Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi “Moyo Wopambana”?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi “Moyo Wopambana”?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi “Moyo Wopambana”?

ALIYENSE amafuna kukhala ndi moyo wabwino. Anthu ena zinthu zikuwayendera bwino kwambiri moti apeza ndalama zambiri ndiponso atchuka. Ena akhala akuyesetsa kupeza moyo wabwino koma alephera momvetsa chisoni.

Kuti munthu akhale ndi moyo wabwino ayenera kuika zinthu zofunika patsogolo pa moyo wake. Ayeneranso kugwiritsa ntchito bwino nthawi, mphamvu ndiponso nzeru zake.

Akhristu ambiri aona kuti kuchita zambiri mu utumiki kwawathandiza kukhala osangalala. Kuchita utumiki wa nthawi zonse kwathandiza achinyamata ndiponso achikulire kukhala ndi moyo wabwino. Komabe anthu ena amaona kuti utumiki ndi wosasangalatsa kwenikweni choncho amaika zolinga zina patsogolo. N’chifukwa chiyani amakhala ndi maganizo amenewa? Kodi mungatani kuti musaiwale zinthu zimene ndi zofunika kwambiri? Kodi mungatani kuti mukhale ndi “moyo wopambana”?​—Yos. 1:8.

Zochitika Zina za Kusukulu Ndiponso Zosangalatsa

Achinyamata achikhristu ayenera kugawa bwino nthawi kuti zochitika zina zisasokoneze kutumikira Mulungu woona. Achinyamata amene amachita zimenezi ndi amene adzakhale ndi moyo wabwino ndipo tiyenera kuwayamikira.

Koma Akhristu ena achinyamata amatengeka kwambiri ndi zochitika zina za kusukulu ndiponso zosangalatsa. Zinthu zimenezi pazokha si zolakwika. Komabe achinyamatawa ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingawononge nthawi yaitali bwanji pochita zinthu zimenezi? Kodi anthu amene ndizicheza nawo ndi otani? Kodi anthu amene ndizichita nawo zinthuzi, ali ndi mtima wotani? Kodi ndiyamba kuika patsogolo zinthu ziti?’ Mutha kuona kuti munthu akhoza kutengeka kwambiri ndi zinthu zimenezi moti sangakhale ndi nthawi kapena mphamvu zochitira zinthu zolimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Choncho ndi bwino kuika zinthu zofunika patsogolo.​—Aef. 5:15-17.

Taganizirani za m’bale wina dzina lake Wiktor. * Iye ananena kuti: “Ndinalowa timu ya mpira ndili ndi zaka 12. Patapita nthawi, ndinalandira mphoto zambirimbiri. Ndikanatha kukhala munthu wotchuka kwambiri.” Kenako Wiktor anamva chisoni atazindikira kuti masewerawa ankasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. Tsiku lina, anayamba kugona akuwerenga Baibulo. Iye anazindikiranso kuti sakusangalala ndi utumiki wakumunda. Wiktor ananena kuti: “Ndinkakhala wotopa kwambiri chifukwa cha masewerawa ndipo ndinazindikiranso kuti ndafooka mwauzimu. Ndinaona kuti sindinkachitanso zinthu zimene ndinayenera kuchita.”

Maphunziro Apamwamba

Mkhristu ali ndi udindo wa m’Malemba wosamalira banja lake choncho ayenera kupezera banja lake zinthu zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Komabe kuti akwaniritse udindo umenewu, kodi ayeneradi kupita ku koleji kapena ku yunivesite?

Ndi bwino kuganizira mmene maphunziro apamwamba angasokonezere ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuti timvetse bwino nkhaniyi, tiyeni tione chitsanzo cha m’Baibulo.

Baruki anali mlembi wa mneneri Yeremiya. Pa nthawi ina, iye anasiya kuganizira mwayi wake wotumikira Yehova n’kumafuna moyo wapamwamba. Yehova anaona zimenezi ndipo kudzera mwa Yeremiya anamuchenjeza kuti: “Ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna.”​—Yer. 45:5.

Kodi “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafunafuna zinali ziti? Mwina ankafuna kukhala wotchuka mu Yuda kapena ankafuna kupeza chuma. Kaya zinthu zinali bwanji, iye anasiya kuganizira zinthu zauzimu, zomwe ndi zofunika kwambiri. (Afil. 1:10) Koma Baruki anamvera chenjezo la Yehova kudzera mwa Yeremiya ndipo anapulumutsidwa.​—Yer. 43:6.

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani imeneyi? Uphungu umene Baruki analandira umasonyeza kuti iye anali ndi vuto linalake. Iye anali kufunafuna zinthu zazikulu. Kodi inuyo mumatha kupeza zinthu zofunika pa moyo? Ngati zili choncho, kodi ndi bwino kuwononga nthawi, ndalama komanso mphamvu zanu pochita maphunziro apamwamba chifukwa chongotsatira zofuna zanu, za makolo anu kapena za achibale anu?

Taganizirani za m’bale wina dzina lake Grzegorz, yemwe amagwira ntchito yolemba mapulogalamu a pakompyuta. Atalimbikitsidwa ndi anzake kuntchito, anayamba maphunziro owonjezera amene ankafuna nthawi yambiri. Atayamba maphunzirowo, anapeza kuti alibiretu nthawi yochita zinthu zauzimu. Iye anati: “Sindinkasangalala chifukwa chikumbumtima changa chinali kundivutitsa. Ndinkalephera kukwaniritsa zolinga zauzimu zimene ndinali nazo.”

Kutanganidwa Kwambiri ndi Ntchito

Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu oona kukhala antchito kapena mabwana abwino ndiponso olimbikira ntchito. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova, osati anthu.” (Akol. 3:22, 23) Ngakhale kuti kulimbikira ntchito n’kofunika, pali chinthu china chimene n’chofunika kwambiri. Chinthu chake ndicho kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wathu. (Mlal. 12:13) Mkhristu akayamba kutanganidwa kwambiri ndi ntchito yake, angasiye kuika zinthu zauzimu patsogolo.

Mkhristu amene wayamba kutanganidwa kwambiri ndi ntchito amatopa kwambiri moti sangachite zinthu zothandiza iyeyo kapena banja lake kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Mfumu Solomo inaona kuti nthawi zambiri “kugwira ntchito mwakhama” kumakhala ngati “kuthamangitsa mphepo.” Ngati Mkhristu akutanganidwa nthawi zonse ndi ntchito akhoza kumasowa mtendere wa m’maganizo. Munthu wotere angayambe kukhala kapolo wa ntchito mpaka kufika potopa kwambiri moti sangapitirizenso kugwira bwino ntchitoyo. Kodi munthu wotereyu ‘angasangalale ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama’? (Mlal. 3:12, 13; 4:6) Nanga angathe kuganiza bwino ndiponso kukhala ndi mphamvu zokwanira kuti asamalire zinthu zofunika kwambiri monga udindo wake m’banja komanso zinthu zauzimu?

Janusz, yemwe amakhala kum’mawa kwa Ulaya, anayamba kutanganidwa kwambiri ndi ntchito yake. Iye anati: “Anthu akunja ankandisirira kwambiri chifukwa ndinali waluso ndipo ndinkamaliza mwachangu ntchito yanga. Koma ndinafooka mwauzimu ndiponso ndinasiya kulowa mu utumiki wakumunda. Kenako ndinasiyanso kusonkhana. Ndinayamba kunyada kwambiri moti ndinasiya kumvera uphungu umene akulu anali kundipatsa ndiponso ndinasiya kucheza ndi anthu mu mpingo.”

Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wopambana

Takambirana zinthu zitatu zimene Mkhristu angatanganidwe nazo mpaka kufika polephera kuchita zinthu zauzimu. Kodi mumatanganidwa ndi chilichonse cha zinthu zitatuzi? Ngati ndi choncho, tiyeni tikambirane mafunso, malemba ndiponso mfundo zimene zingakuthandizeni kuona ngati mungakhale ndi moyo wabwino.

Zochitika zina za kusukulu ndiponso zosangalatsa: Kodi mumatanganidwa ndi zinthu zimenezi? Kodi zikukuwonongerani nthawi imene munkagwiritsa ntchito pa zinthu zauzimu? Kodi panopa simusangalala kwambiri kucheza ndi Akhristu anzanu? Ngati ndi choncho mungachite bwino kutsanzira Mfumu Davide yemwe anachonderera Yehova kuti: “Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo.”​—Sal. 143:8.

Woyang’anira woyendayenda ndi amene anathandiza Wiktor amene tamutchula kale uja. Woyang’anira woyendayendayo anamuuza kuti: “Zolankhula zako zikusonyeza kuti umakonda kwambiri mpira.” Wiktor anati: “Zimenezi zinandikhudza kwambiri. Ndinazindikira kuti ndatayirira kwambiri. Pasanapite nthawi, ndinasiya kucheza ndi anzanga aja n’kupeza anzanga ena mu mpingo.” Masiku ano, Wiktor akutumikira Yehova mwakhama mu mpingo wake. Iye amalimbikitsa achinyamata kuti: “Muzifunsa anzanu, makolo anu kapena akulu mu mpingo ngati akuona kuti zochitika za kusukulu zikukulepheretsani kuyandikira Yehova.”

Mungachite bwino kuuza akulu mu mpingo wanu kuti mukufuna kuchita zambiri potumikira Mulungu. Mwina mungathandize okalamba amene angafune thandizo kapena munthu wocheza naye. Mungawathandize kugula zinthu kapena kugwira ntchito zapakhomo. Kaya ndinu wamkulu kapena wamng’ono, mukhoza kuchita utumiki wa nthawi zonse. Mukakhala mu utumiki mukhoza kuuza ena zinthu zimene zimakuchititsani kukhala wosangalala.

Maphunziro Apamwamba: Yesu anachenjeza za ‘kudzifunira tokha ulemerero.’ (Yoh. 7:18) Kaya musankha zotani pa nkhani ya maphunziro, muyenera ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’​—Afil. 1:9, 10.

Grzegorz, wolemba mapulogalamu apakompyuta uja, anasintha zinthu zina pa moyo wake. Iye anati: “Ndinatsatira malangizo amene akulu anandipatsa ndipo ndinayamba moyo wosalira zambiri. Ndinazindikira kuti sindinkafunikira maphunziro owonjezera. Zimenezi zikanangondiwonongera nthawi ndi mphamvu zanga.” Grzegorz anayamba kuchita zambiri mu mpingo. Patapita nthawi, anapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, imene tsopano imatchedwa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Anasankha ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi yake’ kuti aphunzitsidwe ndi Mulungu.​—Aef. 5:16.

Ntchito: Kodi mukutanganidwa ndi ntchito moti simukhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu? Kodi mumakhala ndi nthawi yokwanira yolankhulana ndi banja lanu? Kodi mukuyesetsa kuti muzikamba bwino nkhani mu mpingo? Kodi mumakambirana nkhani zolimbikitsa pocheza ndi anzanu? Muyenera kutsatira malangizo akuti: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake.” Mukatero, Yehova adzakudalitsani kwambiri ndipo mudzasangalala ‘chifukwa choti mwagwira ntchito mwakhama.’​—Mlal. 2:24; 12:13.

Janusz, yemwe tamutchula kale uja, sizinamuyendere bwino pa ntchito yake. Iye sanali kupeza ndalama ndiponso anali ndi ngongole yaikulu. Kenako iye anabwerera kwa Yehova. Janusz anasintha zinthu pa moyo wake ndipo panopa akutumikira monga mpainiya wokhazikika komanso mkulu mu mpingo. Iye anati: “Ndikamakhutira ndi zinthu zofunika pa moyo n’kumachita khama pa zinthu zauzimu, ndimakhala ndi mtendere m’maganizo ndiponso mumtima.”​—Afil. 4:6, 7.

Muyenera kupeza nthawi yoonanso bwinobwino zolinga zanu ndiponso zinthu zimene mumaika patsogolo. Kutumikira Yehova n’kumene kungakuthandizeni kukhala ndi moyo wabwino kwambiri. Choncho muziika kutumikira Yehova patsogolo pa moyo wanu.

Mwina muyenera kusintha kapena kusiya zinthu zina zosafunika kwambiri n’cholinga choti muzindikire “chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Mukhoza kukhala ndi “moyo wopambana” mukamatumikira Yehova ndi mtima wonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Tasintha mayina ena.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 31]

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Moyo Wopambana?

Popeza kuti pali zinthu zambiri zimene mukhoza kutanganidwa nazo, kodi mungatani kuti musasiye kuika zinthu zofunika patsogolo? Pezani nthawi yoganizira mafunso otsatirawa kuti muone bwino zolinga zanu ndiponso zimene mumaika patsogolo pa moyo wanu.

ZOCHITIKA ZINA ZA KUSUKULU NDIPONSO ZOSANGALATSA

▪ Kodi anthu amene muzichita nawo zinthuzi, ali ndi mtima wotani?

▪ Kodi muziwononga nthawi yochuluka bwanji?

▪ Kodi muyamba kuika zinthu zimenezi patsogolo pa moyo wanu?

▪ Kodi zikukuwonongerani nthawi imene munkagwiritsa ntchito pa zinthu zauzimu?

▪ Kodi anthu amene muzicheza nawo ndi otani?

▪ Kodi mumakonda kucheza ndi anthu amenewa kuposa Akhristu anzanu?

MAPHUNZIRO APAMWAMBA

▪ Kodi inuyo mumatha kupeza zinthu zofunika pa moyo? Ngati zili choncho, kodi ndi bwino kuwononga nthawi, ndalama komanso mphamvu zanu pochita maphunziro apamwamba?

▪ Kuti mupeze zinthu zofunika pa moyo, kodi muyeneradi kupita ku koleji kapena ku yunivesite?

▪ Kodi zizikupatsani mpata wopita ku misonkhano?

▪ Kodi mwatsimikizira kuti “zinthu zofunika kwambiri ndi ziti”?

▪ Kodi mukufunika kulimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Yehova angakuthandizeni kupeza zinthu zofunika pa moyo?

NTCHITO

▪ Kodi zimene mwasankha zimakuthandizani ‘kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti mwagwira ntchito mwakhama’?

▪ Kodi mungathe kuganiza bwino ndiponso kukhala ndi mphamvu zokwanira kuti musamalire zinthu zofunika kwambiri monga udindo wanu m’banja komanso zinthu zauzimu?

▪ Kodi mumakhala ndi nthawi yokwanira yolankhulana ndi banja lanu?

▪ Kodi mukutanganidwa ndi ntchito moti simukhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu?

▪ Kodi ntchito yanu ikukulepheretsani kukamba bwino nkhani mu mpingo?

[Chithunzi patsamba 30]

Yehova anachenjeza Baruki kuti asamafune moyo wapamwamba