Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”

“Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”

“Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”

“Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.”​—1 PET. 5:2.

1. Kodi zinthu zinali bwanji kwa Akhristu pa nthawi imene Petulo ankalemba kalata yake yoyamba?

KUTATSALA nthawi yochepa kuti Mfumu Nero ayambe kuzunza Akhristu ku Roma, mtumwi Petulo analemba kalata yake yoyamba. Cholinga chake chinali kulimbikitsa Akhristu anzake. Pa nthawiyi, Mdyerekezi ‘anali kuyendayenda uku ndi uku’ kuti ameze Akhristu. Koma kuti alimbane naye, Akhristuwo anafunika ‘kukhalabe oganiza bwino’ ndiponso ‘kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.’ (1 Pet. 5:6, 8) Iwo anafunikanso kukhala ogwirizana. Sanafunikire ‘kulumana ndi kudyana okhaokha’ pakuti kuchita zimenezi kukanachititsa kuti ‘awonongane.’​—Agal. 5:15.

2, 3. Kodi tiyenera kulimbana ndi ndani ndipo tikambirana mfundo ziti m’nkhani ino ndiponso yotsatira?

2 Umu ndi mmene zililinso masiku ano. Mdyerekezi akufunafuna mpata woti atimeze. (Chiv. 12:12) “Chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko” chatsala pang’ono kufika. (Mat. 24:21) Akhristu oyambirira anafunika kusamala kuti asamakangane. Nafenso masiku ano tiyenera kupewa mikangano. Kuti zimenezi zitheke, nthawi zina timafunika thandizo la akulu mu mpingo.

3 Tiyeni tione zimene akulu angachite kuti aziyamikira kwambiri mwayi umene ali nawo woweta ‘gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwawo.’ (1 Pet. 5:2) Kenako tiona njira zabwino zowetera nkhosazi. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene mpingo ‘ungalemekezere anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati pawo ndiponso kutsogolera’ gulu la nkhosa. (1 Ates. 5:12) Kukambirana mfundo zimenezi kutithandiza kuti titsutse mwamphamvu Mdani wathu wamkulu pozindikira kuti iye ndi amene tikulimbana naye.​—Aef. 6:12.

Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu

4, 5. Kodi akulu ayenera kuona bwanji gulu la nkhosa? Perekani chitsanzo.

4 Petulo analimbikitsa akulu mu mpingo wa Akhristu oyambirira kuti aziona gulu la nkhosa limene lasiyidwa m’manja mwawo mmene Mulungu amalionera. (Werengani 1 Petulo 5:1, 2.) Ngakhale kuti anthu ankaona kuti Petulo anali mzati mu mpingo, iye sankalankhula ndi akulu ngati kuti iye ndi wapamwamba. M’malomwake ankawalangiza monga akulu anzake. (Agal. 2:9) Bungwe Lolamulira limalangiza akulu mu mpingo kuti aziyesetsa kukwaniritsa udindo wawo waukulu woweta gulu la nkhosa za Mulungu. Limachita zimenezi lili ndi maganizo ngati a Petulo

5 Mtumwiyu analemba kuti akulu ayenera ‘kuweta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwawo.’ Iwo amafunikira kuzindikira kuti nkhosazo ndi za Yehova ndi Yesu Khristu. Analembanso kuti akulu adzayankha mlandu chifukwa cha zimene amachita poyang’anira nkhosa za Mulungu. Tayerekezani kuti mnzanu wapamtima wakupemphani kuti mum’sungire ana ake iye akachoka. Kodi simungawasamalire bwino ndiponso kuwapatsa chakudya? Ngati mwana wina wadwala, kodi simungapite naye kuchipatala? Mofanana ndi zimenezi, akulu mu mpingo ayenera ‘kuweta mpingo, umene Mulungu anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.’ (Mac. 20:28) Akulu amakumbukira kuti nkhosa iliyonse inagulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Khristu Yesu. Podziwa kuti adzayankha mlandu, iwo amadyetsa, kuteteza ndiponso kusamalira gulu la nkhosa.

6. Kodi abusa akale anali ndi udindo wotani?

6 Taganizirani za udindo umene abusa akale anali nawo. Abusawo ankafunika kupirira kutentha masana ndiponso kuzizira usiku kuti asamalire nkhosa zawo. (Gen. 31:40) Nthawi zina ankaika moyo wawo pachiswe chifukwa cha nkhosazo. Davide ali mnyamata anateteza nkhosa zake kwa zilombo zolusa monga mkango ndi chimbalangondo. Pofotokoza zimene anachita ndi zilombozi, Davide anati: “Ndinagwira ndevu zake, n’kuchikantha ndi kuchipha.” (1 Sam. 17:34, 35) Kumeneku kunali kulimba mtima kwabasi chifukwa chimbalangondocho chikanatha kumupha mosavuta. Koma iye sanachite mantha kuteteza nkhosa zake.

7. Kodi akulu mophiphiritsa angakwatule bwanji nkhosa m’kamwa mwa Satana?

7 Masiku ano, akulu ayenera kusamala ndi Mdyerekezi yemwe ali ngati mkango wolusa. Kuti achite zimenezi angafunike kulimba mtima kuti mophiphiritsa akwatule nkhosa m’kamwa mwa Mdyerekezi. Akulu ayenera kugwira ndevu za chilombocho kuti ateteze nkhosa. Iwo ayenera kukambirana ndi abale amene mosazindikira ayamba kukopeka ndi misampha ya Satana. (Werengani Yuda 22, 23.) Akulu sangakwanitse kuchita zimenezi popanda thandizo la Yehova. Amasamalira mwachikondi nkhosa yovulala pomanga mabala ake n’kuipaka mankhwala ochepetsa ululu, omwe ndi Mawu a Mulungu.

8. Kodi akulu amatsogolera kuti nkhosa, ndipo amachita bwanji zimenezi?

8 Abusa akale ankatsogoleranso nkhosa kumalo amene kunali msipu ndi madzi okwanira. Nawonso akulu amatsogolera nkhosa ku mpingo ndiponso kuzilimbikitsa kuti zizisonkhana nthawi zonse. Amachita zimenezi kuti nkhosazo zizidya “chakudya pa nthawi yoyenera.” (Mat. 24:45) Akulu angafunike kukhala ndi nthawi yambiri kuti athandize anthu odwala mwauzimu kuti azilandira chakudya chauzimu cha m’Mawu a Mulungu. Nkhosa imene yasochera ingafune kubwerera m’gulu. M’malo mowopseza anthu oterewa, akulu ayenera kuwafotokozera mfundo za m’Malemba mokoma mtima ndi kuwasonyeza mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wawo.

9, 10. Kodi akulu angathandize bwanji anthu odwala mwauzimu?

9 Kodi mukadwala mumafuna dokotala wotani? Kodi mungakonde dokotala amene amangomvetsera pang’ono n’kukulemberani mankhwala pofuna kuthana nanu kuti aonane ndi wodwala wina? Kapena kodi mungakonde dokotala amene amakumvetserani mofatsa, amafotokoza bwino matenda anu ndiponso kukuuzani mankhwala amene angakuthandizeni?

10 Mofanana ndi zimenezi, akulu ayenera kumvetsera bwino munthu amene akudwala mwauzimu ndiponso kusamalira mabala ake. Zimenezi tingaziyerekezere ndi “kumupaka mafuta m’dzina la Yehova.” (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Mofanana ndi mafuta a basamu a ku Giliyadi, Mawu a Mulungu angachiritse munthu wodwala mwauzimu. (Yer. 8:22; Ezek. 34:16) Munthu wofooka akagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake akhoza kuyambiranso kutumikira Mulungu bwinobwino. Akulu amathandiza kwambiri akamvetsera pamene munthu wodwala mwauzimu akufotokoza vuto lake kenako n’kupemphera naye.

Osati Mokakamizika Koma Mofunitsitsa

11. Kodi n’chiyani chimalimbikitsa akulu kuweta gulu la nkhosa za Mulungu mofunitsitsa?

11 Kenako Petulo anakumbutsa akulu zoyenera kuchita ndiponso zoyenera kupewa akamaweta nkhosa. Akulu ayenera kuweta gulu la nkhosa za Mulungu “osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.” Kodi n’chiyani chimalimbikitsa akulu kuti atumikire abale awo mofunitsitsa? Choyamba, tiyenera kudziwa chimene chinalimbikitsa Petulo kuweta ndiponso kudyetsa nkhosa za Yesu. Kukonda kwambiri Ambuye n’kumene kunamulimbikitsa. (Yoh. 21:15-17) Chifukwa cha chikondi, akulu ‘sakhala moyo wongodzisangalatsa okha, koma amakhala moyo wosangalatsa anthu amene Khristu anawafera.’ (2 Akor. 5:14, 15) Chifukwa chokonda Yesu, Mulungu ndiponso abale awo, akulu amagwiritsa ntchito mphamvu zawo, zinthu zimene ali nazo ndiponso nthawi yawo potumikira gulu la nkhosa. (Mat. 22:37-39) Amadzipereka potumikira nkhosa osati monyinyirika, koma mofunitsitsa.

12. Kodi mtumwi Paulo anadzipereka mpaka pati?

12 Kodi akulu ayenera kudzipereka mpaka pati? Posamalira nkhosa, iwo amatsanzira mtumwi Paulo, yemwe ankatsanzira Yesu. (1 Akor. 11:1) Chifukwa chokonda kwambiri abale a ku Tesalonika, Paulo ndi anzake anali okonzeka kuwapatsa ‘osati uthenga wa Mulungu wokha ayi, komanso miyoyo yawo yeniyeniyo.’ Iwo anachita zinthu modekha “monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira ana ake.” (1 Ates. 2:7, 8) Paulo ankadziwa mmene mayi woyamwitsa amaonera ana ake. Iye amawachitira chilichonse ngakhale kudzuka pakati pa usiku kuti awayamwitse.

13. Kodi akulu ayenera kuyesetsa kukwaniritsa bwino maudindo awiri ati?

13 Akulu ayenera kuyesetsa kwambiri kuti akwaniritse bwino udindo wawo woweta nkhosa komanso wosamalira banja lawo. (1 Tim. 5:8) Nthawi imene akulu amagwiritsa ntchito posamalira mpingo ndi nthawi yamtengo wapatali imene akanatha kukhala ndi banja lawo. Njira ina imene ingawathandize kukwaniritsa maudindo onsewo ndiyo kuitana anthu ena kuti adzakhale nawo pa Kulambira kwa Pabanja. Kwa zaka zambiri, mkulu wina wa ku Japan dzina lake Masanao ankaitana anthu amene sali pa banja kapena mabanja amene bambo awo si Mboni kuti adzachite nawo phunziro la banja. Patapita nthawi, anthu ena amene Masanao anawathandiza anakhala akulu ndipo anatengera chitsanzo chake chabwino.

Wetani Nkhosa ndi Mtima Wonse Osati Mofuna Kupindulapo Kenakake

14, 15. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kupewa kuweta nkhosa chifukwa “chofuna kupindulapo kenakake,” ndipo kodi angatsanzire bwanji Paulo pa nkhani imeneyi?

14 Petulo analimbikitsanso akulu kuweta gulu la nkhosa “osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” Ntchito ya akulu imafuna nthawi yambiri koma sayembekezera kuti anthu awalipire. Petulo anaona kuti m’pofunika kuchenjeza akulu anzake kuopsa koweta gulu la nkhosa chifukwa “chofuna kupindulapo kenakake.” Tingaone kuopsa kwake tikaganizira za atsogoleri achipembedzo a mu “Babulo Wamkulu” amene amakhala ndi chuma chambiri pomwe anthu awo ali pa umphawi wadzaoneni. (Chiv. 18:2, 3) Masiku ano, akulu ayenera kukhala osamala kwambiri kuti asayambe mtima umenewu.

15 Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu achikhristu. Ngakhale kuti iye anali mtumwi ndipo akanatha kuchititsa Akhristu a ku Tesalonika kuti ‘azimulipirira kanthu kalikonse,’ iye ‘sankadya chakudya cha wina aliyense kwaulere.’ M’malomwake ‘ankagwira ntchito mwakhama ndi thukuta lake usiku ndi usana.’ (2 Ates. 3:8) Masiku anonso, akulu ambiri komanso oyang’anira oyendayenda amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Ngakhale kuti amalola kucherezedwa ndi Akhristu anzawo, iwo sawachititsa kuti ‘aziwalipirira kanthu kalikonse.’​—1 Ates. 2:9.

16. Kodi kuweta gulu la nkhosa “ndi mtima wonse” kumatanthauza chiyani?

16 Akulu amaweta gulu la nkhosa “ndi mtima wonse.” Zimenezi zimaonekera akamadzipereka kwambiri pothandiza gulu la nkhosa. Koma izi sizikutanthauza kuti iwo amakakamiza nkhosa kutumikira Yehova kapena kuti amalimbikitsa anthu kutumikira Mulungu mwampikisano. (Agal. 5:26) Akulu amadziwa kuti nkhosa iliyonse ndi yosiyana ndi inzake. Iwo amayesetsa ndi mtima wonse kuthandiza abale awo kutumikira Yehova mosangalala.

Osati Mochita Ufumu pa Gulu la Nkhosa Koma Mukhale Zitsanzo

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani atumwi nthawi zina ankavutika kumvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa zokhudza kudzichepetsa? (b) Kodi ndi mtima uti umene ifenso tiyenera kupewa?

17 Monga tanena kale, akulu ayenera kukumbukira kuti nkhosa zimene akuweta si zawo koma ndi za Mulungu. Iwo amayesetsa kuti ‘asamachite ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu.’ (Werengani 1 Petulo 5:3.) Nthawi zina, atumwi a Yesu ankafunitsitsa udindo koma ali ndi zolinga zolakwika. Mofanana ndi anthu amene ankalamulira anthu a mitundu ina, iwo ankafuna malo apamwamba.​—Werengani Maliko 10:42-45.

18 Abale amene ‘akuyesetsa kuti akhale oyang’anira’ ayenera kuganizira bwino chifukwa chimene akufunira udindowo. (1 Tim. 3:1) Masiku anonso, akulu ayenera kudzifufuza moona mtima kuti aone ngati ali ndi mtima wofuna ulamuliro kapena malo apamwamba umene atumwi ena anali nawo. Ngati atumwi anali ndi vuto limeneli, kuli bwanji akulu masiku ano? Iwo angaone kuti ayenera kuyesetsa kupewa mtima umene wafala m’dzikoli wofuna kulamulira ena.

19. Kodi akulu azikumbukira chiyani akamateteza gulu la nkhosa?

19 N’zoona kuti nthawi zina akulu ayenera kuchita zinthu mwamphamvu. Mwachitsanzo, ayenera kuchita zimenezi poteteza gulu la nkhosa ku “mimbulu yopondereza.” (Mac. 20:28-30) Paulo anauza Tito kuti ‘azilimbikitsa ndi kudzudzula anthu mogwirizana ndi ulamuliro wonse umene wapatsidwa.’ (Tito 2:15) Koma ngakhale pamene akuchita zimenezi, akulu ayenera kuyesetsa kulemekeza anthu amene akuwathandiza. Akulu amadziwa kuti njira imene ingafike munthu pamtima kuti ayambe kuchita zoyenera si kumukalipira koma kumulimbikitsa mokoma mtima.

20. Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yopereka chitsanzo?

20 Chitsanzo chabwino cha Khristu chimalimbikitsa akulu kukonda gulu la nkhosa. (Yoh. 13:12-15) Timalimbikitsidwa kwambiri tikamawerenga mmene Yesu ankaphunzitsira ophunzira ake ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Kudzichepetsa kwake kunalimbikitsa kwambiri ophunzira ake kuti nawonso azichita zinthu ‘modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala owaposa.’ (Afil. 2:3) Masiku anonso, akulu amafunitsitsa kutsatira chitsanzo cha Yesu komanso kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”

21. Kodi akulu akuyembekezera mphoto iti?

21 Pomaliza malangizo ake opita kwa akulu, Petulo ananena za lonjezo lokhudza zam’tsogolo. (Werengani 1 Petulo 5:4.) Akulu odzozedwa adzalandira “mphoto yosafwifwa, yaulemerero” limodzi ndi Khristu kumwamba. Abusa aang’ono a m’gulu la “nkhosa zina” adzakhala ndi mwayi woweta nkhosa za Mulungu padziko lapansi motsogoleredwa ndi “m’busa wamkulu.” (Yoh. 10:16) M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene anthu mu mpingo angathandizire akulu amene aikidwa kuti azitsogolera.

Tibwereze

• N’chifukwa chiyani zinali zofunika kuti Petulo alangize akulu anzake kuweta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe linali m’manja mwawo?

• Kodi akulu ayenera kuweta bwanji anthu amene akudwala mwauzimu?

• N’chiyani chimalimbikitsa akulu kuweta gulu la nkhosa za Mulungu limene lili m’manja mwawo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Mofanana ndi abusa akale, akulu a masiku ano ayenera kuteteza “nkhosa” zimene zili m’manja mwawo