Mulungu ndicho kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Kuchita zimenezi kungathandize banja kudziwa ngati likukwaniritsa cholinga chawo chachikulu chomwe ndi kusangalatsa Yehova. Zingawathandizenso kudziwa ngati zinthu zina zilidi zofunika kwambiri.​—Werengani Afilipi 1:10.

10, 11. Kodi banja lanu likuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu ziti ndipo ndi zolinga ziti zimene mukufuna kudzakwaniritsa m’tsogolo?

10 Kukhala ndi zolinga zing’onozing’ono zimene aliyense m’banjalo angakwanitse kungakuthandizeninso kwambiri. Mwachitsanzo, mungakhale ndi cholinga choti tsiku lililonse muzikambirana lemba la tsiku. Ndemanga zimene aliyense amapereka zingathandize kuti mutu wa banja udziwe mmene aliyense akukondera zinthu zauzimu. Kukhala ndi cholinga chowerenga Baibulo limodzi monga banja nthawi zonse kungathandize kwambiri kuti ana aphunzire kuwerenga mwaluso ndiponso kuti azimvetsa bwino uthenga wa m’Baibulo. (Sal. 1:1, 2) Tiyenera kukhala ndi cholinga choti mapemphero athu azisonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Cholinga china chabwino chingakhale kuyesetsa kusonyeza kwambiri makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Tingachitenso bwino kupeza njira zosonyezera kuti timakonda ndiponso kuganizira anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Kuchita zimenezi monga banja kungathandize ana kuti akhale achifundo ndiponso kuti akhale ndi mtima wofuna kuchita upainiya kapena umishonale.

11 Kodi pali zolinga zimene mungakhale nazo m’banja lanu? Mwina mungakhale ndi cholinga chowonjezera nthawi imene mumathera mu utumiki. Apo ayi mungayesetse kuchepetsa mantha kuti muzilalikira bwinobwino pa telefoni, mumsewu, m’malo a malonda kapena malo antchito. Mungaganizirenso zokatumikira kudera kumene kuli ofalitsa Ufumu ochepa. Mwinanso munthu mmodzi m’banja lanu angaphunzire chinenero chatsopano n’cholinga choti azilalikira kwa anthu olankhula chinenerocho.

12. Kodi mutu wa banja ungathandize bwanji kuti banja lonse lizikonda zinthu zauzimu?

12 Ngati ndinu mutu wa banja, muyenera kuona mmene mungathandizire banja lanu kuti lizikonda kwambiri zinthu zauzimu. Mukatero, muyenera kukhala ndi zolinga zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezo. Zolinga zimene banja lanu lingakhale nazo ziyenera kukhala zoti mungazikwanitsedi ndiponso zogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’banja mwanumo. (Miy. 13:12) Kukwaniritsa zolinga zofunika kwambiri kumatenga nthawi. Choncho nthawi ina imene mumakhala mukucheza kapena kuonera TV, muyenera kuigwiritsa ntchito poyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu. (Aef. 5:15, 16) Chitani khama kwambiri kuti mukwaniritse zolinga za banja lanu. (Agal. 6:9) Ngati banja lanu likuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu, ‘anthu onse adzaona kuti mukupita patsogolo.’​—1 Tim. 4:15.

Muzichita Kulambira kwa Pabanja Mlungu Uliwonse

13. Fotokozani kusintha kumene kunachitika kokhudza misonkhano ya mlungu ndi mlungu, ndipo kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

13 Chinthu china chothandiza kwambiri kuti mabanja ‘akonzekere’ kubwera kwa Mwana wa munthu ndicho kusintha kwa misonkhano ya mlungu ndi mlungu kumene kunayamba pa January 1, 2009. Kukumana m’timagulu kuti tichite msonkhano umene m’mbuyomu unkatchedwa Phunziro la Buku la Mpingo kunatha. Ndiyeno panakonzedwa dongosolo loti msonkhano umenewu uzichitika limodzi ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Kusintha kumeneku kunachitika kuti Akhristu asankhe tsiku limodzi pa mlungu loti azichita Kulambira kwa Pabanja n’cholinga choti azilimbitsa mabanja awo mwauzimu. Tsopano papita nthawi yaitali kuchokera pamene kusinthaku kunachitika. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi imeneyi ndikuigwiritsa ntchito kuchita Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo pandekha? Kodi ndikuyesetsa kuti cholinga cha kusinthaku chikwaniritsidwe?’

14. (a) Kodi cholinga chachikulu chochitira Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo patokha mlungu uliwonse n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani kusankha tsiku loti tiziphunzira kuli kofunika kwambiri?

14 Cholinga chachikulu chochitira Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo patokha n’chakuti tiyandikire kwambiri Mulungu. (Yak. 4:8) Tikamaphunzira Baibulo nthawi zonse n’kumamudziwa bwino Mlengi, ubwenzi wathu ndi iye umalimba. Tikamayandikira kwambiri Yehova m’pamene timayamba kumukonda ndi ‘mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse.’ (Maliko 12:30) Mosakayikira tonsefe timafuna kumvera Mulungu ndi kumutsanzira. (Aef. 5:1) Choncho kuchita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse n’kumene kungatithandize kuchita zimenezi. Kungathandizenso kuti munthu aliyense m’banja ‘akhale wokonzeka’ mwauzimu pamene tikuyembekezera “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21) Kulambira kwa Pabanja n’kothandiza kwambiri kuti tipulumutsidwe.

15. Kodi Kulambira kwa Pabanja kungathandize bwanji kuti anthu m’banja ayambe kukondana kwambiri?

15 Cholinga chachiwiri chochitira Kulambira kwa Pabanja n’kuthandiza anthu onse m’banja kuti azikhala ogwirizana. Kukhala pamodzi n’kumakambirana zinthu zauzimu mlungu uliwonse kumathandiza kuti anthu m’banja ayambe kukondana kwambiri. Mwamuna ndi mkazi amagwirizana kwambiri akaona mnzake akusangalala ndi mfundo yabwino imene aphunzirira limodzi. (Werengani Mlaliki 4:12.) Makolo ndi ana amene amalambirira pamodzi angagwirizane kwambiri chifukwa cha chikondi chomwe “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”​—Akol. 3:14.

16. Kodi alongo atatu akupindula bwanji ndi dongosolo lophunzira Baibulo limodzi mlungu uliwonse?

16 Taganizirani zimene zinachitikira alongo atatu. Iwo apindula kwambiri chifukwa cha dongosolo limeneli loti tizipatula nthawi yophunzira Baibulo. Ngakhale kuti alongowa si apachibale, iwo amakhala mumzinda umodzi ndipo akhala akucheza limodzi kwa zaka zambiri. Pofuna kuti azicheza kwambiri makamaka pokambirana zinthu zauzimu, iwo anagwirizana tsiku loti aziphunzirira Baibulo limodzi. Iwo anayamba kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito buku latsopano lofotokoza buku la Machitidwe (“Bearing Thorough Witness” About God’s Kingdom). Mmodzi mwa alongowa anati: “Timasangalala kwambiri ndi phunziro lathu moti nthawi zambiri limapitirira ola limodzi. Timayesa kuganizira zimene abale athu nthawi ya atumwi ankakumana nazo n’kukambirana zimene tikanachita titakumana ndi zinthu ngati zimenezo. Ndiyeno timayesa kugwiritsa ntchito mu utumiki mfundo zimene taphunzirazo. Zimenezi zathandiza kuti tizisangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira ndipo zotsatira zake ndi zabwino kwambiri kuposa kale.” Kuwonjezera pa kulimbikitsidwa mwauzimu, kuchita zimenezi kwawathandiza kuti panopa azigwirizana kwambiri. Iwo anati, “Timaona kuti nthawi imeneyi ndi yamtengo wapatali kwambiri.”

17. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize kuti Kulambira kwa Pabanja kuzikhala kopindulitsa?

17 Nanga bwanji inuyo? Kodi mukupindula bwanji ndi Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo panokha mlungu uliwonse? Sitingapindule kwenikweni ngati timangochita zimenezi mwa apa ndi apo. Munthu aliyense m’banja ayenera kukonzekera phunziroli ndiponso kudziwa kuti tidzachita nthawi yakuti. Tisalole zinthu zing’onozing’ono kusokoneza dongosolo limeneli. Muyenera kuphunzira zinthu zogwirizana ndi banja lanu kuti aliyense azisangalala ndiponso kupindula. Kodi mungatani kuti muzisangalala pophunzira? Muziphunzitsa m’njira yogwira mtima ndipo muzionetsetsa kuti phunzirolo lizichitika mwaulemu komanso aliyense azimasuka.​—Yak. 3:18. *

‘Khalanibe Maso’ Ndiponso “Khalani Okonzeka”

18, 19. Kodi inuyo ndi banja lanu muyenera kuchita chiyani chifukwa chodziwa kuti Mwana wa munthu ali pafupi kufika?

18 Kuwonjezeka kwa mavuto m’dzikoli kumatsimikizira kuti kuyambira mu 1914 tili m’masiku otsiriza a dziko la Satanali. Armagedo ili pafupi kwambiri. Posachedwapa Mwana wa munthu afika kudzapereka chiweruzo cha Yehova kwa anthu oipa. (Sal. 37:10; Miy. 2:21, 22) Kudziwa zimenezi kuyenera kulimbikitsa banja lanu kukhala lokonzeka.

19 Kodi mukutsatira chenjezo la Yesu lakuti tikhale ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi”? Pamene anthu m’dzikoli akufunafuna chuma, kutchuka kapena udindo, kodi banja lanu likuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu? Kodi mukutsatira dongosolo la Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo panokha mlungu uliwonse? Kodi mukupindula nalo? Malinga ndi mmene nkhani yapitayi inafotokozera, kodi mukuthandiza banja lanu ‘kukhalabe maso’ pokwaniritsa udindo wanu wa m’Malemba monga mwamuna, mkazi kapena mwana? (1 Ates. 5:6) Ngati mukuchita zimenezi ndiye kuti ‘mudzakhala okonzeka’ pamene Mwana wa munthu adzafika.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mupeze mfundo zokuthandizani posankha zoyenera kuphunzira ndiponso kuti phunzirolo lizikhala lopindulitsa komanso losangalatsa, werengani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2009, tsamba 29 mpaka 31.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Fotokozani mmene zinthu zotsatirazi zingathandizire mabanja achikhristu ‘kukhala okonzeka.’

Kukhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi”

Kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa

Kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kukhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi” kungatithandize kuti tisasokonezedwe ndi zinthu za m’dzikoli