“Woyang’anira Wabwino Ndiponso Mnzathu Wapamtima”
“Woyang’anira Wabwino Ndiponso Mnzathu Wapamtima”
JOHN (JACK) BARR, amene anali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamaliza moyo wake wa padziko lapansi Loweruka m’mawa pa December 4, 2010. Iye anali ndi zaka 97. Anthu amanena kuti anali “woyang’anira wabwino ndiponso mnzathu wapamtima.”
M’bale Barr anabadwira mumzinda wa Aberdeen ku Scotland. M’banja mwawo anabadwa ana atatu ndipo iye anali womaliza. Makolo ake onse anali odzozedwa. M’bale Barr ankakonda kukamba zinthu zabwino zimene zinkachitika m’banja lawo iye ali wamng’ono. Iye ankayamikira chitsanzo chabwino cha makolo ake omwe ankawakonda kwambiri.
Pamene ankakwanitsa zaka 13, iye ankavutika kwambiri kulankhula ndi anthu amene sakuwadziwa. Koma anayesetsa kuthana ndi vutoli moti tsiku lina, pa Lamlungu masana mu 1927, ali ndi zaka 14, anauza bambo ake kuti akufuna kupita nawo kukalalikira kunyumba ndi nyumba. Apa m’pamene anayambira kutumikira Yehova. Kuyambira pa tsiku limeneli mpaka pamene anamwalira, M’bale Barr wakhala akugwira mwakhama ntchito yolalikira uthenga wabwino.
Tsiku lina, mayi ake amene iye ankawakonda kwambiri anangotsala pang’ono kufa pa ngozi. Zimenezi zinamuchititsa M’bale Barr kuganizira mozama za cholinga cha moyo. Mu 1929, iye anadzipereka kwa Yehova koma mwayi wobatizidwa unapezeka mu 1934. Mu 1939 anaitanidwa ku Beteli mumzinda wa London ku England. Apa m’pamene anayambira utumiki wake wa nthawi zonse womwe wachita kwa zaka 71.
Mu 1960 pa October 29, M’bale Barr anakwatira Mildred Willett ndipo m’baleyu ankanena kuti uwu unali “ubwenzi wapadera kwambiri.” Mildred anali mpainiya wakhama ndiponso mmishonale. M’bale ndi Mlongo Barr ankadziwika kuti ndi banja la chitsanzo chabwino ndipo ankakondana kwambiri mpaka pamene Mildred anamaliza moyo wake wa padziko lapansi mu October, 2004. Kwa moyo wonse umene iwo anakhala pa banja, ankawerengera limodzi Baibulo tsiku lililonse.
Anthu onse amene ankamudziwa M’bale Barr amakumbukira kuti ankapereka malangizo abwino kwambiri. Nthawi zonse ankawapereka mogwira mtima, mwachifundo ndipo ankakhala ochokera m’Malemba. M’bale Barr anali wolimbikira ntchito, woyang’anira wachikondi ndi wokoma mtima komanso anali mnzathu wokhulupirika. Ndemanga zake, nkhani zake ndiponso mapemphero ake zinkasonyeza kuti iye anali kukondadi choonadi ndiponso kuti anali pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova.
Ngakhale kuti M’bale Barr tidzamusowa kwambiri, tikusangalala naye limodzi chifukwa walandira mphatso ya moyo wosafa. Iye ankaona kuti mphatso imeneyi ndi yamtengo wapatali kwambiri, ankakonda kukamba za mphatso imeneyi ndipo anali kuiyembekezera mwachidwi.—1 Akor. 15:53, 54. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mbiri ya moyo wa John E. Barr ikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1987, tsamba 26 mpaka 31.