Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Achinyamata Ayenera Kubatizidwa?

Kodi Achinyamata Ayenera Kubatizidwa?

Kodi Achinyamata Ayenera Kubatizidwa?

M’BALE wina ku Philippines dzina lake Carlos * ananena kuti, “Ndikusangalala kwambiri kuti mwana wanga wamkazi tsopano ndi mtumiki wa Yehova ndipo ndikudziwa kuti nayenso akusangalala.” M’bale wina wa ku Greece analemba kuti: “Ine ndi mkazi wanga tikusangalala kwambiri kuti ana athu atatu anabatizidwa kukhala Mboni za Yehova adakali aang’ono. Iwo akuchita bwino mwauzimu ndipo amakonda kutumikira Yehova.”

Makolo achikhristu amasangalala ana awo akabatizidwa, koma nthawi zina amaderanso nkhawa. Mlongo wina, amene mwana wake wamwamuna anabatizidwa, ananena kuti, “Ndinasangalala kwambiri koma ndinkaderanso nkhawa.” N’chifukwa chiyani iye ankasangalala ndiponso kudera nkhawa? Mlongoyo anapitiriza kuti, “Ndinazindikira kuti panopa mwana wangayo adzayankhadi mlandu kwa Yehova.”

Achinyamata onse ayenera kukhala ndi cholinga chotumikira Yehova monga Mboni zobatizidwa. Koma nthawi zina makolo oopa Mulungu angakhale ndi maganizo akuti, ‘Ndikudziwa kuti mwana wanga akuchita bwino mwauzimu, koma kodi angakanedi zoipa n’kukhalabe woyera pa maso pa Yehova?’ Makolo ena amadzifunsa kuti, ‘Ngati mwana wanga atayesedwa kuti ayambe kufunafuna chuma, kodi angapitirizebe kutumikira Mulungu mwakhama ndiponso mosangalala?’ Ndiyeno kodi ndi malangizo ati a m’Baibulo amene angathandize makolo kudziwa ngati mwana wawo ali woyenera kubatizidwa?

Choyamba, Ayenera Kukhala Wophunzira wa Khristu

Mawu a Mulungu satchula zaka zimene munthu ayenera kukhala nazo kuti abatizidwe koma amatchula zinthu zauzimu zomuyenereza. Yesu anauza otsatira ake kuti: ‘Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga ndiponso muziwabatiza.’ (Mat. 28:19) Choncho anthu amene amabatizidwa ndi amene ali kale ophunzira a Khristu.

Kodi kukhala wophunzira wa Khristu kumatanthauza chiyani? Buku la Insight on the Scriptures limanena kuti: “Kwenikweni mawu amenewa sanena za munthu amene amangokhulupirira ziphunzitso za Khristu koma amene amamutsatira mosamala kwambiri.” Kodi achinyamata aang’ono angakhale ophunzira enieni a Khristu? Mlongo wina, amene watumikira monga mmishonale ku Latin America kwa zaka zoposa 40, analemba zotsatirazi ponena za iyeyo ndi azichemwali ake awiri: “Tinali titakula ndithu moti tinkatha kudziwa kuti tikufuna kutumikira Yehova komanso kukhala m’Paradaiso. Kudzipereka kwathu kwa Mulungu kunatithandiza kuti tikhale olimba tikakumana ndi mayesero pamene tinali achinyamata. Sitinong’oneza bondo kuti tinadzipereka kwa Mulungu tili aang’ono.”

Kodi mungadziwe bwanji ngati mwana wanu ali wophunzira wa Khristu? Baibulo limanena kuti: “Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” (Miy. 20:11) Tiyeni tione zinthu zina zimene zimasonyeza kuti wachinyamata ‘akupita patsogolo’ monga wophunzira wa Khristu.​—1 Tim. 4:15.

Umboni Wosonyeza Kuti Munthu Ndi Wophunzira wa Khristu

Kodi mwana wanu amakumverani? (Akol. 3:20) Kodi amagwira ntchito zapakhomo? Ponena za Yesu ali ndi zaka 12, Baibulo limati: “Anapitiriza kuwamvera [makolo ake].” (Luka 2:51) N’zoona kuti masiku ano palibe mwana amene amamvera makolo ake pa chilichonse. Koma Akhristu oona ayenera ‘kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.’ Choncho, achinyamata amene akufuna kubatizidwa ayenera kudziwika kuti amamvera makolo.​—1 Pet. 2:21.

Taganizirani mafunso awa: Kodi mwana wanu amakonda kulowa mu utumiki posonyeza kuti ‘akufunafuna Ufumu choyamba’? (Mat. 6:33) Kodi iye amafunadi kuuza anthu ena uthenga wabwino kapena mumachita kumulimbikitsa kwambiri kuti alowe nanu mu utumiki wakumunda ndiponso kumuuza kuti azilankhula ndi eni nyumba? Kodi amazindikira udindo wake monga wofalitsa wosabatizidwa? Kodi amafunitsitsa kubwerera kwa anthu amene asonyeza chidwi? Kodi iye amauza anzake a kusukulu ndiponso aphunzitsi kuti ndi wa Mboni za Yehova?

Kodi amaona kuti kusonkhana n’kofunika? (Sal. 122:1) Kodi amakonda kupereka ndemanga pa Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso pa Phunziro la Baibulo la Mpingo? Kodi amawerenga kapena kukamba nkhani ndi mtima wonse mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu?​—Aheb. 10:24, 25.

Kodi mwana wanu amapewa kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa kusukulu kapena kulikonse n’cholinga choti apitirize kukhala ndi makhalidwe abwino? (Miy. 13:20) Kodi amakonda mtundu wanji wa nyimbo, mafilimu, mapulogalamu a pa TV kapena masewera a pa kompyuta? Nanga amakonda kuwerenga kapena kuonera zinthu zotani pa Intaneti? Kodi mawu ndi zochita zake zimasonyeza kuti amafuna kutsatira mfundo za m’Baibulo?

Kodi mwana wanu amalidziwa bwino Baibulo? Kodi amatha kufotokoza zimene waphunzira pa Kulambira kwa Pabanja? Kodi angathe kufotokoza ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo? (Miy. 2:6-9) Kodi amasangalala kuwerenga Baibulo ndiponso kuphunzira mabuku ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? (Mat. 24:45) Kodi amafunsa mafunso okhudza Baibulo?

Kudzifunsa mafunso amenewa kungakuthandizeni kudziwa ngati mwana wanu akupita patsogolo mwauzimu. Pambuyo poganizira mafunso amenewa, mwina mungaone kuti akufunika kusintha zinthu zina asanabatizidwe. Koma ngati moyo wake ukusonyeza kuti ndi wophunzira wa Yesu ndipo wadziperekadi kwa Mulungu, mukhoza kumulola kuti abatizidwe.

Achinyamata Akhoza Kutamanda Yehova

Pali atumiki a Mulungu ambiri amene anasonyeza kukhulupirika adakali aang’ono. Taganizirani za Yosefe, Samueli, Yosiya ndiponso Yesu. (Gen. 37:2; 39:1-3; 1 Sam. 1:24-28; 2:18-20; 2 Mbiri 34:1-3; Luka 2:42-49) Ana aakazi a Filipo amene ankanenera ayenera kuti anaphunzitsidwa kuyambira ali ana.​—Mac. 21:8, 9.

M’bale wina ku Greece ananena kuti: “Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 12. Sindinanong’onezepo bondo chifukwa cha zimenezi. Kuchokera pa nthawi imene ndinabatizidwayi papita zaka 24 ndipo ndakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 23. Kukonda Yehova n’kumene kwandithandiza kuti ndilimbane ndi mayesero a pa unyamata. Pa nthawi imene ndinali ndi zaka 12 sindinkadziwa Malemba ngati mmene ndikuwadziwira panopa. Komabe ndinkadziwa kuti ndimakonda Yehova ndipo ndinkafuna kumutumikira mpaka kalekale. Ndikusangalala kuti wandithandiza kupitiriza kumutumikira.”

Munthu amene akusonyeza kuti ndi wophunzira weniweni wa Yesu ayenera kubatizidwa, kaya akhale wamng’ono kapena wamkulu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.” (Aroma 10:10) Wophunzira wa Khristu wamng’ono akabatizidwa amakwaniritsa chinthu chachikulu kwambiri pa moyo wake ndiponso wa makolo ake. Musalole kuti chilichonse chikulepheretseni inuyo kapena ana anu kupeza chisangalalo chimenechi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena.

[Bokosi patsamba 5]

Tiziona Ubatizo M’njira Yoyenera

Makolo ena amaona kuti ubatizo wa mwana wawo ndi chinthu chabwino koma amaonanso kuti pangakhale ngozi yake. Iwo amamva ngati mmene munthu angamvere mwana wake akaphunzira kuyendetsa galimoto. Koma kodi kubatizidwa kapena kuchita utumiki wopatulika kungasokoneze moyo wa munthu? Baibulo limayankha kuti ayi. Lemba la Miyambo 10:22 limati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” Timoteyo ali wachinyamata, Paulo anamulembera kuti: “Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.”​—1 Tim. 6:6.

N’zoona kuti kutumikira Yehova si kophweka. Yeremiya anakumana ndi mavuto ambiri pa nthawi imene anali mneneri wa Mulungu. Koma pa nkhani ya kulambira Mulungu woona, iye analemba kuti: “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa makamu.” (Yer. 15:16) Yeremiya ankadziwa kuti kutumikira Mulungu n’kumene kunkamuthandiza kukhala wosangalala. Koma dziko la Satanali limachititsa kuti tizizunzika. Makolo ayenera kuthandiza ana awo kuti azindikire zimenezi.​—Yer. 1:19.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Kodi Mwana Wanga Asabatizidwe Panopa?

Nthawi zina, zimatheka kuti mwana akuyenerera kubatizidwa koma makolo ake amasankha kuti ayembekeze kaye. Kodi angachite zimenezi chifukwa chiyani?

Ndimaopa kuti mwana wanga akabatizidwa, mwina akhoza kudzachita tchimo lalikulu n’kuchotsedwa mu mpingo. Kodi ndi bwino kuganiza kuti wachinyamata amene akuzengereza kubatizidwa sadzayankha mlandu kwa Mulungu chifukwa cha zochita zake? Solomo anauza achinyamata kuti: ‘Dziwani kuti Mulungu woona adzakuweruzani chifukwa cha zochita zanu.’ (Mlal. 11:9) Popanda kuganizira za msinkhu wa munthu, Paulo anakumbutsa tonsefe kuti: “Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”​—Aroma 14:12.

Aliyense amene akulambira Yehova, kaya wobatizidwa kapena wosabatizidwa, adzayankha mlandu kwa Mulungu. Sitiyenera kuiwala kuti Yehova amateteza atumiki ake ndipo ‘sadzalola kuti ayesedwe kufika pamene sangapirire.’ (1 Akor. 10:13) Iwo ‘akakhalabe oganiza bwino’ ndiponso akamayesetsa kulimbana ndi mayesero, Mulungu adzawathandiza. (1 Pet. 5:6-9) Mlongo wina analemba kuti: “Ana amene anabatizidwa amakhala ndi zifukwa zambiri zopewera zinthu zoipa za m’dzikoli. Mwana wanga wamwamuna, amene anabatizidwa ali ndi zaka 15, amaona kuti kubatizidwa kumateteza munthu. Mwanayo anati, ‘Ukabatizidwa suganiza zochita zinthu zosemphana ndi lamulo la Yehova.’ Kubatizidwa kumathandiza kwambiri kuti munthu azichita zinthu zolungama.”

Ngati ana anu munawaphunzitsa kumvera Yehova ndiponso ngati mumawapatsa chitsanzo chabwino, mukhoza kukhala otsimikiza kuti adzapitiriza kumvera Yehova atabatizidwa. Lemba la Miyambo 20:7 limati: “Munthu wolungama amayenda ndi mtima wosagawanika, ndipo ana ake amakhala odala.”

Ndimafuna kuti mwana wanga achite kaye zinthu zina asanabatizidwe. Achinyamata afunika kuphunzira kugwira ntchito kuti kutsogolo adzathe kudzisamalira okha. Koma kulimbikitsa ana kuti aziika patsogolo maphunziro kapena kupeza chuma m’malo mowalimbikitsa kuika kulambira koona patsogolo, kungaike pa ngozi moyo wawo wauzimu. Yesu anayerekezera mawu a Ufumu ndi mbewu. Pofotokoza za “mbewu” zimene sizikula, iye ananena kuti: “Zimene zafesedwa paminga, ndi munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula, ndipo iye amakhala wosabala zipatso.” (Mat. 13:22) Wachinyamata akamalimbikitsidwa kuika patsogolo zinthu za m’dzikoli m’malo mwa zinthu zauzimu, angasiye kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu.

M’bale wina amene watumikira monga mkulu kwa nthawi yaitali anafotokoza za achinyamata amene akuyenera kubatizidwa koma makolo awo akuwaletsa. Iye anati: “Kuletsa mwana kuti abatizidwe kungachititse mwanayo kubwerera m’mbuyo pa zinthu zauzimu ndipo angakhumudwe.” Pa nkhani yomweyi, woyang’anira woyendayenda wina ananena kuti: “Wachinyamata angayambe kumadzikayikira pa zinthu zauzimu. Chifukwa cha zimenezi, iye akhoza kuyamba kuchita zinthu zina m’dzikoli n’cholinga choti asiye kudzikayikira.”

[Chithunzi]

Kodi ndi bwino kuika patsogolo maphunziro a ku yunivesite?

[Chithunzi patsamba 3]

Wachinyamata wamng’ono akhoza kusonyeza kuti ndi wophunzira wa Yesu

[Zithunzi patsamba 3]

Kukonzekera misonkhano ndiponso kuyankha nawo

[Chithunzi patsamba 4]

Kumvera makolo

[Chithunzi patsamba 4]

Kulalikira

[Chithunzi patsamba 4]

Kupemphera payekha