Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhalabe Maso’

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhalabe Maso’

Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhalabe Maso’

“Tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.”​—1 ATES. 5:6.

1, 2. Kodi chimafunika n’chiyani kuti banja likhalebe maso mwauzimu?

PONENA za “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova,” mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Abale simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala. Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala ndiponso ana a usana. Si ife a usiku kapena a mdima ayi.” Iye anawonjezera kuti: “Chotero tisapitirize kugona ngati mmene enawo akuchitira, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.”​—Yow. 2:31; 1 Ates. 5:4-6.

2 Malangizo amene Paulo anapereka kwa Atesalonika ndi othandiza kwambiri kwa Akhristu amene akukhala “nthawi yamapeto.” (Dan. 12:4) Pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira, Satana akuyesetsa kuchititsa Akhristu oona ambiri kuti asiye kutumikira Mulungu. Choncho tingachite bwino kutsatira malangizo anzeru a Paulo akuti tikhalebe tcheru mwauzimu. Kuti banja lachikhristu likhalebe maso, aliyense m’banjalo ayenera kukwaniritsa udindo wake wa m’Malemba. Kodi mwamuna, mkazi, ndiponso ana ali ndi udindo wotani pothandiza kuti banja ‘likhalebe maso’?

Amuna Ayenera Kutsanzira “M’busa Wabwino

3. Malinga ndi 1 Timoteyo 5:8, kodi udindo wina wa mwamuna monga mutu wa banja ndi wotani?

3 Baibulo limanena kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akor. 11:3) Kodi mwamuna, monga mutu wa banja, ali ndi udindo wotani? Malemba amafotokoza za udindo wina wa mutu wa banja ponena kuti: “Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Tim. 5:8) N’zoona kuti mwamuna ayenera kupezera banja lake zinthu zakuthupi. Koma kuti athandize banja lake kukhala maso mwauzimu, ayenera kuchitanso zinthu zina. Iye ayenera kumanga banja lake mwauzimu, kapena kuti kuthandiza aliyense m’banjalo kulimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. (Miy. 24:3, 4) Kodi angachite bwanji zimenezi?

4. Kodi n’chiyani chingathandize mwamuna kumanga banja lake mwauzimu?

4 Popeza kuti “mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo,” mwamuna ayenera kuphunzira ndi kutsanzira mmene Yesu amachitira zinthu monga mutu wa mpingo. (Aef. 5:23) Taganizirani mmene Yesu anafotokozera ubwenzi wa pakati pa iye ndi otsatira ake. (Werengani Yohane 10:14, 15.) Ndiyeno kodi mwamuna angatani kuti amange banja lake mwauzimu? Iye ayenera kuphunzira zimene Yesu, yemwe ndi “m’busa wabwino,” ananena ‘n’kumatsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’​—1 Pet. 2:21.

5. Kodi M’busa Wabwino amadziwa zinthu ziti zokhudza mpingo?

5 Tiyeni tione zimene mutu wa banja ungaphunzire kwa Khristu. M’busa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi nkhosa zake chifukwa cha kudziwana ndi kukhulupirirana. M’busa amadziwa bwino kwambiri nkhosa zake zonse ndipo nkhosa zimadziwa ndi kukhulupirira m’busayo. Zimazindikira ndi kumvera mawu ake. Yesu anati: “Nkhosa zanga ndimazidziwa, izonso zimandidziwa.” Iye samangodziwa zinthu zochepa chabe zokhudza mpingo. Palembali, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kudziwa” akutanthauza “kudziwa bwinobwino aliyense payekha.” Choncho M’busa Wabwino amadziwa bwinobwino nkhosa iliyonse payokha. Iye amadziwa zimene nkhosa iliyonse ikufuna, zimene ingachite bwino ndiponso zofooka zake. Palibe chilichonse chokhudza nkhosa chimene Yesu sadziwa. Nkhosa nazonso zimadziwa bwino kwambiri m’busa ndipo zimakhulupirira kuti iye ndi Mtsogoleri wabwino.

6. Kodi amuna angatsanzire bwanji M’busa Wabwino?

6 Kuti mwamuna achite umutu wake motsanzira Khristu, ayenera kudziona ngati m’busa ndipo anthu amene akuwasamalira ayenera kuwaona ngati nkhosa zake. Iye ayenera kuyesetsa kulidziwa bwino banja lake. Kodi n’zotheka mwamuna kulidziwa bwino banja lake? Inde n’zotheka, koma pokhapokha ngati amakambirana bwino ndi aliyense m’banja, kumvetsera akamafotokoza mavuto awo ndiponso kutsogolera bwino pochita zinthu limodzi ndi banja lake. Ayeneranso kuyesetsa kusankha mwanzeru pa zinthu monga Kulambira kwa Pabanja, kupita ku misonkhano, kulowa mu utumiki ndiponso kuchita zosangalatsa. Ngati mwamuna wachikhristu amadziwa bwino Mawu a Mulungu komanso kudziwa bwino anthu onse a m’banja lake, amatsogolera mwanzeru ndipo zimakhala zosavuta kuti banja lonselo lizimukhulupirira. Iye angakhalenso wosangalala kuona banja lake likulambira Mulungu mogwirizana.

7, 8. Kodi mwamuna angatsanzire bwanji M’busa Wabwino pokonda anthu amene akuwasamalira?

7 M’busa wabwino amakondanso kwambiri nkhosa zake. Tikamaphunzira Mauthenga Abwino ofotokoza za moyo ndi utumiki wa Yesu, timakhudzidwa mtima kwambiri ndi mmene iye ankakondera ophunzira ake. Iye anafika mpaka ‘popereka moyo wake chifukwa cha nkhosazo.’ Amuna ayenera kutsanzira Yesu pokonda amene akuwasamalira. M’malo mopondereza mkazi wake, mwamuna amene amafuna kusangalatsa Mulungu amapitiriza kukonda mkazi wake ngati “mmene Khristu anakondera mpingo.” (Aef. 5:25) Ayenera kulankhula ndi mkazi wake mokoma mtima ndiponso mwachifundo chifukwa mkaziyo ndi woyenera kulemekezedwa.​—1 Pet. 3:7.

8 Bambo, yemwe ndi mutu wa banja, ayenera kutsatira kwambiri mfundo za Mulungu pophunzitsa ana ake. Iye ayeneranso kuwakonda kwambiri. Ngati anawo akufunika kulangidwa, iye ayenera kuchita zimenezo mwachikondi. Ana ena amatenga nthawi kuti amvetse ubwino wa zimene makolo akufuna. Choncho bambo ayenera kukhala woleza mtima kwambiri ndi ana otero. Mwamuna amene nthawi zonse amayesetsa kutsanzira Yesu amathandiza kuti banja lake likhale labata komanso lotetezeka. Banja lake limasangalala ndi chitetezo chauzimu chimene wamasalimo antchula m’nyimbo yake.​—Werengani Salimo 23:1-6.

9. Mofanana ndi Nowa, kodi amuna achikhristu ali ndi udindo wotani ndipo n’chiyani chingawathandize kukwaniritsa udindowu?

9 Nowa anakhala ndi moyo pa nthawi imene anthu oipa a m’masiku ake anatsala pang’ono kuwonongedwa. Koma Yehova anamupulumutsa “pamodzi ndi anthu ena 7, pamene anabweretsa chigumula padziko la anthu osaopa Mulungu.” (2 Pet. 2:5) Nowa anali ndi udindo wothandiza banja lake kuti lipulumuke Chigumula. Mitu ya mabanja achikhristu ili ndi udindo wofanana ndi wa Nowa m’masiku otsiriza ano. (Mat. 24:37) Choncho n’kofunika kuti iwo aziphunzira chitsanzo cha “m’busa wabwino” n’kumayesetsa kumutsanzira.

Akazi Ayenera ‘Kumanga Nyumba Yawo’

10. Kodi mawu akuti “akazi agonjere amuna awo” satanthauza chiyani?

10 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi agonjere amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye.” (Aef. 5:22) Mawu amenewa satanthauza kuti udindo wa mkazi ndi wonyozeka ayi. Asanalenge Hava, yemwe ndi mkazi woyamba, Mulungu woona ananena kuti: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” (Gen. 2:18) Mawu akuti “womuthandiza” ndiponso akuti “mnzake womuyenerera” amasonyeza kuti mkazi ali ndi udindo wolemekezeka. Iye ali ndi udindo wothandiza mwamuna wake posamalira maudindo a m’banja.

11. Kodi mkazi wabwino amamanga bwanji nyumba yake?

11 Mkazi wabwino amayesetsa kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja lake. (Werengani Miyambo 14:1.) Mosiyana ndi mkazi wopusa amene salemekeza mutu wa banja, mkazi wanzeru amalemekeza kwambiri dongosolo lothandiza limeneli. M’malo motsatira mtima wosafuna kumvera kapena kuuzidwa zochita umene wafala m’dzikoli, iye amagonjera mwamuna wake. (Aef. 2:2) Mkazi wopusa amakonda kulankhula zoipa zokhudza mwamuna wake koma mkazi wanzeru amayesetsa kuti ana ake ndiponso anthu ena azilemekeza kwambiri mwamuna wake. Mkazi wanzeru amayesetsanso kuti asapeputse mwamuna wake, yemwe ndi mutu wa banja, pomukakamiza kuti achite zinazake kapena kukangana naye. Mkazi wanzeru amagwiritsanso ntchito ndalama mosamala, koma mkazi wopusa nthawi zambiri amangowononga zinthu zimene banja lazipeza movutikira. Mkazi wabwino amagwirizana ndi mwamuna wake pa nkhani zokhudza ndalama. Nthawi zonse iye amachita zinthu mwanzeru ndiponso sawononga ndalama. Iye sakakamizanso mwamuna wake kuti azigwira ntchito maola ena owonjezera.

12. Kodi mkazi angathandize bwanji banja lake kuti ‘likhalebe maso’?

12 Mkazi wabwino amathandiza banja lake kuti ‘likhalebe maso’ pothandiza mwamuna wake kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu. (Miy. 1:8) Amathandiza kuti Kulambira kwa Pabanja kuziyenda bwino. Iye amakhala mbali ya mwamuna wake popereka malangizo ndi chilango kwa ana. Koma mkazi wopusa sagwirizana ndi mwamuna wake ndipo ana ake amavutika mwakuthupi ndi mwauzimu.

13. N’chifukwa chiyani mkazi ayenera kuthandiza mwamuna wake akamachita zambiri m’gulu la Mulungu?

13 Kodi mkazi wanzeru amamva bwanji mwamuna wake akamachita zambiri mu mpingo wachikhristu? Iye amasangalala kwambiri. Kaya mwamuna wake ndi mtumiki wothandiza, mkulu, ali mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala kapena amathandiza kumanga Nyumba za Ufumu, iye amasangalala ndi zimene mwamuna wakeyo akuchita. Kulankhula ndiponso kuchita zinthu zothandiza mwamuna wake si kophweka nthawi zonse. Koma iye amadziwa kuti mwamuna wake akamachita zambiri m’gulu la Mulungu zimathandiza kuti banja likhalebe maso mwauzimu.

14. (a) Kodi mkazi wanzeru angavutike ndi chiyani, ndipo n’chiyani chingamuthandize? (b) Kodi mkazi amathandiza bwanji kuti banja lake likhale losangalala?

14 Mkazi wanzeru angavutike kuthandiza mwamuna wake ngati mwamunayo wasankha zinthu zimene iye sakugwirizana nazo. Ngakhale izi zichitike, iye amasonyezabe “mzimu wabata ndi wofatsa” ndipo amathandiza kuti zimene mwamuna wakeyo wasankha zitheke. (1 Pet. 3:4) Nayenso mkazi wabwino amayesetsa kutsatira zitsanzo za akazi oopa Mulungu a m’mbuyo, monga Sara, Rute, Abigayeli ndiponso Mariya, yemwe anali mayi a Yesu. (1 Pet. 3:5, 6) Iye amatsanziranso akazi achikulire a masiku ano amene ali ndi “khalidwe loyenera anthu opembedza.” (Tito 2:3, 4) Mkazi wanzeru akamakonda ndi kulemekeza mwamuna wake amathandiza kuti azigwirizana ndiponso kuti banja lonse likhale losangalala. Mkazi wotere amathandiza kuti aliyense akafika pakhomo mtima wake uzikhala m’malo ndiponso azimva kuti ndi wotetezeka. Mkazi wothandiza amakhala wamtengo wapatali kwa mwamuna wauzimu.​—Miy. 18:22.

Achinyamata Ayenera ‘Kuika Maso Awo pa Zinthu Zosaoneka’

15. Kodi achinyamata angathandize bwanji makolo kuti banja lonse ‘likhalebe maso’?

15 Kodi achinyamatanu mungathandize bwanji makolo kuti banja lonse ‘likhalebe maso’ mwauzimu? Taganizirani za mphoto imene Yehova wakulonjezani. Mwina pa nthawi imene munali ana aang’ono, makolo anu ankakuonetsani zithunzi zosonyeza mmene moyo udzakhalira m’Paradaiso. Pamene mumakula, iwo ankagwiritsa ntchito Baibulo ndiponso mabuku achikhristu kukuthandizani kuti muone mmene moyo wosatha udzakhalire m’dziko latsopano. Kuika maganizo anu pa kutumikira Yehova ndiponso kukhala ndi zolinga zogwirizana ndi zimenezi kungakuthandizeni ‘kukhalabe maso.’

16, 17. Kodi achinyamata angatani kuti apambane mpikisano wokalandira moyo?

16 Taganizirani mawu amene Paulo analankhula pa lemba la 1 Akorinto 9:24. (Werengani.) Muyenera kuthamanga n’cholinga choti mupambane m’mpikisano wokalandira moyo. Khalani ndi zolinga zimene zingakuthandizeni kupeza mphoto ya moyo wosatha. Anthu ambiri alephera kuika maso awo pa mphoto chifukwa chosokonezedwa ndi kufunafuna zinthu zakuthupi. Kumenekutu n’kupusa kwambiri! Munthu akamangokhalira kufunafuna chuma sapeza chimwemwe chenicheni. Zinthu zonse zimene mungagule ndi ndalama ndi zakanthawi chabe. Koma inu muyenera kuika maso anu pa “zinthu zosaoneka” chifukwa chakuti zinthu “zosaoneka n’zamuyaya.”​—2 Akor. 4:18.

17 “Zinthu zosaoneka” zikuphatikizapo madalitso amene Ufumu udzabweretse. Pa moyo wanu muyenera kukhala ndi zolinga zimene zingakuthandizeni kupeza madalitsowo. Munthu amapeza chimwemwe chenicheni akamagwiritsa ntchito moyo wake kutumikira Yehova. Munthu akamatumikira Mulungu woona amakhala ndi mwayi wokwaniritsa zolinga zing’onozing’ono ndiponso zikuluzikulu. * Kukhala ndi zolinga zauzimu zimene mungathe kuzikwaniritsa kungakuthandizeni kuti muziika maganizo anu pa kutumikira Mulungu ndipo mukatero mudzapeza mphoto ya moyo wosatha.​—1 Yoh. 2:17.

18, 19. Kodi wachinyamata angadziwe bwanji ngati amakondadi choonadi?

18 Achinyamatanu, dziwani kuti chinthu choyamba chimene chingakuthandizeni kuti mupeze moyo wosatha ndicho kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kodi panopa muli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ine ndimakondadi zinthu zauzimu kapena ndimangozichita chifukwa chotsatira makolo anga? Kodi ndimayesetsa kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu? Kodi ndimayesetsa kuti pulogalamu yanga ya zinthu zauzimu monga kupemphera nthawi zonse, kuphunzira, kupezeka pa misonkhano ndiponso kulalikira, isasokonezeke? Kodi ndikuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu n’kumamuyandikira?’​—Yak. 4:8.

19 Ganizirani chitsanzo cha Mose. Ngakhale kuti ankakhala ndi anthu osalambira Yehova, iye anasankha kudziwika monga wolambira Yehova osati monga mdzukulu wa Farao. (Werengani Aheberi 11:24-27.) Achinyamata achikhristu, nanunso muyenera kuyesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika. Mukamachita zimenezi, mudzapeza chimwemwe chenicheni, moyo wabwino kwambiri panopa ndiponso mudzagwira “mwamphamvu moyo weniweniwo.”​—1 Tim. 6:19.

20. Pa mpikisano wokalandira moyo, kodi ndani amalandira mphoto?

20 M’mipikisano yakale munthu mmodzi yekha ndi amene ankapambana. Koma si mmene zilili ndi mpikisano wokalandira moyo. Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Anthu ambiri athamanga bwinobwino m’mbuyomu ndipo pali ena ambiri amene akuthamanga limodzi ndi inu. (Aheb. 12:1, 2) Munthu aliyense amene sataya mtima amalandira mphoto. Choncho yesetsani kuti mupambane.

21. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 ‘Tsiku la Yehova lalikulu ndiponso lochititsa mantha’ lidzafika ndithu. (Mal. 4:5) Tsiku limeneli siliyenera kufikira mabanja achikhristu modzidzimutsa. Choncho m’pofunika kuti aliyense m’banja azikwaniritsa udindo wake wa m’Malemba. Kodi mungachite zinthu zina ziti kuti mukhalebe maso mwauzimu ndiponso kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Mulungu? Nkhani yotsatira idzafotokoza zinthu zitatu zimene zingathandize kuti banja lonse lizichita bwino mwauzimu.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti mabanja achikhristu ‘akhalebe maso’?

• Kodi mwamuna angatsanzire bwanji M’busa Wabwino?

• Kodi mkazi wabwino angathandize bwanji mwamuna wake?

• Kodi achinyamata angathandize bwanji kuti banja lonse likhale maso mwauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Mkazi wothandiza amakhala wamtengo wapatali kwa mwamuna wauzimu