Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsatirani Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wabwino Kwambiri

Tsatirani Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wabwino Kwambiri

Tsatirani Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wabwino Kwambiri

ANTHU omwe amatsatira ulamuliro wa anthu amagwiritsidwa mwala. Koma si mmene zilili ndi anthu amene amatsatira ulamuliro wa Khristu. Yesu anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Ulamuliro wa Yesu ndi wotsitsimula komanso wolimbikitsa. Iye amaganizira kwambiri anthu otsika ndiponso oponderezedwa moti amawauza kuti abwere pansi pa goli lake lofewa. Ndiyeno kodi tingatsatire bwanji ulamuliro wa Yesu?

Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Pet. 2:21) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mapazi a Yesu? Tiyerekeze kuti muli m’gulu la anthu amene akufuna kudutsa pamalo amene atcherapo mabomba ndipo pa gululo ndi munthu mmodzi yekha amene akudziwa mmene mungadutsire bwinobwino osavulala. N’zosachita kufunsa kuti muzimutsatira mosamala kwambiri mwinanso kuponda pamene waponda. Nafenso kuti tikhale otetezeka, tiyenera kutsatira kwambiri chitsanzo cha Yesu pa moyo wathu. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kumvetsera ndiponso kutsatira mawu ake komanso kugwirizana ndi anthu omuimira.

Tizimvetsera Ndiponso Kutsatira Mawu Ake

Chakumapeto kwa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anati: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe. Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo.”​—Mat. 7:24, 25.

Yesu ananena kuti munthu amene amamvetsera mawu ake ndi kuwachita ndi “wochenjera.” Kodi timasonyeza kuti timalemekeza ndiponso timatsatira Khristu pomumvera ndi mtima wonse kapena timangotsatira malamulo a Yesu amene tikuona kuti ndi osavuta kuwatsatira? Yesu anati: “Ndimachita zinthu zomukondweretsa [Mulungu] nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Tiyeni tiziyesetsa kutsatira chitsanzo chake.

Atumwi anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yogonjera ulamuliro wa Khristu. Pa nthawi ina, Petulo anauza Yesu kuti: “Onani! Ife tinasiya zinthu zonse ndipo takhala tikukutsatirani.” (Maliko 10:28) Izi zikusonyeza kuti atumwi ankaona kuti ulamuliro wa Yesu ndi wapamwamba kwambiri moti analolera kusiya zinthu zawo n’cholinga choti amutsatire.​—Mat. 4:18-22.

Tizigwirizana ndi Anthu Oimira Khristu

Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anatchula njira ina imene tingatsatirire ulamuliro wake. Iye anati: “Wolandira aliyense amene ine ndamutuma walandiranso ine.” (Yoh. 13:20) Yesu ananena za odzozedwa amene amamuimira kuti ndi “abale” ake. (Mat. 25:40) Yesu ataukitsidwa n’kupita kumwamba, “abale” ake anasankhidwa kuti akhale akazembe “m’malo mwa Khristu” n’cholinga choti azipempha anthu kuti agwirizane ndi Yehova Mulungu. (2 Akor. 5:18-20) Kuti titsatire Khristu monga mtsogoleri wathu, tiyenera kugonjera “abale” ake.

Tingachite bwino kudzifunsa ngati timatsatira malangizo a pa nthawi yake ochokera m’Malemba amene timalandira m’mabuku athu ofotokoza Baibulo. Tikamaphunzira Malemba ndiponso kupezeka pa misonkhano ya mpingo, timakumbutsidwa mawu a Khristu. (2 Pet. 3:1, 2) Tikamadya nthawi zonse chakudya chauzimu chimenechi, timasonyeza kuti tikuyamikira chakudyachi ndi mtima wonse. Kodi tiyenera kutani tikalandira malangizo okhudza nkhani inayake mobwerezabwereza? Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amalangiza Akhristu kuti ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Nkhani imeneyi yakhala ikufotokozedwa mu Nsanja ya Olonda kwa zaka zoposa 100. Abale a Khristu akamalemba nkhani zimenezi ndiponso malangizo ena ochokera m’Malemba, amasonyeza kuti amatikonda ndiponso amafuna kuti tizikhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tikamamvera malangizo amenewa, timasonyeza kuti tikutsatira Yesu Khristu, yemwe ndi Mtsogoleri wabwino kwambiri.

Lemba la Miyambo 4:18 limati: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Mtsogoleri wathu Yesu akupita patsogolo nthawi zonse ndipo amasintha zinthu kuti zikhale bwino kwambiri. Njira ina imene tingasonyezere kugwirizana ndi “abale” a Khristu ndiyo kumvera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akasintha mfundo zina zochokera m’Malemba zimene anafotokoza m’mbuyomu.​—Mat. 24:45

Timasonyezanso kuti timagonjera “abale” a Khristu tikamagwirizana ndi oyang’anira amene aikidwa mu mpingo wachikhristu. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu.” (Aheb. 13:17) Mwachitsanzo, mkulu mu mpingo angatilangize za kufunika kochita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse kapena zokhudza utumiki wathu wakumunda. Kapenanso woyang’anira woyendayenda angatipatse malangizo ena ochokera m’Malemba okhudza moyo wathu wachikhristu. Tikamamvera malangizo amenewa ndi mtima wonse timasonyeza kuti tikutsatira Mtsogoleri wathu Yesu.

M’dzikoli mulibe atsogoleri abwino. Koma timatsitsimulidwa kwambiri tikamatsatira Khristu, yemwe ndi Mtsogoleri wachikondi. Tiyeni tiziyesetsa kumvera Mtsogoleri wathu ndiponso kugwirizana ndi anthu amene iye akuwagwiritsa ntchito masiku ano.

[Zithunzi patsamba 27]

Kodi mumatsatira malangizo a m’Malemba akuti musamangidwe m’goli ndi munthu wosakhulupirira?