Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu a Yehova Awina Milandu Imene Yatenga Nthawi Yaitali

Anthu a Yehova Awina Milandu Imene Yatenga Nthawi Yaitali

Anthu a Yehova Awina Milandu Imene Yatenga Nthawi Yaitali

M’CHAKA cha 1995, anthu a Yehova ku Russia anayamba kuimbidwa milandu imene yatenga zaka 15. Pa zaka zonsezi, Akhristu oona amenewa akhala akutsutsidwa ndi anthu odana ndi ufulu wa chipembedzo. Cholinga cha anthu otsutsawo chinali chakuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chitsekedwe ku Moscow ndiponso kumadera ena a ku Russia. Koma Yehova wathandiza abale ndi alongo okhulupirika a ku Russia amenewa kuti awine milanduyi. Kodi milandu imeneyi inayamba bwanji?

ANAPATSIDWANSO UFULU WOLAMBIRA

M’chaka cha 1917, abale a ku Russia analandidwa ufulu wolambira koma chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990 anapatsidwanso ufuluwu. M’chaka cha 1991, boma la Soviet Union linavomereza chipembedzo cha Mboni za Yehova. Boma la Soviet Union litatha, nalonso boma latsopano la Russia linavomereza chipembedzo cha Mboni za Yehova. Boma latsopanoli linavomerezanso kuti boma lakalelo linazunza Mboni za Yehova. M’chaka cha 1993, Dipatimenti Yoona za Chilungamo ku Moscow inavomerezanso kuti Mboni za Yehova zikhale bungwe lovomerezeka. M’chaka chomwechi boma la Russia linapanga malamulo atsopano ndipo ena mwa malamulowo amateteza ufulu wolambira. M’bale wina ananena mosangalala kwambiri kuti, “Sitinkadziwa kuti tilandira ufulu umenewu.” Iye ananenanso kuti, “Takhala tikuyembekezera zimenezi kwa zaka 50.”

Abale ndi alongo a ku Russia anagwiritsa ntchito mwanzeru “nthawi yabwino” imeneyi. (2 Tim. 4:2) Iwo anawonjezera kwambiri ntchito yawo yolalikira ndipo anthu ambiri ankamvetsera. Munthu wina ananena kuti, “Anthu ambiri ankachita chidwi ndi nkhani zachipembedzo.” Pasanapite nthawi yaitali, chiwerengero cha ofalitsa, apainiya ndiponso mipingo chinawonjezeka. Kuchokera mu 1990 kufika mu 1995, chiwerengero cha Mboni ku Moscow chinakwera kuchoka pa 300 kufika 5,000. Chiwerengero cha Mboni za Yehova chitayamba kuwonjezeka ku Moscow, anthu odana ndi ufulu wa chipembedzo anayamba kuchita mantha. Kenako iwo anayamba kutsutsa ndiponso kusumira Mboni za Yehova kukhoti. Milandu imene inayamba nthawi imeneyi inatenga nthawi yaitali kwambiri.

ANAYAMBA KUFUFUZA UMBONI WA MILANDU

Milanduyi inayamba mu June chaka cha 1995. Gulu lina la ku Moscow, lomwe limagwirizana ndi Tchalitchi cha Orthodox ku Russia, linakasumira abale athu mlandu wophwanya malamulo. Gululi linanena kuti likuimira anthu amene sankasangalala kuti amuna awo, akazi awo kapena ana awo ndi Mboni. Mu June 1996, anthu anayamba kufufuza umboni wa mlanduwu koma sanaupeze. Koma gululi linakasumiranso abale mlandu wina wophwanya malamulo. Anthu anafufuzanso mlandu umenewu koma sanapezenso umboni. Gululi linasumanso kachitatu mlandu womwewu. Mboni za Yehova za ku Moscow zinafufuzidwanso koma panalibenso umboni woti ayambe kuwazenga mlandu. Kenako gululi linasumanso kachinayi koma wofufuza sanapezenso umboni. N’zodabwitsa kuti gulu lomweli linapempha kuti afufuzenso. Ndiyeno pa April 13, 1998, munthu amene anafufuzanso mlanduwu, anautseka.

Loya wina anati, “Koma kenako, chinthu china chodabwitsa chinachitika.” Munthu wina woimira loya wa osuma mlandu, amene anafufuza mlanduwu ulendo wachisanu, ananena kuti palibe umboni woti Mboni za Yehova zimaphwanya malamulo. Koma kenako analangiza gulu losuma mlanduwu kuti lisumire abalewo mlandu wowaphera anthu ufulu wawo. Loya wa dera la kumpoto kwa Moscow anagwirizana nazo n’kukasuma mlanduwu. * Pa September 29, 1998, mlandu unayamba kuzengedwa kukhoti la kudera la Golovinsky ku Moscow.

ANAGWIRITSA NTCHITO BAIBULO M’KHOTI

M’kachipinda ka khoti la kumpoto kwa Moscow, loya wa osuma mlandu dzina lake Tatyana Kondratyeva anayamba kutsutsa Mboni za Yehova. Iye anagwiritsa ntchito lamulo limene linasainidwa mu 1997 lonena kuti zipembedzo zenizeni za ku Russia ndi za Orthodox, Chikhristu, Chisilamu, Chiyuda ndiponso Chibuda. * Lamulo limeneli lachititsa kuti zipembedzo zina zisavomerezedwe ndi boma. Makhoti amagwiritsanso ntchito lamuloli kuti atseke zipembedzo zimene zikulimbikitsa chidani. Pogwiritsa ntchito lamulo limeneli, loyayu ananena kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chimayambitsa chidani ndiponso kusokoneza mabanja choncho chiyenera kutsekedwa.

Loya wina woimira abale athu anafunsa kuti: “Kodi ndi ndani mu Mpingo wa Moscow amene waphwanya lamulo?” Loya wa osumawo sanatchule dzina lililonse. Koma ananena kuti mabuku a Mboni za Yehova amachititsa anthu kudana ndi anthu a zipembedzo zina. Pofuna kutsimikizira mfundoyi, iye anawerenga mu Nsanja ya Olonda, Galamukani! ndiponso m’mabuku ena (onani zithunzi pamwambapa). Atafunsidwa kuti afotokoze mmene mabukuwa amayambitsira chidani, iye anati: “Mboni za Yehova zimaphunzitsa kuti chipembedzo chawo n’choona.”

Loya wina, yemwe ndi m’bale, anapereka Baibulo kwa woweruza ndiponso kwa loya wa osumawo n’kuwerenga mawu a pa Aefeso 4:5 akuti: “Palinso Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.” Kenako woweruza, loya wa osumawo ndiponso loya wa abale athu anakambirana malemba ngati Yohane 17:18 ndi Yakobo 1:27. Woweruza anafunsa kuti: “Kodi malembawa amachititsa anthu kudana ndi anthu a zipembedzo zina?” Loya wa osumawo ananena kuti sangayankhe chifukwa si katswiri wa Baibulo. Loya wa abalewa anasonyeza mabuku a Tchalitchi cha Orthodox ku Russia amene amatsutsa kwambiri Mboni za Yehova n’kufunsa kuti: “Kodi mawu a m’mabukuwa akuphwanya lamulo?” Loya wa osumawo ananena kuti sangayankhe chifukwa si katswiri pa nkhani zachipembedzo.

MILANDU YOPANDA UMBONI

Potsutsa Mboni kuti zimasokoneza mabanja, loya wa osumawo ananena kuti Mboni sizikondwerera maholide monga Khirisimasi. Koma kenako anavomereza kuti malamulo a dziko la Russia sanena kuti anthu azikondwerera Khirisimasi. Anthu onse a ku Russia, kuphatikizapo Mboni za Yehova, ali ndi ufulu wosankha kukondwerera Khirisimasi kapena ayi. Ananenanso kuti gulu la Mboni za Yehova ‘limaletsa ana awo kupuma mokwanira ndiponso kusangalala.’ Koma atafunsidwa, ananena kuti sanalankhulepo ndi mwana aliyense woleredwa ndi Mboni za Yehova. Pamene loya wina anamufunsa ngati iye anapezekapo pa misonkhano ya Mboni za Yehova, iye anayankha kuti: “Palibe chifukwa chopitira.”

Loya wa osumawo anapempha pulofesa wa maphunziro a matenda a maganizo kuti apereke umboni. Pulofesayu ananena kuti kuwerenga mabuku a Mboni za Yehova kumayambitsa matenda a maganizo. Loya wina wa abalewo ananena kuti zimene pulofesayu analemba n’kupereka kukhotili zikufanana ndi zimene zinalembedwa ndi atsogoleri a Tchalitchi cha Orthodox ku Moscow. Pulofesayu anavomereza kuti mbali zina zinkafananadi ndendende chifukwa iye anangokopera. Atamufunsa mafunso ena, iye anaulula kuti sanathandizepo wa Mboni za Yehova wodwala matendawa. Koma pulofesa wina wa maphunziro a matenda a maganizo anapereka umboni m’khotili woti anachita kafukufuku ndi Mboni zoposa 100 ku Moscow. Iye anapeza kuti onsewa anali ndi maganizo abwinobwino ndipo anati iwo atakhala Mboni anayamba kukonda kwambiri anthu a zipembedzo zina.

ANAWINA KOMA NKHANI SINATHERE POMWEPO

Pa March 12, 1999, woweruza anasankha anthu ophunzira asanu kuti awerenge mabuku a Mboni za Yehova ndipo anaimitsa kaye mlandu. Koma pa zifukwa zina, Unduna wa Zachilungamo wa boma la Russia unali utalamula kuti gulu lina la anthu ophunzira liwerenge mabuku athu. Pa April 15, 1999, gulu limeneli linanena kuti silinapeze vuto lililonse ndi mabuku a Mboni za Yehova. Choncho pa April 29, 1999, undunawu unavomerezanso chipembedzo cha Mboni za Yehova. Ngakhale kuti zimenezi zinachitika, khoti la ku Moscow linanenabe kuti gulu lina lionenso mabuku athu. Zinali zovuta kumvetsa. Unduna wa Zachilungamo unanena kuti Mboni za Yehova ndi chipembedzo chovomerezeka ndiponso chotsatira malamulo, koma pa nthawi yomweyo Dipatimenti Yoona za Chilungamo ku Moscow inkafufuza Mboni za Yehova pa mlandu wophwanya malamulo.

Pafupifupi zaka ziwiri zinadutsa chiimitsire mlanduwu. Pa February 23, 2001, woweruza dzina lake Yelena Prokhorycheva anapereka chigamulo. Ataona zimene gulu limene analisankha kuti liwerenge mabuku athu lija linapeza, ananena kuti: “Palibe chifukwa choletsera ntchito ya Mboni za Yehova ku Moscow.” Ndiyeno, abale athu anapezeka kuti alibe mlandu uliwonse. Koma loya wa osumawo anakana chigamulochi n’kuchita apilo kukhoti lina la mumzinda wa Moscow. Choncho pa May 30, 2001, khotili linafafaniza chigamulo cha woweruza wa khoti loyambalo. Khotili linalamula kuti mlanduwu uzengedwenso ndi woweruza wina koma osuma mlanduwo asasinthe loya wawo.

ANAPEZEKA NDI MLANDU KOMA NKHANI SINATHERENSO POMWEPO

Pa October 30, 2001, woweruza wina dzina lake Vera Dubinskaya anayamba kuzenganso mlandu. * Loya wa osumawo ananenanso kuti Mboni za Yehova zimayambitsa chidani ndipo anawonjezera kuti kutseka chipembedzo cha Mboni za Yehova kudzathandiza kuteteza ufulu wa Mboni ku Moscow. Poyankha zimenezi, Mboni za ku Moscow 10,000 zinasaina chikalata chopempha khoti kuti likane zimene loyayu ananena.

Loyayu ananena kuti palibe chifukwa choti aperekere umboni wakuti Mboni za Yehova ndi zolakwa. Iye ananena kuti mlanduwu ndi wokhudza mabuku ndi zikhulupiriro za Mboni za Yehova osati ntchito zawo. Ndiyeno ananena kuti apempha munthu woimira Tchalitchi cha Orthodox ku Russia kuti apereke umboni wabwino pa nkhaniyi. Izi zinatsimikizira kuti atsogoleri a chipembedzo ndi amene ankafuna kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chitsekedwe. Pa May 22, 2003, woweruza analamula gulu linanso la akatswiri kuti liwerenge mabuku a Mboni za Yehova.

Pa February 17, 2004, anayambiranso kuzenga mlandu kuti aone zimene gululi linapeza. Gululi linapeza kuti mabuku athu amalimbikitsa anthu kuti asamathetse mabanja ndipo umboni wakuti mabuku athu amayambitsa chidani sunapezeke. Akatswiri ena anavomerezanso zimenezi. Pulofesa wa mbiri ya zipembedzo anafunsidwa kuti: “N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimalalikira?” Iye anauza khotili kuti: “Mkhristu aliyense ayenera kugwira ntchito yolalikira. Izi n’zimene Uthenga Wabwino umanena ndipo Khristu analamula ophunzira ake kuti: ‘Pitani kukalalikira m’mayiko onse.’” Ngakhale zinali choncho, pa March 26, 2004, woweruza analetsa ntchito za Mboni za Yehova ku Moscow. Pa June 16, 2004, khotili linagwirizana ndi chigamulochi. * Pofotokoza maganizo ake pa chigamulochi, m’bale wina, yemwe wakhala m’choonadi nthawi yaitali, ananena kuti: “Mu ulamuliro wa Soviet Union, anthu a ku Russia ankafunika kukhala osakhulupirira Mulungu. Masiku ano, anthu a ku Russia amafunika kukhala a Orthodox.”

Kodi abale anatani? Anachita zofanana ndi Nehemiya. M’masiku a Nehemiya, adani a anthu a Mulungu ankafuna kulepheretsa ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Koma Nehemiya ndi anthu ake sanalole kuti zimenezi zisokoneze ntchito yawo. M’malomwake, ‘anapitiriza kumanga’ ndiponso “anapitiriza kukhala ndi mtima wogwira ntchito.” (Neh. 4:1-6) Nawonso abale athu ku Moscow sanalole kuti otsutsa awasokoneze pa ntchito yolalikira uthenga wabwino imene ikufunika kugwiridwa masiku ano. (1 Pet. 4:12, 16) Iwo sankakayikira kuti Yehova awathandiza ndipo anali okonzeka kupitiriza kulimbana ndi anthuwo kukhoti.

ANAYAMBA KUZUNZIDWA KWAMBIRI

Pa August 25, 2004, abale athu analemba chikalata n’kupereka kwa Vladimir Putin, yemwe pa nthawiyo anali pulezidenti wa Russia. Chikalatachi chinafotokoza mmene Mboni za Yehova zinamvera ntchito yawo italetsedwa. Anthu okwana 315,000 anasaina chikalatachi moti chinali cha mapepala ambiri mpaka kukwana mabuku 76. Pa nthawi yomweyo, atsogoleri a Tchalitchi cha Orthodox ku Russia anasonyeza zimene zinali mumtima mwawo. Munthu wina woimira atsogoleriwa anati: “Timadana kwambiri ndi ntchito za Mboni za Yehova.” Mtsogoleri wina wachisilamu anasangalala ndi chigamulo choletsa ntchito ya Mboni za Yehova ndipo ananena kuti chinali chabwino kwambiri.

Anthu ena ku Russia okhulupirira milandu yabodzayo anayamba kuzunza Mboni za Yehova. Mboni zina zimene zinkalalikira ku Moscow zinkamenyedwa zibakera ndi mateche. Munthu wina atapsa mtima anathamangitsa mlongo wina m’nyumba ina ndipo anamumenya theche kumsana moti mlongoyu anagwa n’kuvulala mutu. Iye anafunika thandizo la kuchipatala koma apolisi sanachite chilichonse kwa womenyayo. Mboni zina zinagwidwa ndi apolisi, kutengedwa zidindo za zala, kujambulidwa ndiponso kutsekeredwa tsiku limodzi. Oyang’anira maholo a ku Moscow anaopsezedwa kuti achotsedwa ntchito akapitiriza kulola Mboni kuti zizichita misonkhano m’maholo awo. Pasanapite nthawi, mipingo yambiri inkakanizidwa kuchita lendi malo oti izisonkhanamo. Mipingo ina 40 inayenera kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi yokhala ndi maholo anayi. Mpingo wina unkayamba Msonkhano wa Onse 7:30 m’mawa. Woyang’anira woyendayenda wina ananena kuti, “Ofalitsa ankafunika kudzuka 5 koloko m’mawa kuti akapezeke pa misonkhano koma anachita zimenezi mosanyinyirika kwa nthawi yoposa chaka.”

“UKHALE UMBONI”

Pofuna kusonyeza kuti chigamulo choletsa ntchito ya Mboni za Yehova ku Moscow chinali chosemphana ndi malamulo, maloya athu anapempha thandizo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Anachita zimenezi mu December 2004. (Onani bokosi lakuti “N’chifukwa Chiyani Chigamulo cha ku Russia Chinaunikidwanso ku France?” pa tsamba 6.) Patapita zaka 6, pa June 10, 2010, khotili linanena kuti Mboni za Yehova sizinalakwe chilichonse. * Khotili linaunika milandu yonse n’kuona kuti inali yopanda umboni. Linanenanso kuti dziko la Russia liyenera kuchotsa chigamulo choletsa ntchito ya Mboni za Yehova ndiponso kukonzanso mavuto amene Mboni za Yehova zakumana nawo chifukwa cha chigamulochi.​—Onani bokosi lakuti “Chigamulo cha Khoti,” patsamba 8.

Zimene khotili linanena pa nkhani ya mmene Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya limatetezera ntchito ya Mboni za Yehova ziyenera kutsatiridwa ku Russia ndiponso mayiko ena 46 amene ali mu Mgwirizano wa Mayiko a ku Ulaya. Oweruza, opanga malamulo ndiponso anthu ena padziko lonse amene amaphunzira za ufulu wa anthu adzachitanso chidwi ndi chigamulochi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti pamene oweruza a khotili ankagamula, anagwiritsa ntchito zigamulo zina 8 zokomera Mboni za Yehova zimene khotili linapereka m’mbuyomu. Linagwiritsanso ntchito milandu 9 imene Mboni za Yehova zinawina m’makhoti akuluakulu a ku Argentina, Canada, Japan, Russia, South Africa, Spain, United Kingdom ndi ku United States. Mboni za Yehova padziko lonse tsopano zingagwiritse ntchito zimene khotili linagamula kuti ziteteze ufulu wawo wolambira.

Yesu anauza otsatira ake kuti: “Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.” (Mat. 10:18) Milandu imene inazengedwa ku Russia pa zaka 15 zimenezi yathandiza kuti abale athu akhale ndi mwayi wolengeza kwambiri dzina la Yehova ku Moscow ndiponso kumadera ena. Zonse zimene zinachitika pa nthawi ya milandu imeneyi zathandiza kupereka “umboni” ndiponso “kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” (Afil. 1:12) Nthawi zambiri Mboni zikamalalikira ku Moscow masiku ano, eninyumba amafunsa kuti, “Kodi ndimayesa kuti anakuletsani anthu inu?” Funso limeneli limapereka mwayi kwa abale kuti afotokozere eninyumbawo zikhulupiriro zathu. Zimenezi zikusonyezeratu kuti palibe chimene chingaimitse ntchito yathu yolalikira za Ufumu. Timapemphera kuti Yehova apitirize kudalitsa ndiponso kusamalira abale ndi alongo athu olimba mtima ku Russia, omwe timawakonda kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Anakasuma mlanduwu pa April 20, 1998. Patapita milungu iwiri, pa May 5, dziko la Russia linalowa nawo m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

^ ndime 10 Nyuzipepala ina inati: “Lamuloli linakhazikitsidwa pomvera zimene a Tchalitchi cha Orthodox ku Russia ananena. Iwo ankafuna kukhalabe chipembedzo chachikulu ku Russia choncho ankafuna kwambiri kuti boma litseke chipembedzo cha Mboni za Yehova.”​—Associated Press, June 25, 1999.

^ ndime 20 N’zochititsa chidwi kuti pa tsiku limene izi zinachitika panali patatha zaka 10 kuchokera pa tsiku limene dziko la Russia linavomereza kuti Mboni za Yehova zinazunzidwa mu ulamuliro wa Soviet Union.

^ ndime 22 Izi zinatanthauza kuti Mboni za Yehova sizikhalanso bungwe lovomerezeka ku Moscow. Otsutsawo ankaganiza kuti zimenezi zilepheretsa abale athu kugwira ntchito yawo yolalikira.

^ ndime 28 Pa November 22, 2010, oweruza 5 omwe ndi akuluakulu a khotili anakana pempho la boma la Russia lakuti iwo aweruzenso mlanduwu. Izi zinachititsa kuti chigamulo chimene chinaperekedwa pa June 10, 2010, chikhale chomaliza ndiponso chitsatiridwe.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

N’chifukwa Chiyani Chigamulo cha ku Russia Chinaunikidwanso ku France?

Pa February 28, 1996, dziko la Russia linasainira Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. (Pa May 5, 1998, dziko la Russia linavomerezeratu panganoli.) Posaina pangano limeneli, dzikoli linavomereza kuti nzika zake zili ndi ufulu wochita zotsatirazi:

‘Ufulu wopembedza ndiponso kulambira kunyumba kwawo kapena pagulu komanso kusintha chipembedzo ngati akufuna.’​—Gawo 9.

‘Ufulu wonena kapena kulemba mwaulemu zimene akuganiza ndiponso kuuza anthu ena mfundo zawo.’​—Gawo 10.

‘Ufulu wosonkhana mwamtendere.’​—Gawo 11.

Anthu kapena mabungwe amene aphwanyiridwa ufulu wa m’panganoli, ndiponso amene sanathandizidwe kumakhoti a kwawo, ayenera kukasuma ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Khoti limeneli lili mumzinda wa Strasbourg ku France. (Onani chithunzi pamwambapa.) M’khotili muli oweruza 47 ndipo chiwerengero chimenechi ndi chofanana ndi cha mayiko amene anasainira Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Zigamulo za kukhoti limeneli ziyenera kutsatiridwa ndi mayiko onse amene anasainira panganoli.

[Bokosi patsamba 8]

Chigamulo cha Khoti

M’munsimu talemba mwachidule mfundo zitatu za m’chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Mlandu wina unali wakuti Mboni za Yehova zimasokoneza mabanja. Khotili linakana zimenezi. Linati:

“Mabanja amasokonekera chifukwa chakuti achibale omwe sali m’chipembedzo safuna kuvomereza ndiponso kulemekeza ufulu wopembedza womwe wachibale wawo ali nawo.”​—Ndime 111.

Khotili silinapezenso umboni wakuti Mboni za Yehova zimaphera anthu ufulu wosankha okha zochita. Linanena kuti:

“Khotili laona kuti n’zodabwitsa kuti makhoti [a ku Russia] sanatchule ngakhale dzina limodzi la munthu amene anaphwanyiridwa ufulu wotsatira chikumbumtima chake.”​—Ndime 129.

Mlandu wina unali wakuti Mboni za Yehova zimachititsa kuti anthu asakhale ndi thanzi labwino chifukwa chakuti zimakana kuikidwa magazi. Khotili linatsutsa zimenezi ponena kuti:

“Munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha zochita. Choncho ayenera kukhalanso ndi ufulu wovomera kapena kukana chithandizo cha kuchipatala, kapenanso kusankha chithandizo china cha mankhwala. Munthu aliyense wamkulu amene angathe kusankha bwino angalole kapena kukana zinthu monga opaleshoni kapena chithandizo china, ngakhale kuikidwa magazi.”​—Ndime 136.